Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 12/8 tsamba 16-17
  • Kodi Mafumu Atatu Anakaona Yesu ku Betelehemu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mafumu Atatu Anakaona Yesu ku Betelehemu?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anali Mafumu?
  • Kodi Analipo Atatu?
  • Chikhulupiriro Chofala Koma Chosalondola
  • Kubadwa Kwake N’koyenera Kukukumbukira
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • A Magi Atatu Chenicheni Kapena Nthano?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi “Anzeru a Kum’mawa” Anali Ndani? Kodi Mulungu Ndi Amene Anawachititsa Kuti Alondole Nyenyezi ya ku Betelehemu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 12/8 tsamba 16-17

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mafumu Atatu Anakaona Yesu ku Betelehemu?

YESU atabadwa, anthu otchuka ochokera Kummaŵa anafika ku Betelehemu kudzapereka ulemu kwa iye monga mfumu ya Ayuda. Kuchokera panthaŵiyo mpaka lero anthu ambiri amene amakondwerera Khirisimasi padziko lonse amakumbukira ulendo umenewo.

M’mayiko ena anthu amamanga malo ofanizira kubadwa kwa Yesu amene amaonetsa alendo a kummaŵa ameneŵa monga mafumu atatu akuyandikira kwa Yesu wakhandayo ndi mphatso. M’mayiko ena, ana amaguba kuzungulira kumene amakhala, atavala zovala za “Mfumu Zoyera.” Ngakhale papita zaka mazana 20, anthu kulikonse akupitirizabe kukumbukira alendo osadziŵika amenewo. Kodi kwenikweni iwo anali ayani?

Kodi Anali Mafumu?

Nkhani ya m’mbiri yonena za chochitika chimenechi ili m’buku la Baibulo la Mateyu. M’menemo timaŵerenga kuti: “Yesu atabadwa . . . Openda nyenyezi a kummaŵa anafika tsiku lina ku Yerusalemu, nafunsa kuti, “Ili kuti Mfumu ya Ayuda yabadwa tsopanoyo? Tinaona nyenyezi yake kumatulukiro kwake, ndipo tadzera kudzam’lemekeza.” (Mateyu 2:1, 2, New American Bible) N’chifukwa chiyani Baibulo limeneli likutcha alendo a kummaŵa ameneŵa kuti openda nyenyezi osati mafumu?

Malemba panopa akugwiritsa ntchito liwu lochulukitsa la Chigiriki lakuti maʹgos. Mabaibulo ambiri amawatchula kuti “Anzeru a kummaŵa,” “openda nyenyezi,” kapena “oyang’anitsitsa nyenyezi” kapenanso amangolemba m’Chigiriki kuti “Amagi.” Liwu limeneli limatanthauza anthu amene amapereka umboni ndiponso maulosi pogwiritsa ntchito malo amene nyenyezi kapena mapulaneti ali. Motero Baibulo limatcha alendo aku Betelehemu ameneŵa kukhala oombeza ula, amene ankachita zamizimu zoletsedwa ndi Mulungu.—Deuteronomo 18:10-12.

Kodi analinso mafumu? Ngati anali mafumu, ndiye kuti mwachionekere Baibulo likanawatcha choncho. Mateyu 2:1-12 amagwiritsa ntchito liwu lakuti “mfumu” nthaŵi zokwana zinayi, kamodzi kutanthauza Yesu ndipo katatu kutanthauza Herode. Koma palibe n’kamodzi komwe pamene limatchula Amagi kukhala mafumu. Pamfundoyi The Catholic Encyclopedia imati: “Palibe Bambo wa Tchalitchi [wolemba mbiri zachikristu wakale] amene amakhulupirira kuti Amagi anali mafumu.” Ndipo ngakhale Baibulo silitero.

Kodi Analipo Atatu?

Nkhani ya m’Baibulo siitchula chiŵerengero cha Amagi. Komabe, zithunzi zosonyeza kubadwa kwa Yesu ndiponso nyimbo za pa Khirisimasi zimagwirizana ndi chiphunzitso chofala chakuti analipo atatu. Mwachionekere, zimenezi zikuchokera pa mfundo yakuti panali mphatso za mitundu itatu. Ponena za mphatsozo, Baibulo limati: “Namasula chuma chawo nampatsa iye [Yesu] mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.”—Mateyu 2:11.

Kodi n’koyenera kuganiza kuti poti Amagi anapereka mphatso za mitundu itatu, ndiye kuti analipo Amagi atatu? Tiyeni tione nkhani ina yonena za mlendo winanso wotchuka ku Israyeli. Mfumukazi ya ku Seba nthaŵi ina inakacheza kwa Mfumu Solomo ndipo inapereka kwa iye “zonunkhira, ndi golidi wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali.” (1 Mafumu 10:2) Ngakhale kuti panali mitundu itatu ya mphatso, munthu yekhayo amene akutchulidwa kuti anapereka zimenezi ndi mfumukazi ya ku Seba. Chiŵerengero cha mphatso zake sichikusonyeza kuti anthu atatu anakaona Solomo panthaŵiyo. Mofananamo, mphatso zitatu zoperekedwa kwa Yesu sizikugwirizana m’pang’ono pomwe ndi chiŵerengero cha anthu amene anabweretsa mphatsozo.

The Catholic Encyclopedia imati: “Wolemba Uthenga Wabwino sanatchulepo chiŵerengero cha Amagi ndipo palibe nkhani iliyonse yotsimikizira chiŵerengerochi. Abambo ena anatchulapo za Amagi atatu; abambo otereŵa ayenera kuti anasonkhezeredwa ndi chiŵerengero cha mphatsozo.” Imapitiriza kuti zithunzi zosiyanasiyana zimasonyeza anthu aŵiri, atatu, anayi, ndipo ngakhale asanu ndi atatu, akuona Yesu. Nkhani zina zimati analipo 12. Palibe njira yotsimikizira za chiŵerengero cha Amagi amenewo.

Chikhulupiriro Chofala Koma Chosalondola

Mosiyana ndi chikhulupiriro chofala, Amagi anayamba kufika ku Yerusalemu osati ku Betelehemu Yesu atabadwa kale. Iwo kunalibe pa nthaŵi yomwe Yesu ankabadwa. Kenako, pamene anapita ku Betelehemu, Baibulo limanena kuti, “pofika kunyumba anaona kamwanako.” (Mateyu 2:1, 11) Choncho, n’zoonekeratu kuti pa nthaŵi imene Amagi anakaona Yesu, n’kuti banja lake litasamukira m’nyumba yeniyeni. Iwo sanam’peze ali gone modyera nyama.

Malinga ndi lingaliro la Malemba, chikhulupiriro chofala chonena za mafumu atatu akulemekeza Yesu pa nthaŵi yake ya kubadwa sicholondola konse. Monga tanenera pamwambapa, Baibulo limaphunzitsa kuti Amagi amene anakaona Yesu sanali mafumu koma openda nyenyezi amene ankachita zamizimu. Nkhani ya m’Malemba siitchula chiŵerengero chawo. Komanso iwo sanakaone Yesu panthaŵi ya kubadwa kwake, koma kuti inali nthaŵi ina, pamene banja lake linali kukhala m’nyumba.

Nkhani yotchuka yonena za mafumu atatu komanso zikhulupiriro zina za nkhani za pa Khirisimasi, ngakhale sizolondola mwa Malemba, nthaŵi zambiri zimaoneka kukhala nthano za pa holide zabwino. Komabe, Akristu amaona kulambira kopanda chinyengo kukhala kwa mtengo wapatali. Ndi m’menenso Yesu mwiniyo anamvera. M’pemphero kwa Atate wake, iye nthaŵi ina anati: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Ananenanso kuti “olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.”—Yohane 4:23.

[Chithunzi patsamba 17]

“Kulambira Amagi,”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena