Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g01 12/8 tsamba 20-25
  • Zachilengedwe Zimadalirana M’njira Zovuta Kuzimvetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zachilengedwe Zimadalirana M’njira Zovuta Kuzimvetsa
  • Galamukani!—2001
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupulula Zamoyo Zosiyanasiyana
  • Mliri wa Kutha kwa Zinthu
  • Kodi Mitundu Yosiyanasiyana Yonseyi N’njofunikadi kwa Ife?
  • Nyama Zokhala Pangozi Kukula—Kwa Vutolo
    Galamukani!—1996
  • Anthu Akupulula Zinthu Zachilengedwe
    Galamukani!—2001
  • Nyama za Kuthengo Zimene Zikuzimiririka Padziko Lapansi
    Galamukani!—1997
  • Chochititsa Nyama Kukhala Pangozi
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—2001
g01 12/8 tsamba 20-25

Zachilengedwe Zimadalirana M’njira Zovuta Kuzimvetsa

“Zinthu zachilengedwe zosiyanasiyana zimatisunga. Timadalira zinthu zachilengedwezi kuti tizikhala ndi moyo tsiku n’tsiku.”—Bungwe Loona Zachilengedwe La United Nations Environment Programme Linatero.

ZINTHU zamoyo padziko lapansi n’zochuluka ndipo n’zosiyanasiyana kwambiri. Mawu akuti “mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe” akusonyeza mitundu yonse ya zachilengedwe za padziko lonse, kungoyambira tizilombo tosaoneka ndi maso paokha, mitengo yaikulu kwadzaoneni, nyongolotsi mpaka ziwombankhanga zikuluzikulu.

Mitundu yosiyanasiyana yonseyi ya zinthu zachilengedwe za padziko lonse ngakhalenso zinthu zina zopanda moyo zimadalirana kwambiri. Zinthu zamoyo zimadalira zinthu zopanda moyo monga mpweya, nyanja zikuluzikulu, madzi abwino, matanthwe ndiponso dothi. Padzikoli anthu ndiwo amaposa zinthu zonse zamoyo ndiponso zopanda moyo.

Akati mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe amatanthauzanso mabakiteriya onse ndiponso tizilombo tina tonse tosaoneka ndi maso. Akuti tizilombo tambiri totere timathandiza kwambiri kuti zomera ndi zinyama zikhale ndi moyo. Komanso akati mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe amatanthauzanso zomera zobiriŵira zimene zikamawombedwa ndi dzuŵa zimatulutsa mpweya umene timapuma. Zomerazi zimagwiritsa ntchito mphamvu ya dzuŵa popanga madzi otsekemera ndipo zamoyo zina zikadya zomerazi zimakhuta n’kupeza mphamvu chifukwa cha madzi ameneŵa.

Kupulula Zamoyo Zosiyanasiyana

N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale kuti zachilengedwe n’zokongola ndiponso n’zosiyanasiyana, ofufuza ambiri akuti anthu akupulula mitundu ya zamoyozi modetsa nkhaŵa kwambiri. Kodi akuzipulula motani?

◼ Kuwononga malo amene zimakhala. Kuwononga malo ndiko kukupulula kwambiri zachilengedwe. Maloŵa amawonongeka podula mitengo n’cholinga chopeza matabwa, pokumba migodi, kudula mitengo pokonza malo odyetsera ng’ombe, kukumba madamu ndiponso kupanga misewu ikuluikulu m’madera amene munali nkhalango. Zachilengedwe zikayamba kuchepa m’dera linalake, mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo imayamba kusoŵa zinthu zimene zimafunika kuti ikhale ndi moyo. Zinthu zachilengedwe akuzilekanitsa ndi zinzake, kuzichepetsa ndiponso akuziwonongeratu. Njira zimene zachilengedwezi zimayendamo aziphwasula. Mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo ikutha. Zinthu zamoyo zokhala malo amodzi zikufa ndi matenda ndiponso zinthu zina zosautsa. Motero, mitunduyi ikutha pang’onopang’ono.

Mitundu inayake ya zamoyo ikatheratu inanso yambiri imayambanso kutha, chifukwa chakuti mitundu inayo imadalira imene yathayo. Kutha kwa mitundu ya zamoyo imene zachilengedwe zina zimadalira kwambiri, monga zamoyo zimene zimathandiza kuti mbewu zibereke, kungayambitsenso mitundu ina yambiri zedi kutha.

◼ Mitundu yobwerekera. Anthu akabweretsa mtundu wachilendo m’gulu linalake la zamoyo, mtunduwo ungathe kulanda malo a mitundu inayo. Mtundu wachilendowo ukhozanso kuwononga zachilengedwe zina m’njira inayake mpaka n’kulandiratu dera lonselo, kapena ukhoza kubweretsa matenda amene mtundu wa pamenepowo sungathe kulimbana nawo. Makamaka m’zisumbu, zimene mitundu ina ya zamoyo inayamba kalekale kukhalamo yokhayokha ndipo siinakhalepo ndi mitundu ina, mitunduyo ingathe kulephera kuzoloŵerana ndi mitundu yachilendoyo ndipo ingafe.

Chitsanzo chabwino kwambiri n’cha mtundu winawake wa ndere “zakupha” umene ukuwononga mitundu ina ya zamoyo za m’nyanja ya Mediterranean. Ndere zimenezi zinafika mwangozi pa gombe la Monaco ndipo tsopano zayamba kuyanga pansi pa nyanjayi. Zili ndi poizoni, ndipo palibe amene akudziŵa nyama iliyonse imene imadya nderezi. Katswiri wina wa sayansi ya zamoyo za m’nyanja, dzina lake Alexandre Meinesz, wa pa yunivesite ya Nice ku France ananena kuti, “Mwina uku n’kuyamba chabe kwa vuto lalikulu kwambiri lokhudza zinthu zachilengedwe.”

◼ Kuziwononga mopitirira muyeso. Zimenezi zachititsa kuti mitundu yambiri ya zinthu zamoyo iyambe kutha. Chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi ndi mtundu wa njiwa zinazake zimene zinatha kalekale. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800, mbalame zimenezi zinali zochuluka kuposa mbalame zina zilizonse ku North America. Njiwazi zinkati zikamauluka kupita kudera lina, zinkauluka m’magulu a njiwa zokwana biliyoni imodzi kapena kuposa, ndipo zikamauluka choncho, kunja kunkachita kam’dima kwa masiku angapo chifukwa cha kuchuluka. Komabe podzafika kumapeto kwa chaka cha 1800, anthu anali atazisaka n’kungotsala pang’ono kuzimaliza, ndipo mu September chaka cha 1914, njiwa imodzi yokha imene inatsalako inafa ili kumalo osungirako zinyama mumzinda wa Cincinnati. N’zimenenso zinachitikira njati za ku America zimene zinali kupezeka m’zidikha zotchedwa Great Plains. Njatizi anazisaka n’kungotsala pang’ono chabe kuti zitheretu.

◼ Kuchuluka kwa anthu. Cha m’ma 1850 anthu padziko lonse anali okwana biliyoni imodzi basi. Koma patangotha zaka 150, anthu awonjezeka n’kukwana mabiliyoni sikisi ndipo ayamba kuchita mantha kuti mwina amaliza zinthu zimene zimawathandiza. Chaka chilichonse anthu akuchuluka ndipo mitundu ya zinthu zachilengedwe zikutha modetsa nkhaŵa kwambiri.

◼ Vuto lodetsa nkhaŵa la kutentha kwa dziko. Malingana n’kunena kwa bungwe loona za kusintha kwa nyengo padziko lonse la Intergovernmental Panel on Climate Change, akuti n’zotheka kuti dziko litentha kwambiri m’zaka 100 zimene taziyambazi. Zikatere ndiye kuti mitundu ina ya zamoyo ingadzafe. Ofufuza akuti zikuoneka kuti kutentha kwa madzi ndiko kukuthetsanso madera enaake am’nyanja (amene zamoyo zosiyanasiyana zam’madzi zimakhala).

Asayansi amanena kuti madzi a m’nyanja zikuluzikulu akadzaza n’kuwonjezeka mtunda wokwana mita imodzi akhoza kuwononga mbali yaikulu ya magombe achinyontho a padziko lonse, amene amakhala ndi zamoyo zambiri zosiyanasiyana. Asayansi enanso amakhulupirira kuti kutentha kwa padziko lonse mwina kungawononge chilumba china chotchedwa Greenland, ndipo madzi oundana chifukwa cha kuzizira kwambiri amene ali kudera lotchedwa Antarctic angasungunuke. Ngati madziwo atasungunuka chifukwa cha kutentha, ndiye kuti zinthu zambiri zachilengedwe zingawonongeke kwambiri.

Mliri wa Kutha kwa Zinthu

Kodi mitundu ya zinthu zamoyo ikutha mofulumira bwanji? N’kovuta kuyankha funsoli bwinobwino. Asayansi sakudziŵabe zinthu zina zambiri zimene zayamba kutha. Choyamba ayenera kudziŵa kuchuluka kwa mitundu ya zamoyo zimene zilipo. Katswiri wa zinthu zachilengedwe wa pa yunivesite ya California ku Berkeley dzina lake John Harte ananena kuti, “padziko lapansi pali mitundu ya zamoyo zodziŵika mayina pafupifupi miliyoni imodzi ndi theka, koma tikudziŵa kuti palinso mitundu ina yambiri yosadziŵika ndipo mwina mitunduyi itha kukwana mpaka mamiliyoni asanu kapena khumi ndi asanu.” Akatswiri ena amati mitunduyi itha kuposa pamenepa mpaka kukwana mamiliyoni 50 kapena kuposa. N’zosatheka kutchula kuchuluka kwake kwenikweni chifukwa chakuti “zamoyo zambiri zitheratu anthu asanazitche n’komwe mayina kapena kuzilongosola mmene zilili,” anatero wasayansi wina dzina lake Anthony C. Janetos.

Asayansi amakono angoyamba kumene kumvetsa zinthu zovuta kumvetsa zimene zimapangitsa kuti zamoyo zizikhalabe bwinobwino ndi moyo m’malo awo achilengedwe. Ngati anthu sadziŵa kuchuluka kwa mitundu ya zinthu zamoyo, kodi angamvetse bwanji njira zosiyanasiyana zovuta kufotokoza za kudalirana kwa zinthu zachilengedwe, ndiponso mmene njirazi zimakhudzidwira zachilengedwe zikamatha? Ndipo kodi angadziŵe bwanji mavuto amene kutha kwa mitundu ya zamoyozi kungabweretse pa zinthu zothandizira kuti padziko lapansili pakhale moyo?

Asayansi akamafufuza kuchuluka kwa zachilengedwe zomwe zatheratu, zimene amapeza zimakhala zoziritsa nkhongono, ngakhale kuti zimasiyanasiyana. Wolemba wina anati, “Theka la nkhalango ndi nyama za padziko lonse zikhoza kutheratu m’zaka 100 zokha.” Harte ananena nkhani yofoolanso kwambiri ponena kuti: “Akatswiri a sayansi ya zinthu zamoyo akuganiza kuti chifukwa cha kutha kwa nkhalango za m’madera amene kumagwa mvula yambiri, zingatheke kuti theka kapena kuposa, la mitundu ya zamoyo, likhoza kutheratu pakangotha zaka 75 zokha.”

Malingana ndi zimene wasayansi wina wa pa yunivesite ya Tennessee, dzina lake Stuart Pimm anaŵerengetsera, magazini ya National Geographic inati “mitundu ya mbalame yokwana 1,100 yatsala pang’ono kutheratu kuchokera pa mitundu yonse imene ilipo padziko yokwana pafupifupi 10,000. N’zokayikitsa ngati mitundu yambiri pamenepa idzakhala ilipobe podzafika [m’zaka za m’ma 2099].” Magazini yomweyo inatchulanso kuti: “Posachedwapa gulu la akatswiri otchuka a sayansi ya zomera linanena kuti chomera chimodzi pa zomera zisanu ndi zitatu zilizonse chingathe kudzatheratu. Pimm ananena kuti ‘Si kuti zinthu zimene zingatheretu ndi zachilengedwe zimene zili m’zilumba zokha kapena zimene zili m’madera amene mumagwa mvula yambiri, kapenanso mbalame zokha kayanso mitundu yochititsa chidwi ya zinyama zimene zimayamwitsa basi. Ndi zinthu zonse ndipo zikutha kwina kulikonse. . . . Kutheratu kwa zinthu zosiyanasiyana ndi mliri wa padziko lonse.’”

Kodi Mitundu Yosiyanasiyana Yonseyi N’njofunikadi kwa Ife?

Kodi pali chifukwa chodera nkhaŵa ndi kutha kwa zinthu zamoyo zosiyanasiyanazi? Kodi mitundu yosiyanasiyanayi ya zachilengedwe n’njofunikadi kwa ife? Akatswiri ambiri otchuka amavomereza kuti mitunduyi n’njofunikadi. Anthu amagwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe popeza chakudya, mankhwala ofunika, komanso amazigwiritsa ntchito m’njira zina zosiyanasiyana. Komanso tangoganizirani mmene mitundu ina ya zinthu zachilengedwe imene anthu sanaidziŵe ingapindulitsire anthu. Mwachitsanzo, akuti pa mitundu 150 ya mankhwala akuchipatala ogwiritsidwa ntchito ku United States, mitundu 120 imachokera ku zinthu zachilengedwe. Motero, nkhalango zikamatha padziko lonse, nawonso anthu amataya mwayi woti angatulukire zitsamba kapena mankhwala atsopano. Mkulu woyang’anira munda wa mitengo ndi maluŵa wa Kew Gardens ku London, wotchedwa Bwana Ghillean Prance ananena kuti, “Mtundu uliwonse wa chinthu chachilengedwe ukangotha, timataya chinthu choti chingadzatithandize m’tsogolo. Timataya chinthu chimene mwina m’tsogolo muno chikanakhala mankhwala a AIDS kapenanso timataya mbewu imene imatha kupirira matenda ena ake obwera ndi tizilombo todwalitsa. Ndiyetu tiyenera kuleka kuwononga zachilengedwe, osati chifukwa choopa kuti dziko lingawonongeke komanso chifukwa chakuti n’zofunika . . . kwa ifeyo kuti tizizigwiritsa ntchito.”

Timafunikanso malo okhala ndi zinthu zachilengedwe kuti ntchito zofunika kwambiri zimene zinthu zonse zamoyo zimadalira zichitike. Malo ndiponso zinthu zake zachilengedwe zimachita ntchito zofunika kwambiri monga kupanga mpweya wabwino umene timapuma, kuyeretsa madzi, kusefa zinthu zimene zimawononga mpweya kapena madzi ndiponso kuteteza kuti nthaka isakokoloke.

Tizilombo timathandiza kuti zomera zizibereka tikamayenda m’maluŵa kapena m’ngayaye za zomerazi. Achule, nsomba ndiponso mbalame zimateteza tizilombo tosautsa. Nkhono ndi nyama zina za m’nyanja zimayeretsa madzi athu. Zomera ndi tizilombo tosaoneka ndi maso ndizo zimathandiza popanga dothi. Ndalama zimene zinthuzi zimabweretsa n’zosasimbika. Malinga ndi mitengo ya zinthu ya mu 1995, akuti dziko lonse linali kupeza phindu la ndalama zokwana pafupifupi madola 3,000 biliyoni chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe.

Komabe ngakhale kuti timadalira zinthu za moyo zosiyanasiyana, dzikoli likuoneka kuti lili pavuto lalikulu la kutha kwa zinthu kumene kukuoneka kuti kungathetseretu zachilengedwezi zimene zimadalirana m’njira zosiyanasiyana zovuta kuzifotokoza. Koma panopa, panthaŵi imene tikuyamba kumvetsa kufunika kwa zinthu zosiyanasiyana zamoyo, m’pamenenso anthu akupitiriza kupulula zinthuzo kuposa kale lonse! Pamenepa, kodi anthu angathetse vuto limeneli? Kodi m’tsogolomu zinthu zosiyanasiyana zamoyo padziko lapansi zidzakhala bwanji?

[Bokosi patsamba 22]

Kodi Moyo N’ngofunika Motani?

Zonse zimene takambirana zokhudza kufunika kwa zinthu zosiyanasiyana zamoyo zingaoneke ngati zikusonyeza kuti tiyenera kuganizira zinthu zina zamoyo malinga ngati zimatithandiza pa zosoŵa zathu. Ena amati kuganiza choncho ndi umbuli. Katswiri wofukula zinthu zakale dzina lake Niles Eldredge anasonyeza kuti anthufe timaona kuti moyo paokha n’ngofunika kwambiri pamene anati: “Anthufe timaonanso zinthu zamoyo zimene zili pafupi nafe kuti n’zofunika pazokha. Zinthuzi ndi monga, mitundu ya zinthu zachilengedwe yochititsa chidwi komanso yokongola kwambiri ndiponso malo a nkhalango zachilengedwe omwe adakali ndi tchire la chikhalire ndi zina zotere. Mwachibadwa, timakonda zinthu zachilengedwe zimenezi ndipo timakhala mtima uli mmalo ndiponso timasangalala tikapeza mwayi woziona.”

[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]

Mitundu ya Zamoyo Zomwe Zikutha Modetsa Nkhaŵa

Bungwe lomwe limaonetsetsa kuti zinthu zachilengedwe zisathe la International Union for Conservation of Nature and Natural Resources ndilo limalemba mitundu ya zamoyo zomwe zikutha modetsa nkhaŵa. Mitundu yochepa chabe ya zamoyo zotere imene anailemba m’chaka cha 2000 ndi iyi:

Mbalame zinazake zazikulu za kunyanja

Mtundu wa mbalame zimenezi uli m’gulu la mitundu 16 ya mbalame zotere. Akuti mbalame zambiri ndithu zotere zimamira m’madzi zikagwidwa mwatsoka ndi mbedza zokhala ndi zingwe zazitali zimene maboti ogwira nsomba amatchera.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chojambulidwa ndi Tony Palliser

Apusi ena ake a ku Asia

Apusi ena ake okongola a ku Asia amapezeka kum’mwera m’chigawo cha pakati ku Vietnam ndi m’madera ena a ku Laos. Apusiŵa akutha chifukwa chakuti malo awo okhala akuwonongedwa ndiponso anthu amawasaka. Anthu amasaka apusiŵa kuti apeze ndiwo kapenanso kuti awachotse ziwalo zina zimene amasakaniza ndi mankhwala a zitsamba.

[Mawu a Chithunzi]

Apusi amene ali pa tsamba 7 ndiponso pa tsamba 32: Anajambulidwa ndi Bill Konstant

Nkhono zinazake za pa chilumba chotchedwa Corsica

Malo amene nkhono zimene zatsala pang’ono kuthazi zimakhala, ndi maekala okwana 20 basi. Maloŵa ali kunja kwa tauni m’dera la Ajaccio, kum’mwera cha kumadzulo kwa gombe la chilumba cha Corsica. Nkhonozi zingathe kutha chifukwa cha chitukuko cha zomangamanga monga kumanga bwalo la ndege ndiponso misewu yabwino yopitira kunyanja.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chojambulidwa ndi G. Falkner

Maluŵa ena ake a ku South Africa

Anthu anatulukira mtundu wa maluŵa ameneŵa m’chaka cha 1987 m’dera lina la ku South Africa lotchedwa Western Cape. Mtundu wa maluŵa ameneŵa unayamba kutha chifukwa cha moto wolusa ndiponso chifukwa chakuti mitundu ina ya mbewu inayamba kulanda malo ake.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chojambulidwa ndi Craig Hilton-Taylor

Zinsomba zinazake zophwatalala za m’nyanja zikuluzikulu

Nsomba zimenezi zimapezeka cha kumadzulo m’nyanja za Indian Ocean ndi Pacific Ocean, komanso kumalo ena oyandikana ndi nyanjazo. Anthu amazigwira kwambiri, choncho zayambanso kusoŵa kwambiri. Vuto linanso limene lingathetse nsombazi ndilo kuwonongeka kwa malo amene zimakhala.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi choperekedwa mwachilolezo cha Sun International Resorts, Inc.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

Kusakaza Zamoyo za M’nyanja

Zinthu zopindulitsa kwambiri za m’nyanja zikuluzikulu, zimene kale zinkaoneka ngati sizidzatha, tsopano zikutha. M’magazini ina ya zachilengedwe yotchedwa Natural History, katswiri wina wofukula zinthu zakale dzina lake Niles Eldredge analongosola za kugwiritsa ntchito nyanja zikuluzikulu mopitirira muyeso. Iye anati: “Umisiri wamakono wapangitsa kuti anthu akhale ndi njira zotsogola kwambiri zogwirira nsomba zam’nyanja mwakuti malo aakulu kwambiri a m’nyanja ayereratu ngati mmene imakhalira nkhalango imene yadulidwa mitengo yonse. Komansotu, umisiriwu umawononga zinthu zambiri. Akamba a m’madzi, nyama zina zikuluzikulu za m’madzi komanso mitundu yambiri ya nsomba zosayenda malonda ndi zamoyo zina za m’madzi zimafa akamagwira nsomba muukonde.”

Pothirira ndemanga pa za ‘kuwonongeka kumene kumachitika pa kupha nsomba zinazake za m’gulu la nkhanu,’ magazini a National Geographic analongosola kuti “m’mphepete mwa gombe la Gulf Coast [kufupi ndi mzinda wa Texas, ku America] zamoyo zochuluka zedi za m’nyanja, makamaka tiana ta nsomba, n’kutheka kuti zimaphedwa pofuna kugwira nsomba zonga nkhanu zimenezi zosakwana ndi theka lomwe la kilogalamu.” Nsomba zosafunikazi amangoti n’zogwidwa mwatsoka. Katswiri wina wa boma wa sayansi ya zinthu zamoyo anadandaula kuti: “Pa nsomba imodzi iliyonse imene amagwira, nsomba zosafunika zongogwidwa mwatsoka zimakhalapo zinayi.” N’zosadabwitsa kuti nyanja zathu zikuluzikulu zasanduka malo ophera mitundu yambiri ya zamoyo zimene zayamba kusoŵa!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]

Zamoyo Zosadziŵika Zimene Zili M’nkhalango

Nkhalango za padziko lathuli n’zodzaza kwambiri ndi zinthu zamoyo, ndipo anthu sanatulukirebe mitundu ina ya zinthu zamoyozi. Katswiri wa zinthu zamoyo ndi malo awo okhala dzina lake John Harte anati: “Nkhalango za m’madera amene kumagwa mvula yambiri n’zochepa kwambiri poyerekezera ndi dziko lonse. Komatu n’kutheka kuti mwina theka kapenanso mbali yaikulu kwabasi ya mitundu yonse ya zinthu zamoyo padziko lonse imakhala m’nkhalango zimenezi. Mbali yaikuluyo ndi mbali ya zinthu zamoyo zimene akuganiza kuti zilinso m’madera ameneŵa koma sanazitulukirebe, chifukwa chakuti akatswiri a sayansi ya zinthu zamoyo akhala akufufuza mbali yochepa kwambiri ya maderaŵa amenenso ali otalikirana. Komanso malo ena okhala zamoyozi sanafufuzidwebe mokwanira, ndipo n’zosakayikitsa kuti panopa maloŵa ali ndi zamoyo zambiri zedi zimene asayansi sakuzidziŵa. Ena mwa malo otere ndi nthaka ya m’nkhalango zakalekale zachinyezi monga za m’chigawo cha Pacific, kumpoto cha kumadzulo kwa dziko la United States.”

Ndani angadziŵe zodabwitsa zimene anthu angapeze ngati atakwanitsa kufufuza zinthu zamoyo zosadziŵika zimene zili m’nkhalango?

[Chithunzi patsamba 21]

Mtundu wina wa njiwa umene pakalipano unatheratu

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./Luther C. Goldman

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena