Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g04 4/8 tsamba 15-17
  • Sungani Nthaŵi!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sungani Nthaŵi!
  • Galamukani!—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kusunga Nthaŵi ndi Inu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Nthaŵi Zonse Mumachedwa?
    Galamukani!—1990
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Nthawi?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—2004
g04 4/8 tsamba 15-17

Sungani Nthaŵi!

“MABWANA ambiri ali ndi vuto la kuchedwa,” inatero magazini yotchedwa USA TODAY. Potchulapo zimene anapeza atafufuza pakati pa mabwana 2,700 magaziniyo inapitiriza kuti: “Amachedwa ku misonkhano itatu pa misonkhano isanu iliyonse.”

M’makampani, kuchedwa sakuona ngati khalidwe loipa chabe. Atafufuza pakati pa anthu 81,000 ofunsira ntchito anapeza kuti: “Kuwononga nthaŵi chifukwa chochedwa ndiponso maulendo ongochokapo mosaloledwa n’kumene kumawonongetsa kwambiri ndalama.” N’zoona kuti vuto la kuchedwa silili m’makampani mokha ayi. Atafufuza pakati pa aphunzitsi aakulu a m’sukulu zasekondale anapeza kuti “khalidwe la kuchedwa ndilo linali vuto lalikulu komanso lochitikachitika kwambiri pakati pa ana asukulu.”

Mlengi wathu anatilenga m’njira yakuti tizitha kuganizira za nthaŵi. Anaika “zounikira zazikulu ziŵiri” dzuŵa ndi mwezi kuti zitithandize kudziŵa nthaŵi. (Genesis 1:14-16) Masiku ano, mawotchi amatithandiza kudziŵa nthaŵi poŵerengetsera maminiti ndi masekondi. Komabe umisiri wotere uli apo, ambirife timavutikabe kugwira nthaŵi, kaya ndi yofikira ku ntchito, ku sukulu, kapena ku zochitika zina zofunikira.

Kodi kwenikweni vuto limakhala kuchepa kwa nthaŵi? N’zoona kuti ntchito ndiponso banja limadya nthaŵi yambiri polisamalira. Komabe mayi wina wa pantchito dzina lake Wanda Rosseland anati: “Ine ndinasiya zodaundaula kuti ndilibe nthaŵi yokwanira chifukwa ndinaona kuti aliyense amakhala ndi maola 24 pa tsiku. Nditaganizira bwinobwino ndinaona kuti pa moyo wamakonowu, sikuti vuto lathu n’kuchepa kwa nthaŵi ayi, koma kuti pali zinthu zambiri zotijejemetsa ndiponso zotisokoneza.”

Taganiziranso za Renee,a yemwe ndi mayi wa ana asanu, wa Mboni za Yehova. Iyeyu anati: “Ndinkavutika kwambiri kukonzekeretsa ana anga kupita kusukulu ndiponso kumisonkhano yachikristu pamene anali aang’ono. Komabe ndinalibe vuto lolephera kugwira nthaŵi. Koma tsopano ana angaŵa atakula, ndinayamba chizoloŵezi choipa chomachedwa.” Kodi inunso muli ndi chizoloŵezi choipachi? Ngati n’choncho dziŵani kuti mungathe kusintha! Zinthu zina zimene mungachitepo ndi izi.

● GANIZIRANI MAPETO AKE. Chizoloŵezi chochedwa chimaoneka ngati vuto laling’ono. Komano taganizirani mawu a m’Baibulo akuti: “Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing’anga; chomwecho kupusa kwapang’ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.” (Mlaliki 10:1) Inde, “kupusa kwapang’ono” chabe poonetsa khalidwe losaganizira enali kungathe kukuwonongerani dzina lanu kwa aphunzitsi kapena abwana anu.

Mayi wina dzina lake Marie ankachita maphunziro enaake pa koleji ndipo anaona kuti anzake ena a m’kalasi mwake “analibe nazo ntchito kwenikweni zosunga nthaŵi,” moti nthaŵi zambiri ankafika mochedwa m’kalasi. Iyeyu anati: “Khalidweli sanapite nalo patali ayi. Mapulofesa athu ena aŵiri sankalola zomachedwa ngakhale pang’ono. Moti mwana wasukulu aliyense akachedwa, ngakhale pang’ono chabe, mapulofesawo ankangolemba kuti sanabwere. Ndipo akakulemba kuti sunabwere kwa masiku ambirimbiri sanali kukukhozetsa bwino.”

Chizoloŵezi chochedwa chingathenso kukuwonongerani mbiri yanu kwa anzanu ndi ena okudziŵani. Munthu wina wachinyamata ndithu dzina lake Joseph anasimba za Mkristu wina yemwe ankadziŵana zaka makumi angapo zapitazo. Ngakhale kuti anthu ankamuponyera kamtengo chifukwa chodziŵa bwino kuphunzitsa, iyeyu anali ndi khalidwe limodzi lochititsa manyazi. Joseph anati: “Iyeyu nthaŵi zonse ankangokhalira kuchedwa basi. Ndikutitu ankachedwa pa chinthu china chilichonse! Ndipo zikuoneka kuti sizinkam’khudza n’komwe. Anthu anayamba kum’sereula chifukwa cha khalidwe lakeli.” Kodi inuyo anthu anayamba kukunenani kuti mumakonda kuchedwa nthaŵi zonse? Ngati n’choncho dziŵani kuti m’posavuta kuti anthuwo aiwaleko zabwino zonse zimene mumachita.

● GANIZIRANI ENA. Kuchedwa n’kusalemekeza ena ndiponso kumawasokoneza. Ndipo kungachititse ena kuona kuti ndinu munthu wodzikuza. Bwana wina analongosola chifukwa chimene mabwana ambiri amachedwera ku misonkhano ponena kuti: “Kungoti ambirife ndife odzikuza.” Komano Akristu amayenera kuchita zinthu moganizira kuti anzawo n’ngowaposa. (Afilipi 2:3) Komanso amayenera kutsatira langizo lochitira ena zomwe amafuna kuti iwowo awachitire. (Mateyu 7:12) Kodi inuyo simunyong’onyeka mukamadikirira ena? Ndiyetu musamachititse ena kuti azikudikirirani.

● PHUNZIRANI NJIRA ZOSUNGIRA NTHAŴI. Kodi mumazengereza kuchita zinthu kenaka n’kuyamba pakalapakala nthaŵi yothaitha? Kodi mumadzipanikiza ndi zochita zambirimbiri pa kanthaŵi kochepa chabe? Mfundo ya pa Mlaliki 3:1, yakuti “kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake” ingakuthandizeni. Kukhala ndi “nthaŵi yake” yochitira zinthu kumakuthandizani kuzichita molongosoka.

Choyamba lembani zinthu zonse zimene mukufuna kuchita. Kenaka tsatirani mfundo yakuti ‘mudziŵe kusankha zimene zili zofunika kwenikweni’ yochokera pa Afilipi 1:10. [Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono] Inde, yambani mwachita kaye zinthu zofunika kwambiri. Ganizirani kuti kodi ndi zinthu zotani zimene muyenera kuzichita basi? Kodi ndi zinthu zotani zimene mungathe kudzazichita nthaŵi ina popanda vuto lililonse? Potsiriza, ganizirani kuti zingakutengereni nthaŵi yaitali motani ndiponso kuti muzichita nthaŵi iti. Zizikhala zinthu zoti mungazikwanitsedi ndipo peŵani kukonzekera zodzachita zinthu zambirimbiri pa kanthaŵi kochepa.

Mayi wina dzina lake Dorothy anati makolo ake ndiwo anamuphunzitsa kusunga nthaŵi. Iye anati: “Ngati tikupita ku msonkhano wachikristu woyamba nthaŵi ya 7:30 madzulo, amayi ankatikonzekeretsa kutatsala ola limodzi ndi mphindi 45. Tinkafunikira nthaŵi yoti tidye, titsuke mbale, tivale, ndiponso tiyende ulendo wa pagalimoto wokafika ku malo amisonkhanowo. Kenaka tinangozoloŵera kusunga nthaŵi m’moyo wathu.” Nthaŵi zina zimathandizanso kukhala ndi nthaŵi yochulukirapo ndithu kuopera zamwadzidzidzi. Dorothy anati: “Posachedwapa ndinanyamuka kukatenga anthu angapo kupita nawo kumsonkhano. Tayala linandiphwera ndili m’njira. Ndinapita kokalikonzetsa komabe ndinakwanitsa kukawatenga anthuwo nthaŵi idakalipo. Nthaŵi zonse ndimanyamuka padakali nthaŵi yokwanira kuti ndisachedwe ngakhale ngati galimoto itavuta panjira kapena ngati mumsewu mutakhala magalimoto ambiri.”

● FUNSIRANI NZERU KWA ENA. Pa Miyambo 27:17, Baibulo limati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, kambiranani ndi anthu amene akukhala moyo wa ngati wa inuyo koma amene amakwanitsa kusunga nthaŵi. Nthaŵi zambiri anthu otereŵa angakuthandizeni maganizo m’njira zambiri.

Renee, yemwe tam’tchulapo uja, anatsimikiza kusintha khalidwe lake lochedwali. Iye anati: “Posachedwapa ndinatsimikiza kuti ndiyesetsa kusintha. Ngakhale kuti zakhala zikundivuta, panopo zikundiyendera ndithu.” Inunso mungatero. Ngati mutatsimikiza n’kumayesetsadi kutero, mungathe kuphunzira kusunga nthaŵi!

[Mawu a M’munsi]

a Mayina ena tawasintha.

[Zithunzi patsamba 16]

Chizoloŵezi chochedwa chingakuwonongereni mbiri kwa mabwana anu ndiponso chimasonyeza kuti simuganizira ena

[Chithunzi patsamba 17]

Kuchita zinthu mwadongosolo kungakuthandizeni kupeŵa kuwononga nthaŵi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena