Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/07 tsamba 6
  • 2. Olemba Ake Ananena Zoona Zokhazokha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2. Olemba Ake Ananena Zoona Zokhazokha
  • Galamukani!—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo ‘Linauziridwadi Ndi Mulungu’?
    Galamukani!—2017
  • Kodi Nkhani Zimene Zili M’Baibulo Ndi Nzeru za Anthu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Baibulo ndi Buku Lapadera
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Anthu Amene Analemba za Yesu
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2007
g 11/07 tsamba 6

Chifukwa Chake Tiyenera Kukhulupirira Baibulo

2. Olemba Ake Ananena Zoona Zokhazokha

Munthu amene amadziwika kuti amanena zoona ndiponso sabisa chilichonse, timamukhulupirira. Koma akatinamiza ngakhale kamodzi, timasiya kumukhulupirira.

OLEMBA Baibulo ananena zoona zokhazokha ndipo sanabise chilichonse. Zimenezi zimatichititsa kukhulupirira zimene analemba.

Zolakwa ndi zolephera. Olemba Baibulo sanabise zolakwa ndi zolephera zawo. Mose analemba za cholakwa chake chimene chinamubweretsera chilango chachikulu. (Numeri 20:7-13) Asafu ananena kuti kwanthawi ndithu ankachitira nsanje anthu oipa chifukwa choona kuti zinthu zikuwayendera bwino. (Salmo 73:1-14) Yona ananena za kusamvera kwake ndi mtima woipa umene anali nawo poyamba, Mulungu atachitira chifundo anthu amene analapa machimo awo. (Yona 1:1-3; 3:10; 4:1-3) Mateyo anafotokoza mosabisa mawu kuti iye anathawa Yesu usiku umene Yesuyo anamangidwa.—Mateyo 26:56.

Anthu amene analemba Malemba Achiheberi anaulula za kung’ung’udza ndi kupanduka kwa anthu a mtundu wawo. (2 Mbiri 36:15, 16) Anthu amenewa analemba za zolakwa za aliyense ngakhale za atsogoleri awo. (Ezekieli 34:1-10) Makalata a atumwi nawonso ananena mosabisa za mavuto aakulu amene Akhristu ena anali nawo ngakhalenso a anthu audindo, ndiponso za mavuto amene mipingo ina inali nawo.—1 Akorinto 1:10-13; 2 Timoteyo 2:16-18; 4:10.

Sanabise choonadi. Olemba Baibulo sanabise zinthu zina zimene ena akanaona kuti n’zochititsa manyazi. Akhristu oyambirira ananena mosabisa kuti anthu ambiri nthawi imeneyo sankawakonda ndipo ankawanyoza kuti ndi anthu opusa ndi osauka. (1 Akorinto 1:26-29) Olemba Baibulo amenewa ananena kuti atumwi a Yesu ankaonedwa kuti ndi “osaphunzira ndiponso anthu wamba.”—Machitidwe 4:13.

Anthu amene analemba Mauthenga Abwino sanalembe zinthu zokometsera Yesu pachilichonse. Mwachitsanzo, iwo analemba kuti iye anabadwira m’banja losauka, sanapite kusukulu zapamwamba za panthawiyo, ndi kuti anthu ambiri anakana uthenga wake.—Mateyo 27:25; Luka 2:4-7; Yohane 7:15.

Choncho, Baibulo lili ndi umboni wochuluka wosonyeza kuti olemba ake ananena zoona zokhazokha. Kodi zimenezi sizikukuchititsani kukhulupirira Baibulo?

[Chithunzi patsamba 6]

Olemba Baibulo monga Yona analemba za zolakwa zawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena