Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 7/09 tsamba 20
  • Mankhwala Odzikongoletsera Ochokera ku Mitengo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mankhwala Odzikongoletsera Ochokera ku Mitengo
  • Galamukani!—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2009
  • Kukongola Kungakhale Kokha kwa pa Khungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Ndichititse Opaleshoni Kuti Ndikhale Wokongola?
    Galamukani!—2002
  • Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—2009
g 7/09 tsamba 20

Mankhwala Odzikongoletsera Ochokera ku Mitengo

◼ Dera la kum’mwera chakumadzulo kwa dziko la Madagascar ndi lotentha kwambiri, ndipo akazi kumeneku amakonda kuyenda mphepete mwa nyanja kufunafuna zigoba za nkhono za m’madzi zomwe amazigulitsa kwa alendo obwera m’dzikoli. Akaziwa amapakapaka nkhope zawo mankhwala ochokera ku mitengo. Amadzipaka mankhwala amenewa ndi cholinga choti khungu lawo lisapse ndi dzuwa komanso kuti azioneka bwino.

Mankhwalawa amapangidwa kuchokera ku mitengo inayake ya maluwa. (masonjoany ndi fihamy) Kupanga kwake n’kosavuta: Akaziwa amatenga makungwa a mitengo n’kuwanyenya pamwala wophwatalala, ndipo amathira madzi pang’onopang’ono mpaka makungwawa ataoneka ngati phala. Kenako amayamba kuzipaka mankhwalawa mwaluso pankhope pawo pogwiritsira ntchito kamtengo kosongoka bwino.

Akazi ena amapaka mankhwalawa nkhope yawo yonse kungosiyapo maso okha, pamene ena amangopaka pachipumi, m’masaya ndi kuchibwano. Mankhwalawa amawagwiritsa ntchito pofuna kubisa zipsera kunkhope, kuteteza khungu kapenanso pofuna kudzikongoletsa. Nthawi zina m’makungwawa amaphatikizamo zinthu zina kuti apange mitundu yosiyanasiyana ya mankhwalawa.

Anthu ambiri sangakhulupirire kuti mankhwala odzikongoletsera amenewa amapangidwa kuchokera ku mitengo. Mosiyana ndi anthu a mayiko ena amene amagwiritsa ntchito mankhwala opangidwa ku fakitale, anthu a m’dziko la Madagascar, amakonda kugwiritsa ntchito mankhwala ochokera ku mitengo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena