Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/11 tsamba 22-23
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Salola Akhristu Kumenya Nkhondo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Salola Akhristu Kumenya Nkhondo?
  • Galamukani!—2011
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zinthu Zitatu Zimene Zimasiyanitsa Aisiraeli ndi Akhristu
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Anasiya Mtundu wa Isiraeli?
  • Kodi N’zotheka Kukonda Adani Athu?
    Galamukani!—2009
  • Akristu Osaloŵerera M’zinthu za Dziko M’masiku Otsiriza
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Tingatani Kuti Tikhale Osiyana ndi Dzikoli?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Galamukani!—2011
g 8/11 tsamba 22-23

Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Mulungu Salola Akhristu Kumenya Nkhondo?

MFUMU Davide ya Isiraeli, ponena za nkhondo zimene inamenya, inati: “[Mulungu] akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo, ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.”—Salimo 18:34.

Ponena za Akhristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngakhale kuti moyo wathu ndi wofanana ndi wa anthu ena onse, sitikumenya nkhondo motsatira maganizo a dzikoli. Pakuti zida za nkhondo yathu si zochokera m’dziko lino.”—2 Akorinto 10:3, 4.

Kodi malemba awiriwa akutsutsana? Kodi pali zifukwa zomveka zimene Mulungu ankalolera Aisiraeli kumenya nkhondo? N’chifukwa chiyani Akhristu sayenera kumenya nkhondo? Kodi Mulungu anasintha mmene amaonera nkhondo? Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tiyeni tiganizire zinthu zitatu zimene zimasiyanitsa mtundu wa Isiraeli ndi mpingo wachikhristu.

Zinthu Zitatu Zimene Zimasiyanitsa Aisiraeli ndi Akhristu

1. Mulungu anapatsa Aisiraeli dziko lawolawo lokhala ndi malire, ndipo nthawi zina mitundu yoyandikana nawo inkawachitira nkhanza. Choncho, Mulungu analamula anthu akewo kuti aziteteza dziko lawo, moti iye ankawathandiza kugonjetsa adani awo. (Oweruza 11:32, 33) Mosiyana ndi mtundu wa Isiraeli, mpingo wachikhristu wapangidwa ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse. Choncho ngati Mkhristu atapita kokamenya nkhondo, ndiye kuti azikamenyana ndi Mkhristu mnzake wadziko lina, yemwe ndi m’bale kapena mlongo wake wauzimu amene Baibulo limamulamula kuti azimukonda kwambiri, ngakhale kumufera kumene.—Mateyu 5:44; Yohane 15:12, 13.

2. Mtundu wa Isiraeli unkakhala ndi mfumu imene inkakhala ku Yerusalemu. Koma mosiyana ndi zimenezi, Akhristu oona amalamulidwa ndi Yesu Khristu, yemwe panopa ali kumwamba ndipo ndi mngelo wamphamvu kwambiri. (Danieli 7:13, 14) Yesu ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Choncho, palibe boma kapena ufumu uliwonse padziko lapansi umene unganene kuti uli kumbali ya Khristu. Kodi zimenezi zikukhudza bwanji otsatira a Yesu? Yankho la funso limeneli lafotokozedwa mu mfundo yachitatu.

3. Mtundu wa Isiraeli, mofanana ndi mitundu ina, unkatumiza amithenga omwe masiku ano tinganene kuti akazembe. (2 Mafumu 18:13-15; Luka 19:12-14) Khristu wachitanso zofanana ndi zimenezo, kungoti pali zinthu ziwiri zimene zikusiyana kwambiri ndi zimene Aisiraeli ankachita. Choyamba, otsatira ake onse ndi akazembe kapena nthumwi. N’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena kuti iyeyo ndi Akhristu anzake ndi “akazembe m’malo mwa Khristu.” (2 Akorinto 5:20) Monga akazembe okonda mtendere, Akhristu oyambirira sankamenya nkhondo. Chachiwiri, otsatira a Yesu amalalikira kwa anthu onse amene amafuna kumvetsera uthenga wawo. Yesu ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Ananenanso kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20.

Komabe, nthawi zina zimamvetsa chisoni kuti otsatira a Khristu salandiridwa bwino akamagwira ntchito yawo yolalikira. Pa chifukwa chimenechi, m’kalata imene Paulo analembera Timoteyo, ananena kuti: “Monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu, khala wokonzeka kumva zowawa.” (2 Timoteyo 2:3) Komabe zida za Timoteyo zinali zauzimu ndipo zinkaphatikizapo Mawu a Mulungu amene ndi “lupanga la mzimu.”—Aefeso 6:11-17.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anasiya Mtundu wa Isiraeli?

Kwa zaka pafupifupi 1,500, mtundu wa Isiraeli unali pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu, ndipo ubwenzi umenewu unkadalira kuti iwo azisunga pangano lawo ndi Yehova. (Ekisodo 19:5) Pangano limeneli lomwe mkhalapakati wake anali Mose, linali ndi Malamulo Khumi komanso malamulo ena, omwe ankalimbikitsa kulambira koona ndiponso makhalidwe abwino. (Ekisodo 19:3, 7, 9; 20:1-17) Koma n’zomvetsa chisoni kuti m’kupita kwa nthawi, mtundu wa Isiraeli unasiya kukhala wokhulupirika kwa Mulungu mpaka kufika popha aneneri ake.—2 Mbiri 36:15, 16; Luka 11:47, 48.

Kenako, Yehova anatumiza Mwana wake, Yesu Khristu, yemwe anabadwira mu mtundu wa Chiyuda. Koma m’malo momulandira monga Mesiya, mtunduwo unamukana. Zotsatira zake zinali zakuti Mulungu anathetsa pangano lake ndi Aisiraeli, ndipo khoma lophiphiritsa lomwe linkalekanitsa Ayuda ndi anthu amene sanali Ayuda linagwa.a (Aefeso 2:13-18; Akolose 2:14) Zimenezi zitangochitika, Mulungu anakhazikitsa mpingo wachikhristu ndipo anasankha Yesu kukhala Mutu wake. Ndipo chaka cha 100 C.E. chisanafike, mpingowu unali utapangidwa ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Mtumwi Petulo yemwe anali Myuda anati: “[Mulungu] amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:35.

A Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira chitsanzo cha Akhristu oyambirira. Iwo amadziwika ndi ntchito yawo yolalikira ndipo salowerera ndale kapena kumenya nawo nkhondo. (Mateyu 26:52; Machitidwe 5:42) Salola chinthu chilichonse kuwasokoneza pa ntchito yawo yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lokhalo limene lidzathetse kuipa konse padzikoli n’kubweretsa mtendere weniweni. Poganizira za chiyembekezo chabwino chimenechi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti: ‘Gwirizananinso ndi Mulungu.’” (2 Akorinto 5:20) Mawu amenewa ndi ofunika kuwalabadira kwambiri makamaka masiku ano chifukwa tili kumapeto kwa “masiku otsiriza” a dziko loipali.—2 Timoteyo 3:1-5.

[Mawu a M’munsi]

a Dzina lakuti “Myuda” poyamba linkangotanthauza Mwisiraeli amene wachokera ku fuko la Yuda. Koma m’kupita kwa nthawi, dzinali linayamba kugwiritsidwa ntchito ponena za Aheberi onse.—Ezara 4:12.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Akhristu ayenera kusonyezana khalidwe lofunika liti?—Yohane 13:34, 35.

● Kodi chida chofunika kwambiri kwa Akhristu ndi chiyani?—Aefeso 6:17.

● Kodi oimira Khristu amalengeza uthenga wofunika wotani?—Mateyu 24:14; 2 Akorinto 5:20.

[Chithunzi patsamba 23]

Mboni za Yehova ndi gulu limene lapangidwa ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana, ndipo iwo samenya nawo nkhondo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena