Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g19 No. 2 tsamba 10-11
  • Muziwaphunzitsa Kukhala Odalirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziwaphunzitsa Kukhala Odalirika
  • Galamukani!—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI MUNTHU WODALIRIKA AMATANI?
  • N’CHIFUKWA CHIYANI KUKHALA ODALIRIKA N’KOFUNIKA?
  • MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA ODALIRIKA?
  • Kodi Kuphunzitsa Ana Ntchito Zapakhomo N’kothandiza Bwanji?
    Galamukani!—2017
  • Konzekerani Kudzawalola Kupita
    Galamukani!—1998
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mmene Mungathandizire Ana Anu Akamalephera Zinazake
    Mfundo Zothandiza Mabanja
Onani Zambiri
Galamukani!—2019
g19 No. 2 tsamba 10-11
Bambo akuthandiza mwana wake kuthirira mtengo

PHUNZIRO 4

Muziwaphunzitsa Kukhala Odalirika

KODI MUNTHU WODALIRIKA AMATANI?

Munthu wodalirika amachita zimene wauzidwa ndipo amachita zimenezo pa nthawi yake.

N’zoona kuti ana amadziwa zinthu zochepa, komabe akhoza kukhala odalirika. Buku lina limanena kuti: “Ana akamakwanitsa miyezi 15 amachita zimene makolo awo awauza. Ndipo akafika miyezi 18 amayamba kutsanzira bwinobwino zimene makolo awo amachita. M’madera ambiri, ana akangofika zaka za pakati pa 5 ndi 7, makolo awo amayamba kuwaphunzitsa ntchito zapakhomo. Ngakhale pa msinkhu waung’ono chonchi, amatha kuwathandiza kugwira ntchito zosiyanasiyana.”​—Parenting Without Borders.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUKHALA ODALIRIKA N’KOFUNIKA?

Pali ana ena omwe amati akachoka pakhomo kuti akadziimire paokha, amabwereranso kwa makolo awo zinthu zikawavuta. Nthawi zina zimenezi zimachitika chifukwa choti mwanayo sanaphunzitsidwe mmene angagwiritsire ntchito ndalama, kusamalira pakhomo komanso kuchita zinthu zina zofunika.

Choncho, n’zofunika kwambiri kuti makolo aziphunzitsa ana awo zinthu zomwe zingadzawathandize akadzakula. Buku lina limati: “Si bwino kumangomuchitira mwana chilichonse mpaka kukula, kenako n’kumusiya kuti akakumane nazo.”​—How to Raise an Adult.

MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA ODALIRIKA?

Muziwagawira ntchito zapakhomo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.”​—Miyambo 14:23.

Ana akakhala aang’ono amasangalala kugwira ntchito limodzi ndi makolo awo. Mukhoza kupezerapo mwayi pamenepa, powagawira ntchito zapakhomo zoti azigwira.

Koma makolo ena safuna kuchita zimenezi. Amanena kuti ana awo amakhala ndi homuweki yochuluka moti amaona kuti si bwino kuwawonjezera zochita zina.

Komatu, ana omwe amagwira ntchito zapakhomo ndi amenenso amachita bwino kusukulu. Izi zili choncho chifukwa amakhala ataphunzira kumalizitsa ntchito iliyonse imene apatsidwa. Buku lina linanena kuti, “Tikanyalanyaza kuphunzitsa ana athu ntchito adakali aang’ono, saona kufunika kothandiza ena . . . Komanso amangoyembekezera kuchitiridwa chilichonse.”

Mogwirizana ndi zomwe bukuli linanena, ntchito zapakhomo zimathandiza ana kuti asamangokhala manjalende komanso kuti asamangoyembekezera kupatsidwa zinthu, koma kuti nawonso azithandiza ena. Ana akamagwira nawo ntchito zapakhomo, amadziona kuti ndi ofunika komanso kuti ali ndi udindo woti akwaniritse.

Muziwaphunzitsa kudziwa kuti ali ndi udindo wokonza zimene alakwitsa.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.”—Miyambo 19:20.

Mwana wanu akalakwitsa zinazake, mwachitsanzo ngati wawononga katundu wa eniake, musamamuyikire kumbuyo. Ayenera kuvomereza zimene walakwitsazo n’kukapepesa anthu amene wawalakwirawo kapena kubweza zimene wawononga.

Mwana wanu akadziwa kuti ali ndi udindo wokonza zimene walakwitsa kapena kuwononga, zidzamuthandiza . . .

  • kuti azichita zinthu moona mtima komanso kuvomereza zimene walakwitsa

  • kuti asamaloze chala anthu ena

  • kuti asamadziikire kumbuyo

  • kuti azipepesa akalakwitsa

Bambo akuthandiza mwana wake kuthirira mtengo

YAMBANI PANOPO KUWAPHUNZITSA

Ana amene amaphunzitsidwa kukhala odalirika amatha kuchita bwino zinthu paokha ngati munthu wamkulu

Muziwapatsa Chitsanzo Chabwino

  • Kodi ndine wakhama, wadongosolo komanso wosunga nthawi?

  • Kodi ana anga amandiona ndikugwira ntchito zapakhomo?

  • Kodi ndikalakwitsa zinazake ndimavomereza komanso kupepesa?

Zimene Makolo Ena Ananena . . .

“Kungoyambira ali aang’ono, ana anga ankandithandiza kuphika, kupinda zovala komanso kukonza m’nyumba. Zinkawasangalatsa akamandithandiza ntchito. M’kupita kwa nthawi zimenezi zinawathandiza kukhala odalirika.”​—Laura.

“Tsiku lina ndinauza mwana wathu kuti aimbire foni wachibale wathu wina ndi kumupepesa chifukwa chomuchitira mwano. Pamene zaka zinkapita, anaphunzira kupepesa akazindikira kuti wanena zinthu zimene zakhumudwitsa ena. Panopa savutikanso kupepesa akalakwitsa zinazake.”​—Debra.

AZIPHUNZIRAPO KANTHU PA ZOMWE ALAKWITSA

A Jessica Lahey omwe amagwira ntchito yauphunzitsi, analemba m’magazini ina kuti: “Ana sangachite zinthu popanda kulakwitsa, choncho n’zofunika kuti makolo azikumbukira kuti ana awo akhoza kuphunzirapo kanthu pa zimene alakwitsazo. Chaka chilichonse, ndinkaphunzitsa ana omwe ankalakwitsa zinazake ndipo makolo awo sankawaikira kumbuyo. Makolowo ankangowathandiza kudziwa zimene angachite kuti akonze zimene alakwitsazo. Ndinaona kuti pakapita nthawi, ana oterowo ndi amene ankachita bwino pa maphunziro komanso ankakhala osangalala.”​—Atlantic.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena