Palibenso Buku Lothandiza Kwambiri Kuposa Baibulo
Baibulo ndi buku lomwe limafalitsidwa komanso kumasuliridwa m’zinenero zambiri kuposa buku lina lililonse. Ndiponso mfundo zake zathandiza anthu ambiri kuposa mabuku ena. Mwachitsanzo taganizirani izi:
MABAIBULO OMWE AMASULIRIDWA KOMANSO KUFALITSIDWA
96.5% ya anthu padzikoli ali nalo
LIKUPEZEKA m’zinenero 3,350 (LONSE KAPENA MBALI YAKE)
5,000,000,000: Chiwerengero cha mabaibulo amene afalitsidwa. Chiwerengerochi n’choposa mabuku ena onse omwe afalitsidwapo
KUTI MUDZIWE ZAMBIRI
PITANI PAWEBUSAITI YATHU YA JW.ORG. PAWEBUSAITIYI MUKHOZA:
Kuwerenga Baibulo (lomwe likupezeka m’zinenero zoposa 260)
Kupanga dawunilodi Baibulo
Kupeza mayankho a mafunso anu
Kuwerenga nkhani zosonyeza mmene Baibulo lathandizira anthu kukhala ndi moyo wabwino
Kuphunzira Baibulo pa intanetia
Kupempha kuti munthu aziphunzira nanu Baibulo
A MBONI ZA YEHOVA AMAKHULUPIRIRA BAIBULO
A MBONI ZA YEHOVA AMADZIPEREKA KUGWIRA NTCHITO YOMASULIRA KOMANSO KUFALITSA BAIBULO.
Pamunsipa pali Mabaibulo omwe takhala tikufalitsa m’mbuyomu.
American Standard Version of 1901
The Bible in Living English by Byington
The Emphatic Diaglott
King James Version
Revised Standard Version
Tischendorf’s New Testament
BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO
180+ Zinenero (LONSE KAPENA MBALI YAKE)
227 MILLION KUCHULUKA KWA MABAIBULO A DZIKO LATSOPANO OMWE AKHALA AKUFALITSIDWA KUCHOKERA MU 1950
a Panopa munthu akhoza kuphunzira m’Chingelezi komanso m’Chipwitikizi. Zinenero zina zibwera m’tsogolomu.