1. Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Kuti Tizivutika?
Chifukwa Chake Kudziwa Yankho la Funsoli Kuli Kofunika
Anthu ambiri safuna kulambira Mulungu chifukwa amaona kuti ndi amene amachititsa kuti tizivutika.
Taganizirani Izi
Modziwa kapena mosadziwa, atsogoleri ambiri azipembedzo amaphunzitsa kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika. Mwachitsanzo, ena amanena kuti:
Ngozi zam’chilengedwe ndi chilango chochokera kwa Mulungu.
Ana amafa chifukwa chakuti Mulungu akufuna kuwonjezera angelo kumwamba.
Mulungu amathandiza magulu omenya nkhondo, ndipo nkhondozi zimachititsa kuti anthu azivutika kwambiri.
Koma kodi zingakhale zotheka kuti atsogoleri azipembedzo aziphunzitsa zolakwika zokhudza Mulungu? Bwanji ngati Mulungu sagwirizana ndi atsogoleri azipembedzo?
KUTI MUDZIWE ZAMBIRI
Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? pa jw.org.
Zimene Baibulo Limanena
Mulungu si amene amachititsa kuti tizivutika.
Ngati amatero, zingakhale zosiyana ndi makhalidwe ake omwe amafotokozedwa m’Baibulo. Mwachitsanzo:
“Njira [za Mulungu] zonse ndi zolungama. . . . Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”—DEUTERONOMO 32:4.
“Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.”—YOBU 34:10.
“Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.”—YOBU 34:12.
Mulungu sagwirizana ndi zipembedzo zomwe zimaphunzitsa zinthu zabodza zokhudza iyeyo.
Zimenezi zikuphatikizapo zipembedzo zomwe zimaphunzitsa kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika, komanso zipembedzo zomwe zimatenga nawo mbali pa nkhondo komanso zachiwawa.
“Aneneriwo akulosera monama m’dzina langa. Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo. Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama . . . ndi chinyengo cha mumtima mwawo.”—YEREMIYA 14:14.
Yesu anadzudzula chinyengo cha zipembedzo.
“Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba. Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’ Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.”—MATEYU 7:21-23.