2. Kodi Mavuto Athu Timawachititsa Tokha?
Chifukwa Chake Kudziwa Yankho la Funsoli Kuli Kofunika
Ngati yankho ndi lakuti inde, ndiye kuti tikhoza kukwanitsa kuchepetsako mavuto athu.
Taganizirani Izi
Kodi anthu achititsa mavuto otsatirawa kufika pati?
Nkhanza.
Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti munthu mmodzi pa anthu 4 alionse, anachitiridwapo zinthu zankhanza ali wamng’ono, ndipo mzimayi mmodzi pa azimayi atatu alionse anachitiridwapo zankhanza kapena kugwiriridwa pa nthawi inayake.
Kuferedwa.
Lipoti la Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse la mu 2018, linanena kuti “anthu pafupifupi 477,000 anaphedwa padziko lonse mu 2016.” Zimenezi zikuwonjezera pa anthu pafupifupi 180,000 omwe akuganiziridwa kuti anaphedwa pa nkhondo ndi zipolowe m’chaka chomwecho.
Matenda.
Fran Smith, yemwe analemba nkhani ina mu magazini ya National Geographic ananena kuti: “Anthu oposa 1 biliyoni amasuta, ndipo fodya ali m’gulu la zinthu zomwe zikuyambitsa matenda 5 akuluakulu amene akupha anthu. Matendawa ndi sitiroko, matenda a mtima, chifuwa, matenda a m’mapapo ndi khansa ya m’mapapo.”
Tsankho.
Katswiri wina wa zamaganizo dzina lake Jay Watts ananena kuti: “Umphawi, kusalana, kusankhana mitundu, kuona kuti akazi ndi osafunika, kuthawa m’dera lomwe ukukhala komanso mtima wampikisano, zikuchititsa anthu kudwala matenda ovutika maganizo.”
KUTI MUDZIWE ZAMBIRI
Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? pa jw.org
Zimene Baibulo Limanena
Anthu ndi amene amayambitsa mavuto ambiri omwe timakumana nawo.
Ena mwa mavutowa amayamba ndi maboma ankhanza, zomwe zimachititsa kuti anthu amene amawalamulira azivutika kwambiri.
“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—MLALIKI 8:9.
Kuvutika kukhoza kuchepetsedwa.
Mfundo za m’Baibulo zimalimbikitsa anthu kukhala ndi moyo wathanzi komanso kukhala mwamtendere ndi anthu ena.
“Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu, koma nsanje imawoletsa mafupa.”—MIYAMBO 14:30.
“Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.”—AEFESO 4:31.