Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 3 tsamba 8-9
  • Zimene Asayansi Sangatiuze

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Asayansi Sangatiuze
  • Galamukani!—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Katswiri Woona za Mmene Ana Osabadwa Amakulira Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
    Galamukani!—2016
  • Kodi Chilengedwe Chonsechi Ndiponso Zamoyozi Zinakhalako Bwanji?
    Galamukani!—2002
  • Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 3 tsamba 8-9
Mphunzitsi wa sayansi akukambirana ndi ophunzira ake.

Zimene Asayansi Sangatiuze

Zikuoneka kuti asayansi anaphunzira zambiri zokhudza chilengedwechi. Komabe, pali mafunso ambiri ofunika omwe sangakwanitse kuyankha.

Kodi asayansi amafotokoza mmene chilengedwe komanso zamoyo zinayambira? Yankho lachidule ndi lakuti ayi. Anthu ena amanena kuti asayansi omwe anaphunzira zakuthambo ndi amene angafotokoze mmene chilengedwechi chinayambira. Komabe pulofesa wina wa ku koleji ya Dartmouth dzina lake Marcelo Gleiser, yemwe amakayikira kuti kuli Mulungu, ananena kuti: “Sitinakwanitsepo kufotokoza mmene chilengedwe chinayambira.”

Komanso pofotokoza mmene moyo unayambira, nkhani ina ya m’magazini ya sayansi (Science News) inanena kuti: “N’zosatheka kudziwa zoona zake za mmene moyo unayambira padzikoli. Miyala komanso zinthu zina zakale zimene zinakwiririka munthaka zomwe zikanasonyeza mmene zinthu zinalili m’masiku oyambirira a dzikoli, zinasiya kupezeka.” Zimenezi zikusonyeza kuti pofika pano sayansi yalephera kupeza yankho la funso lakuti, Kodi chilengedwe komanso zamoyo zinayamba bwanji?

Koma mwina mukhoza kudabwa kuti, ‘Ngati zamoyo zinachita kulengedwa, ndiye ndi ndani amene anazilenga?’ Mwinanso munadzifunsapo mafunso awa: ‘Ngati kulidi Mlengi yemwe ndi wanzeru komanso wachikondi, n’chifukwa chiyani amalola kuti anthu omwe anawalenga yekha azivutika? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthu azilambira m’njira zosiyanasiyana? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthu ena amene amati amamulambira azichita zinthu zoipa zambiri?’

Sayansi singathe kupeza mayankho a mafunso amenewa. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti simungapeze mayankho omveka bwino. Ndipotu anthu ambiri anapeza mayankho m’Baibulo amene anawafika pamtima.

Ngati mungakonde kudziwa chifukwa chake asayansi ena omwe anaphunzira Baibulo amakhulupirira kuti kuli Mlengi, pitani pa jw.org. Fufuzani mavidiyo a mutu wakuti “Zokhudza Mmene Moyo Unayambira.”

Sayansi Komanso Baibulo Zinawathandiza

Georgiy N. Koidan, katswiri wa zamankhwala

“Nthawi zambiri ntchito yanga imakhala ‘yophatikiza’ mamolekyu. Zili ngati kusewera tchesi. Umafunika kuchitiratu pulani masitepe angapo oti uyende. Ngati utaphonya sitepe imodzi molekyu singapangike n’komwe. Ngakhale kuti ntchito yanga imafuna kuchita zinthu zambirimbiri, sizovuta tikayerekezera ndi zimene zimachitika mkati mwa selo kuti lipange mamolekyu. Zimenezi zimandichititsa kuganiza kuti pali Wasayansi Wamkulu yemwe ndi Mlengi.

Nditaphunzira Baibulo ndinazindikira kuti ndi buku lapadera. Baibulo linamalizidwa kulembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo koma ndimaona kuti malangizo ake ndi othandizabe masiku ano. Zomwe limanena pa nkhani yothetsa kusamvana m’banja, kuntchito, komanso ndi anthu ena n’zothandizadi. Ndinafika pomvetsa kuti amene anapereka malangizo othandizawa ndi wanzeru kwambiri kuposa anthufe.”

Yan-Der Hsuuw, katswiri woona za mmene ana amakulira m’chiberekero

“Mwana akamapangika m’mimba, maselo onse amachita zinthu mogwirizana kuti ena apange mitsempha, minofu, mafupa, magazi ndi zinthu zina ndipo pamapeto pake munthu wathunthu amapangika. Mpaka pano sitimvetsabe kuti chimachitika n’chiyani mwana akamapangika m’mimba. Ine ndimaona kuti pali winawake wanzeru kwambiri amene anayambitsa moyo.

Ndimaona kuti zimene Baibulo limanena pa lemba la Salimo 139:15, 16, zokhudza mmene mwana amakulira m’mimba mwa mayi ake ndi zofanana ndi zimene asayansi apeza m’zaka za posachedwapa. Kodi zikanatheka bwanji kuti zinthu zolondola zimenezi zilembedwe kalekalelo ngati wolembayo sanachite kuuzidwa ndi Mlengi?”

Onerani vidiyo yakuti Rocío Picado Herrerou: Mphunzitsi wa Zasayansi ya Zinthu Zamoyo Akufotokoza Zachikhulupiriro Chake. Fufuzani mutu wa vidiyoyi pa jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena