Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tr mutu 8 tsamba 65-74
  • Ncifukwa Ninji Mulungu Wakulola Kuipa Kupitirizabe Mpaka Lero?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ncifukwa Ninji Mulungu Wakulola Kuipa Kupitirizabe Mpaka Lero?
  • Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NSONGA ZOFUNIKAZO
  • NJIRA YA MULUNGU YA KUITHETSERA NKHANIYO
  • KODI ZOTSATIRAPO ZASONYEZANJI?
  • KODI CIYESOCO CIDZAPITIRIZABE KWA UTALI WOTANI?
  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Walola Kuipa?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Nkhani Imene Ikulowetsamo Inu
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Mukulowetsedwa m’Nkhani Yofunika
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
tr mutu 8 tsamba 65-74

Mutu 8

Ncifukwa Ninji Mulungu Wakulola Kuipa Kupitirizabe Mpaka Lero?

1. Kodi mtundu wa anthu wakumana ndi ciani ponena za kuipa?

MU MBIRI yonse yakale ya kuyambira pamene munthu anayamba kukhalapo kwakhalapo kuipa kwakukuru. Ndipo lerolino, mosasamala za kumene mungayang’aneko m’dziko, pali kukhetsa mwazi, upandu, cidani ndi kuipa kwa cikhalidwe ca mtima. Kawirikawiri ali osacimwa, anthu abwino amene amabvutika ndi macitidwe oipa a ena. Iwo angacitiridwe mwaciwawa, kapena kuonongeredwa nyumba zao, okondedwa ao kapena ngakhale miyoyo ya iwo eni. Inu mungakhale mutaziona zinthu zimenezo kapena simunazione zikukucitikirani inuyo. Ngakhale ngati simunakumane nazo, koma inu mosalephera munakumana ndi zinthu zimene zinacititsa kubvutika kwa maganizo, zokumana nazo zonga ngati kusacitiridwa molungama, kusakomeredwa mtima, kupusitsidwa kapena kunyengedwa.

2. Kodi zifukwa zace zimene Mulungu wakulolera kuipa zikuphatikizamo nsonga zimene zinadzutsidwa pa nthawi iti?

2 Ncifukwa ninji Mulungu wakulola kuipa koteroko kufikira m’tsiku lathu? Pali zifukwa zambiri, koma kuti tizizindikire zifukwa zimenezo bwino lomwe ife tiyenera kuzipenda zinthu zimene zinabuka pa nthawi ya cipanduko coyambiriraco. Inu mwina mwace munaciwerenga colembedwa ca ici m’Baibulo m’mutu wacitatu wa Genesis. Pamenepo, tiyeni tilingalire za tanthauzo lenileni la zocitika izi.

3. Mwachidule tacilongosolani cimene cinacitika pa nthawi imene munthu analowa m’kucimwa.

3 Mwacidule, ici ndico cimene cinacitika: Yehova anamuuza munthu kuti moyo wace unadalira pa kumvera kwa Mlengi wace, ndi kuti kusamvera kukanadzetsa imfa. (Genesis 2:17) Mdani wa Mulungu, Satana, anakasokoneza kalongosoledwe komvekera bwino aka. Iye anamuuza mkazi wa Adamu kuti anthu awiri oyambawo akanakucita kusamvera ndipo cikhalirebe “Kufa simudzafai.” Iye anaonjezera kunena kuti kusamvera kumeneko kudzazipititsa patsogolo zinthu kwa iwowo, kumawacititsa maso awo kutsegulidwa, ndi kuti iwo adzakhala ofanana ndi “Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4, 5) Tsopano kodi ndi ciani cimene cinaphatikizidwamo mu kacitidwe aka kopanduka ka Satana?

NSONGA ZOFUNIKAZO

4. Tazichulani nsonga zina zimene zinadzutsidwa ndi cipanduko ca Satana Mdierekezico.

4 Nsonga zingapo kapena mafunso ofunika anadzutsidwa. Coyamba, Satana anakukaikira kunena zoona kwa Mulungu. Mwa kutero, anamucha Mulungu kukhala wabodza, ndipo ici cinacitikira pa nkhani yofunika kwambiri. Caciwiri, iye anakukaikira kudalira kwa munthu pa Mlengi wace kaamba ka moyo wosalekeza ndi cimwemwe. Iye ananena kuti moyo wa munthu kapena kukhoza kwace kwa kuzitsogoza zocitika zace mwacipambano sizinadalire pa kumvera Yehova. Iye ananena kuti munthu akadatha kucita mwa yekha osadalira pa Mlengi wace ndi kukhala wonga ngati Mulungu, akumadzisankhira yekha cimene ciri coyenera ndi colakwika, cabwino ndi coipa. Cacitatu, mwa kumatsutsana ndi lamulo lolongosoledwa ndi Mulungu, iye mwa kutero anasonyeza kuti njira ya Mulungu ya kalamuliridwe iri yolakwa ndipo osati yozipindulitsa zolengedwa zace ndipo mwa njira iyi iye anakutokosa kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira.

5. Monga momwe kwasonyezedwera m’bukhu la Baibulo la Yobu, kodi ndi nkhani ina iti imene inadzutsidwa ndi Satana?

5 Koma macitidwe a Satanawo analidzutsabe funso lina, monga momwe kwasonyezedwera pambuyo pace m’Baibulo m’bukhu la Yobu, mutu 1 ndi 2. Pamenepo, ponena za munthu wochedwa Yobu, kukusonyezedwa kuti Satana anakukaikira kukhulupirika ndi kumvera Yehova Mulungu kwa zolengedwa zonse. M’mau ambirimbiri, Satana ananena kuti awo amene amatumikira Mulungu amamtumikira, osati cifukwa cakuti amamkonda Mulunguyo ndi kulamulira kwace kolungama, koma kokha cifukwa ca zifukwa zadyera, monga ngati madalitso a zinthu zakuthupi zimene Mulungu amawapatsa iwo. Iye ananena kuti, ngati zifukwa zimenezo zinacotsedwa, pamenepo ngakhale munthu wonga ngati Yobu akadafufunuka kucoka kwa Mulungu. (Yobu 1:6-11; 2:4, 5) Inde, cipanduko ca Satana mu Edene cinakupangitsa kukhala kokaikitsa kumvera kwa zolengedwa zonse za Mulungu kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ngati ziyesedwa, kodi izo zidzacitsimikizira cikondi cao kwa Atate wao wakumwambayo ndi kusonyeza kuti iwo anasankha kulamulira kwace koposa ndi kwa wina aliyense?

NJIRA YA MULUNGU YA KUITHETSERA NKHANIYO

6. Kodi Satana anaikaikira nyonga ya Mulungu? Cotero kodi ndi nkhani ya mtundu wanji imene inayenera kuthetsedwa?

6 Conde, taonani kuti Satana sanacipereke cikaikiro ciriconse ponena za nyonga ya Mulungu. Iye sanamtokose Yehova kuti aigwiritsire nchito mphamvu yace kuti amuononge iye monga wotsutsana naye. Koma iye anakutokosa kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira ndi ubwino wa njira yace ya kalamuliridwe. Ndiponso, iye anakukaikira kumvera kwa zolengedwa za Mulungu. Cotero inali nkhani ya cikhalidwe ca mtima imene inayenera kuthetsedwayo.

7. Tacilongosolani citsanzo cimene cimasonyeza za mmene nkhani ya khalidwe la mtima yoteroyo ingathetsedwere.

7 Zinenezo zonama za Satana zotsutsana ndi Mulungu zingacitiridwe fanizo, mwa njira yina, mwaumunthu. Tangolingalirani kuti munthu wokhala ndi banja lalikuru kwambiri akunenezedwa ndi mmodzi wa anthu okhala cifupi naye za zinthu zambiri zonama ponena za njira imene amalisamalirira banja lacelo. Tangolingaliraninso kuti munthu wokhala cifupi nayeyo akunena kuti mamemba a m’banjamo alibe cikondi ceniceni kaamba ka atate waoyo koma amangokhala naye kokha kuti azipeza cakudya ndi zinthu zakuthupi zimene iye amawapatsa iwo. Kodi ndi motani mmene atate wa banjalo angaziyankhire zinenezo zoterozo? Ngati iye angogwiritsira nchito kacitidwe ka ciwawa kulimbana ndi wonenayo, kuteroko sikudzaziyankha zinenezozo. M’malo mwace, kungakhale ngati kuti zinali zoona. Koma kodi ndi yankho labwino cotani mmene likanakhalire ngati munthuyo analilola banja lacelo kuti likhale mboni zace kusonyeza kuti atate waoyo analidi mutu wa banja wolungama ndi wacikondi ndi kuti iwo ali okondwa kukhalira naye limodzi cifukwa cakuti iwo amamkonda iye! Motero iye angatamandidwe kotheratu.—Miyambo 27:11; Yesaya 43:10.

8. Kodi nciani cimene casonyezedwa m’kacitidwe ka Mulungu pa kumaipereka nthawi yokwanira kuti nkhaniyo ithetsedwe mopanda cikaikiro ciriconse?

8 Ici cikupereka citsanzo mwa njira yina ca zimene Mulungu wazicita. Kuonjezerapo, iye wailola nthawi yokwanira—tsopano zaka cifupifupi 6,000—kuti nkhaniyo ithetsedwe mosasiya cikaikiro ciriconse. Iye waipereka nthawi iyi, osangoti kokha kuti azilole zolengedwa zace zokhulupirika kuti zikutsimikizire kudzipereka kwao kwa iye ndi kulamulira kwace, komanso kuti asonyeze kuti mtundu uliwonse wa kulamulira umadzetsa kuipa kokha basi. (Miyambo 1:30-33; Yesaya 59:4, 8) Mwa kumampandukira Yehova Mulungu, Satana anadzikhazikitsa iye mwini monga wolamulira mopikisana. Ndipo, mwa kumakatsatira kacitidwe kamene kananenedwa ndi Satanako, anthu awiri oyambawo anadzilengeza okha kukhala osadalira pa kulamulira kwa Yehova ndipo anakhala mu ciyang’aniro ca Satana. (Genesis 3:6; Aroma 6:16) Mulungu pakumalola ponse pawiri Satana ndi munthu kukucita kuyesayesa kwao konse kwa kucita zinthu ndi kudzilamulira okha osalamulidwa ndi Mlengi wao, kulephera kwao konse kuturutsa boma labwino, lokhala ndi mapindu enieni kaamba ka mtundu wonse wa anthu kudzapangidwa kukhala umboni umene sudzatsutsidwanso konse mtsogolomo. Pa nthawi yino Yehova akawapangitsa awo a pa dziko lapansi amene amamkonda iye kulengeza dzina lace ndi zifuno zace kaamba ka kuwasonyeza njira awo onse amene amacikonda ndi kumacifunafuna cimene ciri coyenera.

9. Kodi nciani cimene Mulungu anamuuza Farao wa ku Igupto cimene ciri cofanana ndi mmene zinthu zakhalira kwa Satana Mdierekezi?

9 Cotero, mkhalidwewo uli wofanana ndi uja umene unamlowetsamo Farao wa ku Igupto amene anakatsatira kacitidwe kofanana ndi ka satana Mdierekezi m’kutsutsana ndi Yehova Mulungu, amene Yehova anamuuza kuti: “Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke pa dziko lapansi. Koma ndithu cifukwa cace ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.”—Eksodo 9:15, 16.

KODI ZOTSATIRAPO ZASONYEZANJI?

10. Kodi ndi motani mmene Satana waigwiritsirira nchito nthawi imene yaperekedwa ndi Mulungu ponena za kumwamba ndi dziko lapansi?

10 Baibulo limasonyeza kuti Satana waigwiritsira nchito nthawiyo kulimanga gulu kumwamba ndi pa dziko lapansi pa limene iye akulamulirapo. Ukulu wa kulamulira kwace dziko lapansi wasonyezedwa mwa ceniceni cakuti iye anamlonjeza Yesu kumpatsa maufumu onse a dziko lapansi kuti asinthanitsane ndi kulambira kwa Yesu. (Mateyu 4:8, 9) Ici ndico cifukwa cace Satana akuchedwa “wolamulira wa dziko ili lapansi.” (Yohane 16:11, NW) Kodi ici catanthauzanji kwa mtundu wa anthu, ndipo kodi nciani cimene cakhala coturukapo ca kacitidwe ka munthu kodalira pa iye mwini osadalira pa Mulungu ndi kulamulira kwace?

11. Kodi nciani cimene cakhala coturukapo comvetsa cisoni ca kacitidwe ka munthu ka kucita mwa iye yekha osadalira pa Mulungu ndi kulamulira kwace?

11 Mbiri yakale imapereka umboni wa ceniceni cakuti ici sicinadzetse mtendere, cikhutiro ndi moyo wamuyaya kwa mtundu wa anthu. Cadzetsa zosiyana ndi zimenezo: zaka zikwi zikwi za kumva ululu, kusauka ndi imfa. Zolembedwa za mbiri yakale ndi mkhalidwe wa zinthu wocititsa mantha m’dziko lerolino ziri umboni wakuti munthu sanacite mwacipambano m’kumalamulira popanda cithandizo ca Mulungu. Anthu awayesayesa maboma a mitundu-mitundu, koma akusowabe cisungiko ndi cimwemwe cokhalitsa. Zoonadi, kwakhalapo kupita patsogolo mu zinthu zakuthupi. Koma kodi kulidi kupita patsogolo pamene anthu amatumiza maroketi ku mwezi, ndipo komabe sangakhalire limodzi mumtendere pa dziko lapansi? Kodi zingakhale zopindulitsa motani kwa iwo kuzimanga nyumba zokhala ndi zinthu zirizonse zimene moyo umazifuna, koma mabanjawo ndi kumasweka mwa cisudzulo ndi kupulupudza? Kodi zinkhondo, zopolowe m’makwalala, kuonongedwa kwa moyo ndi Cuma ndi kufala kwa kusamvera malamulo ziri zinthu za kuzinyadira? Kutalitali! Koma izo ziri zipatso za ulamuliro umene umamnyalanyaza Mulungu. Zoonadi, monga momwe Mlaliki 8:9 amanenera, “wina apweteka mnzace pomlamulira.”

12. (a) Kodi nciani cimene mlembi wochuka ananena ponena za coputira kupanda cimwemwe pa dziko lapansi? (b) Malinga ndi kunena kwa mneneri Yeremiya, kodi munthu angawatsogolere mapazi ace mwacipambano iye yekha?

12 Cotero Mulungu pa kumakulola kuipa kukhalapobe kwa nthawi yaitali kwatsimikizira mopanda cikaikiro kuti kuyerekeza kwa munthu kwa ‘kukhala Mulungu’ kwalephereka momvetsa cisoni. (Salmo 127:1 [126:1, Dy]) Monga momwe mlembi wina wochuka ananenera kuti: “Pamene tilimbikira kufunafuna codzikhululukira, ndi pamene timaturukira kuti kupanda cimwemwe pa dziko lapansi kuli kopangidwa ndi anthu. Colephera cathu cacikuru ndico cakuti ife sitinacithetse cothetsa nzeru conena za boma lodzilamulira.”a Mlembi wa Baibulo wouziridwa Yeremiya moyenerera ananena kuti: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ace. Yehova, mundilangize.”—Yeremiya 10:23, 24; onaninso Miyambo 16:25.

13. Popeza kuti kulamulira kwa Satana kwatsimikizira kukhala kolephera, kodi Mulungu adzakhala akucita molungama kotheratu pa kucita ciani?

13 Cisonkhezero ca Satana pa zocitika za pa dziko lapansi cadzetsa kusagwirizana, kuipa ndi imfa, ndipo kulamulira kwace kwakhala mwanjira ya cinyengo, kukakamizira ndi dyera. Iye wadzitsimikizira iye mwini kukhala wosayenera kukhala wolamulira wa ciriconse. Cotero Yehova tsopano waonekeratu kukhala wosalakwa pa kumuononga wopanduka wonyansa uyu limodzi ndi awo onse amene akhala ndi phande mu kuipa kwaceko. (Aroma 16:20) Koma bwanji ponena za kumvera kwa zolengedwa za Mulungu ku kulamulira kwa Yehova kwacikondiko ndi kudzinenera kwa Satana kwakuti onse angabwerere m’mbuyo ngati angayesedwe?

14. (a) Kodi ndi mosonkhezeredwa ndi maganizo abwino otani mtundu wa anthu wamtumikira Mulungu mofunitsitsa? (b) Yobu pakumausunga umphumphu wace kwa Mulungu mosasamala za citsutso cocokera kwa Satana, kodi Yobu anamtsimikizira Mdierekezi kukhala ciani?

14 Yehova Mulungu anadziwa kuti “cikondi sicimalephera konse” ndipo anadziwa kuti ena a mwa mtundu wa anthu adzamtumikira iye mwa kufuna kwao, mocokera m’cikondi, koma osati cifukwa cakuti anali kupatsidwa psyete kapena kukakamiziridwa. (1Akorinto 13:8) Zikwi zikwi zambiri zacicita ici kupyolera mu zaka mazana-mazana zimene zapitazo. Yobu anali mmodzi wa amenewa. Ngakhale kuli kwakuti Satana anadzetsa citsenderezo cacikuru pa iye ndi kumlanda zace zonse mbembembe, ana limodzi ndi thanzi labwino, Yobu ananenabe kuti: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” (Yobu 27:5) Yobu anamtsimikizira Satana kukhala wabodza.

15. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu anaciyankhira citokoso conyenga ca Satana cotsutsana ndi Yehova? (b) Kodi Adamu wangwiroyo akadakhala wokhulupirika mokwanira kwa Mulungu?

15 Monga momwe taonera, munthu wangwiroyo Yesu anazikana ziyeso zonse za Satana limodzi ndi mapsyete. Kuonjezerapo, pamene anakwapulidwa ndi akalinde nakhomeredwa ku mtengo wozunzirapo mwankharwe kuti afe, Yesu anakusungabe kumvera kwace kwa Mulungu. (1 Petro 2:23) Ici cinatsimikizira kuti Adamu wangwiroyo akadacitanso cimodzimodzi ngati akadafuna kutero, ndi kuti sikuti Mulungu anali wosalungama pa kumakufuna kumvera kokwanira kucokera kwa munthu. (2 Atesalonika 1:4, 5) Mwa kumvera kwace kwa Yehova, Yesu analipereka yankho labwino kopambana ku manenanena onyenga a Satana.

16. (a) Ngakhale kunali kwakuti anatsimikiziridwa kukhala wabodza, ncifukwa ninji Satana amapitirizabe kumawazunza okonda Mulungu? (b) Kodi kumvera kwa atumiki okhulupirika a Mulungu kuli umboni wokhutiritsa maganizo wotani?

16 Koma Satana, maganizo ace pokhala atasokonezeka ndi dyera ndi kunyada, wakana kuti akasiye kacitidwe kace kamisalako. Ngakhale kuli kwakuti kwa nthawi yaitali kwatsimikiziridwa kuti iye anacimwa ndipo ali wabodza, iye amapitirizabe kuwazunza okonda Mulungu. (Cibvumbulutso 12:17) Kuyambira pa imfa ya Yesu Akristu zikwi zambiri amtumikira Yehova Mulungu cifukwa cakuti amamkonda iye ndipo anafuna kulamulira kwace kwacikondi kuti kukhale pa iwo. Ndipo pa tsopano lino, zikwi mazanamazana zikukulengeza kukhala kwao omvera kwa Yehova monga wolamulira wao. (Cibvumbulutso 7:9, 10) Kusunga kwao mokhulupirika Mau a Yehova ndi kulimvera kwao lamulo lace kwawatheketsa iwo kukhala mwacikhutiro, mosasamala za citsutso conse cocokera kwa Satana. Umodziwo, cikondi ndi kusunga umphumphu zimene zinasonyezedwa ndi atumiki a Mulungu mu zaka zonse mazanamazana zapitazo zikupereka umboni waukuru kwambiri wakuti njira ya Yehova ya kalamuliridwe m’cikondi ndiyo njira yokha yoyenera, kuti munthu angakhalebe womvera kwa iye ngakhale ayesedwe kwakukurukuru, ndi kuti Satana ali wabodza wamkuru kopambana wa mu nthawi zonse.

KODI CIYESOCO CIDZAPITIRIZABE KWA UTALI WOTANI?

17. Kodi Mulungu adzakulola kuipa kosatha, ndipo kodi ndi motani mmene bukhu la Baibulo la Danieli limaliyankhira funso limenelo?

17 Yehova wakulola kuipa kufikira m’tsiku lathu m’malo mwakuti aithetse mikangano yonse imene inadzutsidwa ndi Satana. Koma iye sadzakulola kuipa kupitirizabe kosatha. Iye waikhazikitsa nthawi yotsimikizirika pamene adzakuthetsa uko. Mlembi wa Baibulo Danieli ananena za ici kale kale pamene iye analemba kuti: “Kutha kwace kudzakhala pa nthawi yoikika.”—Danieli 11:27.

18. Ngakhale kuli kwakuti nyengo ya nthawi ya zaka cifupifupi 6,000 imaonekera kukhala yaitali kwa munthu, kodi iyo imaonekera kukhala yaitali kwa Mulungu? Cotero kodi Mulungu amaziona zaka cikwi kukhala ngati ciani?

18 Zaka cifupifupi zikwi zisanu ndi cimodzi kuyambira m’tsiku la Adamu kudzafika m’tsiku lathuli zingaonekere kukhala nthawi yaitali pamene tilingalira mu kalingaliridwe kaumunthu ka anthu amene amangokhala cifupifupi kwa zaka makumi asanu ndi awiri okha. Koma popeza kuti Mulungu anaika malire a nthawi, kuli bwino kukazindikira kalingaliridwe kace pa nkhaniyo. Mneneri Mose, pa Salmo 90:4 [89:4, Dy], ponena za iyeyo amati: “Pakuti pamaso panu zaka cikwi zikhala ngati dzulo, litapita.” Caka cimakhala nthawi yaitali kwambiri kwa mwana wa zaka zisanu, koma kwa munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi iyo imakhala nthawi yaifupi. Kulinso cimodzimodzi ndi Yehova, amene amakhala kwamuyaya, zaka cikwi ziri monga ngati tsiku limodzi.—2 Petro 3:8.

19. Ncifukwa ninji kacitidwe ka Mulungu ka kukulola kuipa sikanakhale kacitidwe ka kupanda cilungamo pa ife?

19 Nthawi yokhazikitsidwa iyi mkati mwa imene kuipa kwaloledwa sinakhale kacitidwe kopanda cilungamo kulinga kwa ife. Eya, ngati Mulungu akanautswanyiratu moyo wa onse opandukawo mu Edene, ife sitikanabadwa konse! Ife sitikanakhala nao mwai wa moyo wamuyaya mu dongosolo lace latsopano. Cotero ceniceni cakuti Yehova sanakufupikitse kupirira kwace pa nthawi yoyambirirayo caipatsa ife mwai wa kukhala ndi moyo tsopanolino, ndi kukhala kwamuyaya mtsogolomo. (2 Petro 3:9, 15) Ndiponso, Mulungu waigwiritsira nchito nthawi iyi kuti apereke ciombolo kwa anthu kupyolera mwa Kristu.—Agalatiya 4:4, 5.

20. Kodi ndi motani mmene Baibulo pa Aroma 9:22-24 limalongosolera cifukwa cace Mulungu wakulola kuipa?

20 Kuonjezerapo, Mulungu waigwiritsira nchito nthawiyo kuti azisankhe ndi kuzilinganiza kucokera pakati pa mtundu wa anthu “zotengera zacifundo.” Awa ndiwo amene adzalipanga boma lolungama lomawalamulira awo amene adzakhala kosatha pa dziko lapansi mu dongosolo latsopano. Ha, ndi madalitso otani nanga amene ufumu wakumwamba umenewu umatanthauza kwa mtundu wa anthu! Mkati mwa nthawi imene Mulungu wakhala akulinganiza “zotengera zacifundo” zimenezo, iye wasonyeza cipiriro cacikuru. Iye wawalekerera oipa, “zotengera za mkwiyo.” Iye wacisunthira mtsogolo cionongeko cao. Cifukwa ninji? Baibulo limayankha momvekera bwino: “Kuti iye akadziwitse ulemerero wace waukuru pa zotengera zacifundo.” (Aroma 9:22-24) Ku ufumu wa Mulungu wakumwambawo kudzapita ulemerero wa kutamanda dzina la Mulungu ndi kuwaononga oipa, “zotengera za mkwiyo.” Ndiponso, mwa kumakulola kuipa kupitirizabe kwa kanthawi, mbali zosiyanasiyana za khalidwe la Mulungu zikusonyezedwa zimene sizikanazindikiridwa mwa wamba: cifundo cace ndi kupirira. Izi zimakukuza kumzindikira kwathu Mlengiyo limodzi ndi makhalidwe athu, pamene timtsanzira iye.—Aefeso 5:1.

21. Kodi ndi phindu lina lotani limene ladza mwa kacitidwe ka Mulungu ka kumakulola kuipa kukhalapobe kwa nthawi yace yonse yoperekedwa?

21 Pakhalaponso phindu lenileni lina mu kacitidwe ka Mulungu ka kumakulola kuipa kwa nthawi yaitali monga momwe wacitira. Ngati pa nthawi iriyonse mtsogolomo aliyense adzaisuliza njira ya Mulungu ya kucitira zinthu, sikudzakhalanso koyenera kwa iye kumpatsa ameneyo nthawi yakuti nayenso ayese kucitira mu njira yina. Colembedwa ca zaka zikwi zisanu ndi cimodzi za kulephera kwa Satana, ziwanda zace, limodzi ndi anthu amene ayesa kuziyendetsa zinthu mosadalira pa Mulungu capereka yankho lokwanira. Palibe aliyense amene moyenerera anganene kuti: ‘Iwo sanapatsidwe mwayi,’ kapena kunena kuti, ‘Koma akadawapatsa nthawi yokwanira.’ Nthawi imene yaperekedwayo yakhala yokwanira kutsimikizira kuti njira ya cipanduko motsutsana ndi Mlengiyo yakhala yatsoka kwakukurukuru! Cotero Mulungu adzalungamitsidwa kwakukurukuru pa kumamtswanya mwamsanga wopanduka aliyense amene adzayesa kuuononga mtendere wamtsogolomo wa mu cilengedwe caponseponse.—Salmo 145:20 [144:20, Dy].

22. Kodi Yehova adzakulola kuipa kukhalabe kwa utali wotani, ndipo kodi ndi mwai wotani umene nthawi yotsalirayo imatipatsa ife?

22 Pali nthawi yaifupi cabe imene yatsala Yehova asanaliononge dongosolo loipa ili la zinthu. Nthawi yotsalayi imatipatsa ife mwai wakuti tiimire kumbali yace ndi kuupangitsa ‘mtima wace kusangalala.’ (Miyambo 27:11) Ngati ife tigonjera ku kulamulira kwace mwa kufuna kwathu, iye adzatidalitsa ife ndi moyo wamuyaya mu dongosolo lace tsopano la zinthu. Cosankha ca kuulandira kapena kuukana caikidwa pamaso pa aliyense wa ife.—Deuteronomo 30:19, 20.

23. (a) Kodi ndi motani mmene tiyenera kukuonera kumvera kwa Mulungu? (b) Atumiki okhulupirika a Mulungu ataicita nchito ya kulengeza dzina lace ndi zifuno zace m’dziko lonse lapansi, kodi nciani cimene Yehova adzacicita?

23 Kumvera Mulungu sikuli kobvuta kwenikweni. Ngati tizindikira kuti nzeru ya Yehova iri yaikuru kwambiri koposa yathu, ndi kuti ciriconse cimene iye amacicita ciri kaamba ka ubwino wathu cifukwa cakuti iye ali Mulungu wacikondi, pamenepo tidzamumvera iye mu ciriconse. Ciriconse cimene cingakhale cifuniro ca Yehova, ife tidzafuna kucicita ico, kaya mukhale mu nthawi zobvuta kapena mu zinthu zatsiku ndi tsiku za moyo. Imeneyo ndiyo njira imene atumiki okhulupirika a Mulungu akhala akumalingalirira kwa nthawi yonse. (Danieli 3:16-18; Salmo 119:33-37 [118:33-37, Dy]) Mu zaka za zana loyamba ena a amenewa analiuza khothi lalikuru kuti; “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Macitidwe 5:29) Lerolino, Yehova akugwiritsira nchito atumiki ace okhulupirika kulilengeza dzina lace ndi zifuno zace pa dziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Pamene cimeneco cicitidwa adzamsonyeza Satana mphamvu yace yonse mwa kumtswanya iye limodzi ndi opanduka ena onsewo, kumalithetsa dongosolo loipa ili. Motero, Yehova adzaciyeretsa cilengedwe caponseponseci kucicotsera kuipa konse ndi kuliswa bande la dongosolo lace latsopano lolungama.

[Mawu a M’munsi]

a David Lawrence, U.S. News & World Report, Sept. 25, 1967, tsamba 128.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena