Mutu 11
Masiku Otsiriza a Dongosolo Ili la Zinthu
1. Kodi ndi liti pamene “masiku otsiriza” anayambika, ndipo kodi iwo adzatha limodzi ndi cocitika?
BAIBULO limalankhula za nthawi mu imene tikukhalamo ino kukhala “masiku otsiriza” kapena “nthawi yotsiriza.” (2 Timoteo 3:1; Danieli 11:40) Zenizenizo zimasonyeza kuti iyi iri nyengo ya nthawi yokhala ndi polekezera imene iri ndi ciyambi cace cotsimikizirika ndiponso mapeto ace otsimikizirika. Iyo inayambira mu 1914 pamene Yesu Kristu anaikidwa pa mpando monga mfumu kumwamba. Iyo idzathera pamene Mulungu adzaliononga dongosolo loipa la zinthu limene liripoli. Kodi ndi citonthozo cotani nanga mmene ici cidzakhalira pamene magulu ndi anthu amene amanyenga ndi kutsendereza, ndi onse amene amaciika paupandu cisungiko ca anthu anzao, adzakhala atatheratu!
2. Kodi nciani cimene Yesu ananena pa Mateyu 24:34 ponena za pamene “nthawi ya mapeto” imeneyo idzathera?
2 Kodi nanga ndi liti pamene zimenezo zidzacitika? Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, amapereka yankho lace. Iye atanena za zinthu zambiri zimene zimaidziwikitsa nyengo yoyambira pa 1914 kunkabe mtsogolo kukhala “nthawi yamapeto,” Yesu anati: “Mbadwo uno sudzatha kucoka, kufikira zinthu zonsezi zidzacitidwa.” (Mateyu 24:34) Kodi ndi mbadwo uti umene iye anautanthauza?
3. (a) Kodi ndi mbadwo uti umene Yesu ananena kuti sudzatha kucoka mapeto asanafike? (b) Cotero kodi tingadziwe bwanji kuti tiri pafupi kwenikweni ndi mapeto a dongosolo loipa ili la zinthu?
3 Yesu anali atangotha kunena za anthu amene ‘adzaona zinthu zonsezi.’ “Zinthu zonsezi” ziri zocitika zimene zacitika ciyambire 1914 ndi izo zimene ziyenerabe kucitika kufikira kumapeto a dongosolo loipa ili la zinthu. (Mateyu 24:33) Anthu amene anabadwa ngakhale zaka makumi asanu zapitazo sakanatha kuona “zinthu zonsezi.” Iwo anabadwa pa nthawi imene zinthu zonenedweratuzo zinali zitayamba kale kucitika. Koma pali anthu amene akali cikhalirebe amoyo amene anali amoyo mu 1914 ndipo anaona zimene zinali kucitika pa nthawi imeneyo ndi amene anali acikulire mokwanira kwakuti iwo amazikumbukirabe zocitika zimenezo. Mbadwo umenewu ukukalamba kwambiri tsopano. Ambiri a iwo amwalira kale. Komabe Yesu motsimikizira anati: “Mbadwo uwu sudzatha kucoka kufikira zinthu zonsezi zidzacitidwa.” Ena a iwo adzakhala ali moyo kuti awaone mapetowo a dongosolo loipa ili. Ici cikutanthauza kuti iri nthawi yaifupi yokha imene yatsala mapeto asanafike! (Salmo 90:10 [89:10, DY]) Cotero ino ndiyo nthawi yakuti mucitepo kanthu mwamsanga ngati simufuna kusesedwa limodzi ndi dongosolo loipa ili la zinthu.
CIFUKWA CACE PALI “NTHAWI YA MAPETO”
4. (a) Ncifukwa ninji tingakhale osangalala kuti Mulungu sanaononge mwamsanga awo amene sanali kumtumikira iye pamene ufumu wace unayamba kulamulira mu 1914? (b) Kodi ndi motani mmene Baibulo, pa 2 Petro 3:9, limatithandizira ife kuilingalira nkhani iyi moyenerera?
4 Ngakhale kuli kwakuti Ufumuwo unayamba kulamulira mu 1914, Yehova sanawaononge mwamsanga awo amene sanali kumtumikira iye. Ndi acimwemwe cotani nanga mmene tingakhalire za cimeneco! Pakuti cipiriro ca Mulungu catitheketsa ife kukhala ndi mwai wa kuimira molimba ku ufumu wace, ndipo motero kucipulumuka cionongeko. Baibulo limatithandiza ife kuilingalira nkhani imeneyi mu njira yoyenera, likumati: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike ku kulapa.”—2 Petro 3:9; onaninso Mateyu 24:21, 22.
5. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu anailongosolera nchito ya kulekanitsa imene iye adzaicita pa nthawi iyi? (b) Kodi nciani cimene cidzacitikira awo amene adzalandira cilango pakutha pa “masiku otsiriza” amenewa?
5 Mwa colinga ici, Yehova Mulungu wapereka nthawi kaamba ka nchito ya kulekanitsa mkati mwa “masiku otsiriza” awa. Pamene anali kulongosola za “mathedwe a nthawi ya pansi pano,” Yesu ananeneratu izi, kumati: “Pamene Mwana wa munthu [Yesu Kristu] adzadza mu ulemerero wace, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa cimpando ca kuwala kwace: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pace anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzace, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lace lamanja, koma mbuzi kulamanzere. Pomwepo mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lace lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa cikhazikiro cace ca dziko lapansi: . . . Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Cokani kwa Ine otembereredwa inu, ku moto [wa cionongeko] wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ace: . . . Ndipo amenewa adzacoka kumka ku cilango ca nthawi zonse; koma olungama ku moyo wa nthawi zonse.” (Mateyu 25:31-46) Pamene ciweruzo cikuperekedwa pa mapeto a “masiku otsiriza” awa, oonongedwawo adzalowa mu ‘kudulidwa kosatha.’ Sipadzakhala kubwerera ku moyo mwa ciukiliro kwa iwowo. (2 Atesalonika 1:7-9) Cotero tsopano, mkati mwa “masiku otsiriza” awa, Mulungu mwacifundo wawapatsa anthu kulikonse mwai wa kusankha kuimira ku mbali ya ufumu wace ndi kukhala ndi moyo.
6. (a) Kodi nchito ya kulekanitsayo ikucitidwa motani? (b) Cotero, kodi nciani cimene tiyenera kucicita tsopano ngati tifuna moyo m’kulamulira kwa ufumu wa Mulungu?
6 Kodi ndi motani mmene Mulungu amacicitira cimeneci? Kodi ndi motani mmene nchito ya kulekanitsayo ikucitidwira? Mwa citsogozo ca angelo atumiki okhulupirika a Mulungu pa dziko lonse lapansi amaubukitsa uthenga wa ufumu wa Mulungu kotero kuti anthu oona mtima angamve ndi kucitapo kanthu. Iyiyo ndiyo mbali ya “cizindikiro” comasonyeza za kuyandikira kwa mapeto, akumati: “Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10; onaninso Mateyu 24:14 ndi Cibvumbulutso 14:6, 7.) Pa maziko a mamvetseredwe ao ku uthenga umenewu, ndipo pa malingaliridwe ao kulinga kwa awo amene Yehova amawagwiritsira nchito monga amithenga ace, anthuwo amaweruzidwa kaya ngati adzasungidwa amoyo kapena ai. (Mateyu 25:40, 45) Ngati mufuna moyo mu ufumu wa Mulungu, kuli kofunika kuti mucisonyeze cimeneco tsopanolino mwa kumabvomereza mwaciyanjo ku uthenga wa Ufumuwo ndi kumawauzanso ena kuti atero. Mtsogolomu posacedwapa nchito ya kulalikira imeneyi idzatha. Khomo la mwai lidzatsekedwa. Pamenepo nthawi idzakhala itatha!—Ezekieli 33:8, 9.
NDANI AMENE ADZAONONGEDWA?
7. Kodi ndi motani mmene Yeremiya 25:33 amawalongosolera mapeto a dongosolo loipa ili la zinthu, ndipo kodi ndi motani mmene Baibulo limatithandizira ife kuti tikupewe kukhala pakati pa awo amene adzaphedwawo?
7 M’mau omvekera bwino Malemba amabvumbula kuti, pamene dongosolo loipa ili lifika pa mapeto ace, “Akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi.” (Yeremiya 25:33) Koma inu simufunikira kukhala pakati pa akuphedwawo. M’Mau ace Baibulo Mulungu amalongosola momvekera bwino za mtundu wa anthu, ndi magulu amene adzaonongedwa. Pokhala atacenjezedweratu, anthu amene amafuna moyo, ndi amene amafuna kucita coyenera moona mtima pamaso pa Mulungu, angaturuke m’malo aupanduwo.
8. (a) Kodi ndani amene Mulungu amanena kuti adzaonongedwa? (b) Kodi ndi anthu a mtundu wotani amene Mulungu amawacha oipa? Kodi angazisinthe njira zaozo?
8 Cotero pamenepo, kodi ndani amene Mulungu amanena kuti adzaonongedwa? Monga mmene tikuyembekezerera, ali oipa. “Pophukira oipa ngati msipu, ndi popindula ocita zopanda pace; citero kuti adzaonongedwa kosatha.” (Salmo 92:7 [91:8, Dy]) Koma tiyeni tisasoceretsedwe mwa kumakatenga kalingaliridwe ka dziko ponena za cimene ciri colungama ndi cimene ciri coipa. Mulungu momvekera bwino amatiuza ife kuti zinthu zambiri zimene dziko ili limazilingalira kukhala zofala ndizo zimene ziri zoipa m’maso mwace. Dama, cigololo ndi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha zingaloledwe ndi anthu amakono, koma awo amene amazicita zinthu zimenezo sadzasiyidwa amoyo ndi Mulungu pa mapeto a dongosolo ili la zinthu. Moteronso, awo amene ali abodza, akuba oledzera ndi akupha sadzaloledwa kukhala mu ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10; Cibvumbulutso 21:8) Ena angakhale akumacita zimenezo cifukwa ca atsamwali ao oipa. Koma tsopano, podziwa zimene Mulungu amanena, kuli kofunika kwa amenewa kusintha njira zao ngati afuna kupewa cionongeko. Mu dongosolo latsopano la Mulungu simudzakhala malo kaamba ka anthu amene amacita monyenga ndi amene amauika pa upandu moyo wa anthu anzao.
9. (a) Kodi nciani cimene cidzacicitikira cipembedzo cimene cazikidwa pa cinyengo, ndipo ncifukwa ninji? (b) Ngati ife sitifuna kuwerengeredwa kukhala pakati pa adani a Mulungu amenewo, kodi tiyenera kucitanji?
9 Ndiponso simudzakhala magulu alionse amene amasoceretsa anthu. Ife tamva kale kucokera m’Baibulo kuti siziri zipembedzo zonse zimene zimabvomerezeka ndi Mulungu. Cotero sikuyenera kutidabwitsa ife kuti cipembedzo cozikidwa pa cinyengo cidzatheratu. Gulu lacipembedzo lingakhale ndi nyumba zabwino limodzi ndi kapempheredwe kokometseredwa, koma ngati sicimaphunzitsa coonadi conena za Mulungu ico ndithudi cimatumikira cifuno ca mdani wa Mulungu, Satana Mdierekezi. (1 Akorinto 10:20; 2 Akorinto 11:13-15) Ico cingayese kuwagwiritsira nchito Mau a Mulungu, koma ngati cifunafuna kukhala mbali ya dziko ili mwa kumakhala ndi phande pa zinthu za dziko ili, pamenepo, monga momwe Baibulo limalengezera, ico cifikira kukhala pa “udani ndi Mulungu.” (Yakobo 4:4,; Yohane 15:19) Kodi ife timafuna kuwerengedwa kukhala pakati pa adani a Mulungu? Ngati sitifuna, kuli kwa ife kutsimikizira kwa Mulungu tsopano kuti ife sitikugwirizana nazo, kuti timakondweretsedwa kokha m’coonadi ndi kuti ife enife timakucita kulambira kumene kuli ‘koyera ndi kosadetsedwa pamaso pa Mulungu ndi Atateyo.’—Yakobo 1:27.
10. (a) Kodi ncifukwa ninji Mulungu adzaononga dongosolo lonse la ndale za dziko limene liri pa dziko lapansi? (b) Cotero, kodi ifeyo aliyense payekha tikuyang’anizana ndi cosankha cotani?
10 Ndiponso loyenera kuonongedwa ndilo dongosolo la ndale za dziko limene lautsendereza mwankhanza mtundu wa anthu. Monga momwe mafufuzidwe alionse a mbiri yakale amabvumbulira, gulu ili liri ndi mbiri ya kukhetsa mwazi ndi kufunafuna ulamuliro mwadyera. Moyenerera, Mau a Mulungu amawayerekeza makonzedwe aponseponse a ndale za dziko pa dziko lapansi ndi “cirombo,” ndipo amalongosola cifukwa cace maboma aisonyeza mikhalidwe yonga ngati ya cirombo. Iwo amatiuza ife kuti Satana Mdierekezi, ‘cinjokaco’ wawapatsa maboma a dziko lapansi mphamvu yao ya kulamulira ndi kuti iwo amacita motsogozedwa ndi iye. (Cibvumbulutso 13:2; Danieli 8:20, 21; Luka 4:5-8) Mulungu amacipangitsa cidziwitso cimeneci kukhala copezeka kwa ife kotero kuti tingasankhe mwanzeru kaya ngati tidzakhala ndi phande mu zocitika za ndale za dziko za dzikoli kapena ai. Mulungu amatidziwitsanso ife za cimene iye adzacicita. Mu Danieli 2:44 iye amalankhula za nthawi pamene “Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthawi zonse.” Cimeneco cinacitika mu 1914 C.E. Koma, ponena za cimene ufumu wa Mulungu udzacicita mtsogolomu posacedwapa, mu nkhondo ya Armagedo kapena Harmagedoni, iye amapitirizabe kunena kuti: “Koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse [amene adzakhala alipo pa nthawi yamapetoyo], nudzakhala cikhalire.”—Onaninso Cibvumbulutso 16:14, 16; 19:17-21.
11. (a) Mbali yooneka ndi maso ya dongosolo loipa ili ya zinthu itaonongedwa, kodi Mulungu adzatembenukira kwa ndani? (b) Kodi ndi motani mmene icico cikulongosoledwera pa Cibvumbulutso 20:1-3?
11 Dongosolo lonse looneka ndi maso la Satana litatswanyidwa, kenaka Yehova adzatembenukira kwa Satana Mdierekezi, mulungu wa dongosolo loipa ili la zinthu. Iye adzamtswanya Satana, ndipo iye adzacicita ici posacedwapa. (2 Akorinto 4:4; Aroma 16:20) Pa nthawi imene Mdierekezi anagwetsedwa kucokera kumwamba motsatizana ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumuwo mu 1914, Satana anadziwa kuti anali ndi “kanthawi” kokha komtsalira. (Cibvumbulutso 12:12) Tsopano nthawi imeneyo yafupika kwambiri. Posacedwapa masomphenya olosera amene alembedwa pa Cibvumbulutso 20:1-3 adzakwaniritsidwa: “Ndipo ndinaona mngelo anatsika kumwamba, nakhala naco cifungulo ca phompho, ndi unyolo waukuru m’dzanja mdierekezi ndi Satana, . . . namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikilo pamwamba pace.” Cotero Satana, limodzi ndi ziwanda zace adzacotsedwa. Cisonkhezero cao cidzakhala citatha. Dongosolo loipa la zinthu limene liripoli, m’mbali zace zonse, lidzakhala litatha.
12. (a) Kodi Akristu oona adzakhala ndi phande lirilonse mu cionongeko cimeneco? Kodi ndani amene Mulungu adzamgwiritsira nchito kuti apereke ciweruzo? (b) Pamene cizunzo ciperekedwa pa iwo, kodi ndi motani mmene atumiki a Yehova amacitira?
12 Akristu oona pa dziko lapansi pano sadzakhala ndi mbali mu cionongeko cimeneco. Iyo iri nkhondo ya Mulungu. Iye adzagwiritsira nchito magulu ankhondo a angelo otsogozedwa ndi Kristu kuti apereke cilangoco. Iyenso adzaicititsa mbali imodzi ya gulu la Satana looneka ndi maso kuitembenukira mbali yinayo mwa cidani ca ciwawa. Koma atumiki a Yehova pa dziko lapansi sadzalowa mu ciwawco. (2 Akorinto 10:3, 4) Ngakhale pamene iwo akuzunzidwa, iwo sanayenera kubwezera mwa kumafunafuna kuwalipsira olamulira kapena kumayesa kugwetsa boma. Iwo amayembekezera pa Mulungu. “Musabwezere coipa, okondedwa, koma patukani pa mkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.”—Aroma 12:19.
CIMENE SICIDZATHA KONSE
13. Kodi dzikoli lidzaonongedwa pamene dongosolo ili la zinthu likutha?
13 Kutha kwa dongolo ili la zinthu sikudzakhala kutha kwa ciunda ici cochedwa dziko lapansi. Mau a Mulungu mwiniyo amatsimikizira kuti: “Dziko lingokhalabe masiku onse.” “Anakhazika dziko lapansi pa maziko ace, silidzagwedezeka ku nthawi zonse.” (Mlaliki 1:4, AV; Salmo 104:5 [103:5, Dy]) Siliri dziko lapansili limene liri loipa, koma dongosolo la zinthu limene liri pa ilo.
14. Kodi ndi anthu a mtundu wanji amene adzathedwa, koma kodi ndani amene adzatsala?
14 Kuonjezerapo, suli moyo wonse waumunthu umene udzatha. “Anthu osapembedza” ndiwo amene adzaonongedwa. (2 Petro 3:7) Anthu osakhulupirira amene ali padziko adzathedwa. Koma, atatha kulongosola izi, 1 Yohane 2:17 amaonjezerapo kuti: “Iye amene acita cfuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.” Kunali kuti acipangitse ici kukhala cothekera kuti Yesu Kristu anaupereka moyo wace kaamba ka ubwino wa mtundu wa anthu.—Ahebri 5:9.
15. Kuti tiwapulumuke mapeto a dongosolo loipa ili la zinthu ndi kukhala ndi moyo mu dongosolo latsopano la Mulungu, kodi nciani cimene tiyenera kucicita tsopano?
15 Ciyembekezo cozizwitsaco ca moyo wamuyaya m’kulamulira kwa ufumu wolungama wa Mulungu cikuwayembekezera opulumuka mapeto a dongosolo loipa ili la zinthu. Kodi inu mudzakhala mmodzi wa iwo? Kungatheke kuti inu mukhale mmodzi wao. Koma ngati ndi conco, muyenera kusonyeza “cangu” tsopano, kotero kuti Mau a Mulungu adzausonkhezera kwakukuru moyo wanu. (2 Petro 3:13, 14; Aroma 12:1, 2) Ha, ndi othokoza cotani nanga mmene tingakhalire kuti Yehova, mwa cikondi cace ndi cifuno, wawapanga makonzedwe a cipulumutso!
[Chithunzi patsamba 95]
MKATI MWA MBADWO UMODZI
1914
KUTHA KWA DONGOSOLO LOIPA
Kusayeruzika koonjezereka.
Mtundu ndi mtundu kuukirana.
Zibvomezi
Kuperewera kwa zakudya.
Kuthedwa nzeru kwa mitundu, osaidziwa njira yopulumukira.
Nthawi zowawitsa.
Kusamvera makolo.
Osasunga mapangano.
Anthu osadziletsa.
“MASIKU OTSIRIZA”