Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tr mutu 18 tsamba 157-162
  • Kumvera Lamulo Kwacikristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumvera Lamulo Kwacikristu
  • Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUMVERA KU LAMULO LALIKURULO
  • Mulungu ndi Kaisara
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kulemekeza Ulamuliro Nkofunika kaamba ka Moyo Wamtendere
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kugonjera Kwathu Kochepa ku Maulamuliro Aakulu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Nzika Yabwino Imakhala Yotani?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
tr mutu 18 tsamba 157-162

Mutu 18

Kumvera Lamulo Kwacikristu

1. Ngakhale kuli kwakuti kusamvera lamulo kuli kofala, kodi ndi kacitidwe kotani kamene awo amene amamamatira ku Baibulo amakatsatira?

KUSAMVERA lamulo kuli kofala kwambiri m’dziko lerolino, koma awo amene amakhaladi ogwirizana ndi Baibulo samakuonjezera uko. Iwo amawalabadira Mau a Mulungu, amene amati: “Akhale omvera ku maboma ndi kwa akuru monga olamulira.”—Tito 3:1 NW.

2. Kodi ndi kalingaliridwe kotani ponena za lamulo kamene alambiri oona ayenera kukasiya?

2 Kuli koona kuti ena amene tsopano amakucita kulambira koona kalelo anali ndi khalidwe losamvera lamulo. Iwo angakhale ataziba zinthu zimene zinali za ena. Kapena anakuona kuwamvera malamulo ena kukhala kofunika kokha pamene apolisi anali kuona. Mu ici kapena iwo sanali oipa kwambiri koposa ambiri a m’malo a kawoko. Komabe, Baibulo linawalongosolera momvekera kuti, ngati iwo anafuna kukutsatira kulambira koona, iwo anayenera kuusintha moyo wao.—Aefeso 4:22-29.

3. (a) Kodi kalingaliridwe ka Mkristu kulinga ku maboma a ndale za dziko kayenera kukhala kotani? (b) Ncifukwa ninji Mkristu sayenera kukhala ndi phande mu zipolowe kapena mu ciwawa ca kusamvera boma kuidodometsera nchito ya boma?

3 Pomapereka ndemanga za kalingaliridwe kamene Mkristu ayenera kukhala nako ponena za maboma a ndale za dziko, mtumwi Paulo ananena kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro akuru; pakuti palibe ulamuliro wina koma wocokera kwa Mulungu.” (Aroma 13:1) Ici sicimatanthauza kuti Mulungu anawakhazikitsa maboma amenewa kapena kuti iye amakabvomereza kacitidwe kao. Ena a iwo momvekera bwino amanena kuti iwo ali osakhulupirira mwa Mulungu. Komabe, Mulungu amawalola iwo kukhalabe. Iwo sakanakhoza kulamulira mwa njira iriyonse ngati Mulungu sanalole. (Yohane 19:11) ndipo ngati Mulungu awalola iwo kulamulira, kodi ncifukwa ninji Mkristu aliyense angawadodometse iwo? Ngakhale ngati munthu sakugwirizana nazo zimene boma likucita, ncifukwa ninji iye angalowe m’kucita cipolowe kapena kukhala ndi phande m’kucita ciwawa kumayesa kuliletsa bomalo kuicita nchito yace.? Munthu aliyense womacita zimenezo adzadzilowetsa m’bvuto, osangoti kokha locokera ku boma la dzikolo, komanso locokera kwa Mulungu. Monga momwe Aroma 13:2 amanenera kuti: “Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza coikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza adzadzitengera kulanga.”

4. (a) Kodi ndi mapindu otani amene maboma amatipatsa ife? (b) Kodi ndi kalingaliridwe kotani kamene Akristu ayenera kukhala nako ponena za kusonkha?

4 Ciri cinthu cabwino kusonyeza ulemu woyenera ku boma ndi ciyamikiro kaamba ka mautumiki opindulitsa amene ilo limawacita. Ife tonse tiri naco cifukwa cabwino ca kukondwera kuti maboma amene amatilamulira ife amapereka miseu ya kuyendamo, masukulu akuphunzirako, cinjirizo la ngozi za moto ndi kupenda ngati zakudya ziri bwino. Makhothi a lamulo ndiponse cinjirizo lotsutsana ndi upandu zirinso zopindulitsa kwambiri. Mu nkhani iyi ndi nkhani zina “maulamuliro a akulu” amadzisonyeza okha kukhala ‘atumiki akwaonse a Mulungu,’ omawapereka mautumiki amene amawapindulitsa anthu ace. Cotero pamene timafunsidwa kuti tiwalipiriire mautumiki apoyera amenewa mwanjira ya misonkho, ife tingacite bwino kulikumbukira lemba limene limanena kuti: “cifukwa cace, kuyenera kuti mukhale omvera, si cifukwa ca mkwiyo wokha [monga cilango kwa oswa malamulo], komanso cifukwa ca cikumbumtima. Pakuti cifukwa ca ici mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe cinthu cimeneci. Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ace a msonkho; kulipira kwa eni ace a kulipidwa.”—Aroma 13:5-7.

5. (a) Kodi kumvera Kwacikristu ku maulamuliro a ndale za dziko kuli kopanda malire? (b) Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera kuti pali mbali zirwiri za kuzilingalira?

5 Koma kodi kuwamvera maulamuliro a ndale za dziko kumeneku kumafika pati? Kodi kuli kopanda malire? Kodi kumvera lamulo la anthu kuli kofunika koposa kumvera lamulo la anthu kuli kofunika koposa kumvera lamulo la Mulungu? Ndithudi ai! Onani kuti mu lemba limene langogwidwa mau kumenelo ‘cifukwa cacikuru’ ca kumverako cikunenedwa kukhala comaphatikizapo “cikumbumtima.” Cotero, cikumbumtima ca munthuyo siciyenera kunyalanyazidwa, makamaka ngati cikumbumtima cimeneco caphunzitsidwa ndi Mau a Mulungu. Yesu Kristu anasonyeza kut pali mbali ziwiri za kuzilingalira. Pomasonyeza kuti kunali koyenera kupereka msonkho ku Boma Laciroma, iye anati, “Perekani zace za Kaisara kwa Kaisara,” ndipo iye anaonjezerapo kunena kuti: “Ndi zace za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) Cotero kuli kofunika kwambiri kwa aliyense wa ife kukapenda kacitidwe kace m’moyo wace kuti akhale wotsimikizira kuti, koposa zonse, iye sakuthandizirapo m’kusalimvera lamulo la Mulungu kumene kuli kofalako.—Salmo 1:1-3.

KUMVERA KU LAMULO LALIKURULO

6. Kodi nciani cimene atumwi anacicita pamene iwo analamulidwa kusiya kulalikira? Ndipo kodi iwo anamvera lamulo la ndani kukhala lopambana?

6 Pasanapite nthawi yaitali kucokera pa imfa ya Yesu Kristu, atumwi ace anafunsidwa kuti asonyeze pamene anaima mu nkhani iyi. Iwo analamulidwa ndi olamulira a mu Yerusalemu kuti aleke kulalikira m’dzina la Yesu Kristu. Kodi iwo anabvomerezana ndi zimenezo? Kodi inu mukanasiyadi? Atumwiwo motsimikizira anayankha kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Macitidwe 5:29; onaninso 4:18-20.) Iwo sanalione thayo lao kukhala lopepuka poliyerekeza ndi lamulo la dzikolo, koma pamene kuombana kwacindunji kunabuka kwa pakati pa lamulo la anthu ndi lamulo la Mulungu, iwo anazindikira kuti lamulo la Mulungu ndilo limene linali lalikurukuru. Poona ici, munthu wolemekezeka wa mu khothi limene linali kuwaimba mlandulo mwanzeru anawapatsa uphungu oweruza anzace wakuti asawadodometse Akristu awa, kotero kuti iwowo monga akuru a boma asapezeke kukhala akumamenyana ndi mulungu.—Macitidwe 5:33-39.

7. (a) Kodi nciani cimene Mulungu ananena m’masiku a Mose ponena za kumalambira pamaso pa zifaniziro? (b) Kodi ndi zipangizo zotani za kuzilambira zimene anthu azipanga? (c) Pamene lamulo la dziko limafuna kuti macitidwe a kulambira azicitidwa pamaso pa cifaniziro kapena cizindikiro, kodi Akristu angacite bwino kutsanzira citsanzo ca yani?

7 Sanangokhala malamulo a Mulungu okha onena za kulalikira amene ali ofunika. Palinso nkhani zina. Pomaigogomezera imodzi ya izozo, Yehova anawauza anthu ace mu nthawi ya Mose kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciriconse ca zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo; usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansaje.” (Eksodo 20:4, 5) Komabe, zipangizo zambiri zomapembedzedwa zapangidwa ndi anthu. Zina za izo ziri zacitsulo kapena za matabwa. Zina ndi za nsaru, zokhala ndi cithunzithunzi ca zinthu zina za m’mwamba kapena za pa dziko lapansi zimene zimasokereredwa pamenepo kapena kujambulidwa pamenepo. Nthawi zina mapembedzedwe amene amapangidwa pamaso pa zimenezi amakhala a kufuna kwa anthuwo mwa iwo okha, koma nthawi zina kumakhala kokakamizira mwa lamulo la dzikolo. Kodi ici cimakupereka kusiyana? Ngati lamulo la dziko limafunsira macitidwe a mtundu wakutiwakuti wa kupembedza kuti azicitikira pa cifaniziro kapena cizindikiro, kodi icico cimawacotsera thayo anthuwo la kumvera lamulo la Mulungu pa nkhaniyo? Alambiri okhulupirika a Yehova m’dziko la Babulo sanakhulupirire motero. Baibulo limatiuza ife kuti Ahebri acinyamata atatu, Sadrake, mesake ndi abedinego, anakana kuwatsatira macitidwe amene analamulidwa ndi mfumuyo. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti anaphatikizapo kulambira, ndipo kulambira kwao kunali kokha kwa Yehova. Mulungu anazibvomereza zimene anazicitazo. Koma kodi ndi motani mmene mfumu ya ku Babuloyo inacitira? Poyamba iyo inakwiya moopsa. Komabe, mu nthawi yace, iyo inaliona dzanja la Yehova Mulungu mu nkhaniyo. Pozindikira kuti iwo sanali aupandu ku Bomalo, iyo inapereka lamulo lowapatsa iwo ufulu ndi kuwacinjiriza. (Danieli 3:1-30) Kodi inuyo simumakuyamkira kumvera kwao kwa Mulungu? Kodi inu simumafuna kukhala otsimikizira monga momwe iwowo anacitira pa kumakupereka kulambira kosagawanika kwa Mulungu?

8. (a) Kodi Boma Laciroma linafunsiranji kwa nzika zace, ndipo ncifukwa ninji Akristu oyambirira anakana? (b) Kodi Akristu amenewa anali kusonyeza kusamvera?

8 Nkhani imodzimodziyi ya kulambira inakumanizana ndi Akristu amene anali kukhala mu Cifumu Caciroma. Bomalo linalamulira kuti aliyense aziiochera mfumu lubani kukhala monga cizindikiro ca kumvera. Akristu sakadacicita ici, ngakhale kunali kwakuti iwo anawamvera malamulo enawo. Iwo anazindikira kuti kulambira kunaphatikizidwamo, ngakhale kukhale kwakuti kulambirako kunali kuperekedwa molemekeza cizindikiro kapena munthu. (Mateyu 4:10) Justin Martyr, amene anakhala mu zaka za zana laciwiri, anawalongosola malingaliridwe a Akristu amenewa, akumati: “Kulambira tikupereka kwa Mulungu yekha, koma mu zinthu zina ife timakutumikirani inu [olamulira a ndale za dziko] mosangalala, tikumakudziwani inu monga mafumu ndi olamulira a anthu.” Akristu amenewa kawirikawiri anali kuganiziridwa molakwa, koma zimene anazicitazo sizinasonyeze kusamvera, kodi zinatero? Ndiponso izo sizinawapangitse iwo kukhala aupandu kwa Aroma enawo. Monga momwe bwanamkubwa Waciroma Pliny the Younger ananenera mu kalata ya kwa Mfumu Trajan, iwo anali kukana kucita cinyengo kapena kuba kapena cigololo. Iwo anali anthu amene aliyense akakonda kukhala nawo pafupi, ndiwo cinali cipembedzo cao cimene cinawapangitsa iwo kutero.

9. Konjezera pa kulambira kwathu, kodi ndi cina citinso cimene tiri naco mangawa kwa Mulungu?

9 Kuonjezera pa kulambira kwathu, pali cinthu cina cace cimene tiri naco mangawa kwa Mulungu. Mtumwi wa Yesu Kristu anacichula ico pamene iye anati: “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, . . . apatsa zonse moyo.” (Macitidwe 17:24, 25) Pakanakhala popanda Mulungu palibe aliyense wa ife amene akanakhala ndi moyo. Iye ali Magwero a moyo. (Salmo 36:9 [35:10, Dy]) koma kodi ife tikucita nawo ciani moyo umene iye watilola ife kusangalala nawowo?

10. Kodi ndi motani mmene Malemba amatithandizira ife kukupewa kusamkondweretsa Mulungu mwa njira imene timaigwiritsirira nchito miyoyo yathu?

10 Akristu oona amazindikira kuti, kuti asangalale ndi cibvomerezo ca Mulungu, iwo anayenera kupewa kuugwiritsira nchito moyo wao m’macitidwe amene adzawapangitsa iwo kukhala otsutsana ndi Mulungu. Cotero iwo amakapewa kacitidwe ka anthu a mtundu umenewo amene Baibulo limawalongosola kukhala oyenera kuonongedwa ndi wopereka cilango wa Mulungu pamene dongosolo loipali likutha. (Cibvumbulutso 19:17-21) Iwo amazindikira kuti ciweruzo ca Yehova ciri coona ndi colungama. Ndipo iwo amaiumba miyoyo yao tsopano mogwirizana ndi cifuniro cace. Iwo amazindikira kwenikweni kuti ici cingawadzetsere iwo kusayanjidwa, ngakhale kuzunzidwa, kucokera kwa awo amene zofuna zao zonse ziri mu dongosolo lamakonoli la zinthu. Koma, pokhala ndi cikhulupiriro codzaza cakuti njira ya Mulungu iri yoyenera, iwo amalikweza lamulo lace ndi kulambira kwace, akumazipatsa izozo malo oyamba m’miyoyo yao. (Mika 4:1-3) Pomtsanzira Mwana wa Mulunguyo, Yesu Kristu, iwo amaigwiritsira nchito miyoyo yao, osati pa kumafunafuna zinthu mwadyera kapena kaamba ka cifuniro ca anthu adyera, koma mogwirizana ndi cifuniro ca Mulungu. (1 Akorinto 7:23; 1 Petro 4:1, 2) Pakumatero, iwo amaziperekadi kwa Mulungu zimene ziri zace.

11. Kodi ndi motani mmene kumvera lamulo kunayenera kuitsogozera miyoyo yathu?

11 Kodi mumafuna kukhala ndi cibvomerezo ca Mulungu? Ngati ndi conco, kumvera lamulo kudzakhala nkhani yofunika kwambiri m’moyo wanu. Uko kudzakusonkhezerani inu kuti mukhale ndi ulemu woyenera kaamba ka munthu ndi Cuma ca okhala cifupi nanu. Kudzakupangitsani inu kukhala owalemekeza akuru a boma. Koma, koposa zonse, kudzakupangitsani inu kuupangitsa moyo wanu kukhala wogwirizana kotheratu ndi ziweruzo za Yehova Mulungu, Wopereka Lamulo wamkurukuru woposa onse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena