Mutu 19
Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
1. Ngakhale kuti kwakuti dziko liri lozolowerana ndi ciwawa, kodi ndi motani mmene Baibulo limatiphunzitsira ife ponena za mmene tinayenera kuuonera moyo?
KODI ife tikanakhala acisungiko motani ngati aliyense akadamaulemekeza moyo ndi mwazi mwaumulungu! Koma anthu ambiri samakhala nao ulemu woterowo. Ciwawa ndi kukhetsa mwazi zikuonjezereka kulikonse. M’malo ambiri moyo wa munthu umakhala mu upandu ngati iye ayenda m’makwalala pa nthawi yausiku. Dziko lafikira pa kucizolowera ciwawa kwakuti, ngakhale m’malo mwakuti adzisangalatse, anthu amakhala kwa maora ambiri akumaonera za ciwawa pa wailesi ya kanema kapena pa kanema. Komabe, Baibulo limatiphunzitsa ife kuti moyo uli kanthu kena kace kopatulika. Koma kodi mumauona uwo mwa njira imeneyo?
2. Kodi ndi motani mmene ziphunzitso za Baibulo zonena za moyo ndi mwazi zingawadabwitsire ena?
2 Malingaliridwe osagwirizana ndi Malemba afikira kukhala ofala kwambiri lerolino kwakuti ziphunzitso za Baibulo za nkhaniyo zingawadabwitse ena poyambirira. Komabe, Muyambitsi wa Baibulo, amene alinso Mpatsi wamoyo ndi Mlengi wa mwazi, ndiye amene ali Woidziwa Kwakukurukuru nkhaniyo. Malamulo ace ayenera kumveredwa.—Salmo 36:5-9 [35:6-10, Dy]; Yesaya 55:8, 9.
‘KUKHETSA MWAZI WA MUNTHU’
3. (a) Kodi ndi kwa ndani kumene Mulungu coyamba analankhulako ponena za kuopsa kwace kwa kumaumwa mwazi wa munthu? Cifukwa ninji? (b) Pambuyo pa Cigumula, kodi ndi motani mmene Mulungu anakugogomezera kufunika kwace kwa moyo? (c) Kodi lamulo limenelo linatha nchito?
3 Coyambirira Yehova analankhula ndi Kaini, mwana wa Adamu, ponena za kuopsa kwace kwa kuupha moyo wa munthu. Mulungu anali atamcenjeza kale Kaini kuti mkwiyo wace unalinyalanyaza cenjezolo ndipo anamuukira mbale wace Abele, namupha iye. Pamenepo Mulungu anati: “Mau a mwazi wa mphwako andipfuulira ine kunthaka.” Kaamba ka kukhetsa kwace mwazi mosamvera lamulo Kaini anayenera kuimbidwa mlandu pamaso pa Mulungu. (Genesis 4:6-11) Motsatizana ndi cigumula ca m’tsiku la Nowa, Mulungu kaciwirinso anagogomezera kuti moyo waumunthu uli wamtengo wapatali pamaso pace. Mulungu anati “mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzaufuna.” “Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wace udzakhetsedwa: cifukwa m’cifaniziro ca Mulungu Iye anapanga munthu.” (Genesisi 9:5, 6) Lamulo limenelo likadagwirabe nchito. Ilo limagwirabe nchito kwa mtundu wonse wa anthu lerolino monga mbadwa za Nowa. Kaya kukhale kwakuti maboma aumunthu amacita nawo akupha anzao mogwirizana ndi lamulo laumulungu limenelo kapena ai, Yehova adzawabwezera awo amene amapha moyo mosamvera lamulo.
4. Ngati tifuna moyo wamuyaya, kodi tiyenera kucotsa ciani m’miyoyo yathu, m’malo mwakuti tisauike pa upandu moyo wa ena?
4 Kuti mukhale opanda thayo pamaso pa Mpatsi wa moyoyo, pali zambiri zimene zikufunidwa. Pa 1 Yohane 3:15 kwalembedwa kuti: “Yense wakudana ndi mbale wace ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.” Ngati tifuna moyo wosatha, tifuna kucotsa m’miyoyo yathu kudana ndi anthu anzathu konse. Mulungu sadzawasunga m’dongosolo lace latsopano anthu amene, mofanana ndi Kaini, amalinyalanyaza cenjezo laumungu ndi kuuika paupandu moyo wa ena mwa kupsya mtima kwao. Kalingaliridwe kaumulungu ka moyo kamafunikira kuti ife tiphunzire kuwakonda anthu anzathu.—1 Yohane 3:11, 12; Mateyu 5:21, 22.
5. Kodi kanenedwe ka Malemba ndi kotani ponena za kutaya mimba?
5 Ngati tigwirizana ndi kalingaliridwe ka Mulungu pa nkhani iyi, ife tidzazindikiranso kuti moyo uli wopatulika ngakhale munthuyo akhale wokalamba kwambiri kapena wamng’ono kwambiri. Mau a Mulungu amasonyeza kuti ngakhale moyo wa mwana wosabadwa wokhala m’mimba mwa amace uli wamtengo wapatali kwa Yehova. (Eksodo 21:22, 23; Salmo 127:3 [126:3, Dy]) Ndipo komabe mitayo mamiliyoni ambiri imacitidwa pa dziko lonse lapansi caka ndi caka. Uku kuli kuswa lamulo la Mulungu, pakuti kamunthu kokhala m’mimbako kali colengedwa camoyo ndipo sikanayenera kuonongedwa. Ngati awiri okwatirana afuna kucepetsa ana m’banja mwao pa cifukwa ca kubvuta kwa ndarama zolelera ana, thanzi kapena zifukwa zina, imeneyo iri nkhani ya iwo eni, ndipo njira imene iwo angacitire ici iri nkhani imene iwo eniwo angaisankhe okha. Koma tiyenera kucitsimikizira ceniceni cakuti kucita mtayo sikumasonyeza kulemekeza moyo mwaumulungu.
‘MUSALE MWAZI’
6. (a) Kodi ndani amene ali nako kuyenera kokwanira kwa kunena za cimene cingacitidwe ndi mwazi? (b) Pamene Mulungu anampatsa munthu cilolezo ca kudya nyama, kodi ndi lamulo lotani limene analipereka pa mwazi?
6 Baibulo loyera kawirikawiri limagwiritsira nchito “mwazi” kumatanthauza “moyo.” Ici ciri cifukwa cakuti moyo kapena mphamvu yamoyo imakhala m’mwazimo. (Levitiko 17:11) Popeza kuti Mulungu ndiye Mlengi wa mwazi, iye amadziwa zambiri ponena za uwo koposa aliyense wa ife, ndipo iye ali nako kuyenera kokwanira kwa kunena cimene ciyenera kucitidwa nawo. Kunali coyambirira pambuyo pa Cigumula ca dziko lonseco pamene Mulungu anauloleza mtundu wa anthu kudya nyama. Cotero pa nthawi imeneyo iye anawapatsanso iwo lamulo lace lonena za mwazi, akumati: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, m’mene muli moyo wace, ndiwo mwazi wace, musadye.” (Genesis 9:3, 4) Mnofu wa nyama ungadyedwe, koma osati mwazi.
7. (a) Kodi nciani cimene bungwe lolamulira la akristu oyambirira linacilemba ponena za mwazi? (b) Kodi ndi motani mmene cosankha cimeneco cimasonyezera za kufunika kwace kwa ‘kusala mwazi’?
7 Pambuyo pace lamulo limenelo linaphatikizidwa ‘m’malamulo amene anaperekedwa kwa mtundu wa Israyeli, ndipo Mau a Mulungu amalipangitsa ilo kukhala logwira nchito kwambiri pa Akristunso. Pambuyo pa kuzilongosola momvekera bwino zofuna za Mulungu kaamba ka Akristu, gulu lolamulira la mpingo wa Akristu oyambirira linawalembera osakhala Ayuda amene anakhala okhulupirika: “Pakuti cinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tsasenzetse inu cothodwetsa cacikuru cina coposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.” Cotero, ifenso tiyenera ‘kusala mwazi.’ Ndipo iyo iri nkhani yofunika kwambiri kwa ife, pokhala itagwirizanitsidwa ndi kupewa dama ndi kulambira mafano.
8. (a) Ngati nyama sinakhetsedwe mwazi, kodi mnofu wace unayenera kudyedwa? (b) Kodi mwazi unayenera kusanganizidwa m’cakudya ca mtundu uliwonse? (c) Kodi ncifukwa ninji mwazi waumunthu suli wofunika mocepera?
8 Kuli koonekera bwino kucokera pa zimene Mulungu amanena pa mwazi kuti ife sitinayenera kudya mnofu wa nyama imene sinakhetsedwe mwazi. (Deuteronomo 12:15, 16) Ndiponso sitinayenera kuumwa mwazi wa nyama kapena kuusanganiza ndi zakudya zina. Koma kodi ndi mwazi wa nyama zokha umene ukunenedwawo? Ndithudi Mulungu sanaukanize mtundu wa anthu kudya mwazi wa nyama ndi kuuloleza uwo kuudya mwazi wa anthu, monga ngati kuti unali wopatulika mocepera! Iye anacilongosola ici momvekera bwino pamene iye pambuyo pace anawauza Aisrayeli kuti: “Munthu aliyense . . . wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo.”—Levitiko 17:10.
9. Kodi nciani cimene mlembi wa mu Cikristu coyambirira ananena ponena za (a) cifukwa cace cimene ena anali kumwa mwazi pa nthawi imene ija? (b) kalingaliridwe ka Akristu oyambirira ponena za mwazi?
9 Ici cinazindikiridwa bwino lomwe ndi Akristu oyambirirawo. Ngakhale kunali kwakuti kunali kukhulupiriridwa mofala kuti kumwa mwazi wa munthu wina kudzalipangitsa thanzi la munthuyo kukhala labwino, iwo anadziwa kuti thanzi labwino lokhalitsa, ponse pawiri lakuthupi ndi la kuuzimu, linadalira pa kumvera kwa munthuyo kwa Mulungu. Cotero, Tertullian, mlembi Wacikristu wa mu zaka za zana laciwiri ndi lacitatu C.E., ananena kuti: “Awo amene, pa zionetsero za kuphedwa kwa anthu zapoyera, kaamba kakuti aciritsidwe pa nthenda ya manjenje, anali kuutsopa mwadyera mwazi wa anthu aupandu amene anaphedwera pa bwalolo, pamene uwo unali kukha cucucu pa balalo, nacokapo—kodi iwo ndi a ndani? . . . Cita nazoni manyazi njira zanu zonyansazo pamaso pa Akristu, amene sanaudye ngakhale mwazi wa nyama pa cakudya cao ca zakudya wamba; amene amasala zinthu zopotola ndi zimene zimafa zokha. . . . Kuimveketsa nkhaniyo kotheratu mwa citsanzo cimodzi, inu mumawayesa Akristu ndi masoseji a mwazi, kokha cifukwa cakuti inu mumadziwa bwino lomwe kuti cinthu cimene inuyo mukuwayesera iwowoco kuti acimwe ciri cosaloleka.” Iwo analizindkira lamulo la Mulungu kukhala likumaphatikizapo mwazi wa mtundu uliwonse, wa nyama ndi wa anthu.
10. (a) Talongosolani cifukwa cace cimene kupatsidwa mwazi sikuli kosiyana ndi ‘kuudya.’ (b) Taperekani citsanzo ca mmene ‘kusala mwazi’ sikumatanthauzira kuulowetsera uwo m’matupi athu konse.
10 Bwanji ponena za kagwiritsiridwe ka nchito ka mwazi waumunthu kamene kakucitidwa lerolino? Adotolo a mankhwala, pomaizindikira mphamvu yocirikiza moyo ya mwazi, amagwiritsira nchito mapatsidwe a mwazi mopanda ciletso pakuwaciza odwala ao. Kodi ici ciri cogwirizana ndi cifuniro ca Mulungu? Anthu ena angalingalire kuti kupatsidwa mwazi sikuli “kudya” kwenikweni. Koma kodi sikuli koona kuti pamene wodwala amalephera kudya ndi pakamwa pace, adotolo kawirikawiri amamdyetsera iye mwa njira yofanana ndi imene mapatsidwe a mwazi amacitikira? Tawapendani malemba mosamalitsa ndipo onani kuti iwo amatiuza ife za ‘kusala mwazi’ ndi ‘kusakhudza mwazi.’ (Macitidwe 15:20, 29) Kodi ici cimatanthauzanji? Ngati dotolo anakuuzani inu kuti musamamwe mowa, kodi zikanatanthauza kokha kuti musamaumwere uwo pakamwa panu koma kokha kuti mungaulowetse uwo mwacindunji m’mitsempha yanu? Kutalitali! Coteronso, ‘kusala mwazi’ kumatanthauza kusaulowetsa m’matupi athu.
11. (a) Kodi ‘kusala mwazi’ kumalipereka bvuto lirilonse pa atumiki a Mulungu? (b) Kodi nciani cimene cimawacitikira odwala ambiri amene ampatsidwa mwazi? (c) Kodi adotolo angatsimikizire kuti munthuyo adzafa ngati sapatsidwa mwazi?
11 Kodi ici cimawapangitsa atumiki a Mulungu kukhala paupandu powayerekezera ndi anthu ena amene amalinyalanyaza Baibulo ndi kuulandira mwazi woperekedwa kwa iwo? Ai, sicimakhala cinthu cobvuta kwa iwo. Musaiwale kuti, atangotha kuwauza Akristu kuti ‘asale mwazi,’ Lembalo limati: “Ngati inu mosamalitsa muzipewa zinthu zimenezi, inu mudzalemerera. Thanzi labwino kwa inu!” (Macitidwe 15:29, NW) Mulungu anazipangitsa zimenezo kulembedwa m’Baibulo kaamba ka cifuno cina. Iye amadziwa cimene akunena! Iye amadziwa zambiri ponena za mwazi koposa mmene amadziwira adotolo amene zoyesayesa zao, ngakhale kuli kwakuti zingakhale ndi colinga cabwino, nthawi zonse sizimaturutsa zoturukapo zimene zinafunidwazo. (Marko 5:25-29) Coona ndico cakuti, pamene kuli kwakuti odwala ambiri amacira atapatsidwa mwazi, ena amatenga nawonso matenda ndipo zikwizikwi zimafa caka ndi caka cifukwa ca mwaziwo. Pali mitundu yina ya mankhwala amene samapereka cibvulazo coteroco. Dotolo angamuuze munthu kuti adzafa pa nthawi yaifupi ngati iye salola kuti apatsidwe mwazi, koma wodwalayo angafebe ngakhale atalandira mwaziwo. Ku mbali yina, monga mudziwa, pali odwala ambiri amene amapezanso thanzi labwino mosasamala za zoneneratu za adotolo zakuti adzafa.
12. (a) Kodi ncifukwa ninji sikuli kwanzeru kuyesa kuupulumutsa moyo wa munthuyo mwa kumaliswa lamulo la Mulungu? (b) Kodi moyo wathu watsopano linowu uli wamtengo wapatali koposa kumvera Mulungu?
12 Kaamba ka kuthekera kokaikitsa kwakuti munthuyo akhalebe wamoyo kwa zaka zina zingapo mu dongosolo ili la zinthu, kodi kungakhale kwanzeru kufufunuka kwa Mulungu mwa kumaliswa lamulo lace? Ngati tiyesa kuupulumutsa moyo wathu, mwa kumaliswa lamulo la Mulungu, ife tidzautaya uwo kosatha. Cimeneco ndico cifukwa cace Yesu anati: “Iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa cace Ine, adzaupeza.” (Mateyu 16:25) Cotero kacitidwe kanzeru ndiko ka kukhala ndi cidaliro nthawi zonse mu kulungama kwa lamulo la Mulungu ndi kukhala ndi cikhulupiriro cokwanira cakuti, ngati kufunika kukhalapo, Mulungu adzatipatsa ife moyo kaciwirinso mwa ciukiliro mu dongosolo lace latsopano la zinthu. (1 Atesalonika 4:13, 14) Mu njira imeneyo ife tidzasonyeza kulemekeza moyo mwaumulungu. Ife sitidzaulingalira moyo wathu watsopanoli kukhala wamtengo wapatali kwambiri koposa kumvera kwa Mulungu. M’malo mwace, ife tidzapenyetsetsa pa cogawira ca Mulungu kaamba ka moyo wosatha kaamba ka awo amene amayenda m’njira ya coondadi.
13. (a) M’malo mwa kupatsidwa mwazi, kodi ndi mwa njira yotani yokha imene cipulumutso cingadzere? (b) Kodi nciani cimene tifunikira kucita m’malo mwakuti tikhale ‘opanda liwongo la mwazi wa anthu onse,’ monga momwe anakhalira mtumwi Paulo?
13 Koposa kale lonse, pali kufunika kwa mwamsanga kwakuti anthu ku malo alionse alidziwe lingaliro la Mulungu pa nkhani yonena za moyo. Iwo afunikira kuzidziwa zogawira zimene Yehova Mulungu mwiniyo wazipanga kaamba ka kuupulumutsa moyo. Iye anamtumiza mwana wace Yesu Kristu kudzaukhetsa mwazi wace wa moyo kaamba ka ubwino wa awo amene asonyeza cikhulupiriro, ndipo iye anamuukitsa iye kucokera kwa akufa. (Ahebri 13:20, 21) Sikuli mwanjira ya kupatsidwa mwazi koma kokha mwanjira ya kukhulupirira m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu cakuti cipulumutso cingapezeke. Ndipo kuli kofunika kwambiri kucipeza ndi kucisonyeza cikhulupiriro cimeneco tsopanolino dongosolo lakale ili la zinthu lisanafikire pa mapeto ace. Ngati taphunzira ponena za makonzedwe acikondi amenewa, pamenepo tiyenera kukakamizika kuwauzanso ena ponena za iwo. Kudera nkhawa kwaumulungu kaamba ka moyo wa anthu ena kudzatisonkhezera ife kutero mwa kukangalika ndi kucirimika. (Ezekieli 3:17-21) Ngati tilinyamula thayo limeneli ndi kupirira nalo kufikira kuti onse akhala ndi mwai wa kumva, ife tidzakhala okhoza kunena kuti, monga momwe ananenera mtumwi Paulo: “Ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse. Pakuti sindinakubisirani osakulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.”—Macitidwe 20:26, 27.