Mutu 21
Cosankha Canu ca Kumtumikira Mulungu
1. Kodi ndi zifukwa zotani zimene tiri nazo za kumthokozera ndi kumtamandira Yehova Mulungu?
PALI zambiri za kumthokozera ndi kumtamandira Yehova Mulungu. Iye mwacifundo wawapanga makonzedwe akuti ife tisangalale ndi moyo wamuyaya. Iye walinganiza kale kucotsa ziyambukiro zopereka imfa za ucimo mwa kumpereka Mwana wace kukhala nsembe ya dipo. Cifuno ca Mulungu cakuwapangitsa ana ace kusangalala ndi paradaiso monga kwao kosatha cidzakwaniritsidwa posacedwapa! Kodi makonzedwe acikondi a Mulungu amenewa samaucititsa mtima wanu kusefukira ndi cithokozo kwa Iye?—Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9-11.
2. (a) Pa maziko a zimene tsopano mukuzidziwa, kodi kaimidwe kanu ka maganizo ndi kotani ponena za Yehova? (b) Ngati timamkondadi Yehova, kodi tidzasonkhezeredwa kucita ciani?
2 Zoonadi, palibe aliyense wa ife amene amadziwa zonse ponena za Yehova ndi njira zace. Iye ali wamkuru kwambiri kwakuti anthu nthawi zonse adzakhala akumaphunzira zinthu zatsopano ponena za iye. (Aroma 11:33) Koma pa maziko a zimene mukuzidziwa kale, kodi simunafikire pa kuzindikira kuti ciriconse cimene iye amacicita ciri coyenera ndiponso kuti pali zifukwa zokwanira za kudalirira mwa iye? Kodi inu simuli wokhutiritsidwa maganizo kuti iye amazikondadi zolengedwa zace, kuti iye ali wacifundo ndi wacisomo, komabe, pa nthawi imodzimodziyo, wangwiro mu cilungamo ndi mu nzeru? (Salmo 86:5, 10, 15 [85:5, 10, 15 Dy]) Ngati iyi iri njira imene mumalingalirira ponena za Yehova Mulungu, inu mudzakakamizika kumtumikira Iye, ndipo palibe cimene cidzakubwezerani inu m’mbuyo.
3. (a) Kodi ndi njira ziwiri zotani zimene ziri zowatsegukira anthu onse? (b) Kodi ndi cosankha cotani cimene cidzatsogolera ku cimwemwe cacikurukuru?
3 Pali njira ziwiri zimene ziri zoutsegukira mtundu wa anthu wonse. Imodzi imatsogolera ku imfa ndipo inayo imatsogolera ku moyo wamuyaya. (Deuteronomo 30:19, 20) Kodi ndi iti imene mudzaitsatira? Kusankha kutumikira Yehova kudzakutsogolerani inu ku cimwemwe cacikurukuru, ponse pawiri tsopanolino ndiponso ku nthawi yosatha. Monga momwe wamasalmoyo ananenera kuti: “Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ace.”—Salmo 112:1 [111:1, Dy].
KUDZIPEREKA NDI UBATIZO
4. Pamene munthu asankha kuti iye akufunadi kucita cifuniro ca Mulungu, kodi nciani cimene ciri coyenera kuti iye acicite?
4 Pamene cikondi ca pa Mulungu cikusonkhezerani inu kotero kuti mufuna kucita cifuniro cace, pamenepo kuli koyenera kwa inu kuti mupite kwa iye m’pempero kupyolera mwa Yesu Kristu ndi kucilongosola cikhumbo canu ca kukhala mmodzi wa atumiki ace, mukumayenda m’mapazi a Mwana wace. Kuli koyenera kuti inu mumuuze Yehova kuti inu mufuna kuti mukhale wace ndi kuti mufuna kucita cifuniro cace ponse pawiri tsopano ndiponso ku nthawi yonse imene ikudzayo. (Salmo 104:33 [103:33, Dy]) Mu njira iyi inu mumadzipereka inu mwini kwa Mulungu. Iyi ndi nkhani ya inu mwini, ya mtseri. Palibe wina amene angakucitireni.
5. (a) Mutakupanga kudzipereka kwanu kwa Mulungu, kodi nciani cimene iye amakuyembekezerani inu kucicita? (b) Kodi ndi cithandizo cotani cimene ciripo kwa inu kuti mukukwaniritse kudzipereka kwanu?
5 Mutakupanga kudzipereka kwanu kwa Yehova kuti mucite cifuniro cace, iye adzakuyembekezerani inu kuti mudzakusunga iko. Iyo siri nkhani yopepuka. Tsimikizirani kuti inu muli munthu amene amawasunga mau ace mwanjira ya kumamamatira mokhulupirika ku cosankha ici kapena kudzipereka kwa nthawi yonse imene mukhala wamoyo. (Salmo 50:14 [49:14, Dy]) Mdierekezi adzagwiritsira nchito njira iriyonse yothekera kuti akupangitseni inu kucitaya cikhulupiriro canu kwa Yehova. Koma Yehova mwiniyo adzakhala nanu. Nthawi zonse mungapite kwa iye mwa pemphero, ndipo iye adzakucirikizani inu. Ndiponso, monga momwe mwaphunzirira, Mulungu ali nalo gulu pano pa dziko lapansi, ndipo panopo mudzawapeza Akristu acikulire amene mwacisangalalo adzakupatsani inu cilimbikitso cacikondi ndi kukucirikizani inu.—1 Petro 5:8, 9; 3:12; 1 Atesalonika 5:11.
6. Kodi ncifukwa ninji Yesu anapita kwa Yohane Mbatizi ku mtsinje wa Yordano, ndipo kodi nciani cimene tikuciphunzira kucokera pa ici?
6 Kumasankha mwa munthu mwiniyo kutumikira Yehova ndi kumacisonyeza citsimikiziro cimeneci mwa pemphero kuli kofunika kwambiri. Koma palinso cinthu cina coonjezerapo. Ici cinasonyezedwa ndi Yesu Kristu, amene anatipatsa ife citsanzo ca kucitsatira. Kumbukirani kuti, Yesu anacita zambiri koposa ndi kungowauza Atate wace kuti iye anali atadza kudzacita cifuniro Cace. (Ahebri 10:7) Pamene iye anauyamba utumiki wace monga mlaliki wa ufumu wa mulungu Yesu anapita kwa Yohane Mbatizi, pa Mtsinje wa Yordano, ndipo anabatizidwa m’madzi.—Mateyu 3:13-15.
7. (a) Kodi ndi motani mmene Baibulo limasonyezera kuti Mulungu anaubvomereza ubatizo wa Yesu? (b) Kodi ncifukwa ninji ubatizo umene unalamuliridwa ndi Yesu suli wa makanda?
7 Baibulo limabvumbula kuti Yehova Mulungu anaubvomereza ubatizo wa Yesu. Ilo limanena kuti, pa cocitika cofunika cimene cija, “panatseguka pathambo, ndi Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m’thambo, kuti, Iwe ndiwe mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.” (Luka 3:21, 22) Popeza kuti Yesu anacikhazikitsa citsanzoco, Akristu odziperekanso lerolino ayenera kubatizidwa. Ponena zoona, Yesu analamulira atsatiri ace kuwapanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse ndi kuwabatiza ophunzira atsopano amenewa. Uku sikuli kubatiza makanda. Kuli kubatiza anthu amene afikira kukhala akhulupiriri, pokhala atatsimikizira m’maganizo mwao kutumikira Yehova.—Mateyu 28:19; Macitidwe 8:12.
8. Talilongosolani tanthauzo la ubatizo Wacikristu.
8 Pamenepo, kodi nciani cimene ubatizo Wacikristu umatanthauza? Sikuli kucapa macimo a munthuyo, cifukwa cakuti kuyeretsa macimo kumadza kokha kupyolera mwa cikhulupiriro mwa Yesu Kristu. (Aefeso 1:7) M’malo mwace, uwo uli cisonyezero capoyera, kumasonyeza kuti munthuyo wakupanga kudzipereka kwa lumbiro kwa Yehova Mulungu ndipo akudzipereka iye mwini kucita cifuniro Cace. Motero, ubatizo siuyenera kuonedwa monga wofunika mwapang’ono. Uwo uli wofunika kaamba ka onse amene amayenda m’mapazi a Yesu Kristu momvera.
9. (a) Pomalingalira za njira imene Yesu anabatizidwera, kodi ndi motani mmene ubatizo woyenera Wacikristu umacitidwira? (b) Ngati mufuna kubatizidwa, kodi mungamuuze ndani za ici mu mpingo?
9 Baibulo limanena kuti, pambuyo pa ubatizo wace, Yesu “anaturuka m’madzi.” Iye anali atalowadi m’madzimo kotero kuti Yohane akanammizadi iye kotheratu. (Mateyu 3:16; Yohane 3:23) Cotero, sikunangokhala kuwazidwa madzi cabe. Ubatizo woyenera Wacikristu umacitidwa mwa kumakhala ndi mtumiki wodzipereka wa mulungu—mwamuna, monga momwe analiri Yohane Mbatizi—kuti ammize kotheratu munthuyo m’madzi namdzutsanso. Ngati mwatsimikizira maganizo anu kutumikira Yehova ndipo mufuna kubatizidwa, pamenepo muuzeni woyang’anira wa mpingo wa mboni za Yehova umene mwagwirizana nawowo. Iye adzakuthandizani inu mwacisangalalo, mosalipitsidwa konse kaamba ka ubatizowo.
UTUMIKI WACIKRISTU
10. (a) Kodi ndi kalingaliridwe kotani ka Yesu kamene Mkristu ayenera kukhala nako? (b) Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, kodi nciani cimene cinali cifuniro ca Mulungu kaamba ka iye?
10 Ndithudi, kudzipereka ndi ubatizo siziri mapeto a kucita cifuniro ca mulungu kwa munthuyo. Izo zangokhala ciyambi cabe. Izo zimacisonyeza ciyambi ca moyo wacimwemwe wa kumtumikira Yehova, limodzi ndi ciyembekezo ca kupitirizabe kosatha mokangalika, kumacicita cifuniro cace. Mkristu wodzipereka nthawi zonse anayenera kukhala ndi kalingaliridwe ka Yesu Kristu, amene anati: “Cakudza canga ndico kuti ndicite cifuniro ca iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza nchito yace.” (Yohane 4:34) Mbali yaikuru ya nchito ya Mulungu imene inaperekedwa kwa Yesu pa dziko lapansi inali kulalikira ufumu wa Mulungu, ndi kukhazikitsa maziko a gulu la kulalikira kuipitiriza nchito iyi pambuyo pa imfa yace. Cimeneco ndico cimene cinali cifuniro ca Mulungu kaamba ka iye, ndipo Yesu anacicita ico mokhulupirika.—Luka 4:43; Yohane 17:4.
11. (a) Malinga ndi mau a Yesu a pa Mateyu 24:14, kodi cifuniro ca Mulungu kaamba ka Akristu lerolino ndi cotani? (b) Kodi ncifukwa ninji nchito imeneyi iri yofunika kwambiri?
11 Kodi nciani cimene ciri cifuniro ca Mulungu kaamba ka Akristu lerolino? Ciri cakuti iwo aicite nchito imodzimodziyo ya kulalikira, imene iri yofunika kwambiri. Ulosi wa Baibulo umabvumbula mosalakwa kuti ife tsopano tikukhala ndi moyo mkati mwa “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” Ndipo Yesu ananeneratu ponena za nthawi iyi: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa pa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:2, 14, NW) Ciri cifuniro ca Mulungu cakuti nchito ya kulalikira imeneyi icitidwe tsopano. Cenjezo lonena za mapeto a dongosolo ili lazinthu liyenera kuperekedwa. Ofatsa ayenera kusonyezedwa malo opulumukirapo. Kodi inu mudzakhala ndi phande mu nchito iyi?—Zefaniya 2:2, 3;a Miyambo 24:11, 12.
12. (a) Kodi ndi motani mmene nchito ya kulalikira inayenera kucitidwira? (b) Kodi lamulo la Yesu la ‘kuwapanga ophunzira’ limagwira nchito kwa Akristu onse?
12 Yesu Kristu anakhazikitsa citsanzo m’kumaucita utumiki. Iye analalikira kulikonse, m’mizinda ndi m’midzi, m’nyumba za anthu ndi m’mabwalo—ngakhale kwa mkazi amene anali pa citsime. (Yohane 4:7, 21-24) Mkristu woona lerolino adzatsatira citsanzo ca Yesu. Iye adzalalikira paliponse pamene mwai upezeka. Iye sadzangoyembekezera cabe kuti anthu adze kwa iye. Koma iye adzayesayesa kufunafuna anthu ofuna kumvetsera. Yesu analamulira kuti “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19; onaninso 10:11-13.) Lamulo limeneli limagwira nchito kwa Akristu onse—ogwira nchito wamba ndi akazi okwatiwa okhala panyumba, okalamba ndi anyamata—monga mmene zinakhalira mu zaka za zana loyambirira.—Macitidwe 4:13; Aroma 16:1.
13. Kodi ndi kuti kumene nchito yocuruka ya kulalikira imacitidwirako?
13 Akristu oyambirira anacitsatira cilangizo ca Yesu ndi citsanzo cace, akumakupanga kuyesayesa kwapadera kwa kuwafikira anthu m’nyumba zao. (Luka 8:1; 10:1-6; Macitidwe 5:42) Mtumwi Paulo ananena kuti: “Sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo, ndi m’nyumba m’nyumba.” (Macitidwe 20:20) Iyi ikali cikhalirebe njira yaikuru imene Akristu amaicitira nchito yao yautumiki m’tsiku lathu.
14. Kodi ndi motani mmene Mulungu amatithandizira ife mu utumiki?
14 Awo amene akukhala ndi phande mu nchito yaikurukuru iyi samacita mwa mphamvu za iwo eni. Yehova Mulungu amawacirikiza. Mwa mzimu wace iye amawayeneretsa ndi kuwapatsa mphamvu kaamba ka utumikiwo. (2 Akorinto 3:5, 6; 2 Timoteo 4:17) Kupyolera mwa gulu lace looneka ndi maso iye amakapereka kaphunzitsidwe ndi cithandizo, mosalipiritsa ndarama, kwa mboni zace zonse. Inunso, mungasangalale nawo mapindu a makonzedwe amenewa, pa King’idomu Holo ya kwanuko.
15. Pamene munthu asankha kumtumikira Mulungu, kodi ndi madalitso akuru otani amene amakhala akumuyembekezera iye?
15 Pamene mucipanga cosankha ca mtima wanu wonse ca kumtumikira Yehova Mulungu, inu mudzakhala nao madalitso akuru. Cimwemwe cimene mungakhale mutakhala naco pa kuphunzira coonadi conena za Yehova ndi zifuno zace cidzakuzidwa kwakukurukuru pamene mucigawana ico ndi ena ndi kuwaona masinthidwe abwino amene iwo cimawabweretsa m’miyoyo yao. (Macitidwe 20:35; Yohane 13:17) Pamene inu muwagwiritsira nchito mokwanira Mau a Mulungu m’moyo wanu inu mudzayandikizitsidwa kwa Mlengi wanu. Inu mudzasangalala naco cisamaliro cace cacikondi mu njira zimene inu simunacione ico ndi kale lonse. (Cibvumbulutso 7:9-17) Ndithudi, kacitidwe kanu kanzeru kadzaupangitsa mtima wa Mulungu kusangalala. (Miyambo 27:11) Ndipo mudzasangalaladi kwambiri pamene mudzaona mau a wamasalmoyo akumakwaniritsidwa akuti: “Odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova!”—Salmo 144:15 [143:15, Dy].
[Mawu a M’munsi]
a Sophonias 2:2, 3, Dy.