Phunziro 4
Mmene Tingaŵerengere ndi Kukumbukira
1, 2. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti tizikumbukira zimene timaŵerenga?
1 Kwa aja amene amaŵerenga mongotayirapo chabe nthaŵi, kungoti asangalale, kukumbukira zimene amaŵerenga sikumakhala kofunika kwenikweni. Koma kwa munthu amene akuphunzira ntchito, kumakhala kofunika kwambiri kukumbukira zimene akuŵerenga m’mabuku ake ophunzira. Kupambana mayeso ndi kuloŵa ntchito imene akuifunayo kumadalira zimenezo. Koma kwa mtumwi wachikristu n’kofunika kopambana kuti azikumbukira zimene aŵerenga, kaya akuŵerenga nkhani yosangalatsa kapena yaikulu. Cholinga chake ndicho kuyandikira pafupi kwambiri ndi Yehova ndi kuwongolera utumiki wake, ku chitamando cha Yehova.—Deut. 17:19.
2 Buku lalikulu loŵerenga Mkristu ndilo Baibulo ndi zofalitsa zina zothandiza kumvetsetsa Baibulo. Iye amadziŵa kuti chidziŵitso chopezeka m’Baibulo ndicho chokha chimene chimatsogolera ku moyo wamuyaya. Kumeneku ndiko kuŵerenga kumene kumathandiza munthu kukhala mlaliki waluso, ndipo ndiko kuŵerenga kumene ife timaikirapo mtima kwambiri m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.
3, 4. Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kusankha bwino zimene tiŵerenga?
3 Kuloŵetsa chidziŵitso m’maganizo mwathu mwa kuŵerenga tingakufanizire ndi kuloŵetsa chakudya m’mimba. Pambali zonse ziŵirizi tiyenera kusankha bwino. Wakudyayo, ngakhale pamene akungofuna kuthetsa chilakolako chakudya, amakhala wopusa ngati aloŵetsa m’mimba chinthu chimene sichingathe kupukusika kapena chimene sichimapereka phindu lenileni ku thupi, chimene mwina n’kukhala poizoni. Kuti tipindule nacho kwenikweni, kupeza mapindu okhalitsa, chakudyacho chiyenera kupukusika bwinobwino ndi kuloŵa m’mbali zosiyanasiyana za matupi athu.
4 N’chimodzimodzinso ndi kuŵerenga kwathu. Kaya ikhale nkhani yongosangulutsa kapena yofunika kwambiri, ndi bwino kuti zimene tikuloŵetsa m’maganizo mwathu zikhale zokhoza kupukusika m’maganizo komanso zodzapindulitsa maganizo athu kwa nthaŵi yaitali. Ndithudi, kungakhale kupanda nzeru kudyetsa maganizo zinthu zonama, zopanda umulungu kapena zoipa, zimene zingapangitse kubindikira m’mimba kwauzimu. (Afil. 4:8) Ndi iko komwe, n’kutayiranji nthaŵi kumaŵerenga nkhani zopanda phindu lenileni? Monga mmene timasankhira bwino zakudya, tiyeneranso kusankha bwino zimene tiŵerenga.
5, 6. N’chifukwa chiyani tifunikira kukhazikitsa nthaŵi ya kuŵerenga kwaumwini, ndipo kuŵerengako tingakuchite liti?
5 Pologalamu ya kuŵerenga kwaumwini. Mutasankha zoŵerenga zabwino, mufunikira kutenga sitepe lotsatirapo. Limenelo ndilo kukhazikitsa pologalamu ya kuŵerenga imene idzagwirizana ndi moyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Ngati mulephera kukhazikitsa nthaŵi zoŵerenga m’kati mwa masiku muzingoŵerenga popanda dongosolo ndipo kudzakhala kovuta kwambiri kuti mupindule zenizeni.—Mac. 17:11.
6 Kuŵerenga kosamalitsa kumafuna nthaŵi yokwanira ndi malo amene amalola kusinkhasinkha nkhani mukuiŵerengayo. Koma si kuŵerenga kulikonse kumene kudzafuna nthaŵi yaikulu. Ngati mungapatule mphindi 10 kapena 15 tsiku lililonse kuti muŵerenge, mudzadabwa ndi zimene mungathe kukwanitsa m’nthaŵiyo. Anthu ena amachita kuŵerenga kumeneku m’mamaŵa, kapena usiku asanagone. Enanso amaŵerenga pamene ali m’zoyendera za onse popita kuntchito kapena kusukulu, kapena panthaŵi yopuma masana. Mabanja ena amaŵerengera limodzi kwa mphindi zisanu kapena khumi pambuyo pa chakudya chimodzi tsiku lililonse kapena asanakagone. Kuŵerenga tsiku ndi tsiku kumakhala kopindulitsa kwenikweni.
7. Kodi cholinga chathu poŵerenga Baibulo chiyenera kukhala chiyani?
7 Pologalamu yanu yaumwini iyenera kuphatikizapo nthaŵi ya kuŵerenga Baibulo. Pali phindu lalikulu kuliŵerenga lonse kuyambira kuchikutiro mpaka kuchikutiro. Mungachite zimenezo mwa kuŵerenga machaputala angapo kapena masamba angapo tsiku lililonse kapena mlungu uliwonse. Komabe, cholinga chanu poŵerenga chisangokhala kumaliza nkhaniyo, koma kupeza cholinga chenicheni cha nkhaniyo kuti muzichikumbukira. Sinkhasinkhani zimene nkhaniyo ikunena. Poŵerenga Baibulo mungakhale ndi chidaliro nthaŵi zonse chakuti muli kudya chakudya chauzimu chabwino koposa.
8, 9. Kodi ndi nkhani zina zotani zimene zingakhale zopindulitsa kuziphatikiza m’pologalamu yathu ya kuŵerenga?
8 Nthaŵi ikufunikanso ya kuŵerenga kokonzekera nkhani yokaiphunzira paphunziro la Nsanja ya Olonda ndi misonkhano ina ya mpingo. Ndi bwino kukonzekera kukayankha pamsonkhano, koma kupeza mayankho kusakhale cholinga chanu chachikulu. M’malo mwake, yesetsani kumvetsa zimene mukuŵerenga ndi kuona mmene zikukhudzira moyo wanu.
9 Ndiyeno pali nkhani zina mu Nsanja ya Olonda zosakhala zija zophunzira paphunziro la mlungu ndi mlungu ndi misonkhano ina ya mpingo. Magazini a Galamukani!, nawonso amapereka nkhani zochuluka zopatsa chidziŵitso. Ndipo kodi mwaŵerenganso mabuku ena akale a Sosaite m’chinenero chanu? Ngati mupatula nthaŵi yoŵerenga mabukuwo, dziŵani kuti dalitso lalikulu lilipo patsogolo panu. Kuti munthu akule msanga mwauzimu, kwakukulukulu zimadalira khama la kaŵerengedwe kake.
10-17. Kodi ndi njira zotani za kaŵerengedwe zimene zingatithandize kukumbukira zochuluka zimene timaŵerenga?
10 Zothandiza kukumbukira. Kuti tipindule mokwanira ndi zimene tiŵerenga, tifunikira kuzikumbukira. Anthu kaŵirikaŵiri amati sakumbukira chifukwa chakuti ali ndi chikumbumtima choiŵalaiŵala. Komabe, kaŵirikaŵiri zimangokhala kuti chikumbumtima chawocho sanachiphunzitse bwino kapena sakuchigwiritsa ntchito. Kumakhala kwanzeru kuyesetsa kupeza phindu lalikulu pakuŵerenga kumene timachita. Timatayikidwa zabwino zambiri ngati tiiŵala msanga zimene tiŵerenga. Tifunikira tiphunzire mmene tingaŵerengere ndi kukumbukira. Pali njira zingapo zimene zathandiza oŵerenga aluso. Mwina inunso zingakuthandizeni.
11 Pamene mukuŵerenga, yesetsani kuŵerenga mawu angapo kapena magulu a mawu koposa kuŵerenga liwu limodzi limodzi. Chimenechi chidzakuthandizani pakuŵerenga kwanu ndi kuti mumvetse malingaliro m’malo molimbana ndi mawu. Pakuŵerenga kwa masiku onse, musamatchule mawu kapena kugwedeza milomo pamene mukuŵerenga, ndipo musakhale ndi chizoloŵezi chomabwereza mawu kupatulapo ngati mukufuna kumvetsetsa lingaliro lalikulu. Ndithudi, ngati ili nkhani yofunika ndi yozama, mufunikira kuŵerenga modekha kuti mumvetse lingaliro lake. Mwina mungafune kuiŵerenga mofuula, kapena mwa mawu apansipansi. (Sal. 1:2) Mwachitsanzo, Masalmo ndi Miyambo, sanalembedwere kuŵerenga kothamanga koma kosinkhasinkha.—Sal. 77:11, 12.
12 Kumathandizanso kuŵerenga ndi pensulo m’manja, mukumalemba mzera pansi pamawu ofunika ndipo mwinamwake kuchonga mfundo zapadera zimene mungafune kuzipendanso. Komabe, kulemba mizerako kukhale kwa apa ndi apo, chifukwa ngati mulemba paliponse, mfundo zazikulu sizidzalekanitsika. Pamene mupeza malongosoledwe othandiza kwambiri kapena mfundo imene mukhoza kuigwiritsa ntchito kuyankhira nkhani ina imene anthu ambiri amatsutsa nayo mu utumiki wakunyumba ndi nyumba, kudzakhala kothandiza kulemba tsamba ndi ndime kuchikutiro cha buku lanu. Mukatero mungaipeze mofulumira pamene ifunika. Musalembe m’buku, kupatulapo ngati lili lanu.
13 Simungangoŵerenga nkhani kapena buku popanda kuima, kusinkhasinkha, kuyerekezera zimene mwaŵerengazo ndi zimene mukuzidziŵa kale pankhaniyo. Inde, simungangotero ngati mukufunadi kukumbukira mfundo zazikulu. Phunzirani kupenda mosamalitsa zimene muŵerenga, mukumazindikira zifukwa ndi mafotokozedwe ochirikiza maganizo amene aperekedwa. Ndiponso, khalani maso ndi kuona mapulinsipulo amene akukhudza moyo wanu ndi amene ali chitsogozo pamoyo wa tsiku ndi tsiku. Imani kaye kuti musinkhesinkhe mmene mungawagwiritsire ntchito.
14 Pakuŵerenga kofunika kwambiri m’mabuku a Sosaite, n’kothandiza nthaŵi zonse kupenda choyamba mutu wake ndi mndandanda wa mitu yam’kati. Zimenezi zidzakhomereza m’maganizo mwanu mutu waukulu wa nkhani yonse. Pokonzekera kuŵerenga nkhani ya m’magazini kapena mutu wa m’buku, choyamba yang’anani timitu tating’ono tam’kati mwa nkhani. Timeneti timasonyeza dongosolo la kafutukulidwe ka mutuwo. Zindikirani masentensi okhala ndi mfundo yaikulu, amene kaŵirikaŵiri amakhala kuchiyambi kwa ndime iliyonse. Iwo kaŵirikaŵiri adzakuuzani mwachidule mfundo yaikulu ya ndimeyo. Sumikani maganizo pa kupeza chithunzi chonse cha nkhani imene mukuŵerenga.
15 Njira ina ndiyo kuyesa kuona m’maganizo zimene mukuŵerenga, mukumapanga zithunzi za m’maganizo monga zothandizira kukumbukira. M’maganizo mwanumo, onani anthuwo ndi malowo kumene ali, imvani mapokoso ndi mawu, nunkhizani mafungo abwino, laŵani zakudya ndi zakumwazo, sangalalani nawo kapena imvani nawo chisoni chawocho. Yesani kudziloŵetsa m’chochitika chofotokozedwacho. Tingathe kuyerekezera zilizonse m’maganizo kuti tionenso nkhani za m’Baibulo. Mwa njira imeneyi, nkhani za mbiri ya m’Baibulo zikhoza kukhomerezeka m’maganizo.
16 Pamene mufika kumapeto kwa nkhani, ibwerezeni mwachidule m’maganizo. Ndiyeno yerekezerani nkhani ya m’maganizo mwanu ndi yolembedwayo.
17 Ngati kutheka, kambiranani ndi munthu wina mfundo zomwe mwaŵerenga zikali zatsopano m’maganizo mwanu. Pamene muzifotokoza zimakhomerezeka mozamirapo m’maganizo mwanu, ndiponso munthu winayo angawonjezere m’nkhokwe yanu ya chidziŵitso pankhaniyo. Ngati mwapeza mfundo zothandiza zakumunda, zigwiritseni ntchito mwamsanga mu utumiki wanu wakulalikira. Izinso zidzakhomereza nkhaniyo m’chikumbumtima chanu.
18-20. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kuphunzira kuŵerenga bwino?
18 Phindu la kuŵerenga kogwira mtima. Kuŵerenga kumakhudza moyo wathu mwachindunji. Mtundu wa ntchito imene timachita, maluso amene timakulitsa, kusangalala kwathu ndi moyo, kukula kwathu kwauzimu, zonsezo zimadalira luso lathu la kuŵerenga. Popanda luso la kuŵerenga limeneli munthu amamanidwa zochuluka zofunika kuziphunzira ndi kuzidziŵa. Makolo angathandize ana awo kuphunzira kuŵerenga mwa pologalamu yokhazikika yapanyumba. Nthaŵi ndi nthaŵi, kumakhala bwino kupempha ana anu kuŵerenga mofuula. Mwa chitsanzo, iwo akhoza kuŵerenga lemba ndi ndemanga za tsikulo m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Ngati simutha kuŵerenga bwinobwino mosadodoma, kungakhale kothandiza kwambiri kuŵerenga kwa mphindi 15 mpaka 30 tsiku lililonse. Pamiyezi yoŵerengeka mudzaona zotsatirapo zokhutiritsa.
19 Njira zabwino za kaŵerengedwe, nthaŵi zoikika za kuŵerenga ndi kufufuza, ndi kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zoperekedwa muno kudzakulitsa kwambiri luso lanu la kulalikira. Mudzakhoza kukumbukira ochuluka a mawu a Mulungu amtengo wapatali, kuti muwagwiritse ntchito pamoyo wanu ndi mu utumiki. Ngakhalenso okalamba atha kukulitsa luso lawo la kukumbukira ngati atsatira mfundo zimene zaperekedwa munozi. Wina aliyense asaganize kuti wakalamba moti sangathe kuphunzira kuŵerenga bwino.
20 Chifukwa chimene Mulungu anaikira zifuno zake zazikulu m’buku chinali chakuti ntchito zake zodabwitsa zonse zidziŵike kwa ana a anthu ndi kuti azikumbukire kwa nthaŵi yaitali. (Sal. 78:5-7) Chiyamikiro chathu pa kukoma mtima kwake pankhani imeneyi tingachionetse mwa khama lathu la kuŵerenga ndi kukumbukira Mawu opatsa moyo amenewo.