Phunziro 17
Kalembedwe ka Makalata
1, 2. Kodi makalata amachita ntchito zabwino zotani?
1 Mumpingo woyambirira wachikristu, makalata anagwira ntchito m’njira zosiyanasiyana. Anali njira yolankhulana pakati pa mipingo. (Afil. 1:1) Anagwira ntchito yolimbikitsira omwe anali ndi maudindo apadera. (2 Tim. 1:1, 2, 6) Makalata analimbikitsa okhulupirira atsopano kapena omwe anali m’zovuta. (1 Ates. 1:1-7; 3:1-7) Ndipo Akristu oyambirira anagwiritsa ntchito makalata kulankhula ndi aja amene anali ogwirizana nawo kwambiri m’ntchito ya Ambuye.—3 Yoh. 1, 14.
2 Atumiki ateokalase a lerolino alinso ndi zifukwa zambiri zolembera makalata, ndipo makalatawo amatheketsa zabwino zambiri. Nthaŵi zina makalata antchito kapena amalonda angakhale ofunika. Akuluakulu a boma angafunikire kuwalembera kalata yokhudza ntchito ya Ufumu. Anthu ena okhala m’nyumba zalendi koma zovuta kulikakpo, ndiponso aja okhala kumalo akutali, kaŵirikaŵiri njira yokha imene tingawafikire nayo ndi “uthenga wabwino” ndi ya makalata. Mwina ofalitsa ena a mumpingo wanu anasamuka, kapena muli ndi achibale amene amakhala kutali, ndipo mungawalembere kalata pofuna kuwaonetsa kuti mumawaganizira. Komanso pamakhala nthaŵi zimene mumafunikira kulemba kalata yoyamikira munthu kapena yopepesa maliro.
3. Kuti makalata athu ayenerane ndi utumiki wathu, kodi ayenera kukhala otani?
3 M’pofunika kuti makalata athu akhale oyenerana ndi utumiki wathu wa kwa Mulungu. Ayenera kukhala aubwenzi, olembedwa mosamala komanso osonyeza chikondi chathu kwa owaŵerenga. Ayenera kukhala abwino ndi olimbikitsa, osati osonyeza mzimu woipidwa ndi wodandaula, amene amafooketsa chikhulipiriro ndi kuvutitsa maganizo a woŵerenga. “Chikondi chimangirira,” amatero Mawu a Mulungu. (1 Akor. 8:1) Ndiponso, ganizirani za maonekedwe a kalatayo, ndi chithunzi chimene idzachipereka. Kuti kalata ioneke yaudongo, ndi bwino kuti ikhale ndi mpata woyenera komanso wofanana m’mbali mwake ndi m’munsi mwakemo. Kuphaipha kapena kufutafuta zimene mwalemba kumapereka chithunzi choipa. Samalaninso za sipeling’i yabwino komanso kalembedwe koyenera ka chinenero. Komabe, ngati zimenezi simukuzidziŵa kwenikweni, musagwe mphwayi kumalembera anzanu makalata. Mzimu waubwenzi, chikondi ndi kuganizira ena, kaŵirikaŵiri zimakwirira zolakwa za sipeling’i ndi galamala. Koma mutha kuwongolera sipeling’i mwa kugwiritsa ntchito dikishonale, ndipo kalembedwe ka chinenero mungakawongolere mwa kuona mmene odziŵa amalembera. Pokumbukira mfundo zimenezo, tiyeni tsopano tione mosamalitsa mitundu yolekanalekana ya makalata amene tingalembe mokhudzana ndi utumiki wathu.
4. Longosolani mmene kalata yantchito kapena yamalonda iyenera kulembedwera.
4 Makalata antchito kapena amalonda. Pamene mulemba kalata yantchito kapena yamalonda, n’koyenera kulemba dzina lanu, keyala kapena adiresi ndi deti pamwamba pa kalatayo. Umenewu umatchedwa mutu ndipo umaonekera kulamanja pamwamba pa pepalalo. (M’makalata opita ku Watch Tower Society, mutuwo ukhalenso ndi dzina la mpingo wa wotumizayo, ngati ikunena zokhudzana ndi mpingo.) “Keyala yam’kati” imakhala kumanzere kwa pepalalo koma pansi pang’ono pa mutuwo. Pamenepo timalembapo dzina ndi keyala ya kampani kapena munthu amene tikum’lembera kalatayo. Chotsatira pansi pake ndi mawu olonjera. Polembera makampani kapena anthu amene si Mboni za Yehova, mawu olonjera oyenera ndi awa: “Wokondedwa Bwana,” “Azibambo,” “Wokondedwa Bambo——,” ndi ena otero. Polembera Sosaite ndi ena amene ndi Mboni za Yehova, n’chizoloŵezi chathu kumalemba mawu olonjera akuti “Abale Okondedwa” kapena “Mbale Wokondedwa——.” Ndiyeno pali mawu omalizira monga akuti “Ndine wanu.” Polembera anzathu a m’gulu la Yehova, mawu oyenera omalizira amakhala akuti “Ndine mbale wanu” kapena “Ndine mtumiki mnzanu.” Mawu ameneŵa amayambira pakati pa pepala ndipo amatsatiridwa ndi koma (comma). Pansi pake penipenipo, lembani dzina lanu. Ngati kalatayo ikupita ku Sosaite m’malo mwa mpingo kapena dera, wolembayo asonyezenso udindo wake, monga “Woyang’anira Wotsogoza” kapena “Woyang’anira Dera,” pansi penipeni pa dzina lake.
5, 6. Kodi n’chiyani chiyenera kukhala choyambirira m’kalata, ndipo n’chiyani chimathandiza kaŵirikaŵiri kulandira yankho labwino?
5 Pachiyambi penipeni pa kalata yanu, tchulani cholinga chake. Mukatero wolandirayo adzadziŵa mwamsanga chifukwa chake mwalemba kalatayo. Ngati kalatayo ikukhudza zimene munalemberana m’kalata ina m’mbuyomu, ndi bwino kutchula kalatayo ndi nkhani yake. Ndipo ngati mukulembera kampani kapena bungwe lalikulu lokhala ndi madipatimenti ambiri, kumakhalanso kothandiza kusonyeza chizindikiro chimene chinali pakalata imene munalandira kuchokera ku kampaniyo. Ponena za thunthu la kalata, mudzaona kuti n’kothandiza kuyamba ndime yatsopano pamene mufika pankhani ina kapena mfundo ina yosiyana. Izi zimathandiza kupangitsa mfundo zolekanalekana m’kalata yanu kuonekera bwino ndipo kaŵirikaŵiri sivuta kuyankha. Ngati kalatayo imaphatikiza nkhani ziŵiri, zantchito ndi zaumwini, ndi bwino kusamalira kaye zantchito.
6 Kufotokoza zinthu mofupikitsa n’kofunika kwambiri polemba kalata, komabe uthenga umene mukuuperekawo uyenera kukhala womvekera bwino ndi wokwanira. Ngati kalata yanu ikhala ilibe mawu osafunika kapena malingaliro obwerezabwereza, imakhala yogwira mtima kwambiri. Komanso cholinga chake cha kalata yanu chidzamveka mosavuta ngati mulibe mawu osakhudzana ndi nkhani yake. Ndiponso, m’pofunika kumathokoza ena moona mtima kaamba ka khama lawo pazinthu. Ngakhale m’kalata yantchito yonena za vuto linalake, kaŵirikaŵiri yankho limakhala labwinopo pamene mugwiritsa ntchito mawu monga akuti, “Ndikuyamikira kwambiri zimene mukundichitira (kapena zimene mungandichitire) pankhani imeneyi.”
7-9. Kodi tinganene chiyani m’kalata imene cholinga chake ndi kupereka umboni?
7 Kuchitira umboni. Kulemba makalata n’kothandiza polalikira uthenga wa Ufumu. M’madera ena muli nyumba zazikulu zam’mwamba kapena mahotela okhalamo anthu ndipo n’kovuta kugwiriramo ntchito mwaufulu. Koma okhalamowo tikhoza kuwalembera makalata. Ndiponso, pali anthu ena amene nthaŵi zambiri sitiwapeza panyumba pamene tili m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, koma amalandira makalata. Ndipo njira yokha imene wofalitsa amene satha kuchoka panyumba angalalikire uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu, ndiyo mwa kulemba makalata.
8 Polemba kalata yochitira umboni za Ufumu wa Mulungu, ndi bwino kuyamba mwatchula dzina lanu. Munganenenso chimene mwalembera kalata m’malo mokam’chezera maso ndi maso. Chidwi chanu chidzagwira mtima woŵerengayo. Ndiyeno longosolani zimene munafuna kumuuza mutakaonana naye maso ndi maso. N’zosavuta ngati mugwiritsa ntchito njira zimene mwaphunzira m’sukulu yateokalase. Mungagwiritse ntchito ulaliki wa m’Malemba wochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu waposachedwapa kapena kunena m’mawu anu mfundo zina zochokera mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! yaposachedwapa kapena m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Mungaperekenso thirakiti, magazini kapena kabuku ndi kulimbikitsa munthuyo kuziŵerenga. Fotokozani chifukwa chake uthenga umenewo uli wofunika kwambiri. Monga momwe mumachitira m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, mungam’limbikitse kuti aone malembawo m’Baibulo lake. Ndiyeno, pofuna kukulitsa chidwi chimene mwina mwadzutsa kale, muuzeni mmene angakupezereni ndipo m’pempheni kuti akatero. Perekani dzina lanu ndi keyala yoonekera bwino kotero kuti akafuna kukuthokozani kapena kulembetsa Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!, adzadziŵe kolembera kalata.
9 Kunja kwa envulopu, nthaŵi zonse sonyezani keyala yanu yobwezera. Onetsetsani kuti mwaikapo masitampa okwanira, makamaka ngati mwaikamo chofalitsa. Ngati masitampa sanakwanire, wolandirayo angalipitsidwe ndalama zotsalazo, ndipo zimenezo zingawononge chithunzi cha khama lanu lofuna kupereka umboni wabwino.
10, 11. N’chifukwa chiyani makalata olembera achibale ndi mabwenzi amakhala opindulitsa, ndipo angaphatikizemo chiyani?
10 Kwa achibale ndi mabwenzi athu. M’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku timapereka nthaŵi ndi maganizo athu ku zinthu zimene timaziona kukhala zofunika kwambiri. Koma kodi timapatula nthaŵi yolankhulana ndi achibale athu okondedwa ndi mabwenzi apamtima kudzera m’makalata? Makolo amayamikira kwambiri makalata ochokera kwa ana awo, ndipo ananso amapindula ndi makalata olemba makolo awo. “Kulankhulana” mwa makalata kumathandiza kwambiri onse m’banja kukhala ogwirizana, ngakhale atatalikirana malo okhala. Kunena zoona, mabwenzi ndi achibale anu amalimbikitsidwa polandira umboni wakuti muli bwino, kalata yosimba nkhani zosangalatsa yochokera kwa inu, kaya yolemba pamanja kapena yotaipa. Kodi mukukayikira? Chabwino, tangoganizani zimene zimachitika kwa inu. Kalata yabwino ndi chimodzi mwa zinthu zoŵerengeka zimene mumazilandira ndi chisangalalo chachikulu. Kaŵirikaŵiri imakupatsani chimwemwe chinachake. Mumasangalala podziŵa kuti munthu wina amakuganizirani, kodi sichoncho? Kumbukirani, mkhalidwe waukulu wa Akristu ndiwo wakuti iwo amakondana wina ndi mnzake; ndipo njira imodzi yosonyezera zimenezo ndiyo mwa kulankhulana ngakhale pamene muli otalikirana.
11 Koma kodi mudzalembamo nkhani zanji? Kodi mumasangalala ndi zokumana nazo zokondweretsa? Kaŵirikaŵiri zimene zimakusangalatsani zimakondweretsanso anthu ena. Mwina ndi chokumana nacho chanu pamene munali mu utumiki, kapena chokumana nacho chimene munamva kwa ena. (Koma sikwanzeru kuuza ena nkhani zopanda chitsimikizo chenicheni.) Nthaŵi zina mungafune kukumbutsana zinthu zimene zinakuchitikirani muli limodzi ndi amene mukum’lemberayo. Zimenezi zimalimbitsa ubwenzi. Mungalembenso za zinthu zatsopano zimene mwaphunzira. Ndiponso bwanji osalemba za zinthu zimene mwakhala mukuchita posachedwapa, mwinamwake malo kumene munakacheza? Nkhani zoterozo nthaŵi zonse zimakhala zokondweretsa kwa mabwenzi. Kodi amene mukum’lemberayo ndi wodwala? M’limbikitseni. Muonetseni kuti mumam’ganizira ndipo m’funireni kuchira msanga. Mungatchulenso kanthu kena kapadera kamene kanachitika kumsonkhano mumpingo, kanthu kolimbikitsa kamenenso kangapangitse tsikulo kukhala losangalatsa kwa wodwalayo. Ndipo ponena zoti mulembe, ngati muli ndi vuto loiŵala msanga zochitika za posachedwapa kapena zimene munali kuganiza, bwanji osamazilemba papepala pamene muzikumbukira? Ndiyeno pamene mukhala pansi kuti mulembe kalata, nkhanizo zizikhala zili pomwepo.
12, 13. Kodi makalata athu angawalimbikitse motani ena m’njira ya choonadi?
12 Ponenanso za zimene mungalembe, kodi pangakhalenso kanthu kena kamene mungaganize kopindulitsa wolandira kalatayo koposa kum’limbikitsa ndi choonadi? Mwina ndi munthu amene munkaphunzira naye Baibulo amene tsopano anasamukira kutawuni ina. Ngati mum’lembera kalata yosonyeza kuti mumam’ganizira ndi yom’limbikitsa, kodi sizingam’thandize kukhalabe ndi chidwi pa choonadi? Ndiyenonso, taganizirani mmene makolo amamvera pamene mwana wokhala kutali alemba kalata nayamikira makolo ake pokhala okhulupirika kwa Yehova kwa zaka zambiri ndi pophunzitsa anawo kudziŵa njira za Yehova. Ndiponso, bwanji za aja amene anasamukira m’dera kumene kuli kusoŵa kwakukulu chifukwa kulibe Mboni, kapena amene analoŵa utumiki waumishonale kapena wa pa Beteli? Ndithudi chimakhala chilimbikitso chachikulu kwa iwo pamene alandira makalata owathokoza kaamba ka utumiki wawo wokhulupirika kwa Yehova! (Ower. 11:40) Ndipo iwo amayamikira kwambiri ngati m’makalatamo mumaphatikizapo zochitika m’mipingo imene iwo analimo.
13 Kometsani makalata anu mwa kusalemba za inu nokha basi. Onetsani chidwi chanu chofuna kudziŵa za amene mukum’lemberayo mwa kufunsa za moyo wake, mapulani ake, pamene zafika zimene anakulemberani m’mbuyomu, mabwenzi anu nonse, ndi zakupita patsogolo kwa aja amene amaphunzira nawo Baibulo. Chidwi choterocho mwa munthu wina chimalimbikitsa kwambiri ndipo chimatsegulira mpata wolemberana nkhani zina m’tsogolo muno.
14, 15. Kodi muyenera kuchitanji kuti mapeto a kalata yanu akhale atanthauzo?
14 Mutafika kumapeto a thunthu la kalata yanu, kodi mudzaimaliza motani? Mapeto atanthauzo ali ofunika kwambiri. Ngati tingoti, “Ndingomaliza tsopano pakuti malo andithera,” sitimapereka chithunzi chabwino cha ife eni. Bwanji osaganiza za mawu ena atanthauzo? Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zosangalatsa zomalizira makalata ake. Chitsanzo: “Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu chikhale ndi mzimu wanu, abale.” (Agal. 6:18; 2 Akor. 13:14) Mtumwi Yohane anamaliza imodzi ya makalata ake motere: “Mtendere ukhale nawe. Akulankhula abwenzi. Lankhula abwenzi ndi kutchula maina awo.” (3 Yoh. 14) Gwiritsani ntchito mawu omalizira ogwirizana ndi nkhani ya m’kalata yanuyo ndi oyenerana ndi unansi wanu ndi munthuyo.
15 Kulemba makalata n’kosavuta ngati mumaonetsetsa zinthu zochitika m’moyo wa tsiku ndi tsiku. N’zambiri zimene zikuchitika zokwaniritsa maulosi a Baibulo. Dongosolo la zinthu lakaleli, kuphatikizapo zipembedzo zake, likuwonongeka mofulumira kwambiri. Komabe, ntchito ya Yehova ikupitabe patsogolo modabwitsa chifukwa ili ndi dalitso lake. Abale anu amakondwera kumva mbiri ya kufutukuka kwateokalase m’dera lanu. Zilibe kanthu ndinu ndani, alipo anthu ena amene angakondwere kumva m’kalata yanu za chikondi chanu, ndi nkhani za kukhosi kwanu. Ndipo kuonetsa chidwi chotero kwa ena ndi mbali ya utumiki wathu, pakuti chikondi chathu cha pa abale sichiyenera kutha kokha chifukwa chakuti tatalikirana. Ndithudi, titha kuchikulitsa mwa kulemberana makalata.