Phunziro 21
Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
1-3. N’chifukwa chiyani mfundo zolunjika zili zofunika kuti nkhani ikhale yopatsa chidziŵitso?
1 Nkhani zopindulitsa zimayamba ndi kukonzekera kosamalitsa, ndipo zimenezo zimafuna nthaŵi ndi khama. Koma zotsatirapo zake zimakhala mapindu enieni! Mwa kutero mumaŵirikiza nkhokwe yanu ya chidziŵitso cholongosoka komanso mumakhala ndi kanthu kena kopindulitsa koti mukagaŵire kwa omvetsera anu. M’malo molankhula chisawawa, mumakhala ndi mfundo zomveka bwino zoti mupereke, ndipo mumadziŵa kuti zimene mukunenazo n’zoona. Chimenechi chimathandiza omvetsera kumvetsa Mawu a Mulungu mokulirapo, ndi kulemekeza Yehova. Pambali yakuti mfundo zopatsa chidziŵitso, tidzafotokoza makamaka zimene mumanena m’nkhani yanu. Mwachidule, pendani mbali zosiyanasiyana za mfundoyo. Ndiyo mfundo yoyamba pasilipi la Uphungu wa Kulankhula.
2 Mfundo zolunjika. Nkhani yolankhulidwa mwachisawawa imakhala yosagwira mtima ndi yosadalirika. Imakhala yosatsimikizika kwenikweni. Imasiya omvetsera ali okayika. Kuti iwo akakumbukire mfundozo, ziyenera kukhala zolunjika, ndi zoona. Zimenezi zimapereka umboni wakuti mlankhuliyo anafufuza ndipo akuidziŵa bwino nkhani yakeyo.
3 Luso limeneli mungakhale nalo pokonzekera mwa kudzifunsa kuti, Chifukwa chiyani? Liti? Kuti? ndi zina zotero. Kaŵirikaŵiri sikokwanira kungonena kuti chinachake chinachitika. Tchulani malo, madeti, kapenanso zifukwa zake. Sikokwanira kungonena chinthu choona. Fotokozani chifukwa chake chili choona; nenaninso chifukwa chake kuli kopindulitsa kuchidziŵa. Ngati mukupereka malangizo, fotokozani mmene chinthu chiyenera kuchitidwira. Mlingo wake wa kufotokoza zimenezo umadalira kuchuluka kwa zimene omvetsera akuzidziŵa kale. Motero ganizirani za omvetserawo kuti mudziŵe mbali zimene zingafunikire kuzifotokoza.
4-6. Kuti nkhani yanu ikhale yopatsa chidziŵitso omvetsera anu, ndi mfundo ziti zimene muyenera kukumbukira?
4 Zopatsa chidziŵitso omvetsera. Chimene chingapatse chidziŵitso gulu lina la omvetsera chingakhale chosawonjezera kalikonse pa chidziŵitso cha gulu lina, kapena chingawasiye mumdima weniweni. Choncho, n’kwachionekere kuti nkhani iyenera kuyenerana ndi omvetserawo. Mwachitsanzo, polankhula nkhani yonena za mmene timagwirira ntchito yathu, mfundo zake tingazilongosole mosiyana kotheratu pamsonkhano wautumiki poyerekeza ndi polankhula kwa munthu wokonzekera kudzipatulira kwa Yehova, kapena polankhula nkhani kwa anthu akunja.
5 M’pofunika kukumbukira mbali zimenezo ngakhale posamalira nkhani zosiyanasiyana m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Polankhula nkhani ina iliyonse tiyenera kugwirizanitsa mfundo zake ndi mtundu wa omvetsera ake, chochitika, ndi cholinga cha nkhaniyo. Mbali zimenezi zidzadziŵika ndi mtundu wa nkhaniyo ndi chochitika chimene mlankhuliyo wakonza. Koma nkhani yolangiza nthaŵi zonse imakhala m’njira yolankhula ku mpingo. Nkhani zinazo zingasiyanesiyane, ndipo mtundu wa omvetsera ndi cholinga cha nkhaniyo zidzadalira chochitika chimene chakonzedwa. Nthaŵi zonse, onse aŵiri wophunzira ndi phungu angadzifunse kuti, Kodi nkhaniyi ikuyenerana ndi mtundu wa omvetseraŵa? Kodi nkhani imeneyo idzaperekadi chidziŵitso kwa omvetsera ndi kuwalangiza kanthu kena?
6 Pokonzekera dzifunseni kuti, Kodi cholinga changa pankhaniyi n’chiyani? Kodi pazimene ndikufuna kunenazo, munthuyo kapena anthuwo akudziŵapo kale ziti? Kodi ndifunikira kuyala maziko otani kuti mfundo zimenezi zikamveke bwino? Kodi ndingazifotokoze motani m’njira yosiyana kotheratu ku gulu la anthu osiyana kotheratu? Kuyerekezera kaŵirikaŵiri kumathandiza kupeza njira yabwino. Yesani njira zosiyanasiyana ku magulu a anthu osiyanasiyana pokonzekera nkhani, kungoti muone kusiyana kwake poganizira za omvetsera ndi kupangitsa nkhaniyo kukhala yopatsa chidziŵitso omvetsera amene mudzalankhulira nkhaniyo.
7, 8. Kodi tingapangitse motani nkhani zathu kukhala ndi mfundo zothandiza?
7 Mfundo zothandiza. Pali zambiri zoti ziphunziridwe, koma si zonse zothandiza. Kwa ife, mfundo zopatsa chidziŵitso ndi zija zokhudza zinthu zimene tifunikira kudziŵa zofunika pamoyo wathu wachikristu, ndi pautumiki wathu. Timafuna kudziŵa mmene tingagwiritsire ntchito chidziŵitso chimene tachipezacho.
8 Wophunzira pokonzekera, ndi woyang’anira sukulu popereka uphungu, angasinkhesinkhe mfundo imeneyo mwa kudzifunsa kuti: Kodi ndi mfundo zothandiza zotani zimene zili m’nkhaniyi? Kodi mfundozo zingathandize munthu popanga zosankha? Kodi mfundo zoperekedwazo zingagwirizanitsidwe ndi utumiki wakumunda? Kodi zimakweza Mawu a Mulungu ndi kusonyeza cholinga chake? Nkhani zoŵerengeka zingapereke chidziŵitso chonsecho, koma kuti ikhale yothandiza, mfundo zake ziyenera kukhala zoti omvetserawo akhoza kuzigwiritsa ntchito m’njira ina.
9-11. N’chifukwa chiyani kunena mawu olondola kuli kofunika kwambiri?
9 Kunena mawu olondola. Mboni za Yehova ndi gulu la choonadi. Tiyenera kulankhula choonadi chokhachokha ndi kukhala olondola nthaŵi zonse pachilichonse chimene tinena. Tiyenera kumatero osati ponena za chiphunzitso chokha komanso pamene tigwira mawu a anthu ena, tikamanena za ena kapena mmene tikuwafotokozera iwo, komanso ponena za nkhani zasayansi kapena zochitika zapanyuzi.
10 Tikanena mawu olakwa kwa omvetsera iwo angamabwereze mawuwo moti cholakwacho n’kumakula. Zolakwa zimene zimaonekera kwa omvetsera zimawapangitsa kukayikira ngakhale mfundo zina zimene mlankhuliyo anganene, mwinanso kukayikira ngakhale uthenga weniweniwo. Wokondwerera watsopano pakumva mawu oterowo, ndipo pokhala atamvapo ganizo lina likuperekedwa panthaŵi ina, angaone kuti pali kusagwirizana maganizo pakati pa Mboni za Yehova ndipo angaleke kusonkhana ngakhale popanda kuulula chifukwa chake chenicheni.
11 Phungu sayenera kusanthula liwu ndi liwu pazimene wophunzira akunena, makamaka watsopano m’choonadi, amene sanazame kwenikweni m’zinthu zakuya za Mawu a Mulungu. M’malo mwake, ayenera kuchita mwaluso pothandiza wophunzirayo kulingalira bwino ndi kum’sonyeza mmene angamalankhulire zolondola zokhazokha mwa kukonzekera bwino pasadakhale.
12, 13. Kodi phindu lake la mfundo zowonjezera zothandiza kumveketsa bwino nkhani n’lotani?
12 Mfundo zowonjezera zothandiza kumveketsa bwino nkhani. Malingaliro operekedwa chifukwa cha kusinkhasinkha kapena amene angapezedwe mwa kufufuza kowonjezera angathandize kwambiri pankhaniyo ndipo nthaŵi zina angathandize kupeŵa kumangobwereza mfundo zodziŵika kale kwa omvetserawo. Zimapangitsa nkhaniyo kumveka yatsopano, zimakopa chidwi cha omvetsera, ndipo zingapangitse nkhani yozoloŵereka kwambiri kukhala yokondweretsa kwenikweni. Ndiponso, zimapatsa mlankhuliyo chidaliro. Iye amalankhula nkhaniyo mwansangala podziŵa kuti ali ndi mfundo zina zosiyanapo zoti afotokoze.
13 Mbuna ina yofunika kupeŵa ndiyo kunena zinthu zongoganizira. Tifunikira kugwiritsa ntchito zofalitsa za Sosaite ndi kuzidalira. Fufuzani m’ma Indexes a Sosaite, ndi mawu am’tsinde a malemba. Tsimikizani kuti zimene mukunenazo zikupereka chidziŵitso cholondola, osati cholakwika.
**********
14-16. Nanga tiyenera kuchita chiyani pokonzekera nkhani kuti tifotokoze zinthu mosavuta?
14 Pokonzekera nkhani yanu m’pofunikanso kuganizira za mmene muti mukanenere zimene mukukanenazo. Ichi n’chimene silipi la Uphungu wa Kulankhula limatcha “Kumveka bwino.” Kulephera kusamalira bwino mbali imeneyi kungakulepheretseni kuwafika pamtima omvetsera anu, kapena kungawalepheretse iwo kukumbukira zimene amvazo. Pamfundo imeneyi pali mbali zitatu zazikulu zoti tifotokoze.
15 Kufotokoza kosavuta kumva. Mwa ichi sititanthauza kuti tiyenera kuloŵeza pamtima mawu oti tikalankhule. Koma tiyenera kupenda maganizo oti tikafotokoze ndi mfundo zina zotsimikizika. Zimenezi zidzatheketsa nkhani yogwirizanika bwino komanso kafotokozedwe kosavuta ka maganizo, m’mawu ozoloŵereka. Nkhani yocholoŵana m’maganizo mwa mlankhuli imakhalanso yocholoŵana poilankhula.
16 Tiyenera kupeŵa kukonzekera pamene nthaŵi yatha kale. Mfundo iliyonse ya m’nkhani tiyenera kuiganizira bwino lomwe kufikira itakhala yofeŵa ndi yosavuta kwa mlankhuliyo. Kupenda mfundo zimenezi pokonzekera kulankhula nkhani kudzazipangitsa kukhazikika bwino m’maganizo mwa mlankhuliyo kwakuti zidzatuluka mosavuta polankhula ndipo zidzamveka bwino lomwe kwa omvetsera monga momwe zilili kwa mlankhuliyo.
17, 18. N’chifukwa chiyani mawu osazoloŵereka ayenera kufotokozedwa?
17 Kufotokoza mawu osazoloŵereka. Kuphunzira kwathu Malemba ndi mabuku a Watch Tower Society kwatipatsa mawu ena achilendo kwa anthu osazindikira kwenikweni ntchito yathu. Ngati tikanati tifotokoze choonadi cha Baibulo kwa omvetsera ena, tikumagwiritsa ntchito mawu oterowo, zambiri zimene tinganene sizingamveke kapena nkhani yathu ingamveke yopanda tanthauzo m’pang’ono pomwe.
18 Ganizirani omvetsera anu. Kodi kuzindikira kwawo zinthu kuli pamlingo wotani? Kodi amadziŵa zochuluka motani za ntchito yathu? Kodi ndi anthu angati amene angamve mawuwo mosavuta mofanana ndi mlankhuli? Mawu monga “teokalase,” “otsalira,” “nkhosa zina,” ngakhale “Armagedo” ndi “Ufumu,” angapereke ganizo losiyana kwa wakumvayo ndipo mwina osamvapo chilichonse. Ngakhale mawu monga “mzimu,” “helo” ndi “kusafa” afunikira kumveketsedwa bwino ngati womvetserayo sakudziŵa bwino za ntchito yathu. Koma ngati nkhaniyo ikulankhulidwa ku mpingo, mawu otero safunikira kuwafotokoza. Chotero m’pofunika kuganizira za amene mukuwalankhulira nkhaniyo.
19, 20. Kodi tingapeŵe motani kukhala ndi mfundo zochuluka kwambiri?
19 Kusachulukitsa mfundo. Nkhani ikhoza kukhala ndi chidziŵitso chochuluka kwambiri kwakuti mfundo zake n’kusefukira kwambiri kwa omvetserawo moti n’kubunthitsa luso lawo logwira zinthu kapena osamvapo chilichonse. Kuti munthu akwaniritse cholinga cha nkhani yake, safunikira kutchula mfundo zambiri zimene sadzatha kuzifotokoza momveka bwino m’nthaŵi imene wapatsidwa. M’posafunika kufotokoza zambiri kuposa zimene omvetsera angamvetse. Ndiponso, mfundo zofotokozedwa kwa munthu wakunja kapena wokondwerera watsopano ziyenera kufeŵetsedwa kwambiri poyerekeza ndi kuzifotokozera mpingo. Apanso, phungu ayenera kuganizira za omvetserawo amene mlankhuliyo akulankhulako nkhani yake.
20 Kodi wophunzira adzadziŵa bwanji mlingo wa mfundo zimene angaike m’nkhani yake? Kuyerekeza kungakhale kothandiza pokonzekera. Pendani zimene mufuna kukalankhula. Kodi n’zingati mwa mfundozo zimene omvetsera anu akudziŵa kale, mwina pang’ono chabe? Kodi n’zingati zimene zidzakhala zatsopano kotheratu? Ngati iwo akudziŵapo kale zambiri, zimenezo zimakhala maziko abwino ofutukulirapo mfundo zatsopano zambiri m’nthawi imene mwapatsidwayo. Koma ngati omvetserawo sakudziŵapo chilichonse pankhaniyo, pamenepo m’pofunika kuti musamale kwambiri za kuchuluka kwa zimene muti munene ndi utali wa nthaŵi imene mudzafotokozera mfundo zimenezo kuti zimveke bwino kwa omvetserawo.