Phunziro 29
Kulankhula Nkhani Mosadodoma, Mokambirana Komanso Motchula Bwino Mawu
1-4. Tchulani zochititsa ndi zizindikiro za kalankhulidwe kododoma.
1 Pamene muimirira kutsogolo kwa omvetsera kuti mulankhule nkhani, kodi nthaŵi zambiri mumavutika kuti mupeze mawu oyenerera? Kapena, poŵerenga mofuula, kodi mumapunthwapunthwa pofuna kutchula mawu ena? Ngati zili choncho, muli ndi vuto la kudodoma. Munthu wosadodoma amakhala wokonzekera bwino kugwiritsa ntchito mawu. Sitikutanthauza munthu “wongosefukira ndi mawu,” amene amangobwetuka mosaganiza kapena mosaona mtima. Tikunena za kulankhula kwamyaa kapena kokoma kumvetsera, kotuluka mosavutikira kapena kuti mwaufulu. Kusadodoma kwaikidwa pasilipi la Uphungu wa Kulankhula kuti kumveketsedwe bwino.
2 Kaŵirikaŵiri kudodoma kumakhalapo polankhula chifukwa chosaganiza bwinobwino ndi kusakonzekera mokwanira. China ndi kusoŵa mawu kapena kusasankha bwino mawu. Ndiponso kudodoma kumakhalapo poŵerenga, makamaka chifukwa chosachita pulakatisi yoŵerenga mofuula, ngakhale kuti apanso kusadziŵa mawu ambiri kungapangitse wina kudodoma kapena kuŵerenga mozengereza. Mu utumiki wakumunda, kudodoma kungachititsidwe ndi zonse tatchulazo kuphatikizapo mantha ndi kukayika. Zikatero ndiye kuti vutolo n’lodetsadi nkhaŵa chifukwa nthaŵi zina omvetsera anu adzakuchokerani mukuyang’ana. N’zoona kuti m’Nyumba ya Ufumu omvetsera sangatuluke kwenikweni, koma maganizo awo akhoza kuchoka ndi kumayendayenda moti zambiri zimene munganene zingangopita pachabe. Choncho ndi nkhani yaikulu; kusadodoma ndi luso lofunikiradi kuliphunzira.
3 Alankhuli ambiri amakhala ndi chizoloŵezi choipa chokonda kunena mawu monga akuti “ndipo-e-e” kapena mawu ena otero. Ngati simukudziŵa kuti ndi kangati pamene mumatchula mawu otero polankhula, mungayese kumapanga pulakatisi yakuti munthu wina azikumvetserani ndi kumabwereza mawuwo nthaŵi iliyonse pamene muwanena. Mungadabwe zimene mungapeze!
4 Anthu ena nthaŵi zonse amalankhula mobwerezabwereza mawu, ndiko kuti, amayamba sentensi, kenako n’kudzipomboneza okha ndi kuyambiranso. Ngati muli ndi vuto la chizoloŵezi choipa chimenecho, yesani kuchigonjetsa m’kulankhula kwanu kwa tsiku ndi tsiku. Yesetsani kumaganiza kaye ndi kuona bwino lingaliro m’maganizo mwanu. Ndiyeno nenani lingaliro lonselo popanda kuima kapena kusintha malingaliro pamene muli m’kati mwa kulankhula.
5-10. Kodi ndi maganizo otani amene aperekedwa pofuna kulankhula nkhani mosadodoma?
5 Chinthu china. Nthaŵi zonse polankhula timagwiritsa ntchito mawu. Choncho mawu ayenera kudza mwachibadwa ngati tikudziŵa bwino chimene tikufuna kunena. Simufunikira kuchita kuganizira mawu. Ndi iko komwe, ndi bwino kuchita pulakatisi kungofuna kutsimikiza kuti mfundo yakutiyakuti yakhazikika bwino m’maganizo mwanu, ndiyeno mawuwo n’kumawaganizira polankhula pomwepo. Ngati mutero, ndipo ngati musumika maganizo anu pamfundoyo, osati mawu amene mukuwalankhula, mawuwo adzafika okha ndipo malingaliro anu mudzawalankhula mmene mukuwamveradi. Koma mutangoyamba kuganizira mawu m’malo mwa mfundo kulankhula kwanu kudzakhala kodukaduka.
6 Ngati vuto lokudodometsani polankhula ndi kusadziŵa mawu ochuluka, m’pofunika kukhala ndi phunziro la mawu la nthaŵi zonse kuti muwonjezere mawu anu. Poŵerenga Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena a Sosaite, yesetsani kutolamo mawu achilendo kwa inu ndi kuwawonjeza m’kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku.
7 Popeza kuti kudodoma poŵerenga kumakhalapo chifukwa cha mawu amene simunawazoloŵere, khalani ndi pulakatisi yanthaŵi zonse ndi yadongosolo labwino, yoŵerenga mawu mofuula ngati ndilo vuto lanu.
8 Njira imodzi imene mungachitire zimenezo ndi kusankha ndime imodzi kapena ziŵiri za nkhaniyo ndi kuziŵerenga bwinobwino mwakachetechete kufikira mutamvetsa ganizo lonse la ndimeyo. Sankhani magulu a maganizo, mukumawaika chizindikiro ngati kuli kofunika. Ndiyeno yambani kuchita pulakatisi yoŵerenga ndimeyo mofuula. Popanga pulakatisiyo, ŵerengeni ndime yonseyo mobwerezabwereza kufikira mutakhoza kuŵerenga magulu a maganizo onsewo popanda kudodoma kulikonse kapena kuima m’malo olakwika.
9 Mawu achilendo kapena ovuta ayenera kutchulidwa mobwerezabwereza kufikira mutakhoza kuwatchula mosavuta. Mutatha kutchula liwulo panokha, ŵerengani sentensi yonseyo imene ili ndi liwulo kufikira mutakhoza kulitchula m’sentensi mosavuta monga mmene mumachitira ndi mawu amene mumawadziŵa bwino.
10 Ndiponso, chitani pulakatisi kuŵerenga kosakonzekera. Mwachitsanzo, nthaŵi zonse ŵerengani lemba la tsiku ndi ndemanga zake mofuula nthaŵi yoyamba imene muyang’anapo. Zoloŵerani kulola diso lanu kutenga mawu m’magulu, osonyeza ganizo lonse, osati kungoona liwu limodzi panthaŵi imodzi. Ngati muchita pulakatisi, mukhoza kulitha luso limeneli lolankhula ndi kuŵerenga mogwira mtima.
**********
11-15. Kodi kulankhula kokambirana kumadalira motani mawu ogwiritsidwa ntchito?
11 Luso lina lofunika polankhula lopezeka pasilipi la uphungu ndilo “Mkhalidwe wokambirana.” Ndi luso limene mumaligwiritsa ntchito pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku, koma kodi mumakhala nalo pamene munyamuka kukakamba nkhani? Mwa njira inayake, anthu amene amalankhulana ndi ena mosavuta ngakhale ndi anthu ambiri kaŵirikaŵiri amalankhula nkhani monga mwalamulo, ndipo pamene auzidwa kuti akakonzekere pasadakhale kuti “akakambe nkhani” amalankhula ngati kulalika. Komabe, njira yogwira mtima koposa polankhula poyera ndiyo yolankhula mokambirana.
12 Kugwiritsa ntchito mawu okambirana. Kuti kulankhula mokambirana kukhale kogwira mtima kumadalira mawu ogwiritsidwa ntchito. Pokonzekera nkhani yolankhula kuchokera m’maganizo, si bwino kwenikweni kubwereza mawu mmene alembedwera. Mmene mawu amalembedwera amasiyana ndi mmene munthu angalankhulire. Choncho, fotokozani mfundo zimenezo malinga ndi mmene mumalankhulira. Peŵani kugwiritsa ntchito masentensi ocholoŵana kwambiri.
13 Pamene muli kupulatifomu lankhulani mmene mumalankhulira masiku onse. Musalankhule modzikweza. Kusiyana kudzangokhala kwakuti kalankhulidwe ka nkhani imene mwaikonzekera bwino kadzakhala kowongokerapo kuposa ka masiku onse, chifukwa maganizo ake mudzawaganizira mosamalitsa pasadakhale, ndipo adzatuluka mwamyaa. N’chifukwa chake mawu anuanu muyenera kuwalankhula bwino.
14 Zimenezo zikusonyeza kufunika kochita pulakatisi tsiku ndi tsiku. Polankhula, musasinthe mawu. Peŵani mawu “opeka achinyamata.” Peŵaninso kubwerezabwereza mawu amodzimodzi pofuna kupereka ganizo losiyana limene mungakhale nalo. Phunzirani kulankhula zatanthauzo. Nyadirani kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku, ndipo pamene muli papulatifomu, mawu adzangofika mosavuta ndipo mudzakhoza kulankhula mwa mkhalidwe wokambirana zimene omvetsera alionse adzasangalala nazo ndi kuzivomereza mosavuta.
15 Zimenezo zimakhala choncho makamaka mu utumiki wakumunda. Ndipo m’nkhani zanu za wophunzira, ngati mukulankhula ndi mwininyumba, yesani kulankhula ngati munali mu utumiki wakumunda, mukumagwiritsa ntchito mawu amene mukanagwiritsa ntchito kumeneko m’njira yachibadwa ndi yosavuta. Mukatero nkhani yanu mudzailankhula momasuka ndi mwachibadwa, ndipo chofunika kwambiri, idzakuthandizani kumapereka maulaliki ogwira mtima kwambiri mu utumiki wakumunda.
16-19. Fotokozani mmene kalankhulidwe kangayambukire luso lokambirana.
16 Kulankhula nkhani m’njira yokambirana. Mkhalidwe wokambirana sumangodalira mawu amene muwagwiritsa ntchito. Komanso njira imene mukulankhulira nkhaniyo n’njofunikanso kwambiri. Zimenezo zimaphatikizapo kamvekedwe ka mawu, ndi kalankhulidwe kachibadwa. Umangochitika mosavuta mofanana ndi kulankhula kwa masiku onse, ngakhale kuti panthaŵiyi mumakhala mukulankhula kwa omvetsera.
17 Kulankhula kokambirana n’kosiyana kwambiri ndi kulankhula kopereka nkhani. Sikumakhala ndi mzimu uliwonse wa kalankhulidwe “kolalikira” kapena kulankhula mwa mtundu wina wosati wachibadwa.
18 China chimene chimalepheretsa achatsopano kulankhula m’njira yokambirana ndicho kukonzekera kwambiri kakambidwe kenikeniko ka mawu a m’nkhaniyo. Pokonza nkhani, musaganize kuti muyenera kukonzekera liwu ndi liwu kufikira mutaloŵeza mawu onse pamtima. Pokonzekera nkhani yolankhula kuchokera m’maganizo, muyenera kusumika maganizo pa kupenda mosamalitsa mfundo zimene mukukazifotokoza. Pendani zimenezo monga malingaliro kapena maganizo kufikira zitasanjika bwinobwino m’maganizo mwanu. Ngati mwaziyala mwadongosolo ndi kuzikonzekera bwino siziyenera kukhala zovuta, ndipo polankhula nkhaniyo malingaliro ake ayenera kutuluka momasuka ndi mosavuta. Pokhala zili motero, ndipo ngati zilankhulidwa ndi cholinga cholankhulana, mkhalidwe wokambirana udzangobwera wokha pokamba nkhaniyo.
19 Njira imodzi imene mungatsimikizire zimenezo ndiyo kuyesetsa kulankhula kwa anthu osiyanasiyana mwa omvetserawo. Lankhulani mwachindunji kwa mmodzi panthaŵi imodzi. Ganizani monga kuti munthu ameneyo wafunsa funso, ndiyeno mukuliyankha. Yerekezani kuti mukulankhulana panokha ndi munthuyo pofotokoza mfundo imeneyo. Kenako pitani kwa wina mwa omvetserawo, choncho basi mmodzi ndi mmodzi.
20-23. Kodi munthu angatani kuti kuŵerenga kwake kukhale kwachibadwa?
20 Kupitiriza ndi kalankhulidwe kokambirana poŵerenga ndi limodzi mwa maluso ovuta kwambiri a kulankhula, komanso ndi limodzi mwa ofunika kwambiri. Ndithudi, kuŵerenga kwathu kwapoyera kochuluka kumachokera m’Baibulo, poŵerenga malemba okhudzana ndi nkhani yolankhula kuchokera m’maganizo. Tiyenera kuŵerenga Baibulo ndi mzimu wake wa zimene tikuŵerengazo ndi tanthauzo lake. Kuŵerengako kuyenera kukhala kwaumoyo. Komabe, atumiki oona a Mulungu salankhula mosintha mamvekedwe a mawu mmene atsogoleri achipembedzo amachitira. Atumiki a Yehova amaŵerenga Mawu Ake mwa chigogomezo chachibadwa malinga ndi kalankhulidwe ka munthuyo, zimene zili zoyenerana ndi chilankhulo chamoyo cha Buku limeneli.
21 Zikufanana ndi poŵerenga Nsanja ya Olonda kapena ndime paphunziro la buku. Apanso, mawu ndi kalembedwe ka masentensi sikali mwa mtundu wokambirana, choncho kuŵerenga kwanu sikungamveke monga ndi kukambirana nthaŵi zonse. Koma, ngati mumvetsa ganizo la zimene mukuŵerenga komanso kuziŵerenga mwachibadwa ndi mwatanthauzo, zidzamveka ngati mukulankhula kuchokera m’maganizo, kupatulapo kuti mwina mungamveke waukumu pang’ono. Chifukwa chake, muyenera kukhala ndi chizoloŵezi chomalembamo zizindikiro zimene zingakuthandizeni, ngati mungakonzekere pasadakhale, ndi kuti muchite zonse zotheka kuti mukalankhule nkhani mwachibadwa bwinobwino.
22 Poŵerenga kapena polankhula mokambirana, kunena moona mtima ndi mwachibadwa ndi zinthu zofunika kwambiri. Lolani mtima wanu kusefukira ndipo lankhulani mwanjira yokopa omvetsera anu.
23 N’kosatheka kungovala kulankhula kwabwino pokonzekera chochitika chinachake, mofanana ndi mmene sitingavalire makhalidwe abwino. Koma ngati mugwiritsa ntchito kulankhula kwabwino tsiku ndi tsiku kudzaonekera papulatifomu, mofanana ndi mmenenso makhalidwe abwino osonyezedwa panyumba amakaonekera pakati pa anthu.
**********
24, 25. N’chifukwa ninji kutchula mawu molakwa kuli kosafunika?
24 Katchulidwe ka mawu. Kutchula mawu koyenera n’kofunikanso, ndipo kwaikidwa pakokha pasilipi la Uphungu wa Kulankhula. Ngakhale kuti Akristu ena sanaphunzire kwambiri kusukulu za dziko, monga mmene anaonera Petro ndi Yohane kukhala opulukira ndi anthu wamba, n’kofunikabe kupeŵa matchulidwe a mawu olakwika kuti asafooketse ulaliki wathu. Vuto limeneli titha kuliwongolera mosavuta titachita nalo khama.
25 Ngati munthu atchula mawu m’njira yolakwika kwambiri, n’kutheka kuti amaperekanso malingaliro olakwika kwa om’mvetsera, chinthu chosafunika m’pang’ono pomwe. Mutamva wina akutchula mawu molakwa m’nkhani yake, kaŵirikaŵiri kumakhala ngati getsi lamphamvu kwambiri limene lang’anima ku maganizo anu. Nthaŵi zina mumatha kusiya kum’tsatira ndi kuyamba kuganizira liwu limene sanalitchule bwino. Mungaleke kumva zimene akulankhula ndi kumangomvetsera mmene akulankhulira.
26, 27. Kodi pali mavuto otani okhudzana ndi katchulidwe ka mawu?
26 Tinganene kuti ilipo mitundu itatu ya mavuto okhudzana ndi katchulidwe ka mawu. Umodzi ndiwo kutchula mawu molakwika basi, monga kutchula mawu mwa mtundu wina kapena kutchula malembo molakwika. Zinenero zamakono zambiri zili ndi matchulidwe ofanana, komanso Chicheŵa chili ndi matchulidwe ake apadera. Komanso pali matchulidwe ena amene ndi olondola ndithu koma owonjeza, omveka ngati kuyerekedwa kapena kunyada, ndipo zimenezo n’zosafunika. Vuto lachitatu ndilo kalankhulidwe kosasamala, kumangotchula mawu mosamvekera bwinobwino, kudulira mawu ena ndi zina zotero. Tipeŵenso zimenezo.
27 Nthaŵi zonse polankhula timagwiritsa ntchito mawu amene tinawazoloŵera bwino; choncho kutchula mawu sikukhala vuto kwenikweni. Vuto lalikulu limakhala poŵerenga. Koma Mboni za Yehova ndi anthu okonda kwambiri kuŵerenga pamaso pa anthu komanso paokha. Timaŵerengera anthu Baibulo pamene tipita kunyumba ndi nyumba. Nthawi zina timapemphedwa kuŵerenga ndime paphunziro la Nsanja ya Olonda, paphunziro la Baibulo la panyumba kapena paphunziro la buku la mpingo. N’kofunika kuti kuŵerengako kuzikhala kolondola, komanso mawu azitchulidwa moyenera. Ngati sitisamala zimenezo, zimapereka chithunzi chakuti sitikudziŵa zimene tikulankhula. Ndiponso zimafooketsa uthenga wathu.
28-34. Kodi munthu angathandizidwe motani kuwongolera katchulidwe ka mawu?
28 Uphungu pa katchulidwe ka mawu suyenera kuperekedwa mopambanitsa. Ngati ndi liwu limodzi kapena aŵiri okha amene sanatchulidwe bwino, mungangopereka uphungu wam’seri. Koma ngati mawu angapo atchulidwa molakwa m’kati mwa nkhani, ndipo ngati mawu amenewo timawagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri mu utumiki wathu wakumunda kapena m’kulankhula kwathu kwa tsiku ndi tsiku, kudzakhala kum’thandiza wophunzirayo ngati woyang’anira sukulu amuwongolera kuti aphunzire kuwatchula moyenerera.
29 Ndiponso, ngati poŵerenga m’Baibulo wophunzirayo atchula molakwa dzina limodzi kapena aŵiri achihebri, sikuti ali ndi chofooka chachikulu. Koma ngati watchula molakwa mayina ambiri, ungakhale umboni wakuti sanakonzekere bwino, ndipo uphungu uyenera kuperekedwa. Wophunzira ayenera kuphunzitsidwa mmene angadziŵire matchulidwe oyenera ndi kumachita pulakatisi.
30 N’chimodzimodzinso ndi katchulidwe ka mawu kolondola koma kowonjeza. Ngati kamawononga nkhani yake ndipo amakachita nthaŵi zonse, wophunzirayo ayenera kuthandizidwa. Komanso m’pofunika kuzindikira kuti anthu ambiri akamalankhula mofulumira kwambiri mawu ena samveka kwenikweni. Pamenepo musaperekepo uphungu. Koma ngati wophunzirayo akhala ndi chizoloŵezi chimenecho chosamveketsa bwino mawu moti kumakhala kovuta kumva zimene akunena, kapena ngati zimawononga uthenga wake, pamenepo m’pofunika kuti athandizidwe kuti azilankhula modekha ndi kumveketsa bwino mawu.
31 Komabe phungu wanu adzakumbukira kuti matchulidwe oyenerera amasiyana m’madera osiyanasiyana. Motero iye adzasamala popereka uphungu pa zakatchulidwe ka mawu koyenera. Sadzafuna kuti onse atsatire matchulidwe ake.
32 Ngati muli ndi vuto la katchulidwe ka mawu, kuwongolera sikudzakuvutani mutaikirapo mtima. Ngakhale akatswiri olankhula nkhani, pamene apatsidwa nkhani yoŵerenga amafunsira kwa odziŵa matchulidwe a mawu amene sanawazoloŵere. Samangotchula chitchuletchule. Choncho funsirani kwa odziŵa matchulidwe ake.
33 Njira ina imene mungawongolere katchulidwe ka mawu ndiyo mwa kuŵerengera pamaso pa munthu wina wodziŵa bwino katchulidwe ka mawu, ndi kumpempha kuti azikuimitsani ndi kukuwongolerani pamene mwalakwitsa.
34 Njira yachitatu ndiyo kumvetsera mosamala kwa alankhuli okhoza bwino. Ganizirani pamene mukumvetsera; onetsetsani mawu amene iwo akuwatchula mosiyana ndi mmene mumawatchulira inuyo. Alembeni mawuwo; kawafunseni kwa odziŵa ndipo chitani pulakatisi yomawatchula. Mudzaona kuti posakhalitsa inunso mudzawongolera katchulidwe kanu. Kalankhulidwe kosadodoma ndi kokambirana, limodzi ndi katchulidwe koyenera, zidzakweza kalankhulidwe kanu.