Mutu 7
Kumvera Kumakutetezerani Inu
KODI mukanakonda ngati inu mukadatha kuchita chinthu chiri chonse chimene inu munachifuna? Kodi ziripo nthawi pamene inu mumafuna kuti munthu ali yense asakuuzeni cha kuchichita? Tsopano, khalani oona mtima ndi kundiuza ine.—
Koma kodi nchiti chimene chiri chabwino kwambiri kaamba ka inu? Kodi kulidi kwanzeru kuchita chinthu chiri chonse chimene mukufuna? Kapena kodi zinthu zimayenda bwino pamene inu mumawamvera atate anu ndi amai wanu?—Mulungu amanena kuti inu muyenera kuwamvera makolo anu, chotero payenera kukhala chifukwa chabwino kaamba ka iko. Tiyeni tione ngati tingachipeze icho.
Kodi inuyo muli ndi zaka zingati?—Kodi mukudziwa zaka zimene atate wanu ali nazo?—Kodi mai wanu ali ndi zaka zingati?—Iwo akhala kwa nthawi yaitali koposa mmene inuyo mwakhalira. Ndipo pamene munthu amakhala kwa nthawi yaitali ndi pameneso iye amakhala ndi nthawi yochuruka ya kuphunzira zinthu. Iye amamva zinthu zochuruka, ndipo amaziona zinthu zochuruka ndipo amachita zinthu zochuruka chaka chiri chonse. Chotero ana angathe kuphunzira kuchokera kwa achikulire.
Kodi ndani amene wakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali koposa inu kapena ine kapena munthu wina ali yense?—Yehova Mulungu wakhala kwa nthawi yaitali. Iye amazidziwa zochuruka koposa inu ndipo iye amazidziwa zochuruka koposa ine. Pamene iye amatiuza ife chimene chiri chabwino kaamba ka ife, ife tingathe kukhala otsimikizira kuti icho chiri choyenera. Ngati ife tichichita chimene iye amachinena, kudzatitetezera ife. Ife tiyenera masiku onse kumumvera iye.
Chotero mukuonatu, ine ndifunikira kukhalanso womvera. Ndifunikira kumumvera Mulungu. Kuli kaamba ka ubwino wanga. Ndipo kumabweretsa zabwino kwa inunso pamene inu mumumvera Mulungu.
Tiyeni titenge Baibulo lathu ndi kuona chimene Mulungu amawauza ana kuchita. Kodi mungalipeze bukhu la Aefeso?—Tidzawerenga pa Aefeso chaputara chachisanu ndi chimodzi, vesi loyamba, lachiwiri ndi lachitatu. Ilo limati: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale nthawi yaikuru padziko.”
Chimenecho chiri m’Baibulo. Chotero ali Yehova Mulungu amene ali kumakuuzani inu kukhala omvera kwa makolo anu.
Kodi kumatanthauzanji ‘kulemekeza’ atate wanu ndi amai wanu?—Kumatanthauza kuti inu muyenera kuwasonyeza iwo ulemu. Inu muyenera kuwamvera iwo ndi kuchita zimene iwo amazinena popanda kudandaula. Ndipo Mulungu amalonjeza kuti ngati inu mumvera, ‘kudzakuyenderani bwino.’
Ndikuidziwa nkhani yonena za anthu ena amene miyoyo yao inapulumutsidwa chifukwa chakuti iwo anali omvera. Kodi mungafune kuimva iyo?—
Anthu amenewa anali kukhala mu mzinda waukuru wa Yerusalemu kalekale. Ochuruka a anthuwo mu mzinda umenewo anali oipa. Iwo sanamumvetsera Mulungu. Yehova anamtumiza Mwana wache kudzawaphunzitsa iwo. Koma iwo sanamverebe. Kodi nchiani chimene Mulungu akawachitira iwo? —
Mphunzitsi Wamkuruyo anawachenjeza iwo kuti Mulungu adzauchititsa mzinda waowo kuonongedwa. Iye ananena kuti magulu a ankhondo a asilikari akamanga misasa mozungulira mzindawo ndi kuuononga uwo. Iyenso anawauza anthuwo mmene iwo akadapulumukira ngati iwo anachikonda chimene chinali choyenera. Ichi ndicho chimene iye anachinena:
‘Pamene muona magulu a ankhondo atamzinga Yerusalemu yense, pamenepo ndiyo nthawi ya kuturuka m’Yerusalemu ndi kuthawira ku mapiri.’—Luka 21:20-22.
Kudachitika monga momwedi Yesu adanenera kuti kukachitika. Magulu ankhondo a Roma anadza kudzamuukira Yerusalemu. Iwo anamanga misasa mozungulira. Ndiyeno kaamba ka chifukwa china iwo anachoka. Ochuruka a anthuwo anaganizira kuti upanduwo unapita. Iwo anakhalabe mu mzindawo. Koma kodi nchiani chimene Yesu ananena kuti iwo ayenera kuchita?—
Kodi nchiani chimene inuyo mukanachichita ngati mukanakhala kuti inu munali kukhala m’Yerusalemu?—Awo amene anamkhulupiliradi Yesu anasiya nyumba zao ndi kuthawira kutali ndiYerusalemu m’mapiri. Osati ndiwo akulu okha amene anapita; ana ananka limodzi ndi iwo.
Koma kodi anatetezeredwadi chifukwa chakuti iwo anali omvera?—Kwa chaka chathunthu palibe chiri chonse chimene chinamchitikira Yerusalemu. Kwa zka zitatu palibe chiri chonse chimene chinachitika. Koma kenaka m’chaka chachinai magulu a ankhondo a Roma anabweranso. Ponena za awo amene anali atakhalabe mu Yerusalemu tsopano kunali kochedwa kwambiri kuti apulumuke. Nthawi imeneyi magulu a ankhondowo anauononga mzindawo. Ochuruka a anthu m’katimo anaphedwa.
Koma kodi nchiani chimene chinawachitikira awo amene anali atamumvera Yesu?—Iwo anali kutali kwambiri ndi Yerusalemu. Chotero iwo sanabvulazidwe. Kumvera kunawatetezera iwo.
Ngati inu muli omvera, kodi kumeneko kudzakutetezeraninso inu?—Inde. Taimani ndikusonyezeni kuchitika kwache. Ine ndingakuuzeni inu kusasewera mu mseu. Kodi nchifukwa ninji ndimachita chimenecho?—Chiri chifukwa chakuti inu mungagundiwe ndi galimoto ndi kuphedwa. Koma tsiku lina inu mungaganizire kuti: ‘Pa tsopano linoli kulibe magalimoto. Sindidzabvulala. Ana ena amasewera mu mseu, ndipo sindinawaone iwo atabvulala.”
M’menemo ndimo mmene ochuruka a anthuwo m’Yerusalemu anganizilira. Magulu a ankhondo a Roma atachoka, kunaonekera ngati kuli bwino. Ena anali kumakhalabe mu mzindawo. Chomwecho iwo anakhalanso. Iwo anali atachenjezedwa, koma iwo sanamvere. Monga choturukapo chache, iwo anataya miyoyo yao. Ndipo ana amene amasewera mu mseu angathenso kuitaya miyoyo yao. Ha, ndi kwabwino kwambiri chotani nanga mmene kuliri kumvera!
Kumvera nthawi zina zokha sikuli kokwanira. Koma ngati inu masiku onse mumamvera, kudzakutetezeranidi inu.
Kodi ndani amene amakuuzani inu kuti, “Mverani akukubalani”?—Ndi Mulungu. Ndipo, kumbukirani kuti, iye amanena zimenezo chifukwa chakuti iye amakukondanidi inu.
(Pano pali malemba ena abwino kwambiri omasonyeza kufunika kwa kumvera: Mlaliki 12:13; Akolose 3:20; Miyambo 23:22.)