Mutu 13
Awo Amene Anakhala Ophunzira a Yesu
INE NDIRI kuganizira za mtumiki wa Mulungu wabwino koposa amene anakhala pa dziko lapansi. Kodi inu mukumdziwa ameneyo?—Eya chabwino. Yesu Kristu.
Kodi inu mukuganizira kuti inuyo ndi ine tingathe kukhala ngati iye?—Eya, Baibulo limanena kuti iye anakhazikitsa chitsanzo kuti ife tichitsatire. Ndipo iye amatiitana ife kuti tikhale ophunzira ache.
Kodi kukhala ophunzira a Yesu kumatanthauzanji?—Kumatanthauza zinthu zingapo. Kuti tikhale ophunzira a Yesu, ife tiyenera kuphunzira kuchokera kwa iye. Koma sizokhazo. Ife tiyeneradi kuchikhulupilira chimene iye amachinena. Kodi inuyo mumachikhulupiliradi chiri chonse chimene Yesu amachinena?—Ngati ife timakhulupiliradi, tidzachita chimene iye amatiuza ife, eti?—
Anthu ambiri amanena kuti iwo amamkhulupilira Yesu. Koma kodi iwo onse alidi ophunzira ache? Kodi inu mukuganiza kuti iwo alidi?—
Ai; ochuruka a iwo sali. Iwo angamapite ku charichi kamodzikamodzi. Koma ambiri a iwo sanakhale konse ndi nthawi ya kuphunzira chimene Yesu anachiphunzitsa. Ngati inu muyesa kulankhula nawo za Yesu, iwo anganene kuti iwo sali okondwera nazo. Ndipo iwo samakhala ndi phande m’nchito yolalikira imene Yesu anawauza ophunzira ache kuichita. Chotero iwo sali kwenikweni ophunzira ache.
Kodi ndi anthu a mtundu wotani amene amakhala ophunzira a Yesu? Kodi mukuwadziwa?—Kukadakhala kokondweretsa kuonana ndi ena a awo amene anali ophunzira a Yesu pamene iye anali munthu pa dziko lapansi.
Ena a iwo anali asodzi. Tsiku lina pamene Yesu anali kumayenda m’mbali mwa Nyanja ya Galileya iye anamuona Petro ndi mbale wache Andreya. Iwo anali kumaponya khoka m’nyanjayo. Yesu anapfuula kwa iwo kuti: “Nditsatireni ine.”
Atayenda pang’ono, Yesu anawaona amuna ena awiri amene anali munthu ndi mphwache. Maina ao anali Yakobo ndi Yohane. Iwo anali m’bwato limodzi ndi atate wao, akumakonza makoka ao. Yesu anaitana Yakobo ndi Yohane kuti akhale ophunzira achenso.
Ngati Yesu akadakuitanani, kodi inuyo mukadachitanji? Kodi inuyo mukadatsagana naye Yesu pomwepo?—Amuna amenewa anadziwa amene Yesu anali. Iwo anadziwa kuti Yesu anali atatumidwa ndi Mulungu. Chotero pomwepo iwo anaisiya nchito yao ya kupha nsomba namtsatira Yesu.—Mat. 4:18-22.
Kuli koonekera bwino kuti amuna amenewa anali ofunitsitsa. Iwo anafuna kuchita chimene chinali choyenera, ndipo chimenecho chiri chofunika. Koma iwo sanali angwiro. Tamlingalirani Petro. Panali nthawi zina pamene iye adanena chinthu cholakwa, ndipo chinamlowetsa iye m’bvuto. Koma iye anali ndi mtima wabwino. Iye sanayese kuchipanga icho kuonekera ngati kuti iye sanachite cholakwa chiri chonse pamene iye anadziwa kuti adachita cholakwa. Iye anamvetsera ndipo anali wofunitsitsa kusintha. Ngati ife tiri ofunitsitsa ngati Petro, ife tingathe kukhalanso ophunzira a Yesu.
Yesu analankhulanso kwa wolamulira wina wachinyamata wolemera. Kodi munthu wonga ngati ameneyu akatha kukhala wophunzira wa Yesu?—Iye adasonyeza chikondwerero. Iye adamfunsa Yesu kuupeza kwache moyo wamuyaya. Yesu adamfotokozera iye chimenechi. Koma pamene munthuyo adamva kuti kukhala wophunzira wa Yesu kudayenera kukhala kofunika kwambiri m’moyo mwache koposa ndi ndarama zache, iye adakhala wosakondwa. Yesu adamuitana iye kuti: “ Idza khala mtsatiri wanga.” Koma munthuyo sadagwirizane naye. Iye adakonda ndarama zache kwambiri koposa mmene iye adamkondera Mulungu.—Luka 18:18-25, NW.
Yesu adawaitana anthu a mitundu yonse kukhala ophunzira ache. Ngakhale awo amene adakhala ndi miyoyo yoipa adatha kusintha. Koma iwo ayenera kukhala ofunitsitsa kuphunzira ndi kutembenuka ndi kuyenda njira yoyenera. Iwo ayeneradi kufuna kumkondweretsa Mulungu. Kodi chimenecho ndicho chimene inuyo mumafuna kuchichita?—
Ophunzira okha awo amene talankhula za iwo kufikira pa tsopano lino anali amuna. Kodi chimenecho chimatanthauza kuti amuna okha akakhala ophunzira a Yesu?—Ai. Akazi anakhalanso ophunzira. Baibulo limasimbadi za banja lina m’limene ana akazi anai anali otanganitsidwa kumawauza ena za Mulungu. Ha, ndi banja lachimwemwe chotani nanga mmene limenelo linayenera kukhalira!—Machitidwe 21:8, 9.
Pamene Yesu anali kuphunzitsa, iye anali ndi chikondwelero chapadera ndi ana ang’ono. Kodi nchifukwa ninji iye anachita choncho?—Iye anadziwa kuti ana akathanso kukhala ophunzira ache. Nzoona kuti akulu angathe kuchita zinthu zina zimene ana sangathe kuzichita. Koma akulu sindiwo anthu okha amene angathe kuphunzira kuchokera kwa Yesu. Ndipo iwo sindiwo anthu okha amene angathe kulankhula za Mulungu. Inu mungathe kuzichita zinthu zimenezonso.
Kodi inu mukufuna kukhala wophunzira wa Yesu?—Ine ndikufuna. Chimenecho chiridi chinthu chabwino koposa chimene ali yense wa ife angathe kuchichita.
Koma, kumbukirani kuti, kumangonena kokha kuti ife ndife Akristu sikumatipanga ife kukhala ophunzira a Mphunzitsi Wamkuruyo, ati?—Ngati ife tiridi ophunzira ache, kuyenera kusonyezeka m’chiri chonse chimene ife tichichita.
Ife sitidzayerekezera kukhala Akristu kokha pamene ife tipita ku misonkhano kumene ife timalankhula za Mulungu, koma kenako kukhala oipa pa nthawi zina. Ife tidzakhala ndi moyo monga Akristu pa nyumba pano.
Kodi kukhala Mkristu kumaphatikizamonso mmene inu mumachitira pamene inu mukusewera ndi ana ena?—Kodi iko kuyenera kuchiyambukira chimene munthu amachichita pamene iye ali pa nchito?—Inde, ngati ife tiridi ophunzira a Yesu, pamenepo ife tiyenera kuchita motero tsiku lonse lathunthu, mosasamala kanthu za kumene ife tiri.
(Tsopano werengani pamodzi chimene Baibulo limachinena ponena za ophunzira a Yesu pa Mateyu 28:19, 20, Yoh. 8:31, 32 ndi Luka 6:13-15.)