Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 18 tsamba 75-78
  • Chifukwa Chimene Anthu Amachitira Zoipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chimene Anthu Amachitira Zoipa
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Amene Amachita Zinthu Zoipa Angasinthe?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yesu Anasankha Saulo
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Wozunza Aona Kuunika Kwakukulu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Pa Njira ya ku Damasiko
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 18 tsamba 75-78

Mutu 18

Chifukwa Chimene Anthu Amachitira Zoipa

KODI sikukanakhala kodabwitsa ngati munthu ali yense anali wabwino?—Pamenepo palibe munthu ali yense amene akanambvulaza wina ali yense.

Koma kodi alipo munthu wina ali yense amene kwenikweni ali wabwino nthawi zonse? Kodi inu mukuganiza bwanji?—Baibulo limatiuza ife kuti Yehova Mulungu masiku onse ali wabwino. Ndipo Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo, masiku onse amachita chimene chiri choyenera. Koma palibe ali yense wa ife ali wabwino nthawi zonse.

Ife tingayeseyese kukhala abwino. Koma pali nthawi zina pamene ife timaganizira zinthu zoipa, kodi sichoncho?—Ndipo nthawi zina ife timachita zinthu zoipa. Munthu woyambayo, Adamu, mwadala sanamumvere Mulungu. Chimene iye anachichita chinali choipa kwambiri. Monga choturukapo chache, ife tonse tinabadwa opanda ungwiro. Ife tonse tiri ana a Adamu. Chimenecho ndicho chifukwa chimodzi chifukwa chache anthu amachita zinthu zoipa. Ngakhalebe kuli kwakuti iwo samafuna kukhala oipa.

Koma anthu ena amachita zinthu zoipa mwadala. Iwo amawada anthu ena ndi kuchita zinthu kuwabvulaza iwo. Kodi inu mukuganizira kuti munthu wonga ngati ameneyo angasinthenso ndi kuphunzira kukhala wabwino?—

Baibulo limapereka zitsanzo za anthu oipa amene anasintha. Ine ndidzakuuzani za mmodzi wa iwo. Ndipo, limodzi, tiyeni ife tione ngati ife tingathe kudziwa chifukwa chache iye anali woipa.

Dzina la munthuyo linali Saulo. Saulo anali munthu wachipembedzo kwambiri. Iye anali wa ku kagulu kachipembedzo kochedwa Afarisi. Iwo anali ndi Mau a Mulungu, koma iwo anasamalira kwambiri ziphunzitso za ena a atsogoleri ao a iwo okha. Kodi inu mukuganiza kuti chimenecho chinali chanzeru?—Icho chikanatha kutsogolera ku bvuto lalikuru.

Tsiku lina pamene Saulo anali m’Yerusalemu wophunzira wa Yesu wochedwa Stefano anagwidwa. Iwo anamtengera iye ku khothi. Ena a oweruzawo pa khothilo anali Afarisi. Ngakhale kuli kwakuti zinthu zoipa zinanenedwa ponena za iye, Stefano sanali ndi mantha. Iye analankhula ndi kuwapatsa oweruzawo umboni wabwino wonena za Mulungu ndi wonena za Yesu.

Koma oweruza amenewo sanazikonde zimene iwo anazimva. Iwo anakhala okwiya kwambiri. Iwo anamgwira Stefano ndi kumtengera iye kunja kwa mzindawo. Iwo anamgwetsera iye pansi, ndi kumponya miyala kufikira iwo atamupha iye.

Saulo anali pomwepo kumayang’ana pamene Stefano anali kuphedwa. Iye anaganizira kuti kunali kwabwino kumupha iye. Koma kodi ndi motani mmene iye anathera kuganizira chinthu choipa choterocho?—

Eya, Saulo anakula monga Mfarisi. Moyo wache wonse iye anaphunzitsidwa kuti iwo anali olondola. Iye anayang’ana kwa amuna amenewa kaamba ka chitsanzo chache. Chotero iye anawatsanzira iwo.

Tsopano popeza kuti Stefano anafa, Saulo anafuna kuwatha otsalira a ophunzira a Yesu. Iye anayamba kumapita m’nyumba mwao mwenimweni ndi kumawaturutsa ponse pawiri amuna ndi akazi. Pamenepo iye ankawachititsa iwo kuponyedwa m’ndende. Ambiri a ophunzira anasamuka m’Yerusalemu kuthawa Saulo. Koma iwo sanaleke kumalalikira ponena za Yesu.—Machitidwe 8:1-4.

Chimenechi chinamchititsa Saulo kuwada ophunzira a Yesu moonjezereka kwambiri. Chotero iye anapita kwa mkulu wa ansembe nalandira chilolezo cha kuwagwira Akristu mu mzinda wa Damasiko. Koma ali pa ulendo wa ku Damasiko chinthu chozizwitsa chinachitika.

Kuunika kunang’anima kuchokera kumwamba kowala kwambiri chakuti iko kunamchititsa khungu Saulo. Ndipo mau anati: “Saulo, Saulo, kodi nchifukwa ninji iwe uli kumandizunza ine?” Ameneyo anali Ambuye Yesu womalankhula ali kumwamba! Chotero Saulo anatsogozedwa wakhungu ku Damasiko.

Masiku atatu pambuyo pache Yesu anaonekera m’masomphenya kwa mmodzi wa ophunzira ache wochedwa Hananiya. Yesu anauuza Hananiya kukamzonda Saulo kukachotsa khungu lache ndi kukalankhula naye. Saulo tsopano anali wokonzekera kumvetsera. Pamene Hananiya analankhula naye, Saulo anachilandira choonadi chonena za Yesu. Maso ache analandira kupenya kwao. Kakhalidwe kache konse kanasintha. Iye anakhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu.—Machitidwe 9:1-22, NW.

Tsopano kodi inu mukuona chifukwa chache chimene Saulo anakhalira woipa kwambiri?—Iye anali ataphunzitsidwa zinthu zolakwa. Iye anali kumawatsatira anthu amene sanali okhulupirika kwa Mulungu. Ndipo iye anali wa ku kagulu ka anthu amene anawaika malingaliro a anthu patsogolo pa Mau a Mulungu. Koma Saulo anasintha chifukwa chakuti iye kwenikweni sanachide choonadi.

Pali anthu ambiri lero lino amene ali ngati Saulo. Iwo angathe kusintha, koma sikuli kwapafupi. Chifukwa chimodzi ndicho chakuti munthu wina ali kumagwira nchito zolimba kumchititsa munthu ali yense kuchita zoipa. Kodi inu mukumdziwa ameneyo?—Yesu analankhula za iye pamene iye analankhula ndi Saulo kuchokera kumwamba. Iye anamuuza Saulo kuti: ‘Ine ndiri kumakutuma iwe kukawatsegula maso a anthu, kuwatembenuza iwo kuchokera ku mdima kunka ku kuunika ndi kuchokera ku mphamvu ya Satana kunka kwa Mulungu.’—Machitidwe 26:17, 18, NW.

Inde, ndiye Satana Mdierekezi amene wachichititsa chiphunzitso chonse cha zinthu zoipa. Iye amawafuna anthu kukhala oipa. Chotero ngati ife tichita chimene chiri choipa, pamenepo Mdierekezi amakondwera. Koma ife timafuna kumkondweretsa Yehova, ati?—Kodi ndi motani mmene ife tingakhalire otsimikizira kuchichita chimenechi?—

Ife tidzamkondweretsa Mulungu ngati ife masiku onse timvetsera Baibulo ndi kuchita chimene ilo limanena. Pamene Baibulo limasonyeza kuti ife takhala tikumachita kanthu kena koipa, ife tiyenera kuleka kamakachita iko. Pamene ife tiphunzira kuchokera m’Baibulo ponena za zinthu zimene Mulungu amatifuna ife kuzichita, ife tiyenera kukhala achidwi kuzichita izo. Pamene ife tichita chimene chimamkondweretsa Mulungu ife tiri kumazichita zinthu zabwino, chifukwa chakuti Mulungu ali wabwino.

(Kaamba ka chithandizo m’kumachipewa chimene chiri choipa, werengani limodzi Miyambo 3:5-7; 12:15; 2:10-14; Salmo 119:9-11 [118:9-11, MO].)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena