Mutu 20
Ana Anaukitsidwa kwa Akufa
KODI sikuli kodabwitsa kudziwa kuti munthu wina amakukondani?—Chiri chinthu chabwino kwambiri kukhala ndi anthu amene kwenikweni amakusamalirani. Kodi inu mumadziwa kuti alipo munthu wina amene amakukondani inu kwambiri koposa mmene munthu wina ali yense pa dziko lapansi amachitira?—Ameneyo ndiye Yehova Mulungu.
Kodi ndi kwakukuru motani mmene Yehova amatikondera ife?—Kodi iye amangoganizira za ife pamene ife tiri panopo, ndipo kenaka kutiiwala ife pamene ife tamwalira? Kapena kodi iye kwenikweni amatikumbukira ife?—Baibulo limanena kuti ngakhale ‘imfa kapena moyo, kapena zinthu ziripo kapena zinthu zirinkudza, sizidzakhala zokhoza kutilekanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu.’—Aroma 8:38, 39, NW.
Chotero Mulungu samaiwala. Iye amawakumbukira anthu amene amamtumikira iye, ndipo iye amawakumbukiranso ana ao ang’ono. Ngakhale ngati iwo atamwalira, iye adzawabwezeretsa iwo ku moyo kachiwiri.
Pamene Mwana wa Mulungu Yesu anali pa dziko lapansi, iye anasonyeza kuti Yehova amawasamalira ana ang’ono. Yesu ankakhala ndi nthawi ya kulankhula ndi ana za Mulungu. Iye anaigwiritsiradi nchito mphamvu ya Mulungu kuwaukitsa ana kwa akufa! Kodi inu mungafune kumva mmene Yesu anachichitira ichi kaamba ka banja lina?—
Kunali munthu wina wochedwa Yairo. Iye ndi mkazi wache ndi mwana wao wamkazi wa usinkhu wa zaka khumi ndi ziwiri anali kukhala pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Atate ndi maiwo anamkonda mwana wao wamkaziyo kwambiri. Iye anali mwana wao mmodzi yekha.
Chotero inu mungathe kuyerekezera mmene iwo analiri achisoni pamene mtsikana wao wamng’onoyo anayamba kudwala kwambiri. Iwo anachita chinthu chiri chonse chimene iwo akadatha kumchiza iye, koma iye anangopitilira patsogolo. Yairo anatha kuona kuti mwana wache wamkaziyo adzafa. Ndipo panalibe chiri chonse chimene iye kapena adotolo akadatha kuchichita kumthandiza iye.
Koma mwinamwache Yesu akathandiza. Yairo anali atamva za munthu wodabwitsa ameneyu ndi mmene iye anali kuchiritsira anthu. Chotero Yairo anapita kukamfunafuna iye. Iye anampeza Yesu pa gombe la Nyanja ya Galileya akuphunzitsa anthu ambiri.
Yairo anayenda pakati pa khamulo ndi kugwa pa mapazi a Yesu. Iye anati kwa iye: ‘Mwana wanga wamng’ono wamkazi ali kudwala kwambiri. Kodi chonde mudzafika ndi kumthandiza iye? Ndikukupemphani kuti mudze.’
Pomwepo Yesu anapita limodzi ndi Yairo. Khamu limene linadza kudzamuona Mphunzitsi Wamkuruyo linatsatiranso. Koma iwo atayenda kaulendo pang’ono, amuna ena anadza kuchokera ku nyumba ya Yairo, namuuza iye kuti: “Mwana wako wamkazi wafa! Nkumbvutiranjinso mphunzitsiyo?”
Yesu anawamva amunawo akunena chimenechi. Iye anadziwa mmene Yairo anakhalira wachisoni kumtaya mwana wache mmodzi yekha. Chotero iye anamuuza iye kuti: ‘Usaope. Ingokhala ndi chikhulupiliro mwa Mulungu. Mwana wako wamkazi adzakhala bwino.’
Chotero iwo anapitirizabe kumayenda kufikira iwo anafika ku nyumba ya Yairo. Panopo mabwenzi a banjalo anali kulira. Iwo anali ndi chisoni chifukwa chakuti bwenzi lao laling’onolo linafa. Koma Yesu anawauza iwo kuti: ‘Lekani kulira. Mwanayo sanafe, koma iye ali kugona.’
Pamene Yesu ananena chimenechi, anthuwo anayamba kumamseka. Pakuti iwo anadziwa kuti mtsikanayo anafa. Koma Yesu ananena kuti mtsikanayo anali chabe kugona m’malo mwakuti awaphunzitse anthu amenewo phunziro. Iye anawafuna iwo kudziwa kuti mwa njira ya mphamvu ya Mulungu iye akadatha kumbwezeretsa ku moyo munthu wakufa mosabvuta kwambiri monga momwe ife tikadadzutsira munthu ku tulo.
Yesu tsopano analamulira kuti ali yense aturuke m’chipindacho kusiyapo atatu a atumwi ache ndi atate ndi mai wa mwanayo. Pamenepo iye analowa kumene mwanayo anali. Iye anamgwira iye dzanja, nati: ‘Buthu, dzuka!’ Ndipo pomwepo iye anadzuka nayamba kuyenda! Atate ndi maiwo anangodzazidwa ndi chisangalalo.—Marko 5:21-24, 35-43; Luka 8:40-42, 49-56.
Kodi inuyo munayamba mwakhala ndi bwenzi limene linafa?—Kodi inu mukakondwera ngati munthu ameneyo akadakhalanso ndi moyo kotero kuti inu mukadatha kusangalala kukhala naye kachiwiri? —Kodi nu mukuganiza kuti chimenechi chingathe kuchitika?—
Popeza kuti Yesu adatha kumbwezeretsa mtsikana ameneyo ku moyo, iye angathe kuchita chimodzimodzicho kaamba ka ena, ati?—Koma kodi iye adzachichitadi icho?—Inde, chifukwa chakuti Yesu mwiniyo anati: “Ora lirinkudza m’limene awo onse ali m’manda achikumbukiro adzamva mau ache ndi kuturuka.” Ndipo nthawi imeneyo irinkudza posachedwa, pansi pa ulamuliro wa ufumu wa Mulungu.—Yohane 5:28, 29, NW.
Tangoganizirani mmene kudzakhalira kodabwitsa kuwalandira anthu obweleranso ku moyo! Ena a iwo adzakhala anthu amene ife tinawadziwa. Ndipo ife tidzadziwa amene iwo ali pamene iwo abweranso kuchokera kwa akufa, monga momwedi Yairo anamdziwira mwana wache wamkaziyo pamene Yesu anamuukitsa iye. Enanso adzakhala anthu amene anamwalira zaka zikwi zambiri zapitazo. Koma kokha chifukwa chakuti iwo anakhalako kalekale, Mulungu sadzawaiwala iwo.
Kodi sikuli kodabwitsa kudziwa kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wache Yesu amatikonda ife kwakukuru motero?—Iwo amatifuna ife kukhala ndi moyo, osati kwa zaka zowerengeka zokha, koma kosatha!
(Ponena za chiyembekezo chodabwitsa cha Baibulo kaamba ka akufa, werenganinso Machitidwe 24:15, 1 Akorinto 15:20-22 ndi Yesaya 25:8.)