Mutu 21
“Machimo Ako Akhululukidwa”
PAMENE inu muchita chimene chiri choyenera chimakupangitsani inu kumva bwino, ati?—Inu mumadziwa kuti atate ndi mai wanu amakondweretsedwa, ndi kuti Yehova Mulungu yemwenso. Koma mosasamala kanthu mmene ife tingayesere zolimba, nthawi zina ife timachita chimene chiri cholakwa, ati?—Pamene ife tichita chimene Mulungu amanena kuti chiri cholakwa, chimenechi ndicho uchimo.
Mphunzitsi Wamkuruyo, Yesu Kristu, anasonyeza kuti uchimo umachita kanthu kena koipa kwa ife tonse. Iye anasonyeza chimenechi pamene iye anawachita amodzi a machitidwe ache odabwitsa kapena zozizwitsa.
Pa nthawi imeneyi Yesu analinkukhala m’tauni ina pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Khamu la anthu linadza kudzamuona iye komweko. Anthu ambirimbiri anadza chakuti panalibenso malo akuti ena alowe m’nyumbamo. Palibe munthu wina akadatha kumene kufika pafupi ndi chitseko.
Koma anthu ambiri anapitirizabe kumadza. Gulu limodzi la anthu linadza ndi munthu amene anali wodwala kwambiri. Iye anafa ziwalo. Kunafunikira amuna anai kumnyamulira iye pa kama kapena machira, chifukwa chakuti iye sakadatha kuyenda.
Kodi inu mukuchidziwa chifukwa chache chimene iwo anafuna kumtengera munthu wodwala ameneyu kwa Yesu?—Iwo anakhulupilira kuti Yesu akadatha kumchiritsa iye matenda amenewo.
Koma, limodzi ndi anthu onsewo m’nyumbamo, kodi iwo akadatha motani kumfikitsa munthu wakufa ziwaloyo kwa Yesu?—Amunawo anapeza njira. Iwo anakwera pamwamba pa chindwi. Ilo linali chindwi lathyathyathya. Ndipo iwo anapanga chiboo chachikuru pa ilo. Ndiyeno iwo anamtsitsira munthu wodwalayo ali pa machira ache kudzera pa chiboo chimenecho ndi kulowa m’chipinda pansipo. Ha, ndi chikhulupiliro chotani nanga chimene iwo anali nacho!
Anthu onse m’nyumbamo anadabwa pamene iwo anaona chimene chinali kumachitika. Munthu wakufa ziwaloyo ali pa machira ache anatsitsiridwa pansi penipeni m’chipindacho. Kodi Yesu anali wokwiya chifukwa cha zimene amunawo anazichita?—Ai kutalitali! Iye anali wokondwa kuchiona chikhulupiliro chao. Iye anati kwa munthu wakufa ziwaloyo: “Machimo ako akhululukidwa.”
Anthu ena sanganizire kuti kunali koyenera kuti Yesu anene choncho. Iwo sanaganizire kuti iye akadatha kukhululukira machimo. Chotero, kuti asonyeze kuti iye akadathadi, Yesu anati kwa munthuyo: “Dzuka, nyamula machira ako, nupite kwanu.”
Pamene Yesu ananena zimenezo, munthuyo anachira! Iye sanalinso wakufa ziwalo. Tsopano iye sanafunikire anthu ena kuti amtembe. Iye anali wokhoza kudzuka yekha ndi kuyenda ndi kunyamulanso machira ache.
Anthu amene anaziona zimenezi anali odabwa. M’miyoyo yao yonse iwo anali asanachione chinthu chiri chonse chodabwitsa ngati chimenecho.—Marko 2:1-12, NW.
Kodi nchiani chimene ifeyo tikuchiphunzira kuchokera m’chozizwitsa chimenechi!—Ife tikuphunzira kuti Yesu anali ndi mphamvu ya kukhululukira machimo ndi kuwachiza anthu odwala. Koma ife tikuphunziranso kanthu kenanso. Ife tikuphunzira kuti anthu amadwala chifukwa cha uchimo.
Kodi inu munayamba mwadwala?—Popeza kuti tonsefe tingathe kudwala, kodi chimenechi chimatanthauza kuti ife tonse tiri ochimwa?—Inde, Baibulo limanena kuti ife tonse tabadwira mu uchimo.
Kodi mukuchidziwa chimene icho chimatanthauza kubadwira mu uchimo?—Kumatanthauza kuti ife tonse tabadwa opanda ungwiro. Ife tonse timazichita zinthu zolakwa nthawi zina ngakhalebe kuli kwakuti ife sitimafuna kutero. Ife tinakhala otero chifukwa chakuti mwamuna ndi mkazi woyambayo, Adamu ndi Hava, sanamumvere Mulungu. Iwo anachimwa pamene iwo analiswa lamulo la Mulungu. Ndipo ife tonse tinalandira uchimo kuchokera kwa Adamu.
Kodi inu mukudziwa mmene ife tinaulandilira uchimo wathu kuchokera kwa iye?—Taimani ndikulongosolereni m’njira imene inu mungathe kumva. Mwinamwache inu mwapanga mapae amatope m’chiwaya. Kodi nchiani chimene chidzachitika ku pae yamatopeyo ngati inuyo mutiwiza chiwayacho? Kodi mukuchidziwa?—Chizindikiro chimodzimodzicho chidzaoneka pa mapae amatope onsewo amene inu muwapanga m’chiwaya chimenecho, ati?—
Adamu anali ngati chiwaya chimenecho, ndipo ife tiri ngati mapae amatope. Iye anakhala wopanda ungwiro pamene iye analiswa lamulo la Mulungu. Kunali ngati kuti iye analandira kutiwanizika kapena chizindikiro choipa. Chotero pamene iye anabala ana, kodi iwo akanakhala ngati chiani?—Ana ache onse akalandira chizindikiro chimodzimodzi chimenechi cha kupanda ungwiro.
Ana ochuruka samabadwa ndi kupanda ungwiro kwakukuru kumene inu mungathe kukuona. Iwo samakhala opanda mkono, kapena okhala ndi chiboo m’nthiti mwao. Koma kupanda ungwiro kumene iwo ali nako kuli kwakukuru kwambiri kotero kuti iwo amakhala odwala, ndipo m’kupita kwa nthawi, amafa.
Ndithudi, anthu ena amadwala mwakawirikawiri koposa ena. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Kodi chiri chifukwa chakuti iwo abadwa ndi uchimo wambiri?—Ai. Koma iko kungakhale chifukwa chakuti iwo samakhala ndi chakudya chokwanira cha kuchidya. Kapena iwo angadye keke ndi maswiti zochuruka. Iwo angakhale maso kufikira pakati pa usiku ndi kusapeza tulo tokwanira. Kapena iwo angakhale asanabvale zobvala zoyenera iwo asanalowe mu mvula kapena chisanu.
Kodi idzakhalapo nthawi pamene ife sitidzadwala? Kodi ife tidzalekana nawodi uchimo?—Eya, kodi nchiani chimene Yesu anamchitira munthu wakufa ziwalo ameneyo?—Iye anawakhululukira machimo ache, ndi kumchiritsa iye. M’njira imeneyi Yesu anasonyeza chimene iye adzawachitira awo onse amene amayesayesa zolimba kuchita chimene chiri choyenera.
Ngati ife tisonyeza kuti ife sitikuukonda uchimo, kuti ife timachida chimene chiri cholakwa, iye adzatichiritsa ife. Iye adzauchotsa uchimo umene ife tsopano tiri nao. Iye adzatichitira chimenechi posachedwapa mwa njira ya ufumu wa Mulungu.
Uchimo sudzachotsedwa mwa kamodzinkamodzi. Chimenecho chidzachitidwa m’kati mwa nyengo ya nthawi. Pa nthawi imeneyo, pamene uchimo wathu watha potsirizira pache, ife sitidzadwala konse kachiwiri. Ife tonse tidzakhala ndi thanzi langwiro. Ha, ndi dalitso lotani nanga limenelo lidzakhalira!
(Kaamba ka malingaliro oonjezereka othandiza onena za mmene uchimo umamyambukilira munthu ali yense ndi chimene ife tingachite ponena za uwo, werengani Aroma 3:23; 5:12; 6:12-14, 23 ndi 1 Yohane 2:1.)