Mutu 22
Munthu Amene Anaiwala Mulungu
PANALI munthu wina amene anadza kudzamuona Yesu tsiku lina. Iye anadziwa kuti Yesu anali wanzeru kwambiri. Iye anati kwa Yesu: ‘Mphunzitsi, uzani mbale wanga kuti andipatse zina za zinthu zimene iye ali nazo.’ Munthuyo anaganizira kuti iye anali ndi kuyenera ku zina za zinthu zimenezo.
Ngati inuyo mukanakhala Yesu, kodi nchiani chimene inu mukanachinena?—Yesu anaona kuti munthuyo anali ndi chothetsa nzeru. Koma chothetsa nzerucho sichinali chakuti iye anafuna chimene mbale wache anali nacho. Chothetsa nzeru cha munthuyo chinali chakuti iye sanachidziwe chimene chinali moonadi chofunika m’moyo.
Chotero Yesu anamuuza iye fanizo. Ilo linali lonena za munthu wina amene anaiwala Mulungu. Kodi inu mungafune kulimva ilo?—
Munthu wina anali wolemera kwambiri. Iye anali ndi minda ndi nkhokwe zambiri. Zakudya zimene iye anazibzala zinakula bwino kwambiri. Iye analibe malo m’nkhokwe zachezo oikamo zakudya zonse. Kodi iye akachita chiani?
Munthu wokhuphukayo anati mu mtima mwache: ‘Ndidzapasula nkokwe zanga ndi kumanga zazikuru. Pamenepo ndidzakundika zakudya zanga ndi zinthu zanga zonse zabwino m’nkhokwe zatsopano zimenezi.’
Munthu wokhuphukayo anaganizira kuti chimenechi chinali chinthu chanzeru kuchichita. Iye anaganizira kuti iye anali wochenjera kwambiri kukundika zinthu zambiri. Iye anati mu mtima mwache: ‘Ndiri ndi zinthu zambiri zabwino zokundikidwa. Izo zidzakhala nane zaka zambiri. Chotero tsopano ndingathe kupumula. Ndidzadya, kumwa ndi kudzisangalatsa ndekha.’
Koma panali kanthu kena kolakwika ndi kuganizira kwa munthu wachumayo. Kodi icho chinali chiani?—Iye anali kumangoganiza kokha ponena za iye mwini ndi chikondwelero chache. Koma iye anaiwala Mulungu.
Chotero Mulungu analankhula ndi munthu wachumayo. Iye anamuuza iye kuti: ‘Munthu wopusa iwe. Usiku uno iwe udzafa. Pamenepo kodi ndani amene adzakhala ndi zinthu zimene iwe wazikundika?’
Kodi munthu wachuma ameneyo akadatha kuzigwiritsira nchito zinthu zimenezo iye atamwalira?—Ai; munthu winawachenso akazitenga izo. Yesu anati: “Kulinso chimodzimodzi ndi munthu amene amadzikundikira yekha chuma koma sali wachuma kwa Mulungu.”—Luka 12:13-21, NW.
Inu simukufuna kukhala ngati munthu wachuma ameneyo, eti?—Chifuno chache chachikuru m’moyo chinali kupeza zinthu za kuthupi. Chimenecho chinali cholakwa chache. Iye masiku onse anafuna zoonjezereka.
Anthu ambiri ali ngati munthu wachuma ameneyo. Iwo masiku onse amafuna zochuruka. Koma chimenechi chingathe kutsogolera ku zothetsa nzeru zazikuru.
Mwachitsanzo, inu muli ndi zidole, ati?—Kodi zina za zidole zimene inu muli nazo ziri zotani? Ndiuzeni.—
Bwanji ngati mmodzi wa mabwenzi anu ali ndi galimoto labwino, kapena chidole cha mwana kapena chidole cha mtundu wina chimene inu mulibe? Kodi kukakhala koyenera kwa inu kuyesayesa kumlanda iye?—
Pangakhale nthawi zina pamene chidole chimaonekera ngati chofunika kwambiri. Koma kodi nchiani chimene chimachichitikira icho patapita nthawi?—Icho chimakhala chakale. Icho chingasweke, ndipo kenako ife sitimachifunadi icho konse. Ndithudi, inu muli ndi kanthu kena kamene kali kamtengo wapatali kwambirimbiri koposa zidole. Kodi mukuchidziwa chimene icho chiri?—Chimenecho ndicho moyo wanu. Ndipo moyo wanu umadalira pa kumachita chimene chimamkondweretsa Mulungu, ati?—Chotero inu musakhale ngati munthu wachuma wopusa ameneyo.
Sindiwo ana okha amene amachita zinthu monga ngati munthu wachuma ameneyo. Achikulire ochuruka amachitanso. Ena a iwo amafuna zochuruka koposa zimene iwo ali nazo. Iwo angakhale ndi chakudya kaamba ka tsikulo, zobvala za kuzibvala ndi malo okhala. Koma iwo amafuna zoonjezereka. Iwo amafuna zobvala zambiri. Ndipo iwo amafuna nyumba zokulirapo. Zinthu zimenezi zimadya ndarama. Chotero iwo amagwira nchito zolimba kuti apeze ndarama zochuruka. Ndipo pamene iwo apeza ndarama zambiri ndi pamenenso iwo amafuna zochuruka.
Achikulire ena amakhala otanganitsidwa kwambiri kumayesayesa kupeza ndarama chakuti iwo samakhala ndi nthawi ya kukhala limodzi ndi banja lao. Ndipo iwo alibe nthawi kaamba ka Mulungu. Kodi ndarama zao zingawakhalitsebe iwo ndi moyo?—Ai; Mulungu yekha angathe kuchita chimenecho. Kodi iwo angathe kuzigwiritsira nchito ndarama zao iwo atamwalira?—Ai; chifukwa chakuti akufa ali osakhoza konse kuchita kanthu kali konse.
Kodi chimenecho chimatanthauza kuti kuli kolakwa kukhala ndi ndarama?—Ai. Ife tingathe kugula nazo chakudya. Ife timagula nazo zobvala. Baibulo limanena kuti kukhala ndi ndarama kuli chinjirizo. Koma ngati ife “tikonda” ndarama, pamenepo ife tidzakhala ndi bvuto. Ife tidzakhala ngati munthu wachuma wopusa ameneyo amene anadzikundikira yekha chuma ndipo sanali wachuma kwa Mulungu.—Mlaliki 7:12.
Mphunzitsi Wamkuruyo ananena kuti munthu wachuma ameneyo anali wopusa chifukwa chakuti iye sanali “wachuma kwa Mulungu.” Kodi kumatanthauzanji kukhala “wachuma kwa Mulungu”?—Kumatanthauza kumuika Mulungu pa malo oyamba m’miyoyo yathu. Anthu ena amanena kuti iwo amamkhulupilira Mulungu. Iwo angawerengedi kuchokera m’Baibulo kamodzi kamodzi. Ndipo iwo amaganizira kuti chimenecho chiri chokwanira. Koma kodi iwo alidi “achuma” kwa Mulungu?—
Munthu amene ali wachuma ali ndi zambiri koposa ndi pang’ono. Iye ali ndi zochuruka. Ngati iye ali “wachuma kwa Mulungu,” moyo wache umadzazidwa ndi malingaliro ambiri onena za Mulungu. Iye amakonda kumalankhula za Mulungu kawirikawiri. Iye masiku onse ali kumazichita zinthu zimene Mulungu amamuuza iye kuzichita. Ndipo iye amaiononga nthawi yache limodzi ndi anthu amene amamkonda Mulungu.
Kodi umenewo ndiwo mtumdu wa anthu umene ife tiri? Kodi ife tiri “achuma kwa Mulungu”?—Ngati ife tiphunziradi kuchokera kwa Mphunzitsi Wamkuruyo, ife tidzakhaladi.
(Nawa malemba ena oonjezereka amene amasonyeza lingaliro loyenera kukhala nalo kulinga ku zinthu za kuthupi: 1 Timoteo 6:6-10; Miyambo 23:4; 28:20; Ahebri 13:5.)