Mutu 24
Chitandizo Chochokera kwa Angelo
ANTHU ena amanena kuti iwo amakhulupilira chokha chimene iwo angathe kuchiona. Koma kumeneko ndiko kupusa. Pali zinthu zenizeni zankhaninkhani zimene ife sitinazione konse ndi maso athu. Kodi inu mungathe kuchichula chimodzi?—
Bwanji mpweya? Ife timaupuma uwo. Kodi ife tingathe kuukhudza uwo?—Tukulani dzanja lanu. Tsopano ndidzakupiza pa ilo. Kodi mukuumva uwo?—Inde, koma ife sitingathe kuuona mpweya, kodi tingathe?—
Kodi palinso anthu amene ife sitingathe kuwaona?—Inde. Mulungu ndi mmodzi wa iwo. Ine sindinamuone konse iye, koma ndaziona zinthu zimene iye wazipanga. Inunso mwaziona zinthu zimenezo, ati?—Chotero ife timadziwa kuti Mulungu ali weniweni.
Ndipo Baibulo limanena kuti Mulungu anapanga unyinji wa anthu kuti ukhale naye kumwamba. Mulungu angathe kuwaona iwo, ndipo iwo angathe kumuona Mulungu. Koma iye anawapanga iwo motero kuti ife sitikadatha kuwaona iwo. Iyenso anawapanga iwo amphamvu kwambiri, amphamvu kwambiri koposa anthu. Iwo amachedwa angelo.
Mphunzitsi Wamkuruyo anawadziwa angelo. Pamene iye anali kumwamba iye anali mngelo. Ndipo iye anakhala limodzi ndi angelo ena. Iye anawadziwa mamiliyoni ambiri a iwo. Ndipo angelo amenewo ali okondweretsedwa ndi ife ngati ife timtumikira Yehova.
Kunali munthu wina wochedwa Danieli amene anamtumikira Yehova. Danieli anakhala m’Babulo. Anthu ambiri kumeneko sanamkonde Yehova. Iwo anamchititsadi Danieli kuponyedwa m’dzenje la mikango chifukwa chakuti iye sankaleka kupemphera kwa Yehova. M’menemo Danieli anali ndi mikango yanjala yonse imeneyo. Kodi nchiani chimene chikachitika? “Mulungu anatumiza mngelo wache ndi kutseka pakamwa pa mikangoyo.’ Danieli sanabvulazidwe konse! Angelo angathe kuchita zinthu zodabwitsa.—Danieli 6:18-22, NW.
Nthawi ina Petro anali m’ndende. Petro anali mtumwi wa Mphunzitsi Wamkuruyo. Anthu ena sanachikonde icho pamene iye anawauza iwo kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu. Chotero iwo anamuika Petro m’ndende. Asilikari anali kumamlondera Petro kutsimikizira kuti iye sanathawe. Kodi analipo munthu wina ali yense amene akadamthandiza Petro?—
Petro anali kugona pakati pa alonda awiri, ndipo m’mikono mwache munali unyolo. Koma Baibulo limati: “Taonani! Mngelo wa Yehova anadza, ndipo kuunika kunayamba kuwala m’chipinda cha ndendecho. Pomamkhudza Petro pambali pache, mngeloyo anamdzutsa Petro, kumati, “Dzuka! Fulumira!”’
Atatero, maunyolo a Petro analakatika m’mikono mwache! Ndipo mngeloyo anati kwa iye: ‘Bvala, bvala nsapato zako nunditsatire.’ Alondawo sadathe kuwaletsa iwo chifukwa chakuti mngelo anamthandiza Petro. Tsopano iwo anafika pa chipata chachitsulo, ndipo kanthu kachilendo kanachitika. Chipatacho chinatseguka chokha! Petro ndi mngeloyo anaturuka. Mngelo ameneyo anali atammasula Petro.—Machitidwe 12:4-11, NW.
Kodi angelo adzatithandizanso ife?—Inde, iwo adzatero. Kodi chimenecho chimatanthauza kuti iwo sadzatilola ife konse kubvulala?—Ngati inu mukanathamanga m’khwalala kutsogolo kwa galimoto, kodi mngelo akanakuchinjirizani?—Ai. Angelo samatiletsa ife kuti tisabvulale ngati ife tichita zinthu zopusa. Ngati inuyo mukanalupha pa nyumba yaitali, kodi angelo akanakuwakhani?—Mdierekezi anayesayesa kumchititsa Yesu kuchita chimenecho pa nthawi ina. Koma Yesu sakadachichita icho. Ife tingathe kuphunzira kuchokera m’chimenecho.—Luka 4:9-13.
Mulungu wawapatsa angelowo nchito yapadera kuti achite. Baibulo limalankhula za mngelo amene amawauza anthu kuli konse kulambira Mulungu.—Chibvumbulutso 14:6, 7.
Kodi ndi motani mmene angelo amachitira chimenecho? Kodi iwo amapfuula ali kumwamba kotero kuti munthu ali yense angathe kuwamva?—Ai; koma Akristu oona pa dziko lapansi amalankhula kwa ena ponena za Mulungu, ndipo angelowo amawatsogoza iwo m’nchito yao. Angelowo amatsimikizira kuti awo amene amafunandi kudziwa za Mulungu ali ndi mwai wakuti amve. Ife tingathe kukhala ndi phande m’nchito imeneyo, ndipo angelowo adzatithandiza ife.
Koma bwanji ngati anthu amene samamkonda Mulungu atipangira ife bvuto? Bwanji ngati iwo anayenera kutiika ife m’ndende, monga momwe iwo anachitira kwa Petro? Kodi angelo akatimasula ife?—Iwo angathe. Koma chimenecho sindicho chimene iwo masiku onse amachichita.
Nthawi ina pamene mtumwi Paulo anali mkaidi, angelowo sanammasule iye nthawi yomweyo. M’ndendemo munali anthu amene anafunanso kumva za Mulungu ndi Kristu. Kunali olamulira amene anafunanso kumva. Paulo akanatengeredwa pamaso pao, ndipo iye akanatha kulalikira kwa iwo. Koma angelowo masiku onse anadziwa kumene Paulo anali, ndipo iwo anamthandiza iye. Iwo adzatithandizanso ife, ngati ife timtumikiradi Mulungu.—Machitidwe 27:23-25.
Pali nchito ina yaikuru imene angelowo adzaichitanso, ndipo iwo adzaichita iyo posachedwa. Nthawi ya Mulungu ya kuononga anthu onse oipa iri pafupi kwambiri. Onse amene samamlambira Mulungu woonayo adzaonongedwa. Awo amene amanena kuti iwo samawakhulupilira angelo chifukwa chakuti iwo sangathe kuwaona iwo adzaona mmene iwo akhalira olakwa. Koma kudzakhala kochedwa kwambiri. Palibe ali yense wa oipawo adzapulumuka. Angelo adzawapeza iwo onse.—2 Atesalonika 1:6-8.
Kodi chimenecho chidzatanthauzanji kwa ife?—Ngati ife tiri ku mbali imodzimodzi monga angelowo, iwo adzakhala ngati abale kwa ife. Sipadzakhala chiri chonse cha kuchiopa. Iwo adzatithandiza ife.
Koma kodi ife tiri ku mbali imeneyo?—Ife tiriko ngati ife timtumikira Yehova. Ndipo, ngati ife timtumikira Yehova, ife tidzakhala tikumawauza anthu ena kumtumikiranso iye.
(Kuti muphunzire zochuruka ponena za mmene angelo amaisonkhezelera miyoyo ya anthu, werengani Salmo 34:7 [33:7, MO], Mateyu 18:10 ndi Machitidwe 8:26-31.)