Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 27 tsamba 111-114
  • Adedwa kaamba ka Kuchita Chabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Adedwa kaamba ka Kuchita Chabwino
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Kuchita Zinthu Zabwino Kumavuta
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yesu, Mphunzitisi Wamkuru
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 27 tsamba 111-114

Mutu 27

Adedwa kaamba ka Kuchita Chabwino

KODI INU mumachikonda chimene chiri chabwino?—Tonsefe tinganene kuti timatero, kodi sitingatero? Koma kodi ife timachikondadi icho kwambirimbiri chakuti ife tikanachichita chimene chiri chabwino ngakhale ngati ena anatida ife kaamba ka icho?—Kumafunikira kulimba mtima kuchichita chimenecho, ati?—

Kodi inu mukuganiza kuti Mphunzitsi Wamkuruyo anali ndi mtundu umenewo wa kulimba mtima? Kodi iye anachita chabwino ngakhale pamene ena anamuda iye kaamba ka icho?—

Kawirikawiri anthu anamkonda Yesu kaamba ka zinthu zabwino zimene iye anazichita. Pa nthawi ina anthu onse a mu mzinda anasonkhana pa khomo penipeni pa nyumba imene iye anali kukhala. Iwo anadza chifukwa chakuti Yesu anali kumawachiritsa anthu odwala.—Marko 1:33.

Koma nthawi zina chimene Yesu anachiphunzitsa chinasonyeza kuti anthuwo sanachikhulupilire choonadi. Kodi munthu ali yense anakonda kumumva iye pa nthawi imeneyo?—Kodi iwo anali ofunitsitsa kuzisintha zikhulupiliro zao?—Sikuti munthu ali yense anali wotero. Kunena zoona, ena a iwo anasonyeza udani weniweni kaamba ka Yesu chifukwa chakuti iye analankhula choonadi.

Chimenechi chinachitika tsiku lina mu mzinda wache wa Yesu wa Nazarete. Yesu analowa m’sunagoge. Ku sunagoge ndiko kumene anthu Achiyudawo anasonkhanako.

Yesu anaimilira ndi kukamba nkhani yabwino kwambiri kuchokera m’Malemba. Anthuwo choyamba anaikonda. Iwo anadabwa ndi mau okoma amene anaturuka pakamwa pache. Iwo sanathe kukhulupilira kuti ameneyu anali mnyamata amene anakulira mu mzinda wao wa iwo eni.

Koma kenako Yesu ananena kanthu kenanso. Iye anasimba ponena za nthawi pamene Mulungu anasonyeza chiyanjo chapadera kwa anthu amene sanali Ayuda onga iwo. Pamene Yesu ananena chimenechi, awo amene anali m’sunagogeyo anakwiya. Kodi mukudziwa chifukwa chache?—

Iwo anaganizira kuti iwo anali anthu okha oyenera kukhala ndi chiyanjo chapadera cha Mulungu. Iwo anaganizira kuti iwo anali abwino koposa anthu ena. Chotero iwo anamda Yesu kaamba ka chimene iye anachinena. Ndipo kodi mukuchidziwa chimene iwo anayesayesa kuchita kwa iye?—

Baibulo limati: ‘Iwo anamgwira Yesu ndi kumturutsira kunja kwa mzindawo. Iwo anamtsogolera iye pamwamba pa phiri ndipo anali kunka kukamponya iye kutseri kwache ndi kumupha iye! Koma Yesu anawathawa iwo.’—Luka 4:16-30.

Ngati chimenecho cikadachitika kwa inu, kodi inuyo mukadabweleranso kulankhula ndi anthu amenewo ponena za Mulungu kachiwiri?—Chimenecho chikafunikira kulimba mtima, ati?—Eya, pafupifupi chaka chimodzi pambuyo pache Yesu anabweleradi ku Nazarete. Ndipo Baibulo limati: “Iye anayamba kuwaphunzitsa iwo m’sunagoge mwao.” Yesu sanaleke kumalankhula choonadi chifukwa cha kuopa anthu amene analibe chikondi kaamba ka Mulungu.—Mateyu 13:54, NW.

Pa tsiku lina Yesu anali m’malo kumene kunali munthu wina amene dzanja lache linali lonse lopuwala kapena lopunduka. Yesu anali ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kumchiritsa munthu ameneyo. Koma anthu ena amene anali pomwepo anali kumayesayesa kumpangira Yesu bvuto. Kodi nchiani chimene Mphunzitsi Wamkuruyo akadachichita?—

Choyamba iye anasonyeza chimene chinali chinthu choyenera kuchichita. Iye anafunsa kuti: ‘Ngati inuyo munali ndi nkhosa imene inagwera m’dzenje lalikuru pa sabata, kodi inuyo mukadaiturutsamo?’

Inde, iwo akadachita chimenecho kaamba ka nkhosa, ngakhale pa tsiku la sabata, tsiku pa limene iwo anayembekezeredwa kupuma. Chotero Yesu anati: ‘Kuli kwabwinodi kumthandiza munthu pa tsiku la sabata, chifukwa chakuti munthu ali wopambana kwambiri koposa nkhosa!’ Ha, ndi koonekera bwino chotani nanga mmene iko kunaliri kuti Yesu ayenera kumthandiza munthu ameneyu mwa kumamchiritsa iye!

Chotero Yesu anamuuza munthuyo kutansa dzanja lache. Nthawi yomweyo ilo linachiritsidwa monga linalo! Ha, ndi wachimwemwe chotani nanga mmene munthuyo analiri!

Koma bwanji ponena za anthu ena amenewo? Kodi iwo anali okondwa?—Ai. Iwo anamuda Yesu ngakhale moonjezereka. Iwo anapita ndi kupanga malindi a kumupha iye!—Mateyu 12:9-14.

Anthu ali otero lero lino. Ena amakonda chimene chiri choyenera. Ena satero. Mosasamala kanthu za chimene ife tichichita, ife sitingathe konse kuwakondweretsa iwo onse. Chotero ife tiyenera kusankha amene ife kwenikweni tikufuna kumkondweretsa.

Kodi inu mumafuna yani monga mabwenzi anu? Kodi inu mumafuna anthu abwino kukhala mabwenzi?—Kodi inu mukumfuna Yehova Mulungu kukhala bwenzi lanu?—Pamenepo inuyo masiku onse muyenera kuchita chimene chiri choyenera.

Koma ngati inuyo muchita chabwino, kodi Mdierekezi adzakukondani inu?—Ndipo, kwenikweni, kodi inu mumamfuna Mdierekezi kukukondani inu?—

Pali anthu amene Mdierekezi amawakonda. Baibulo limawacha iwo “dziko lapansi.” “Dziko lapansi” lapangidwa ndi anthu onse amene sali atsatiri a Mphunzitsi Wamkuruyo. Mphunzitsi Wamkuruyo anati: “Ngati inu mukanakhala mbali ya dziko lapansi, dziko lapansi likanakonda chimene chiri chache cha ilo. Tsopano chifukwa chakuti inu simuli mbali ya dziko lapansi, koma ine ndakusankhani inu m’dziko lapansi, pa chifukwa cha chimenechi dziko lapansi lida inu.”—Yohane 15:18, 19, NW.

Anthu ena a dziko amanena kuti iwo amamkhulupilira Yesu, koma iwo samawaphunzitsa ena choonadi chonena za Mulungu monga momwe Yesu anachitira. Ngati inu muwasonyeza iwo kuchokera m’Baibulo kuti iwo sali kumaphunzitsa choonadi, kodi iwo adzachikonda chimenecho?—Ai, ochuruka a iwo sadzachikonda. Koma inu mungamupeze munthu wina wonga munthu uja wa dzanja lopuwala. Iye anali wokondwera kuti Yesu sanachibise choonadi.

Pali anthu amene amachibisa choonadi. Iwo amaopa chimene anthu ena amachiganizira. Iwo ali odera nkhawa kwambiri ponena za chimene anthu ena angachinene chakuti iwo amaleka miyoyo yao yonse kumachita chimene iwo amadziwa kuti chiri choyenera. Ha, ndi zamanyazi chotani nanga! Iwo amachiphonya chimwemwe chochuruka kwambiri m’moyo. Ndipo iwo amachiphonyanso chibvomerezo cha Mulungu. Ife sitikufuna kukhala otero, ati?—

(Werengani limodzi malemba awa kuti asonyeze kuti ife sitiyenera konse kuwalola mantha a chimene anthu ena angachiganizire kutilepheretsa ife kumachita chimene chiri choyenera: Miyambo 29:25; 1 Samueli 15:24; Mateyu 26:69-75; Yohane 12:42, 43.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena