Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 28 tsamba 115-118
  • Mbusa Wachikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbusa Wachikondi
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Amene Angatitonthoze
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yesu Amasamalira Nkhosa Zake
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Abusa Achikondi, Nkhosa Zokhulupirira
    Galamukani!—1988
  • Yehova Ndi Mbusa Wathu
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 28 tsamba 115-118

Mutu 28

Mbusa Wachikondi

KODI INU munayamba mwaona kukhala osungulumwa—Kodi inuyo munayamba mwadabwa ngati munthu ali yense samakukondaninso—Kapena kodi inu munayamba mwatayika?—Kodi munamva bwanji? Kungakupangitseni inu kuopsyedwa, ati?—

Mphunzitsi Wamkuruyo pa nthawi ina ananena mwambi wonena za munthu wina amene anatayika. Koma sanali mwana amene anatayikayo. Inali nkhosa.

Inu mukudziwa chimene nkhosa iri, ati?—Iyo ndi kanyama kakang’ono m’kamene munthu amapezamo ubweya. M’njira zina inu muli ngati nkhosa. Kodi chimenecho chiri motani?

Eya, nkhosa siziri zazikuru kapena zamphamvu kwambiri. Ndipo izo zimachita mantha pamene izo zatayika. Izo zimafuna chikondi ndi kukoma mtima. Ndipo izo zimafuna munthu wina kuzisamalira izo ndi kuzichinjiriza izo, monga momwe inu mumachitira. Munthu amene amasamalira nkhosa machedwa mbusa.

Mu mwambi wache Yesu anasimba za mbusa wina amene anali ndi nkhosa zana limodzi. Koma kenako imodzi ya nkhosazo inatayika. Iyo ingakhale itatanganitsidwa kumadya udzu pamene nkhosa zinazo zinachoka. Kapena iyo ingakhale itangofuna kuona chimene chinali kutseri kwa phirilo. Koma nkhosa imeneyo isanachidziwe icho, iyo inali kutali ndi zinazo. Kodi mungayerekezere mmene nkhosa yaing’onoyo inalingalirira pamene iyo inaunguzaunguza ndi kuona kuti inali yokha yokha?—

Kodi nchiani chimene mbusayo akachichita pamene iye akapeza kuti nkhosa imodzi inali kusoweka? Kodi iye akanena kuti muli monse chinali chifukwa cha nkhosayo chotero sadzadera nkhawa nayo? Kapena kodi iye akazisiya nkhosa makumi asanu ndi anaizo m’malo abwino ndi kupita kumaifunafuna imodzi yokhayo? Kodi nkhosa imodzi ikafanana ndi bvuto lalikuru limenelo?—Ngati inuyo mukadakhala nkhosa yotayika imeneyo, kodi inuyo mukadafuna kuti mbusayo akufunefuneni?—

Mbusayo anazikonda kwambiri nkhosa zache zonse, ngakhale ija imene inatayikayo. Chotero iye anapita kukaifunafuna yosowekayo.

Tanganizirani mmene nkhosa yotayika imeneyo inaliri yokondwa pamene iyo inamuona mbusa wache alinkudza. Ndipo Yesu ananena kuti mbusayo anakondwera kuti iye anaipeza nkhosa yache. Iye anakondwera nayo koposa nkhosa makumi asanu ndi anai zimene sizinatayikezo.

Tsopano, kodi ndani amene alipo amene ali ngati mbusa wa m’mwambi wa Yesu ameneyo? Kodi ndani amene amatisamalira ife mofanana ndi mmene mbusa ameneyo anazichitira nkhosa zache?—Yesu ananena kuti Atate wache wa kumwamba amatero. Ndipo Atate wache ndiye Yehova Mulungu.

Yehova ndiye Mbusa Wamkuru wa anthu ache. Iye amawakonda onse awo amene amamtumikira iye, ngakhale ana ang’ono ngati inu. Iye samafuna ali yense wa ife kubvulala kapena kuonongedwa. Kodi sikuli kodabwitsa kudziwa kuti Mulungu amatisamalira ife motero?— —Mateyu 18:12-14.

Kodi inuyo mumamkhulupiliradi Yehova Mulungu?—Kodi iye ali Munthu weniweni kwa inu?—

Nzoona kuti ife sitingathe kumuona Yehova. Ichi chiri chifukwa chakuti iye ndi Mzimu. Iye ali ndi thupi limene liri losakhoza kuonedwa ndi maso athu. Koma iye ali Munthu weniweni, ndipo iye angathe kutiona ife. Iye amadziwa pamene ife tifunikira chithandizo. Ndipo ife tingathe kulankhula naye m’pemphero, monga momwedi inu mumalankhulira kwa atate wanu ndi amai. Yehova amatifuna ife kuchita chimenechi.

Chotero, ngati muyamba kuona kukhala osukidwa kapena osungulumwa, kodi nchiani chimene inu muyenera kuchichita?—Lankhulani ndi Yehova. Yandikirani pafupi ndi iye. Ndipo iye adzakutonthozani ndi kukuthandizani inu. Kumbukirani kuti Yehova amakukondani, ngakhale pamene inu mumaona ngati kuti muli nokha nokha.

Tsopano, tiyeni titenge Mabaibulo athu. Tidzawerenga limodzi kanthu kena kamene kayenera kuisangalatsa mitima yathu. Pitani ku Salmo la makumi awiri mphambu atatu, ndipo tidzayamba ndi vesi loyamba.a

Pamenepo ilo limati: “Yehova ndiye Mbusa wanga. Sindidzasowa kanthu. Iye amandigonetsa ine pansi m’mabusa amsipu; iye amanditsogoza ine pafupi ndi malo opuma amadzi ambiri. Iye amautsitsimutsa moyo wanga. Iye amanditsogolera ine m’mabande a chilungamo kaamba ka chifukwa cha dzina lache. Chinkana ndiyenda m’chigwa cha mthunzi waukuru, sindiopa kanthu koipa, pakuti inu muli ndi ine; tsatsa lanu ndi ndodo yanu ndizo zinthu zimene zimanditonthoza ine.”(NW.)

Imeneyo ndiyo njira imene anthu amalingalirira ngati Mulungu wao ali Yehova. Kodi mmenemo ndimo mmene inuyo mumalingalirira?—

Monga momwe mbusa wachikondi amalisamalilira gulu lache la nkhosa, chomwechonso Yehova amawasamalira bwino lomwe anthu ache. Iwo amaona kukhala otsitsimulidwa chifukwa cha zinthu zabwino zimene iye amawachitira iwo. Iye amawasonyeza iwo njira yoyenera kuyendamo, ndipo iwo mokondwa amatsatira. Ngakhale pamene bvuto liripo ponseponse, iwo samachita mantha. Mbusa amagwiritsira nchito tsatsa lache kapena ndodo yache kuzichinjirizira nkhosazo ku zirombo zimene zingazibvulaze izo. Ndipo anthu a Mulungu amadziwa kuti iye adzawachinjiriza iwo. Iwo amaona kukhala osungika chifukwa chakuti Mulungu ali ndi iwo.

Yehova amazikondadi nkhosa zache, ndipo iye mokoma mtima amazisamalira izo. Baibulo limati: ‘Monga mbusa iye adzazitsogolera nkhosa zache za iye mwini. Iye adzazisonkhanitsira pamodzi zazing’ono ndi mikono yache. Zazing’onozo iye adzazithandiza limodzi ndi chisamaliro.’—Yes. 40:11.

Kodi icho chimakupangitsani inu kumva bwino kudziwa kuti Yehova ali wotero?—Kodi inu mukufuna kukhala mmodzi wa nkhosa zache?—

Nkhosa zimamvetsera mau a mbusa wao. Izo zimakhala pafupi ndi iye. Kodi inu mumamumvetsera Yehova?—Kodi inu mumakhala pafupi ndi iye—Pamenepo inu simufunikira konse kuchita mantha. Yehova adzakhala nanu.

(Yehova mwachikondi amawasamalira awo amene amamtumikira iye. Werengani limodzi chimene Baibulo limachinena ponena za ichi pa Masalmo 37:25 [36:25, MO]; 55:22 [54:24, MO]; Yesaya 41:10; Luka 12:29-31.)

[Mawu a M’munsi]

a Salmo 22, Malembo Oyera

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena