Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 32 tsamba 131-134
  • “Achimwemwe Ali Amtendere”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Achimwemwe Ali Amtendere”
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndi Bwino Kuchita Ndewu?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Galu Wanu Sangavulaze Ana?
    Galamukani!—1997
  • Nkhondo ya Kuchita Chimene Chiri Chabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Nthaŵi Zonse Umafuna Kukhala Woyamba?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 32 tsamba 131-134

Mutu 32

“Achimwemwe Ali Amtendere”

KODI INU mukuwadziwa anyamata ali onse amene masiku onse ali kumayesayesa kunyada ndi kubvuta?—Kodi inu mumakonda kukhala ndi iwo? Kapena kodi inu mukadakonda kukhala ndi munthu wina amene ali wamtendere?—

Mphunzitsi Wamkuruyo amadziwa mtundu wa munthu amene Mulungu amamkonda. Iye anati: “Achimwemwe ali amtendere, popeza kuti iwo adzachedwa ‘ana a Mulungu.’” Amenewo ndiwo mtundu wa anthu umene ife tikufuna kukhala, eti?—Ife tikufuna kukhala amtendere.—Mateyu 5:9, NW.

Koma nthawi zina anthu ena amachita zinthu zimene zimatikwiyitsa ife. Ndipo ife tingalingalire kufuna kumawabwezera iwo mofanana. Nthawi ina ichi chinachitika kwa ophunzira a Yesu.

Iwo anali kumayenda limodzi ndi Yesu kunka ku Yerusalemu. Pamene iwo anali atayenda ulendo wautalipo, Yesu anatuma ena kutsogola ku mudzi wina kukapeza malo akuti iwo akapumulirepo. Koma anthuwo kumeneko sanawafune iwo kuti akhale. Anthu amenewo anali ndi chipembedzo china. Ndipo iwo sanamkonde munthu ali yense amene anapita ku mzinda wa Yerusalemu kukalambira.

Ngati chimenecho chikadachitika kwa inu, kodi inuyo mukadachitanji? Kodi mukadakwiya? Kodi inuyo mukadafuna kuti inuyo muwabwezere iwo molingana?—

Chimenecho ndicho chimene ophunzirawo Yakobo ndi Yohane anafuna kuchita. Iwo anati kwa Yesu: ‘Kodi mukufuna kuti ife tiuze moto utsike kuchokera kumwamba ndi kuwaononga iwo?’ Koma Yesu anawauza iwo kuti sikunali koyenera kuwachitira anthu ena motero.—Luka 9:51-56.

Nzoona kuti anthu angakhale achipongwe kwa ife nthawi zina. Ana ena sangafune kuti inu musewere m’masewera ao. Iwo anganenedi kuti, “Ife sitikukufunani pano.” Pamene kanthu kena konga kameneko kachitika, kangathe kutichititsa ife kukhumudwa, ati?—Tinaglingalire kukhala tikufuna kuchita kanthu kena kuti tiwabwezere iwo molingana. Koma kodi tiyenera kutero?—

Bwanji osatenga kope lanu la Baibulo? Ndipo tiyeni tibandakule pa Miyambo chaputara cha makumi awiri mphambu anai, vesi la makumi awiri mphambu asanu ndi anai. Pamenepo pamati: “Usanene, Ndidzamchitira zomwezo anandichitira ine; ndidzabwezera munthuyo monga mwa machitidwe ache.”

Kodi chimenecho chimatanthauzanji kwa inu?—Icho chiri kumanena kuti ife sitiyenera kuyesa kubwezera. Ife sitiyenera kukhala achipongwe kwa munthu wina chifukwa chakuti iye anali wachipongwe kwa ife. Mulungu samatifuna ife kuchita chimenecho.

Koma bwanji ngati munthu wina ayesayesa kuyambana nanu ndeu? Iye angayeseyese kukuchititsani inu kukwiya mwa kumakutukwanani. Iye angakusekeni ndi kunena kuti mukuchita mantha. Mwinamwache iye akukuchani mkazi. Kodi nchiani chimene inu muyenera kuchita? Kodi inuyo muyenera kudzilola nokha kulowetsedwa m’ndeu?—

Kachiwirinso, tiyeni tione chimene Baibulo limachinena. Bandakulani pa Mateyu chaputara chachisanu ndi vesi la makumi atatu mphambu asanu ndi anai. Pamenepo Yesu amati: “Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.”

Kodi Yesu mwa chimenecho anatanthauzanji? Kodi iye anatanthauza kuti ngati wina akumenya iwe ndi nkhonya yache ku mbali imodzi ya nkhope yako, iwe uyenera kumlola iye akumenyenso ku mbali inayo?—Ai, iye sanatanthauze chimemecho.

Kupanda sikuli kofanana ndi kumenya ndi nkhonya. Uko kuli kofanana pang’ono ndi kukankha kapena kubwanyula. Munthu amachichita ichi kuti ayambe ndeu. Iye amafuna kuti ife tikwiye. Ndipo ngati ife tikwiya ndi kubwanyula kapena kukhula msonyo mobwezera, kodi nchiani chimene chimachitika?—Mwinamwache tidzalowa m’kumenyana.

Yesu sanawafune atsatiri ache kuchita motero. Chotero iye ananena kuti ngati munthu wina atipanda ife, ife sitiyenera kupanda mobwezera. Ife sitiyenera kukhala okwiya ndi kulowa m’kumenyana. Ngati titero, ife timasonyeza kuti ife tiri osasiyana ndi uyo amene anaiyamba ndeuyo.

Ngati bvuto liyamba, chinthu chabwino kwambiri ndicho kuchokapo. Munthu winayo angakankhe kapena kubwanyula kambirimbiri. Koma kumeneko mwinamwache kudzakhala kutha kwache. Pamene inu muchoka, sikumasonyeza kuti inu muli wofooka. Kumasonyeza kuti inu muli wamphamvu kaamba ka chimene chiri choyenera.

Tsopano, kodi nchiani chimene tiyenera kuchita ngati tiwaona anthu ena akumenyana? Kodi tiyenera kulowamo ndi kuthandizira mmodzi kapena winayo?—

Baibulo limatiuza ife chimene chiri choyenera. Bandakulani pa Miyambo chaputara cha makumi awiri mphambu asanu ndi chimodzi ndi vesi la khumi ndi chisanu ndi chiwiri. Ipo pamati: “Wakungopita ndi kubvutika ndi ndeu yosakhala yache akunga wogwira makutu a garu.”

Kodi nchiani chimene chikachitika ngati inu mukadawagwira makutu a garu? Kukampweteka garuyo, ndipo iye akakulumani, ati?—Pamene garuyo ayesayesa kuti apsyanthuke, ndi pameneso inu mumawagwira zolimba makutu ache. Ndipo ndi pameneso garuyo akachita ukali kwambiri. Ngati mumsiya iye, mwinamwache iye akakulumani zolimba. Koma kodi mungathe kungoimabe pomwepo ndi kuwagwira makutu ache kosatha?—

Eya, umenewo ndiwo mtundu wa bvuto m’limene tikakhalamo ngati ife tinalowelera m’ndeu ya pakati pa anthu ena. Ife sitingamdziwe amene anaiyamba ndeuyo kapena chifukwa chache chimene iwo ali kumenyanira. Munthu mmodzi angakhale akumenyedwa, koma mwinamwache iye anaba kanthu kena kuchokera kwa winayo. Ngati ife tikadamthandiza iye, ife tikadakhala tikumaithandiza mbala. Chimenecho sichikakhala chabwino, ati?—

Chotero, kodi nchiani chimene inu muyenera kuchichita ngati muona ndeu?—Ngati iri pa sukulu, mungathe kuthamanga ndi kumuuza mphunzitsi. Ndipo ngati kuli kutali ndi sukulu, mungathe kuitana mpolisi.

Ngakhale pamene anthu ena amafuna kuchita ndeu, ife tingathe kukhala amtendere. Iwo angafune kuchita ndeu. Koma tingathe kusonyeza kuti ife tiri amphamvu kaamba ka chimene chiri choyenera.

(Uphungu wabwino woonjezereka umene ungathe kumthandiza munthu kusalowa m’ndeu ukupezeka pa Aroma 12:17-21, Salmo 34:14 [33:14, MO] ndi 2 Timoteo 2:24.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena