Mutu 6
Mzimu Umene Umabwerera kwa Mulungu
SIPAYENERA kukhala chikaikiro m’maganizo mwa wofufuza ali yense woona mtima kuti chimene Baibulo limachicha “moyo” sichiri mbali yosakhoza kufa ya munthu imene imapitirizabe kukhalabe kukhalako kozindikira pambuyo pa imfa. Komabe pamene asonyezedwa umboni wochuluka wonena za mkhalidwe weniweni wa moyo, anthu ena amapereka zigomeko zina mwa kuyesa-yesa kuchirikiza chikhulupiriro chao chakuti kanthu kena m’kati mwa munthu kapitirizabe kukhalako pambuyo pa imfa.
Lemba limodzi la Baibulo limene limagwiritsiridwa ntchito kawiri-kawiri ndiro Mlaliki 12:7, limene limati: “Pfumbi ndi kubwerera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwerera kwa Mulungu amene anaupereka.” M’bukhu lake lochedwa Commentary, m’tsogoleri wachipembedzo cha Methodist cha Wesleyan Adam Clarke akulemba ponena za vesi limene’li kuti: “Panopo munthu wanzeru’yo akupanga kusiyanitsa koonekera bwino kopambana pakati pa thupi ndi moyo: izi siziri zimodzi-modzi; izo zonse siziri zopangika ndi zinthu zakuthupi. Thupi, limene liri lopangika ndi zinthu zakuthupi, limabwerera ku pfumbi, ku malo ake oyamba; koma mzimu, umene suli wopangika ndi thupi, umabwerera kwa Mulungu.” Mofananamo, A Catholic Commentary on Holy Scripture imati: “Moyo umabwerera kwa Mulungu.” Motero ndemanga zonse’zi zimasonyeza kuti moyo ndi mzimu ndi zofanana.
Komabe, mokodweretsa, ophunzira ena Achiroma Katolika ndi Achiprotesitanti amapereka lingaliro losiyana kotheratu. Mu “Glossary of Biblical Theology Terms” yoonekera mu Catholic New American Bible (lofalitsidwa ndi P.J. Kenedy & Sons, New York, 1970), timawerenga kuti: “Pamene ‘mzimu’ ukugwiritsiridwa ntchito mosiyana ndi ‘thupi,’ . . . cholinga sindicho kusiyanitsa mbali yopangika ndi zinthu zakuthupi ndi yosapangika ndi zinthu zakuthupi ya munthu. . . ‘Mzimu’ sumatanthauza moyo (soul).” Pa Mlaliki 12:7 katembenuzidwe kamene’ka kamagwiritsira ntchito, osati liu’lo “mzimu,” koma mau akuti “mpweya wa moyo (life).” Interpreter’s Bible Yachiprotesitanti ponena za mlembi wa Mlaliki imati: “Koheleth samatanthauza kuti umunthu wa munthu umapitirizabe kukhalako.” Polingalira kusiyana-siyana kwa malingaliro kotera’ko, kodi tingathe kukhala otsimikizira chimene kweni-kweni mzimu uli ndi m’lingaliro limene umabwerera kwa Mulungu?
Pa Mlaliki 12:1-7 ziyambukiro za ukalamba ndi imfa zikusonyezedwa m’chinenero cha ndakatulo. Pambuyo pa imfa, thupi potsirizira pake limabvunda ndipo kachiwiri’nso limakhala mbali ya pfumbi la dziko lapansi. “Mzimu,” nawo’nso, “umabwerera kwa Mulungu [woona].” Chotero imfa ya munthu imagwirizanitsidwa ndi kubwerera kwa mzimu kwa Mulungu, kumene’ku kukumasonyeza kuti moyo (life) wa munthu mwa njira ina umadalira pa mzimu umene’wo.
M’chinenero choyambirira lemba pa Mlaliki 12:7, liu Lachihebri lotembenuzidwa kukhala “mzimu” kapena “mpweya wa moyo (life)” ndiro ru‵ahha. Liu Lachigriki lofanana nalo ndiro pneuʹma. Pamene kuli kwakuti moyo (life) wathu umadalira’di pa njira ya kupuma, liu la Chinyanja’lo “mpweya” (monga momwe otembenuza ambiri amatembenuzira kawiri-kawiri mau akuti ruʹahh ndi pneuʹma) siliri katembenuzidwe kena koyenerera ka “mzimu.” Ndipo’nso, mau ena Achihebri ndi Chigriki, akuti, ne·sha·mahʹ (Chihebri) ndi pno·eʹ (Chigriki), amatembenuzidwa’nso kukhala “mpweya.” (Onani Genesis 2:7 ndi Machitidwe 17:25.) Komabe kuli koonekera bwino lomwe kuti, m’kugwiritsira ntchito “mpweya” monga katembenuzidwe kena ka “mzimu,” otembenuza akusonyeza kuti mau a chinenero choyamba amanena kanthu kena kamene kalibe umunthu koma kali kofunika kaamba ka kupitirizabe kwa moyo.
MZIMU UDZIWIKITSIDWA
Chakuti moyo (life) wa munthu umadalira pa mzimu (ruʹahh kapena pneuʹma) chikulongosoledwa motsimikizira m’Baibulo. Timawerenga kuti: “Ngati inu [Yehova] muchotsa mzimu [ruʹahh] wao, izo zifa, ndipo zimabwerera kupfumbi kwao.” (Salmo 104:29, NW) “Thupi lopanda mzimu [pneuʹma] liri lakufa.” (Yakobo 2:26) Chifukwa cha chimene’cho, mzimu ndiwo umene umapatsa moyo thupi.
Koma mphamvu yopatsa moyo imene’yi sindiyo mpweya chabe. Chifukwa ninji siziri choncho? Chifukwa chakuti moyo umakhalabe m’maselo a thupi kwa nyengo yaifupi kupuma kutaleka. Chifukwa cha chimene’chi zoyesa-yesa za kutsitsimutsa zingathe kupambana, ndipo’nso ziwalo za thupi zingathe kumezetseredwa kuchokera kwa munthu wina kumka kwa munthu wina. Koma zinthu zimene’zi ziyenera kuchitidwa mofulumira. Pamene mphamvu ya moyo’yo (life) yangochoka m’maselo a thupi, zoyesa-yesa za kutalikitsa moyo (life) zimakhala zopanda pake. Mpweya wonse m’dziko lapansi sukatha kukhalitsa’nso moyo ngakhale selo limodzi chabe. Utaonedwa motere, “mzimu” mwachionekere uli mphamvu ya moyo yosaoneka, yogwira ntchito m’selo liri lonse lamoyo la thupi la munthu.
Kodi mphamvu ya moyo (life) imene’yi imagwira ntchito mwa munthu yekha? Zimene zalongosoledwa m’Baibulo zingatithandize kufika pa lingaliro labwino ponena za chimene’chi. Ponena za kuonongedwa kwa moyo wa munthu ndi wa nyama m’chigumula cha pa dziko lonse lapansi, Baibulo limasimba kuti: “Zonse zimene m’mphuno zao munali mpweya [ne·sha·mahʹ] wa mzimu [ruʹahh] wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.” (Genesis 7:22) Pa Mlaliki 3:19 nsonga yaikulu yofanana’yo ikunenedwa mogwirizana ndi imfa kuti: “Chomwe chigwera ana a anthu chigwera’nso nyama’zo; ngakhale chowagwera n’chimodzi-modzi; monga wina’yo angofa momwemo zina’zo zifa’nso; inde onse’wo ali ndi mpweya (mzimu) [ruʹahh] umodzi; ndipo munthu sapambana nyama.” Chifukwa cha chimene’cho, munthu sapambana zinyama pamene pafika pa mzimu wopatsa moyo thupi lake. Mzimu wosaoneka umodzi-modzi’wo kapena mphamvu ya moyo uli mwa zonse’zo.
Kweni-kweni, mzimu kapena mphamvu ya moyo yogwira ntchito mwa zinyama ndi munthu yemwe ungayerekezeredwe ndi kuyenda kwa nyetsi kapena mphamvu ya magetsi kulowa m’makina kapena chipangizo. Mphamvu ya magetsi yosaoneka’yo ingagwiritsiridwe ntchito kuchita ntchito zosiyana-siyana, kumadalira pa mtundu wa makina kapena chipangizo chopatsidwa mphamvu’cho. Zitofu zingapangitsidwe kutulutsa kutentha, mafani kutulutsa mphepo, makompyuta kuwerengera masamu, ndipo mawailesi akanema kutulutsa’nso zithuzi-thunzi, mau ndi mapokoso ena. Mphamvu yosaoneka imodzi-modzi’yo imene imatulutsa mau m’chipangizo china ingatulutse kutentha m’china, kuwerengera masamu m’china. Koma kodi mphamvu ya magetsi’yo imatenga mikhalidwe imene kawiri-kawiri imakhala yocholowana-cholowana ya makina kapena zipangizo m’mene imagwiramo ntchito kapena ikuchitamo zinthu? Ai, imangokhala mphamvu ya magetsi—mphamvu chabe kapena mpangidwe wa nyonga.
Mofananamo, anthu ndi zinyama zomwe ‘ziri ndi mzimu umodzi wokha,’ mphamvu imodzi yokhalitsa moyo. Mzimu kapena mphamvu ya moyo (life) imene imatheketsa munthu kuchita ntchito za moyo si wosiyana konse ndi mzimu umene umatheketsa zinyama kutero. Mzimu umene’wo sumasunga mikhalidwe ya maselo a thupi lakufa’lo. Mwa chitsanzo, ponena za maselo a ubongo, mzimu sumasunga chidziwitso chosungidwamo ndi kupitirizabe njira za kuganiza popanda maselo amene’wa. Baibulo limatiuza kuti: “Mpweya [ruʹahh] (mzimu) wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake: tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.—Salmo 146:4.
Izi pokhala ziri choncho, kubwerera kwa ruʹahh kapena mzimu kwa Mulungu sikukadatanthauza kupitirizidwa kwa kukhalako kozindikira. Mzimu sumapitiriza njira za munthu zolingalirira. Uli chabe mphamvu ya moyo imene iribe kukhalako kozindikira popanda thupi.
M’MENE MZIMU UMABWERERERA KWA MULUNGU
Pamenepa, kodi ndi motani m’mene, mphamvu yosaoneka ndi yosakhala munthu kapena mzimu imene’yi imabwererera kwa Mulungu? Kodi umabwerera ku malo ake eni-eni kumwamba?
Njira mu imene Baibulo limagwiritsirira ntchito liu’lo “bwerera” simafunikiritsa kuti ife, m’chochitika chiri chonse, tiganize za kuyenda kweni-kweni kuchokera pa malo ena kumka pa ena. Mwa chitsanzo, Aisrayeli osakhulupirika anauzidwa kuti: “Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu.” (Malaki 3:7) Mwachionekere zimene’zi sizinatanthauze kuti Aisrayeli anayenera kuchoka pa dziko lapansi ndi kupita kumene kumakhala Mulungu. Kapena’nso kutanthauza kuti Mulungu akachoka ku malo ake kumwamba ndi kuyamba kukhala pa dziko lapansi ndi Aisrayeli. M’malo mwake, ‘kubwerera’ kwa Israyeli kwa Yehova kunatanthauza kutembenuka ku njira yolakwa ndi kugwirizana’nso ndi njira yolungama ya Mulungu. Ndipo ‘kubwerera’ kwa Yehova kwa Israyeli kunatanthauza kutembenuzira kwake chisamaliro chachiyanjo kwa anthu ake kachiwiri’nso. Mu zochitika zonse’zi kubwerera’ko kunalowetsamo mkhalidwe, osati kuyenda kweni-kweni kuchokera ku malo ena kumka ku ena.
Chakuti kubwerera kwa kanthu kena sikumafunikiritsa kuyenda kweni-kweni chingathe kulongosoledwa mwa fanizo ndi chimene chimachitika m’kusinthidwa kwa bizinesi kapena chuma kuchokera ku ulamuliro wa munthu wina kumka kwa wina’nso. Mwa chitsanzo, m’dziko lina ulamuliro wa njanji ungasinthidwe kuchoka m’kagulu ka bizinesi kumka m’manja mwa boma. Pamene kusintha kotero’ko kuchitika, zipangizo zonse za njanji ndipo ngakhale zolembedwa zonse zingakhalebe kumene ziri. Ndiwo ulamuliro pa izo umene umasintha.
Ziri chimodzi-modzi ndi mzimu kapena mphamvu ya moyo. Pa imfa palibe kuyenda kweni-kweni kuchokera pa dziko lapansi kumka ku malo akumwamba kufunikira kuchitika kuti uwo ‘ubwerere kwa Mulungu.’ Koma mphatso kapena chilolezo cha kukhala’ko monga cholengedwa chanzeru, imene munthu’yo anali nayo pa nthawi ina, tsopano imabwerera kwa Mulungu. Chija chimene chikufunika kupatsa moyo munthu’yo, ndiko kuti, mzimu kapena mphamvu ya moyo chiri m’manja mwa Mulungu.—Salmo 31:5; Luka 23:46.
Mkhalidwe’wo ungayerekezeredwe ndi uja wa munthu wotsutsidwa amene akunena kwa woweruza kuti, ‘Moyo wanga uli m’manja mwanu.’ Iye amatanthauza kuti chimene chidzachitikira moyo wake chiri ndi woweruza’yo. Wotsutsidwa’yo alibe chosankha m’nkhani’yo. Chachoka m’manja mwake.
Mofananamo, ponena za munthu wakufa, iye samakhala ndi ulamuliro pa mzimu wake kapena mphamvu ya moyo. Uwo wabwerera kwa Mulungu mu lingaliro lakuti iye amalamulira ziyembekezo za moyo wam’tsogolo wa munthu’yo. Ziri kwa Mulungu kusankha ponena zakuti kaya iye adzabwezeretsa mzimu kapena mphamvu ya moyo kwa wakufa’yo.
Koma kodi zimene’zi kweni-kweni zimatsekeratu kuthekera kuli konse kwa moyo pambuyo pa imfa? Kodi palibe kanthu kena’nso kokalingalira?
BWANJI ZA KUBADWA’NSO KAPENA KUSAMUKA KWA MOYO?
Anthu mamiliyoni ambiri a zikhulupiriro zosiyanasiyana zachipembedzo, kaya zochedwa Zachikristu kapena zosakhala Zachikristu, amakhulupirira kuti anthu anakhalako asanakhale ndi moyo wao watsopano lino’wu ndipo adzapitirizabe kukhala ndi moyo pambuyo pa imfa yao. Ngakhale kuli kwakuti malingaliro ao amasiyana-siyana kwambiri, iwo onse ali ndi chikhulupiriro chakuti mbali ina ya munthu imabadwa’nso kapena imasamukira m’thupi lina.
Popereka mbali imodzi ya chigomeko chochirikiza chikhulupiriro m’kubadwa’nso, bukhu lakuti A Manual of Buddhism limalongosola kuti: “Nthawi zina timakhala ndi zokumana nazo zodabwitsa zimene sizingalongosoledwe kusiyapo kokha mwa kubadwa’nso. Kodi ndi mwa kawiri-kawiri chotani m’mene timakumanira ndi anthu amene ife sitinakumane nawo ndi kale lonse ndipo komabe cham’kati timaona kuti iwo ali odziwika kwambiri kwa ife? Kodi ndi mwakawirikawiri chotani pamene timafika pa malo osiyana-siyana ndipo komabe ndi kuona kukhala okhutiritsidwa maganizo kuti tiri ozidziwa kwambiri ziri zonse za pa malopo?
Kodi munayamba mwaona zinthu zotero’zo? Mutakumana ndi munthu, kodi munayamba mwakhala ndi lingaliro lakuti mwam’dziwa kwa nthawi yaitali? Kodi n’chiani chimene chimachititsa chokumana nacho chotero’cho?
Pali zofanana zambiri mwa anthu. Mwina mwake, pambuyo pa kuganizira, inu mwininu munazindikira kuti munthu’yo anali ndi mikhalidwe yaumunthu ndi maonekedwe a thupi zofanana ndi zija za wachibale wina kapena bwenzi.
Momwemo’nso inu mungakhale mutakhala mu mzinda wina kapena kuona zithunzi-thunzi zake. Ndiyeno, pocheza mu mzinda wina, mungaone zofanana zina kotero kuti mukulingalira kuti simuli kweni-kweni pakati pa zinthu zachilendo ndi zosazolowereka.
Chotero, pamenepa, kodi si kwanzeru kunena kuti malingaliro a kudziwa anthu ndi malo osadziwidwa kale sali, ochititsidwa ndi moyo wakale, koma ochititsidwa ndi zokumana nazo za moyo wamakono? Kweni-kweni, ngati anthu onse akanakhala’di anali ndi kukhalako kwakale, kodi iwo onse sakanadziwa zimene’zi? Nanga, n’chifukwa ninji, mamiliyoni ambiri alibe mpang’on pomwe lingaliro kapena ganizo la kukhala atakhala ndi moyo kale? Ndipo’nso, kodi ndi motani m’mene munthu angapewere zolakwa za moyo wake wakale ngati sangathe kuzikumbukia konse? Kodi miyoyo yakale imene’yo ikakhala ya phindu lotani?
Ena angapereke kulongosola kwakuti ‘moyo ukanakhala wolemetsa ngati anthu akanadziwa tsatane-tsatane wa miyoyo yao yakale.’ M’menemo ndimo m’mene Mohandas K. Gandhi anaulongosolera, kuti: “Kuli kukoma mtima kwa chilengedwe kuti sitimakumbukira kubadwa kwakale. Ubwino wake uli pati kaya wa kudziwa mwatsatane-tsatane kubadwa kosawerengeka kumene ife takupanga? Moyo ukanakhala wolemetsa ngati tikananyamula katundu wamkulu wotero’yo wa zikumbukiro. Munthu wanzeru mwadala amaiwala zinthu zambiri, monga momwe’di loya amaiwalira milandu ndi nsonga zake mwamsanga pamene yatha.” Kumene’ko ndi kulongosola kokondweretsa, koma kodi ndi kozikidwa pa maziko olimba?
Pamene kuli kwakuti mphamvu yathu ya kukumbukira zinthu zambiri zimene takumana nazo ingakhale yochepa, maganizo athu ndithudi samakhala opanda kanthu kotheratu ponena za izo. Loya angaiwale nsonga zeni-zeni za milandu ina, koma chidziwitso chopezedwa m’kuchita nayo chimakhala mbali ya nkhokwe yake ya chidziwitso. Iye akanakhala’di wotayikiridwa kwambiri ngati iye akanaiwala kweni-kweni kanthu kali konse. Ndipo’nso, kodi n’chiani, chimene chimachititsa anthu kubvutika maganizo kwambiri—kuiwala-iwla kapena chikumbukiro chabwino? Kodi nkhalamba imene iri ndi chikumbukiro chabwino cha nkhokwe yake ya chidziwitso ndi kudziwa zinthu ziri bwino kwambiri koposa nkhalamba imene yaiwala kotheratu kanthu kali konse?
Kweni-kweni, kodi pakanakhala “kukoma mtima” kotani m’kufunikira kuphunzira’nso zinthu zimene munthu anaziphunzira kale m’kati mwa kukhalako kwake kwapapitapo? Kodi mukanakulingalira kukhala “kukoma mtima kwa chilengedwe” ngati zaka khumi ziri zonse za moyo wanu munaiwala kotheratu kanthu kali konse kamena munakadziwa ndipo munafunikira kuyamba kuphunzira chinenero kachiwiri’nso ndiyeno kuyamba kukulitsa nkhokwe ya chidziwitso ndi kudziwa zinthu, kokha kuti idzafafanizidwe? Kodi kumene’ku sikukanakhala kogwiritsa mwala? Kodi kumene’ku sikukanachititsa zopinga zoopsya? Nangano, n’kuyerekezereranji kuti, kumachitika zaka makumi asanu ndi awiri kapena makumi asanu ndi atatu ziri zonse? Kodi munganene kuti Mulungu wachikondi akadakhala atapanga kubadwa’nso kumene’ko kukhala mbali ya chifuno chake kaamba ka mtundu wa anthu?
Ambiri amene amalandira chiphunzitso cha kubadwa’nso amakhulupirira kuti awo okhala ndi moyo woipa adzabadwa’nso mu mtundu wotsika kapena monga tizirombo, mbalame kapena zinyama. Komabe nanga, n’chifukwa ninji kuli kwakuti, pali kuonjezeka kwakukulu kwambiri kwa chiwerengero cha anthu pa nthawi imene upandu ndi chiwawa zikuonjezeka pa mlingo wosafanana ndi wina uli wonse? Ndipo’nso, kodi n’chifukwa ninji ngakhale awo okhala mu mtundu wotsika kopambana amapambana pamene apatsidwa mwai wa maphunziro? Mwa chitsanzo, New York Times ya pa October 26, 1973, inasimba kuti mtsikana wa usinkhu wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi wa gulu lotsika anali mtsikana wanzeru kopambana m’sukulu pa Kallipashim, India. Iye anali waudongo kwambiri koposa mtsikana wa m’gulu lapamwamba, la Brahman. Kodi zimene’zi zingafotokozedwe motani? Kodi si zoona kuti chiphunzitso cha kubadwa’nso kapena kusamuka kwa moyo sichingapereka kulongosola zinthu zotero’zo kokhutiritsa?
Talingalirani’nso, za zipatso, zimene chiphunzitso chimene’cho chabala. Kodi sichinachotsere anthu ambiri mkhalidwe wolemekezeka, ukumawakakamiza kuyamba ntchito zonyozeka pansi pa mikhalidwe yogwirira ntchito yoipa, yokhala ndi kuthekera kochepa kwa kuongolera mkhalidwe wao m’moyo kupyolera mwa maphunziro?
KODI BAIBULO LIMAPHUNZITSA KUBADWA’NSO?
Ndithudi, anthu ena angasonyeze kuti kulingalira kwanzeru sikumachotsa kweni-kweni kuthekera kwa kubadwa’nso. Yankho lao la zigomeko zochulidwa papita’zo lingakhale lakuti: ‘Ngakhale Baibulo limaphunzitsa kubadwa’nso. Chimene’chi chiri chimodzi cha zinthu zambiri zimene anthu sangazilongosole mokwanira.’
Popeza kuti okhulupirira m’kubadwa’nso amalowetsa Baibulo m’kukambitsirana’ko tiyenera kufuna kulingalira zimene limanena’di. Kodi pali kweni-kweni umboni wotani wa Baibulo wokhulupiririra m’kubadwa’nso? Bukhu lochedwa What is Buddhism? Likuyankha kuti: “Kwa wowerenga Wachikristu tikasonyeza kuti [chiphunzitso cha kubadwa’nso] chikupereka bwino lomwe m’mbali zosakwanira zoonongedwa za ziphunzitso za Kristu zonga zimene ziripobe kufikira tsopano. Mwa chitsanzo, talingalirani, mphesekera zofala zimene zinalipo zakuti iye anali Yohane M’batizi, Yeremiya kapena Eliya wobweran’sno (Mat.xvi, 13-16). Ngakhale Herode anaonekera kukhala akuganiza kuti iye anali ‘Yohane M’batizi woukitsidwa kwa akufa.’”
Bwanji ponena za zigomeko zotero’zo? Kodi Yesu Kristu iye mwini ananena kuti anali Yohane M’batizi, Yeremiya kapena Eliya? Ai, mau amene’wa ananenedwa ndi anthu amene sanalandire Yesu monga momwe iye analiri kweni-kweni, ndiko kuti, Mesiya wolonjezedwa kapena Kristu. Yesu sakanakhala konse Yohane M’batizi, pakuti pamene anali pafupi-fupi zaka za kubadwa makumi atatu mnyamata’yo, Yesu anabatizidwa ndi Yohane, amene anali wokulirapo. (Mateyu 3:13-17; Luka 3:21-23) Mfumu Herode anatulutsa lingaliro lopanda nzeru lakuti Yesu anali Yohane woukitsidwa kwa akufa, chifukwa cha malingaliro ake okhala ndi liwongo kwambiri chifukwa cha kukhala atapha Yohane.
Koma kodi palibe mau achindunji a Yesu Kristu amene amaonedwa kukhala akuchirikiza chikhulupiriro cha kubadwa’nso kapena kusamuka kwa moyo? Inde, pali amodzi. Pa nthawi ina Yesu Kristu anagwirizanitsa Yohane M’batizi ndi mneneri wakale Wachihebri Eliya, kuti: “Eliya anadza kale, ndipo iwo sanam’dziwa iye, koma anam’chitira [zonse] zimene anazifuna iwo . . . . Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane M’batizi.” (Mateyu 17:12, 13) M’kulongosola kuti, “Eliya anadza kale,” kodi Yesu anatanthauza kuti Yohane M’batizi anali Eliya wobadwa’nso?
Yankho la funso limene’li liyenera kutsimikiziridwa pa zimene Baibulo lonse limanena. Ayuda ambiri kalekale m’nthawi ya utumiki wa pa dziko lapansi wa Yesu anaganiza’di kuti Eliya akabwera kweni-kweni. Ndipo ulosi wa Malaki unasonya m’tsogolo ku nthawi pamene Yehova Mulungu akatumiza mneneri Eliya. (Malaki 4:5) Komabe, Yohane M’batizi, sanadzione kukhala Eliya wobvala thupi kapena monga thupi lina la mneneri Wachihebri amene’yo. Pa nthawi ina Ayuda ena anam’funsa kuti, “Ndiwe Eliya kodi?” Yohane anayankha kuti, “Sindine iye.” (Yohane 1:21) Komabe, kunali kutanenedweratu kuti, Yohane akalambula njira Mesiya ‘wokhala ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya’ asanadze. (Luka 1:17) Chifukwa cha chimene’cho pamene Yesu anagwirizanitsa Yohane M’batizi ndi Eliya iye anali kungosonyeza m’mene ulosi’wo unakwaniritsidwira mwa Yohane amene anagwira ntchito yofanana ndi ija ya Eliya wakale.
Ndime ina ya Malemba yochulidwa ndi okhulupirira m’kusamuka kwa moyo ndiyo Aroma 9:11-13: “Asanabadwe [Esau ndi Yakobo] kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitana’yo, chotero kunanenedwa kwa [Rebeka], Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono. Inde monga kunalembedwa [pa Malaki 1:2, 3]: Ndinakonda Yakobo, koma ndimamuda Esau.” Kodi ndime imene’yi simasonyeza kuti kusankha kwa Mulungu kunazikidwa pa zimene Yakobo ndi Esau anali atachita m’kati mwa miyoyo ya kubalidwa kwao ndi Rebeka kusanakhale?
Bwanji osaiwerenga’nso? Onani kuti imanena kweni-kweni kuti kusankha kwa Mulungu kunapangidwa ali yense wa iwo asanachite cha bwino kapena choipa. Chotero kusankha kwa Mulungu sikunadalire pa mbiri ya ntchito zakale m’moyo wakale.
Pamenepa, kodi ndi maziko otani, Mulungu akadapanga chosankha kubadwa kwa anyamata’wo kusanachitike? Baibulo limabvumbula kuti Mulungu ali wakhoza kuona mwana wosabadwa ndipo, chifukwa cha chimenecho, amadziwa kaumbidwe ka zinthu zopereka khalidwe (genes) ka anthu asanabadwe. (Salmo 139:16) Pogwiritisira ntchito kudziwiratu kwake, Mulungu anazindikira m’mene anyamata’wo akakhalira kweni-kweni ponena za khalidwe ndi umunthu ndipo motero iye anatha kupanga chosakha cha uyo amene akakhala woyenerera kwambiri dalitso lalikulu kwambiri. Mbiri yopangidwa ndi anyamata awiri’wo m’moyo imatsimikizira nzeru ya kusankha kwa Mulungu. Pamene kuli kwakuti Yakobo anasonyeza kukondweretsedwa ndi zauzimu ndi chikhulupiriro m’malonjezo a Mulungu, Esau anasonyeza mkhalidwe wokonda zinthu zakuthupi ndi kusayamikira zinthu zopatulika.—Ahebri 11:21; 12:16, 17.
Ponena za kugwira mau kwa mtumwi Paulo m’Malaki ponena za ‘kukonda Yakobo’ kwa Mulungu ndi ‘kuda Esau,’ kumene’ku nako’nso, kumasonyeza lingaliro la Yehova ponena za iwo lozikidwa pa kaumbidwe kao ka zinthu zopereka khalidwe (genes). Pamene kuli kwakuti analembedwa ndi Malaki zaka mazana ambiri pambuyo pa nthawi ya moyo wao, mau’wo anatsimikizira zimene Mulungu anali atsasonyeza ponena za anyamata’wo asabadwe.
Funso limene linafunsidwa ndi ophunzira a Yesu ndiro chitsanzo china’nso chochulidwa ndi ena mochirikiza kusamuka kwa moyo. Ponena za munthu wakhungu chibadwire, ophunzira anafunsa kuti: ‘Anachimwa ndani, amene’yo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona?” (Yohane 9:2) Kodi mau amene’wo samabvumbula kuti munthu’yo anayenera kukhala ndi kukhalako kwakale?
Ai! Yesu Kristu sanagwirizane ndi lingaliro liri lonse lakuti mwana womakula m’mimba mwa amai wake anali atachimwa mwa iye yekha asanabadwe. Yesu anati: “Sanachimwa amene’yo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.” (Yohane 9:3) Ndiko kuti, zolakwika ndi zirema za anthu monga ngati khungu la munthu amene’yu zinapereka mwai wakuti ntchito za Mulungu zionekere mu mpangidwe wa kuchiritsa kozizwitsa. Pakanakhala popanda munthu ali yense wobadwa ali wakhungu, anthu sakanafika pa kudziwa kuti Mulungu angathe kupenyetsa munthu wobadwa ali wakhungu. Yehova Mulungu polola mtundu wa anthu wochimwa kukhalapo, wagwiritsira ntchito zolakwika ndi zirema zao kusonyeza zimene angawachitire.
Chotero pamene kuli kwakuti pangakhale malemba a Baibulo amene anthu ena amalingalira kuti amachirikiza lingaliro la kubadwa’nso, kupenda kosamalitsa kumasonyeza zosiyana ndi zimene’zo. Kunena zoona, palibe pali ponse m’Baibulo pamene timapeza kuchulidwa kuli konse kwa kubadwa’nso kapena kusamuka kwa moyo, mzimu kapena kanthu kena’nso kamene kamapulumuka imfa ya thupi. Ena ayesa ‘kulowetsa’ m’Malemba Oyera lingaliro la kubadwa’nso kapena kusamuka kwa moyo. Sindiko chiphunzitso cha Baibulo.
Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti kukhalako kozindikira sikumapitirizabe mwa njira ya moyo kapena mzimu umene umatuluka m’thupi pa imfa. Popatsa chiweruzo cha imfa munthu woyamba’yo chifukwa cha kusamvera Mulungu sanaike pamaso pake chiyembekezo chiri chonse cha kubadwa’nso kapena kusamuka kwa moyo. Adamu anauzidwa kuti: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe pfumbi ndi kupfumbi’ko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Inde, munthu’yo anayenera kubwerera ku pfumbi lopanda moyo la pansi.
Pamenepa, kodi tiziti kuti, moyo uno ndiwo wokha umene ulipo? Kapena, kodi pali makonzedwe a moyo wam’tsogolo amene ali opezeka m’njira ina? Kodi makonzedwe amene’wa angakupangitse kukhala kofunika kwa amoyo kuthandiza akufa, kapena kodi akufa ngosati n’kuthandizidwa konse ndi amoyo?
[Chithunzi patsamba 51]
Mzimu uli wofanana kwambiri ndi mphamvu ya magetsi, imene imachititsa zinthu zambiri kugwira ntchito koma simatenga mikhalidwe yao