Mutu 13
Bwanji Ponena za Moto wa Gehena?
‘ZOONA,’ wina anganene kuti, ‘Hade samagwiritsiridwa ntchito konse m’Baibulo kusonyeza malo a chizunzo chamoto. Koma kodi Baibulo silimanena za “moto wa helo”?’
Zoona, matembenuzidwe ambiri a Malemba Achikristu Achigriki (mofala ochedwa “Chipangano Chatsopano”) amagwiritsira ntchito mau’wo “moto wa helo” kapena “moto wambiri wa helo.” Motero liu Lachigriki lotembenuzidwa kukhala “helo” ndiro geʹen·na (Gehena). Koma kodi Gehena ndi dzina la malo a chizunzo chamoto? Inde, amatero ochitira ndemanga ambiri a Chikristu cha Dziko. Komabe iwo amadziwa bwino lomwe kuti moyo suli wosakhoza kufa. Iwo amadziwa’nso kuti Malemba amasonyeza kuti kusakhoza kufa kukuperekedwa monga mfupo kokha pa awo amene Mulungu amawasankha kukhala oyenerera kuilandira, ndipo osati monga themberero pa oipa kotero kuti akazunzidwe kosatha.—Aroma 2:6, 7; 1 Akorinto 15:53, 54.
Ochitira ndemanga ena a Chikristu cha Dziko amabvomereza kuti Gehena sali malo a chizunzo chamoto chamuyaya. The New Bible Commentary (tsamba 779) imati: “Gehena linali mpangidwe Wachihelene wa dzina la chigwa cha Hinomu pa Yerusalemu m’mene moto unali kuyaka chiyakire kuti upsyereze zinyalala za mzinda’wo. Umene’wu uli chithunzi-thunzi champhamvu cha chionongeko chotheratu.”
Kodi n’chiani chimene chiri choonadi cha nkhani’yo? Njira yabwino kwambiri yodziwira ndiyo kupenda chimene Baibulo leni-leni’lo limanena.
Liu’lo “Gehenna” likupezeka nthawi khumi ndi ziwiri m’Malemba Achikristu Achigriki. Kamodzi likugwirisiridwa ntchito ndi wophunzira Yakobo, ndi nthawi khumi ndi imodzi limapezeka m’mau onenedwa kukhala atanenedwa ndi Yesu Kristu ndipo limanena za chiweruzo chachitsutso. Malemba amene’wa amati:
“Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe [mwa njira imene’yo akumaweruza molakwa ndi kutsutsa mable wake kukhala wopanda pake mwamakhalidwe]: adzakhala wopalamula gehena. Wamoto.”—Mateyu 5:22.
“Musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma maka-maka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.”—Mateyu 10:28.
“Ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kugehena, inde, ndinena ndinu opani amene’yo.”—Luka 12:5.
“Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupita-pita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m’mene akhala wotere, mum’sandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri. Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa gehena?”—Mateyu 23:15, 33.
“Ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: n’kwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m’gehena, m’moto wosazima. Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m’moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m’gehena. Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m’Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m’gehena; kumene’ko mphutsi yao siikufa, ndi moto suzimidwa.”—Marko 9:43-48; onaninso ndime zokhala ndi mau ofanana’wo pa Mateyu 5:29, 30; 18:8, 9.
“Ndipo lirime ndiro moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lirime, ndiri lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena [ndiko kuti, kugwiritsiridwa ntchito mosayenera kwa lirime n’koononga mofanana ndi Gehena; kungayambukire’di moyo wonse wathunthu mu umene munthu amalowa mwa kubadwa kwakuti ungachititse kuyenerera kwake chiweruzo cha Gehena].”—Yakobo 3:6.
Onani kuti, pamene kuli kwakuti malemba amene’wa amagwirizanitsa moto ndi Gehena, palibe liri lonse la iwo limanena za kukhala’ko kuli konse kozindikira, kubvutika kuli konse, pambuyo pa imfa. M’malo mwake, monga momwe kwasonyezedwera pa Mateyu 10:28, Yesu anasonyeza kuti Mulungu angathe “kuononga,” osati thupi lokha, koma munthu wathunthu, moyo, m’Gehena. Kodi kweni-kweni chionongeko chimene’chi n’cha mtundu wanji? Kuzindikiridwa kwa chimene’chi kukupezedwa mwa kupendedwa kosamalitsa kwa liu’lo “Gehena.”
GEHENA—CHIGWA CHA HINOMU
Ngakhale kuli kwakuti likupezeka m’Malemba Achikristu Achigriki, “Gehena” latengedwa m’mau awiri Achihebri, Gaʹi ndi Hin·nomʹ, otanthauza Chigwa cha Hinomu. Chigwa chimene’chi chiri kumwela ndi kumwela chakumadzulo kwa Yerusalemu. M’masiku a Mafumu osakhulupirika a Yudeya Ahazi ndi Manase Chigwa cha Hinomu chinatumikira monga malo ochitira madzoma achipembedzo a kulambira mafano, kuphatikizapo chizolowezi chonyasa cha kupereka nsembe ana. (2 Mbiri 28:1, 3; 33:1, 6; Yeremiya 7:31; 19:2, 6) Pambuyo pake, Mfumu yabwino Yosiya inaletsa kulambiridwa kwa mafano kochitiridwa kumene’ko ndipo inapangitsa chigwa’cho kukhala chosayenerera kugwiritsiridwa ntchito kaamba ka kulambira.—2 Mafumu 23:10.
Mau ongopatsirana-patsirana amalongosola kuti Chigwa cha Hinomu pambuyo pake chinakhala malo otayira zinyalala. Ndipo Baibulo limapereka chitsimikiziro cha zimene’zi. Mwa chitsanzo, pa Yeremiya 31:40, Chigwa cha Hinomu mwachionekere chikuchedwa “chigwa” . . . chamitembo, ndi cha phulusa.” Panali’nso “Chipata cha kudzala,” chipata chimene chikuonekera kukhala chitatsegulidwa ku malekezero akuma’mawa kwa Chigwa cha Hinomu ndi pokumanira pake ndi Chigwa cha Kidroni.—Nehemiya 3:13, 14.
Chakuti Gehena ayenera kugwirizanitsidwa ndi mbali zosakaza za dzala la mzinda chiri chogwirizana kotheratu ndi mau a Yesu Kristu. Ponena za Gehena, iye anati, “mphutsi yao siikufa, ndi moto wao suzimidwa. (Marko 9:48) Mau ake mwachionekere amasonyeza cheni-cheni chakuti moto unayaka chiyakire pa dzala la mzinda’wo, mwina mwake ukumaonjezeredwa ndi kuonjezeredwa kwa sulfure. Kumene moto’wo sunafike, nyongolotsi kapena mphutsi zikabadwa ndi kudya zimene sizinapsye ndi moto.
Kuyenera kuzindikiridwa’nso kuti Yesu, m’kuchula Gehana m’njira imene’yi, sanayambitse lingaliro losagwirizana kotheratu ndi Malemba Achihebri. M’Malemba oyambiriri’wo kanenedwe kofanana kwambiri kamapezeka ponena za chimene chidzagwera anthu opanda umulungu.
Yesaya 66:24 amaneneratu kuti anthu okhala ndi chiyanjo cha Mulungu “adzatuluka ndi kuyang’ana mitembo ya anthu amene anandilakwira Ine [Mulungu], pakuti mbozi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.” Mwachionekere chimene’chi sichiri chithunzi-thunzi cha chizunzo chozindikira koma cha chionongeko choopsya. Chimene chatsala, si miyoyo yozindikira kapena “mizimu yopanda thupi,” koma “mitembo.” Lemba’lo limasonyeza kuti ndizo, osati anthu, koma mphutsi kapena mbozi zokhala pa iyo zimene ziri zamoyo. Palibe kuchulidwa kuli konse pano kwa “moyo wosafa” uli wonse.
Mu ulosi wa Yeremiya Chigwa cha Hinomu chikugwirizanitsidwa mofananamo ndi chionongeko cha anthu opanda chikhulupiriro. “Taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzachedwa’nso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu. Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi Yerusalemu m’malo ano; ndipo ndizagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndizapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m’mlengalenga, ndi cha zirombo za dziko lapansi.”—Yeremiya 19:6, 7.
Onani kuti kuchula kwa Yeremiya Chigwa cha Hinomu kulibe chisonyezero mpang’ono pomwe cha chizunzo chozindikira pambuyo pa imfa. Chithunzi-thunzi chimene chikusonyezedwa ndicho cha chionongeko chotheratu, “mitembo” ikumadyedwa ndi mbalame ndi zinyama zodya zakufa.
CHIZINDIKIRO CHA CHIONONGEKO
Pamenepa, mogwirizana ndi umboni wa Baibulo, Gehena kapena Chigwa cha Hinomu moyenerera akatha kutumikira monga chizindikiro cha chionongeko koma osati cha chizunzo chamoto chozindikira. Joseph E. Kokjohn, m’magazini Achikatolika ochedwa Commonweal, akubvomereza chimene’chi, kuti:
“Mwachionekere, malo otsiriza a chirango, ndiwo Gehena. Chigwa cha Hino[mu], chimene pa nthawi ina chinali malo kumene nsembe za anthu zinaperekedwera kwa milungu yachikunja, koma m’nthawi za Baibulo chinali chitakhala kale dzala la mzinda, mulu wa zinyalala kunja kwa Yerusalemu. Panopo pfungo ndi utsi ndi moto zinali chokumbutsa cha nthawi zonse kwa okhalamo za chimene chinachitikira zinthu zimene zinali zitatumikira chifuno chao—izo zinaonongedwa.”
Chakuti chionongeko chophiphiritsiridwa ndi Gehena chiri chosatha chikusonyezedwa kwina’nso m’Malemba Oyera. Mtumwi Paulo, polembera kalata Akristu a ku Tesalonika, ananena kuti awo owasautsa “adzamva chirango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemeero wa mphamvu yake.”—2 Atesalonika 1:6-9.
Umboni wa Baibulo motero umamveketsa bwino lomwe kuti awo amene Mulungu amawaweruza kukhala osayenerera moyo adzalandira, osati chizunzo chamuyaya m’moto weni-weni, koma “chiongeko chosatha.” Iwo sadzasungidwa amoyo kuli konse. Chifukwa cha chimene’cho moto wa Gehena uli chizindikiro chabe cha kutheratu ndi kukwanira kwa chionengeko chimene’cho.
Kuyenera kuzindikiridwa kuti, polankhula ndi atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake, Yesu Kristu anati: “Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa gehena?” (Mateyu 23:33) Kodi n’chifukwa ninji zinali chonchi? Chinali chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzo amene’wo anali onyenga. Iwo anafuna kuonedwa ndi kuchedwa ndi maina aulemu apamwamba, koma iwo analibe nkhawa kaamba ka awo amene iwo anayenera kuwathandiza mwauzimu. Iwo analemeza ena ndi malamulo amiyambo, nanyalanyaza chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Iwo anali aphunzitsi onyenga, akumaika miyambo ya anthu pamwamba pa ulamuliro wa Mau a Mulungu.—Mateyu 15:3-6; 23:1-32.
Kodi mwaona zinthu zofanana’zo pakati pa atsogoleri achipembedzo a lero lino, maka-maka m’Chikristu cha Dziko? Kodi zidzawayendera bwino kwambiri koposa atsogoleri achipembedzo Achiyuda m’nthawi ya utumiki wa pa dziko lapansi wa Yesu? Kutali-tali kumene, pakuti atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko mosamvera ananamizira Mulungu ndi “mbiri yabwino yonena za Ambuye wathu Yesu.” Chotero malinga ngati iwo apitirizabe kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga iwo ali pa upandu wa kulandira ‘chirango ha chionongeko chosatha.’
Chifukwa cha chimene’cho choonadi chonena za Gehena chiyenera kutithandiza kuzindikira kufunika kwa kupewa kugwirizana ndi chipembedzo chonyenga. Osati kokha atsogoleri’wo koma’nso, monga momwe Yesu anasonyezera, awo amene amachirikiza aphunzitsi onyenga achipembedzo ali mu upandu. Kunena zoona, Yesu Kristu, ananena za otembenuka a alembi ndi Afarisi kukhala akusanduka ‘ana a gehena oposa iwo kawiri.’ (Mateyu 23:15) Motero, anthu amene mwakhungu akupitirizabe kutsatira kuphunzitsa konyenga kwachipembedzo lero lino sangayembekezere kupulumuka chiweruzo chachirango cha Mulungu.
Pamene chikutipangitsa kulingalira mwamphamvu ponena za mkhalidwe wathu wa ife eni, chimene’chi chingathe’nso kukhala chitsimikiziritso chotonthoza kwa ife. Kodi ziri choncho motani? M’chakuti tingatsimikizire kuti Yehova Mulungu sadzasiya cholakwa chachikulu chosaperekeredwa chirango. Ngati anthu sakufuna kugwirizana ndi malamulo ake olungama ndipo mwadala akupitiriza m’njira yoipa, iye sadzawalola kwa nthawi yaitali kupitirizabe kudodometsa mtendere wa anthu olungama.
[Mapu patsamba 113]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
MAPU A YERUSALEMU A M’ZAKA ZA ZANA LOYAMBA
MALO A KACHISI
CHIGWA CHA HINOMU (GEHENA)