Mutu 18
Chifukwa Chake Ambiri Amene Ali ndi Moyo Tsopano Ali ndi Mwai wa Kusafa Konse
NTHAWI yakuti ufumu wa Mulungu uyambe kuyendetsa zochitika zonse za dziko lapansi iri pafupi kwambiri. Inu mungakhale pakati pa awo odzaona madalitso akulu amene udzadzetsa kwa mtundu wa anthu. Kumene’ko sindiko kunena kopanda maziko. Pali umboni wochuluka wokuchirikiza, kuphatikizapo umboni umene inu mwininu mwauona.
Zaka mazana ambiri zapita’zo Yehova Mulungu anabvumbula nthawi yeni-yeni yopereka ulamuliro pa uyo amene iye akamuika kukhala mfumu pa dziko la mtundu wa anthu. Iye anagwiritsira ntchito zizindikiro kutero ndipo napereka china cha chidziwitso’cho mwa njira ya loto.
Chakuti njira zolankhulirana zotero’zo zinagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kupereka chidziwitso chofunika kwambiri chimene’chi kwa anthu sichiyenera kupereka zikaikiro. Lingalirani zimene anthu amakono akuchita tsopano m’kupereka chidziwitso. Mauthenga obisika amatumizidwa m’zizindikiro kudzera m’lengalenga. Pambuyo pake mauthenga a m’zizindikiro amene’wa “amamasuliridwa” mwina ndi anthu kapena makina. Mkhalidwe umene’wu wotumizira chidziwitso uli ndi chifuno. Umabisa tanthauzo la chidziwitso’cho kwa awo amene sali ochiyenerera.
Momwemo’nso, kugwiritsira ntchito zizindikiro kwa Mulungu sikunakhale kopanda chifuno. Kuzindikiridwa kwa zizindikiro zimene’zo kunafunikira kuphunzira kosamalitsa. Koma anthu ambiri ali osafunitsitsa kukhala ndi nthawi kuti azindikire, chifukwa cha kusakonda kweni-kweni Mulungu ndi choonadi. Chifukwa cha chimene’cho, “zinsinsi [zopatulika] za Ufumu” ziri zobisikabe kwa iwo.—Mateyu 13:11-15.
LOTO LAKAKE LOLOSERA
Chimodzi cha ‘zinsinsi zopatulika’ zimene’zo chiri m’bukhu la Baibulo la Danieli. Bukhu limene’lo limapereka zofunika zodziwira nthawi yoperekera ulamuliro wa ufumu kwa mfumu yosankhidwa ya Mulungu. M’chaputala chachinai cha bukhu limene’lo mudzapeza mutalongosoledwa loto lotumizidwa ndi Mulungu la Mfumu Nebukadinezara ya Babulo. Kodi n’chiani chimene chinali cholinga kapena chifuno cha loto limene’li ndi kukwaniritsidwa kwake? Cholembedwa’cho chimalongosola kuti:
“Kuti amoyo adziwe kuti Wam’mwamba-mwamba alamulira m’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.”—Danieli 4:17.
Zimene zinali m’loto’lo kwakululu-kulu zinali izi: Mtengo waukulu unaonedwa ukulikhidwa molamulidwa ndi mngelo “woyera.” Chitsa cha mtengo’wo pamenepo chinamangidwa ndi mkombero kuti chisaphuke. Unayenera kukhala chimangidwire chomwecho pakati pa “msipu wa kuthengo” kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri.”—Danieli 4:13-16.
Kodi n’chiani chimene chinali tanthauzo la loto limene’li? Kulongosola kouziridwa kwa mneneri Danieli kwa Nebukadinezara kunali kwakuti:
“Mtengo mudauona . . . ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.
“Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengo’wo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m’nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa mu msipu wa kuthengo, nichikhale chikhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitam’pitirira nthawi zisanu ndi ziwiri; kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamulo cha Wam’mwamba-mwamba chadzera mbuye wanga mfumu: kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng’ombe, nimudzakupitirirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam’mwamba-mwamba alamulira m’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.
“Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.”—Danieli 4:20-26.
Chotero loto limene’li linali ndi kukwaniritsidwa koyambirira pa Mfumu Nebukadinezara. Kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri,”kapena zaka zisanu ndi ziwiri zeni-zeni, Nebukadinezara anali wopenga. Komabe, ufumu wake, unasungidwira iye kotero kuti, atachira misala yake, iye anayambira’nso ntchito yake ya ufumu.—Danieli 4:29-37.
UFUMU WA “WOLUBUKIRA WA ANTHU”
Koma cholembedwa chatsatane-tsatane chimene’chi chonena za mtengo wolikhidwa’wo sichinali cholekezera m’kukwaniritsidwa kwake kwa Mfumu Nebukadinezara. Kodi tikudziwa zimene’zi motani? Chifukwa chakuti, monga momwe kunalongosoledwera m’masomphenya eni-eni’wo, chimagwirizanitsa ufumu wa Mulungu ndi ulamuliro wochitidwa ndi uyo amene iye am’sankha. Ndipo kodi ndani amene ali wosankhidwa wa Mulungu kaamba ka ufumu’wo? Yankho loperekedwa kwa Mfumu Nebukadinezara linali lakuti: “wolubukira wa anthu.”—Danieli 4:17.
Zeni-zeni za mu mbiri zimatsimikizira mosatsutsika kuti kudzichepetsa sikunasonyezedwe ndi olamulira aumunthu a ndale za dziko. Maboma a anthu ndi olamulira ao adzikweza ndipo adzipangira mbiri yoipa kwambiri, yothirana nkhondo zokhetsa mwazi kwambiri. Chifukwa cha chimene’cho sikuyenera kukhala kodabwitsa kuti Baibulo limayerekezera maboma a anthu opanda ungwiro kapena maufumu ndi zirombo ndipo limasonyeza kuti iwo onse potsirizira pake adzalandidwa ulamuliro wao. (Danieli 7:2-8) Ponena za amene adzalowa m’malo mwao, Baibulo liri ndi mau awa a mneneri Danieli:
“Ndinaona m’masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anam’yandikizitsa pamaso pake. Ndipo anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse am’tumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.”—Danieli 7:13, 14.
Munthu wolongosoledwa pano si wina’nso koposa Yesu Kristu, amene akusonyezedwa m’Malemba kukhala ponse pawiri “Mwana wa munthu” ndi “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.” (Mateyu 25:31; Chibvumbulutso 19:16) Iye mofunitsitsa anasiya malo ake apamwamba kumwamba nakhala munthu, ‘wochepera kwa angelo.’ (Ahebri 2:9; Afilipi 2:6-8) Monga munthu, Yesu Kristu, ngakhale ataputidwa kwambiri, anadzitsimikizira kukhala :wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” (Mateyu 11:29) “Pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsya, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.”—1 Petro 2:23.
Dziko la mtundu wa anthu linaona Yesu Kristu kukhala wosanunkha kanthu, likumakana kum’patsa ulemu umene iye moyenerera anauyenerera. Mkhalidwe’wo unali monga momwe unali utanenedweratu ndi mneneri Yesaya kuti: “Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wom’bisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinam’lemekeza.”—Yesaya 53:3.
Sipangakhale chikaikiro kuti Yesu akuyenerana ndi kulongosoledwa kwa “wolubukira wa anthu.” Chifukwa cha chimene’cho, loto lolosera lonena za mtengo wolikhidwa liyenera kusonya ku nthawi imene iye akalandira ulamuliro pa dziko la mtundu wa anthu. Imene’yi ikakhala pa mapeto a “nthawi zisanu ndi ziwiri.” Kodi “nthawi” zimene’zi n’zautali wotani? Kodi zikuyamba liti? Kodi zikutha liti?
UTALI WA “NTHAWI ZISANU NDI ZIWIRI”
Zaka zoposa mazana asanu ndi limodzi pambuyo pa loto la Nebukadinezara, Yesu Kristu anaonekera pa dziko lapansi, akumalengeza kuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Iye anatha kunena zimene’zi chifukwa chakuti iye, monga Woyembekezera kukhala Mfumu, analipo. Koma iye pa nthawi imene’yo sanalandire ufumu pa dziko la mtundu wa anthu. Motero, pa chochitika china pamene ena molakwa ananena kuti “Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo,” Yesu Kristu anapereka fanizo losonyeza kuti nyengo ya nthawi yaitali ikalowetsedwamo asanapeze mphamvu ya ufumu imene’yo. (Luka 19:11-27) Chifukwa cha chimene’cho, nkoonekera bwino kuti, m’kukwaniritsidwa kokulirapo kwa ulosi wa Danieli “nthawi zisanu ndi ziwiri” zikulowetsamo nyengo, osati ya zaka zisanu ndi ziwiri zokha, koma ya zaka mazana ambiri.
Umboni ndi wakuti “nthawi zisanu ndi ziwiri” zimene’zi zinakwana masiku 2,520, ndiko kuti, zaka zolosera zisanu ndi ziwiri za masiku 360 chiri chonse. Chimene’chi chikutsimikiziridwa m’mbali zina za Baibulo zimene zimachula “nthawi,” “miyezi” ndi “masiku.” Mwa chitsanzo, Chibvumbulutso 11:2 chimachula nyengo ya “miyezi makumi anai mphambu iwiri,” kapena zaka zitatu ndi theka. M’vesi lotsatirapo nyengo imodzi-modzi’yo ikuchulidwa kukhala “masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.” Tsopano, ngati mukanagawa masiku 1,260 ndi miyezi 42, mukanapeza masiku 30 pa mwezi uli wonse. Chifukwa cha chimene’cho chaka cha miyezi 12 chikakhala cha utali wa masiku 360. Chifukwa cha zimene’zi, “nthawi zisanu ndi ziwiri,” kapena zaka zisanu ndi ziwiri, zikakhala za utali wa masiku 2, 520 (7 x 360).
Kusalakwika kwa kuwerengera kumene’ku kukutsimikiziridwa ndi Chibvumbulutso 12:6, 14, kumene masiku 1, 260 akuchulidwa kukhala ‘nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi,” kapena ‘nthawi zitatu ndi theka’ (“zaka zitatu ndi theka,” The New English Bible). Zisanu ndi ziwiri pokhala zikuchulukitsidwa ndi zitatu ndi theka, “nthawi zisanu ndi ziwiri” zikakhala zokwanira masiku 2,520 (2 x 1,260).
Ndithudi, popeza kuti zimagwirizana ndi kulandira kwa Yesu ufumu pa dziko la mtundu wa anthu, “nthawi zisanu ndi ziwiri” za ulosi wa Danieli zatenga nyengo ya nthawi yochuluka kwambiri koposa masiku 2,520 a maora makumi awiri mphambu anai. Kodi pali njira iri yonse yotsimikizirira utali wa liri lonse la “masiku “amene’wa? Inde, njira ya Baibulo yowerengerera masiku olosera amene’wa ndiyo: “Tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi.” (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Pogwiritsira ntchito imene’yi ku “nthawi zisanu ndi ziwiri,” tikuona kuti izo zikukwana zaka 2,520.
CHIYAMBI CHA “NTHAWI ZISANU NDI ZIWIRI”
Pokhala titadziwa uali wa “nthawi zisanu ndi ziwiri, tsopano tiri okhoza kufufuza pamene izo zinayamba. Kachiwiri’nso tikusumika maganizo athu ku chimene chinachitikira Nebukadinezara m’kukwaniritsidwa kwa loto lonena za mtengo wolikhidwa. Lingalirani mkhalidwe wake:
Pa nthawi imene Nebukadinezara anapenga iye anali kuchita ulamuliro wa dziko, pakuti Babulo pa nthawi’yo anali ulamuliro waukulu pa dziko lapansi. Ponena za Nebukadinezara kulikhidwa kwa mtengo wophiphiritsira’wo kunatanthauza kuima kwakathawi kwa ulamuliro wake monga wolamulira wa dziko lonse.
Cholinga chonse cha zimene Mulungu anachita m’chochitika cha Nebukadinezara chinalowetsamo ulamuliro wochitidwa ndi mfumu yosankhidwa ndi Mulungu mwini. Kutaya mpando wachifumu kwa Nebukadinezara kwa “nthawi zisanu ndi ziwiri” chifukwa cha chimene’cho kunayenera kukhala kophiphiritsira. Kophiphiritsira chiani? Kophiphiritsira kuima kwakanthawi mu ulamuliro kapena ufumu kolinganizidwa ndi Mulungu popeza kuti, m’chochitika cha Nebukadinezara, Yehova Mulungu anali uyo amane anam’lola kupeza malo a ulamuliro wa dziko lonse ndipo pambuyo pake analanda malo a ntchito amene’wo kwa iye kwakanthawi, monga momwe mfumu yeni-yeni’yo inabvomerezera. (Danieli 4:34-37) Chotero chimene chinagwera Nebukadinezara chinayenera kukhala chophiphiritsira kuchotsedwa kwa ulamuliro ku ufumu wa Mulungu. Chifukwa cha chimene’cho, mtengo weni-weni’wo unaimira ulamuliro wa dziko pa dziko lapansi.
Pa nthawi ina boma linali ndi mpando wake wachifumu mu Yerusalemu linali ufumu wa Mulungu. Olamulira a mzera wachifumu wa Davide ananenedwa kukhala akukhala pa “mpando wachifumu wa Yehova” ndipo analamulidwa kulamulira mogwirizana ndi lamulo lake. (1 Mbiri 29:23) Chifukwa cha chimene’cho Yerusalemu anali malikulu a boma la Mulungu m’lingaliro la kuimira.
Chotero pamene Ababulo otsogozedwa ndi Nebukadinezara anaononga Yerusalemu, ndi pamene dziko lokhala mu ulamuliro wake linapasulidwa kotheratu, ulamuliro wa dziko lonse unapita m’manja mwa Amitundu popanda chidodometso chiri chonse chochokera ku ufumu woimira wa Yehova. Wolamulira Wapamwamba-mwamba’yo anadziletsa kuchita ulamuliro wake m’njira imene’yi. Kudziletsa kuchita ulamuliro pa dziko lapansi mwa ufumu wake kukuyerekezeredwa ndi kumangidwa mkombero kwa chitsa cha mtengo chotsala’cho. Pa nthawi ya kuonongedwa kwake ndi kupasulidwa kotheratu kwa Yerusalemu, monga mzinda wamalikulu woimira chisonyezo cha boma la ulamuliro wa Yehova, anayamba ‘kuponderezedwa.’ Chifukwa cha chimene’cho, zimene’zo zikutanthauza kuti, “nthawi Nebukadinezara anaononga Yerusalmeu ndi pamene dziko la Yuda linapasulidwa kotheratu. Kodi chochitika chimene’cho chinachitika liti?
Baibulo ndi mbiri ya dziko zingathe kugwiritsiridwa ntchito kutsimikizira 607 B.C.E. kukhala deti la chochitika chimene’cho.a Umboni’wo uli wotere:
Olemba mbiri a dziko ali ogwirizana ndi Babulo anagwera m’manja mwa Koresi Mperesi m’chaka cha 539 B.C.E. Deti limene’li likuchirikizidwa ndi zolembedwa zonse za mu mbiri zopezeka za m’nthawi zakale. Baibulo limabvumbula kuti m’chaka chake choyamba cha ulamuliro, Koresi anatulutsa lamulo lolola akapolo Achiisrayeli kubwerera ku Yerusalemu ndi kukamanga’nso kachisi. Pokhala panali choyambirira ulamuliro wa nthawi yaifupi wa Dariyo Mmedi pa Babulo mwachionekere chinayambira mu 538 kudzafika mu 537 B.C.E. (Danieli 5:30, 31) Popeza kuti kuyenda mtunda wautali kwambiri kunalowetsedwamo, muyenera kukhala munali mu “mwezi wachisanu ndi chiwiri” wa 537 B.C.E. (osakhala 538 B.C.E) m’mene Aisrayeli anabwerera’nso m’mizinda yao, kuthetsa kukhala bwinja kwa Yerusalemu ndi dziko la Yuda. (Ezara 3:1, 6) Komabe, chifukwa cha chimene’cho anadzicha ‘akapolo m’dziko lao-lao.’—Nehemiya 9:36, 37.
Bukhu la Baibulo la 2 Mbiri (36:19-21) limasonyeza kuti nyengo ya zaka makumi asanu ndi awiri inapita kuyambira pa nthawi ya kuonongedwa kwa Yerusalemu ndi kupasulidwa kwa dziko lokhala mu ulamuliro wake kufikira pa kubwezeretsedwa. Iro limati:
“[Nebukadinezara] anatentha nyumba ya Mulungu, nagamula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma. Ndi iwo amene anapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babulo, nakhala iwo anyamata ake, ndi ana ake, mpaka mfumu ya Peresiya idachita ufumu; kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masambata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.”
Kuwerengera zaka makumi asanu ndi awiri kubwerera m’mbuyo kuyambira pa nthawi imene Aisrayeli anafika’nso m’mizinda yao, ndiko kuti, mu 537 B.C.E., kukutifikitsa ku 607 B.C.E. Chifukwa cha chimene’cho, munali m’chaka chimene’cho, pamene Yerusalemu, malikulu a boma la Mulungu m’lingaliro la kuimira, anayamba kuponderezedwa ndi mitundu Yachikunja.
MAPETO A “NTHAWI ZISANU NDI ZIWIRI”
Yesu Kristu anachula kupondereza Yerusalemu kumene’ku pamene iye kwa ophunzira ake anati: “Yerusalemu adzaponderezedwa ndi mitundu, kufikira nthawi za amitundu zitakwaniritsidwa.” (Luka 21:24, NW)”Nthawi zoikidwiratu” zimene’zo zinayenera kutha zaka 2,520 pambuyo pa 607 B.C.E. M’menemu mukakhala m’chaka cha 1914 C.E. Kodi kupondereza Yerusalemu kunatha pa nthawi imene’yo?
Zoona, mzinda wa Yerusalemu wa pa dziko lapansi sunakhale ndi kubwezeretsedwa kwa mfumu mu mzera wachifumu wa Davide mu 1914 C.E. Koma chinthu chotero’cho sichinayenera kuyembekezeredwa. Kulekeranji kutero? Mzinda wa pa dziko lapansi wa Yerusalemu sunali’nso ndi kupatulika kuli konse kwapadera mwa lingaliro la Mulungu. Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu Kristu analongosola kuti: “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri ndi woponya miyala awo otumidwa kwa iye—ndinafuna kangati kusonkhanitsa ana ako mu mkhalidwe umene thadzi limasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko mwake, koma anthu inu simunafuna! Taonani! Nyumba yanu ikusiyidwa bwinja kwa inu.” (Luka 13:24, 35, NW) Ndipo’nso, ufumu wokhala m’manja mwa Yesu Kristu suli boma la pa dziko lapansi wokhala ndi Yerusalemu kapena mzinda wina uli wonse wonga malikulu ake. Uwo uli ufumu wakumwamba.
Chifukwa cha chimene’cho, kunali kumwamba kosaoneka’ko kumene chaka cha 1914 C.E. chinali ndi kukwaniritsidwa kwa Chibvumbulutso 11:15: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.” Chimene Yerusalemu anaimira, ndiko kuti, boma Laumesiya lolamulira mwa chibvomerezo cha Mulungu, pa nthawi imene’yo sichinali kuponderezedwa. Kachiwiri’nso panali mfumu ya mzera wachifumu wa Davide imene, mwa kuikidwa ndi Mulungu, inachita ulamuliro pa zochitika za mtundu wa anthu. Zochitika zooneka zimene zachitika pa dziko lapansi pano mokwaniritsa ulosi wa Baibulo chiyambire 1914 C.E. zimatsimikizira kuti zimene’zi ziri choncho.
Umodzi wa maulosi amene’wa ukupezeka m’chaputala chachisanu ndi chimodzi cha bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso. M’menemo kuperekedwa kwa ulamuliro waufumu kwa Yesu Kristu ndi zochitika zotsatirapo zikulongosoledwa m’mau ophiphiritsira.
Ponena za kulandira ufumu kwa Yesu cholembedwa’cho chimati: “Taonani, kavalo woyera, ndipo wom’kwera’yo anali nao uta; ndipo anam’patsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” (Chibvumbulutso 6:2) Pambuyo pake, bukhu la Chibvumbulutso mosalakwitsa likudziwikitsa wokwera pa kavalo amene’yo, kuti: “Taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakum’kwera wochedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.. . . Ndipo ali nalo pa chobvala chake ndi pa nchafu yake dzina lolembedwa, Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye.”—Chibvumbulutso 19:11-16.
Ponena za chimene chikachitika pa dziko lapansi pano pambuyo pa kulandira kwa Yesu “korona” wa ufumu wamphamvu pa dziko lonse la mtundu wa anthu, Chibvumbulutso chapatula 6 chikupitiriza kuti:
“Anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anam’patsa iye wom’kwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anam’patsa iye lupanga lalikulu. Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu nichinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye wom’kwera anali nao muyeso m’dzanja lake. . . . Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachinai, ndinamva mau a chamoyo chachinai nichinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye wom’kwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za pa dziko.”—Vesi 4-8.
Kodi mau amene’wa sanakwaniritsidwe? Kodi lupanga la nkhondo ya dziko silinalunde kuyambira 1914 kumkabe m’tsogolo? Ndithudi! Nkhondo Yoyamba ya Dziko inasonyeza kuphedwa kwa anthu pa mlingo uwene sunadziwidwe ndi kale lonse. Asilikari ankhondo oposa mamiliyoni asanu ndi anai anafa ndi mabala, matenda ndi zochititsa zina. Imfa za anthu wamba zochititsidwa mwachindunji ndi nkhondo nazo’nso zinali mamiliyoni ochuluka. Nkhondo yachiwiri ya dziko lonse inapha chiwerengero chokulirapo kwambiri’di cha anthu. Iyo inaphetsa anthu wamba ndi asilikali ankhondo oyerekezeredwa kukhala mamiliyoni makumi asanu mphambu asanu.
Kodi kuperewera kwa zakudya, mofanana ndi kavalo wakuda, sikunafale pa dziko lapansi? Inde, m’mbali zambiri za Yurope munali njala m’kati ndi pambuyo pa nyengo ya Nkhondo Yoyamba ya Dziko Lonse. Mu Rasha mamiliyoni ambiri anafa. Pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya dziko lonse panadza chimene The World Book Encyclopedia (1973) imachilongosola kukhala “kuperewera kwa zakudya kwa pa dziko lonse kwakukulu kopandana mu mbiri.” Ndipo lero lino cheni-cheni choopsya n’chakuti mmodzi mwa anthu atatu ali pa dziko lapansi mwapang’ono-pang’ono akubvutika ndi njala kapena akukhala ndi kudya mosakwanira.
Mliri wakupha nawo’nso unatenga ake. M’miyezi yowerengeka chabe, m’kati mwa 1918-1919, mliri wa folowenza yochokera ku Spanya wokha unapha pafupi-fupi 20,000,000. Palibe tsoka limodzi liri lonse limene ndi kale lonse linachititsa chionongeko chachikulu kopambana chotero’cho cha moyo pakati pa mtundu wa anthu.
Ndithudi zinthu zimene’zi zakhala zazikulu mokwanira zosati n’kusaonedwa. Joseph Carter, m’bukhu lake lakuti 1918 Year of Crisis, Year of Change akuti: “M’chirimwe chimene’cho [cha 1918] zoopsya zokha-zokha zinaunjikana, pakuti atatu mwa Okwera pa kavalo Anai a Chibvumbulutso—nkhondo, njala, ndi mliri—zinali’di kuli konse.” Kufikira lero lino okwera pa akavalo ophiphiritsira’wo sanaleke kukwera kwao.
Motero pali umboni wooneka wakuti 1914 C.E. mikombero yoletsa’yo inachotsedwa ku chitsa chophiphiritsira cha loto la Nebukadinezara. Yehova Mulungu anayamba kuchita ulamuliro kupyolera mwa ufumu wa Mwana wake, Ambuye Yesu Kristu. Koma kodi n’chifukwa ninji umene’wu sunaongolere mikhalidwe pa dziko lapansi? Kodi n’chifukwa ninji nthawi ya kupatsa ulamuliro wa kulamulira pa mtundu wa anthu kwa Kristu yagwirizanitsidwa ndi bvuto?
Izi ziri chifukwa chakuti Satana Mdierekezi akulimbana ndi ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu. Iye analimbana nawo pa nthawi ya kupatsidwa ulamuliro pa mtundu wa anthu. Koma iye analephera m’nkhondo’yo ndipo anatsitsidwa limodzi ndi ziwanda zake kuchokera kumwamba koyera. Pokhala atakwiya, iye ndi ziwanda zake akusonkhezera bvuto liri lonse limene iwo angathe kulisonkhezera pakati pa mtundu wa anthu kuti asakaze ali yense ndi chiri chonse. Ndicho chifukwa chake, pambuyo pa kulongosola nkhondo’yo kumwamba ndi chotulukapo chake, cholembedwa cha Baibulo chimapitiriza kuti: “Kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kam’tsalira kanthawi.”—Chibvumbulutso 12:7:12.
Kodi nyengo ya nthawi yotsalira mdani wa Ufumu’yo njaifupi motani? Yesu Kristu anabvumbula kuti nthawi ya kudza kwake mu ulemerero Waufumu ndi kuchotsedwa kwa dongosolo la zinthu lopanda umulungu kukakhala m’kati mwa nthawi ya moyo wa mbadwo umodzi wa anthu. Iye anati: “Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonse’zi zidzachitidwa.”—Mateyu 24:3-42.
Chifukwa cha chimene’cho, ena a mbadwo umene unali ndi moyo mu 1914 C.E. ayenera kukhala pakati pa anthu oti aone kutsiriza kwa Yesu kugonjetsa kwake ndi kutenga ulamuliro wotheratu wa zochitika za dziko lapansi. Zimene’zo zikutanthauza’nso kuti ambiri amene tsopano ali ndi moyo ali ndi mwai wa kusafa konse. Kodi ziri choncho motani?
CHIFUKWA CHAKE AMBIRI AMENE ALI NDI MOYO TSOPANO SADZAONA IMFA
M’kutsiriza kugonjetsa kwake, Yesu Kristu monga mfumu adzachitapo kanthu kokha motsutsana ndi awo amene akukana kugonjera ku ulamuriro wake. Potonthoza okhulupirira anzake amene anali kubvutika ndi chizunso, mtumwi wouziridwa Paulo analemba za zimene’zi, kuti: “N’kolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa bvumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osam’dziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemerero wa mphamvu yake.”—2 Atesalonika 1:6-9.
Ndithudi si anthu onse akukana “kudziwa” kapena kuzindikira ulamuliro wa Mulungu m’miyoyo yao. Si onse ali osamvera ‘uthenga wabwino wonena za Yesu Kristu.’ Ngakhale kuli kwakuti ngowerengeka, poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu cha dziko, pali gulu la Akristu limene likuyesa-yesa zolimba kudzitsimikizira kukhala atumiki odzipereka a Mulungu ndi ophunzira okhulupirika a Yesu Kristu. Awo amene tsiku la chiweruzo cha Mulungu liwapeza ali odzipereka kotheratu kwa Yehova Mulungu angakhale ndi chitsimikiziro chakuti iwo sadzafafanizidwa ndi chiweruzo chimene’cho. Baibulo limati:
“Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. Chifukwa chake ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo am’tumikira Iye usana ndi usiku m’Kachisi mwake; ndipo iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi, sadzamva’nso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chiri chonse; chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.”—Chibvumbulutso 7:14_17.
Chiyembekezo pamaso pa khamu lalikulu la opulumuka “chitsautso chachikulu” ndicho, osati imfa, koma moyo. “Mwanawankhosa,” ndiko kuti, Ambuye Yesu Kristu, adzakhala akuwatsogolera ku “akasupe a madzi a moyo.” Umene’wu suli moyo wa zaka makumi asanu ndi awiri kapena makumi asanu ndi atatu zokha, koma wamuyaya. Iye adzakhala akugwiritsira ntchito kwa iwo mapindu a nsembe yake yotetezera machimo, akumawamasula ku uchimo ndi ziyambukiro zake zochititsa imfa. Pamene iwo momvera alabadira chithandizo chake, iwo adzafika ku ungwiro waumunthu, popanda kufunika kwa kufa.
Sipadzakhala chidodometso chochokera kwa Satana ndi makamu ake auchiwanda kudodometsa kupita kwao patsogolo. “Chisautso chachikulu” chitathetsa dongosolo la zinthu loipa la padziko lapansi, Satana adzaponyedwa m’phompho kwa zaka chikwi. Kulongosola kophiphiritsira kwa Baibulo kwa chochitika chimene’chi kumati: “Ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho; ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakhale’yo, ndiye Mdierekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi, nam’ponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyenge’nso amitundu.” (Chibvumbulutso 20:1-3) Motero, monga ngati afa, Satana ndi ziwanda zake sadzakhala’nso okhoza kuchititsira bvuto mtundu wa anthu.
Baibulo limasonyeza mwachindunji mbadwo umene unali ndi moyo mu 1914 C.E. kukhala umene udzaona’nso kuyambitsidwa kwa ulamuliro wa Ufumu wopanda chidodometso cha Satana. Chifukwa cha chimene’cho, ambiri amene ali ndi moyo lero lino adzakhala ndi mwai wa kusafa konse. Iwo adzapulumuka chionongeko cha dongosolo lopanda umulungu liripo’li ndipo pambuyo pake kumasulidwa mwapang’ono-pang’ono ku uchimo ndi kufikitsidwa ku ungwiro waumunthu. Monga anthu opanda uchimo iwo pa nthawi imene’yo adzakhala omasuka ku mphotho ya uchimo—imfa.—Aroma 6:23.
Zimene’zi zikupangitsa kukhala kofunika kwambiri kwa inu kuziika ku mbali ya Mfumu Yesu Kristu, ngati simunachitebe motero, ndi kukhala ndi moyo tsopano monga mmodzi wa nzika zake zokhulupirika. Ndizo zimene mboni Zachikristu za Yehova zikuyesa-yesa kuchita, ndipo izo ziri zofunitsitsa kuthandiza ena kuchita chimodzi-modzi.
[Mawu a M’munsi]
a Olemba mbiri a dziko amakono mofala samapereka 607 B.C.E. kukhala deti la chochitika chimene’chi, koma iwo ali odalira pa zolemba za anthu amene anakhala ndi moyo zaka mazana ambiri icho chitachitika. Ndipo’nso, Baibulo liri ndi umboni wochokera kwa mboni zoona ndi maso, ndipo limapereka zeni-zeni zimene zikunyalanyazidwa ndi olemba a dziko. Ndipo’nso, kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo pa mapeto a “nthawi zisanu ndi ziwiri” kumatsimikizira deti’lo mosasiya chikaikiro. Ponena za chifukwa chimene maumboni a kuwerengera zaka za Baibulo ali odalirika kwambiri koposa mbiri ya dziko, onani bukhu lakuti Aid to Bible Understanding, tsamba 322-348.