Mutu 21
Kodi Ndi Motani M’mene Mungakhalire ndi Moyo Woposa Uno?
MWA chidziwitso chonse chapita’cho n’koonekera bwino kwambiri kuti pali zochuluka, zochuluka kwambiri ku moyo kuposa zimene tikuziona tsopano. Tangoganizirani—Yehova Mulungu waika pamaso pa mtundu wa anthu chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo pano pa dziko lapansi pansi pa mikhalidwe yolungama, popanda matenda ndi imfa! Ungakhale wanu kuti musangalale nawo, osati kwa zaka zana limodzi kapena zaka chikwi chimodzi, koma kosatha. Ndipo nthawi imene zimene’zi zidzakwaniritsidwa yayandikira pafupi kwambiri!
Kodi inu mudzakhala pakati pa awo amene adzapindula ndi kukwaniritsidwa kwa chifuno chabwino kwambiri cha Mulungu kaamba ka munthu ndi malo ake okhala, dziko lapansi? Ndithudi inu mungakhale pakati pao. Koma mufunikira kuchitapo kanthu mosazengereza. Tsopano tikukhala ndi moyo pa nthawi imene chenjezo la Baibulo liri lofulumira kwambiri: “Usanakugwereni mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 2:2, 3.
“Mkwiyo waukali wa Yehova” uli pa onse amene asocheretsa anthu anzao mwa kunena bodza ponena za Mulungu ndi chifuno chake. Ndipo iye samaona kukhala opanda liwongo awo amene amachirikiza anthu otero’wo mwa kufika pa maulaliki ao achipembedzo kapena kukhala ziwalo za magulu ao. Nthawi imene yatsala kuti chiweruzo cha Mulungu chiperekedwe yafupika, Ngati muli wokonda chilungamo mufunikira kuchitapo kanthu mofulumira kumvera lamulo Lamalemba la kusiya zigwirizano zonse ndi ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Lingalirani mwamphamvu chisonkhezero cha Mau a Mulungu, chimene chimati: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”—Chibvumbulutso 18:4.
Koma si kokwanira kungosiya zigwirizano ndi magulu amene alekerera ndi kusonkhezera chisalungamo. Baibulo limachenjeza kuti ‘mkwiyo wa Mulungu, wochekera Kumwamba uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama,’ inde, pa machita-chita eni-eni’wo ndi awo amene akupitiriza kuwachita. (Aroma 1:18) Silimatisiya okaikira konse ponena za chimene machita-chita amene’wo ali. Iro limawasonyeza bwino lomwe ndi kufulumiza onse amene akakhala ndi chibvomerezo cha Yehova kuchotsa zinthu zotero’zo m’miyoyo yao. Kukonda Yehova ndi kuyamikira ubwino wake kungapangitse kusintha kotero’ko kukhala kothekera.—Aefeso 4:25-5:6; Akolose 3:5, 6.
Ino sindiyo nthawi ya kufuna-funa kudzilungamitsa, tikumalingalira kuti ntchito zabwino zimene munthu amachita tsiku ndi tsiku zimakwirira zolakwa zake. Kudzikhazikitsira miyezo yao ya iwo eni ya chabwino ndi choipa kunatsogolera ku tsoka kwa Adamu ndi Hava. Ndipo ngakhale m’nthawi yathu mwambi wa Baibulo’wo uli woona umene umati: “Iri’po njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 16:25) Pamenepa, tsopano ndiyo nthawi, ya kuphunzira njira za Yehova, ‘kufuna-funa chilungamo’ chake. Ino’nso ndiyo nthawi ya ‘kufuna-funa chifatso,’ ndiko kuti, kukhala wogonjera ku chiweruzo cha Mulungu ndi kulandira modzichepetsa chiongolero ndi chiphunzitso chake ndi kugwirizana ndi chifuniro chake. Kokha mwa kuchita zimene’zi kudzakuthekerani ‘kubisidwa m’tsiku la mkwiyo wa Yehova.’
Musanene, monga momwe ena anenera, kuti njira yanu ya moyo yakhala yoipa kwambiri kuti Mulungu akukhululukireni. M’malo mwake, pezani chitonthozo m’mau onenedwa kwa Aisrayeli osakhulupirika akale, akuti: “Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwera kwa Yehova; ndipo Yehova adzam’chitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.” (Yesaya 55:7) Ndipo’nso, pezani chilimbikitso m’lonjezo lake limene limati: “Ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.”—Yesaya 1:18.
Yehova Mulungu samakondwera ndi kupereka chiweruzo pa ali yense koma amafuna kuti onse asangalale ndi moyo. (2 Petro 3:9) Komabe, Yehova sangalekerere ndipo sadzalekerera chisalungamo. Chifukwa cha chimene’cho, n’kofunika kwa onse amene akakhala ndi chibvomerezo chake kulapa mkhalidwe wao wakale ndi kusintha njira zao kuti zigwirizane ndi chifuno chake cholungama.—Yesaya 55:6.
Chinthu choti muchite tsopano ndicho kuyamba kuphunzira chimene Mulungu amafuna kwa inu, kulandira chidziwitso chofunika kwambiri chimene chiri m’Mau ake, ndi kenako kuchita mogwirizana nacho. Imene’yi ndiyo njira imene imatsogolera ku moyo wakuyaya. (Yohane 17:3) Mboni Zachikristu za Yehova mokondwa zidzakupatsani chithandizo chao m’kupeza chidziwitso cholongosoka cha Baibulo, kwaulere. Izo zikukulandirani’nso ku Making’idomu Holo ao, kumene zimakambitsirana Mau a Mulungu nthawi zonse.
NJIRA YOPINDULITSA KWENI-KWENI
Mwa kulabadira zinthu zimene mukuphunzira m’Baibulo, mudzaona masinthidwe opindulitsa m’moyo wanu. Mudzaona kuti kugwiritsiridwa ntchito kwa malamulo a khalidwe labwino a Baibulo kudzapititsa patsogolo zigwirizano pa nyumba, pa ntchito ndi m’kukhala kwanu pamodzi kwa tsiku ndi tsiku ndi anthu anzanu. (Aroma 12:17-21; 13:8-10; Aefeso 5:22-1 Petro 3:1-7) Kumene’ku kudzathandizira kwambiri kupangitsa moyo wanu kukhala wachimwemwe kwambiri, wokhutira ndi watanthauzo kwambiri ngakhale tsopano.
Ndithudi, kumene’ku sikukutanthauza kuti mudzakhala opanda mabvuto ndi zitsenderezo za dziko. Inu mudzapitirizabe kukhala pakati pa anthu amene alibe kukonda chilungamo, ndipo ena a iwo mosakaikira adzayesa-yesa kukugwetsani ulesi kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito Baibulo m’moyo wanu. (2 Timoteo 3:12; 1 Petro 4:4) Koma, pamene mukuonjezera chidziwitso cha Mau a Mulungu, mudzapeza kuti inu muli okhoza kulimbana ndi mabvuto a moyo bwino kwambiri koposa m’mene amachitira awo amene amadalira pa kulingalira ka anthu chabe. M’malo mwa kupsya mtima chifukwa zosalungama zimene mungabvutika nazo, mudzadziwa chifukwa chake ndipo mudzakhala ndi chikhulupiriro champhamvu chakuti ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu posachedwa udzathetsa zinthu zonse’zi zimene zimadodometsa kusangalala ndi moyo kokwanira.—2 Petro 3:11-13.
Pamene mukupeza chikhulupiriro m’makonzedwe achikondi a Mulungu a moyo wamuyaya, mudzapeza chimasuko ku chisonkhezero chotsendereza chimene chiyembekezo cha imfa chakhala nacho pa anthu onse. Zinyengo zimene zaphunzitsidwa ponena za imfa sizidzaononga’nso kusangalala kwanu ndi moyo. Lingaliro losaona patali lakuti moyo uno ndiwo wokha umene ulipo lingataye mphamvu imene lingakhale linalo nayo kulinga ku kukuyesani kuti muswe malamulo oyenera a khalidwe labwino ndi chikumbu mtima chabwino moyesa-yesa kutsogola m’dziko. Chikhulupiriro chozikidwa pa chidziwitso cholongosoka cha Mau a Mulungu chidzapangitsa kukhala kothekera kwa inu kusangalala ndi moyo tsopano kuposa kale ndi kusangalala ndi chiyembekezo chabwino kwambiri cha m’tsogolo—moyo wosatha m’dongosolo latsopano lolungama la Mulungu.
Kuyamikira makonzedwe achikondi amene Mulungu wapangira mtundu wa anthu kusonkhezeratu mwa inu chikhumbo chachikulu cha kudziwa ndi kuchita chifuno chake. Kukusonkhezerenitu, ndi mtima woona, kugwirizana ndi wamasalmo amene anati: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.”—Salmo 25:4, 5.