Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
1, 2. (a) Kodi mafunso amene andandalikidwa m’ndime yoyamba ndiwo amene inu mwafunsa? (b) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene imachititsa anthu kufunsa mafunso oterowo?
Ngati Mulungu aliko, kodi waloleranji zinthu, zambirimbiri zowopsa kuchitikira anthu m’kati mwa nthawi yonseyi? Ngati akutisamaladi, kodi akuloleranji kuipa ndi kubvutika kupitirizabe
2 Kuli konse anthu oganiza amafunsa mafunso amenewa. Ndipo amakhala ndi chifukwa chabwino, chifukwa chakuti kwa zaka mazana ambiri banja la anthu lavutika kwambiri ndi nkhondo zoopsa, kuperewera kwa zakudya, umphawi, upandu ndi matenda. Kupanda chilungamo ndi chitsenderezo zachititsanso chisoni chachikulu kwambiri. Chimodzimodzinso masoka onga ngati zigumula ndi zivomezi, Nthawi zambiri, anthu opanda liwongo amavutika osati chifukwa cha liwongo lao la iwo eni. Kodi zonsezi ziri umboni wakuti Mulungu sakusamala zimene zikutichitikira? Kodi pali chiyembekezo chiri chonse chotsimikizirika cha dziko labwinopo, dziko m’limene tingasangalale kotheratu ndi moyo pa dziko lapansi, popanda mavuto onsewa?
3. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kukhala okhoza kupeza mayankho a mafunso amenewa?
3 Mafunso oterowo amafuna mayankho owona ndi okhutiritsa. Koma si kowona, kapena kokhutiritsa, kuuzidwa kuti, “Nchifuniro cha Mulungu kuti tizivutika,” kapena, “Izi ndi zinthu zimene sitingazimvetsetse.” Ngati Mulungu analenga chilengedwe chonse chochititsa mantha cha dongosolo lodabwitsa chotero, ndithudi iye ayenera kukhala ndi chifukwa chabwino chololera anthu kukhala osalongosoka kwambiri. Ndipo kodi Mlengi woteroyo sakasamala kwambiri zolengedwa zake zaumunthu kutiuza chifukwa chake iye walolera kuipa? Kodi sikukakhala ndi tanthauzo kwa iye kuongola mikhalidwe yoipa imeneyi m’nthawi yokwanira ngati iye ali ndi mphamvu ya kutero? Atate ali yense wachikondi akachitira zimenezo ana ake ngati akadatha. Ndithudi Mlengi wamphamvuyonse, wanzeru zonse ndi wachikondi sadzachitira mosiyana ana ake a pa dziko lapansi.
Kodi Ndani Angayankhe Bwino Kwambiri?
4. Kodi ndani amene ali wokhoza bwino kwambiri kutiuza chifukwa chake Mulungu akulola kuipa
4 Kodi ndani angayankhe bwino kwambiri mafunso onena za kulola kwa Mulungu kuipa? Eya, ngati inu mukananenezedwa cholakwa china, kodi mukanafuna anthu kumvetsera kokha zimene ena ananena ponena za icho? Kapena kodi mukanafuna kudzinenera kuti muchotse nkhaniyo m’maganizo mwa munthu ali yense amene mowona mtima anafuna kudziwa? Ndi Mulungu amene akunenedwa kukhala ndi liwongo la kulola kuipa. Popeza kuti iye akudziwa bwino kwambiri chifukwa chake iye akukulola, kodi sikukakhala bwino kumlola kudzinenera? Kuyang’ana kwa anthu kaamba ka mayankho sikudzakhala kokhutiritsa, popeza kuti nthawi zambiri iwo amakhala ndi malingaliro owombana ponena za nkhani zimenezi.
5. Kodi nkoyenera kukhulupirira kuti Mulungu analemba Baibulo? (2 Petro 1:21; Habakuku 2:2)
5 Kodi Mulungu amapereka kuti mayankho? Pali magwero amodzi okha amene Mlengi akunena kukhala atawalamula kutiuza zimene zinachitika ndi chifukwa chake. Magwero amenewo ndiwo Baibulo, limene likufotokoza kuti: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu.”(2 Timoteo 3:16)a Izi siziyenera kukhala zodabwitsa, chifukwa chakuti ngati Mulungu anali ndi mphamvu ya kulenga chilengedwe chonse chodabwitsa, ndithudi iye akanatha kukhala wolemba bukhu. Anthu chabe angathe kutumiza mau ndi malingaliro, ngakhale zithunzithunzi m’mphepo yosaoneka kuwailesi kapena wailesi yanu yakanema. Motero sikakhala nchito yaikulu konse kwa Mlengi wamphamvuyonseyo kutumiza maganizo ake kwa anthu olemba okhulupirika ndi kuona kuti iwo akuwalemba bwino lomwe. Ndicho chifukwa chake mtumwi Paulo anatha kunena mwachidaliro kuti: “Pakulandira mau a . . . Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.
6. Kodi ndi ku utali wotani umene mbiri ya Baibulo imafika, ndipo chifukwa cha chimenecho, kodi lingatipatse chidziwitso chotani? (Luka 1:1-4 wonani Luka 3:23-38.)
6 Mwina mwake inu simunapende Baibulo. Komabe mungakondwere kudziwa kuti liri ndi cholembedwa cha mu mbiri chokwanira kotheratu ndi chokhala ndi madeti chimene chiripo lero lino. Kunena zoona, wolemba mbiri wina wa m’zaka za zana loyamba, Luka, sing’anga wa mankhwala, anali wokhoza kulondoloza mzera wobadwira wa Yesu wa ku Nazarete kupyola zaka zikwi zinayi za mbiri, sitepe ndi sitepe, dzina ndi dzina, mpaka kwa munthu woyamba. Popeza kuti Baibulo limafika ku chiyambi chenicheni cha kukhalako kwa munthu, lingatiuze amene ali wochititsa kuipa, chifukwa chake Mulungu anakulola, ndi m’mene kudzachotsedwera.
Kodi Mulungu Ndiye Wochititsa?
7. Pamene zolakwa zichitidwa, kodi ndani amene ayenera kuimbidwa mlandu?
7 Ngati munthu wina wake anachita upandu, kodi mukanamva bwanji ngati mukananenedwa kuti inu ndinu amene mwachita? Mukanalingalira zimene’zi kukhala zosalungama kwambiri. Chilungamo chimafuna kuti waliwongo alangidwe ndi wopanda chifukwa achotseredwe liwongo. Ngati dilaivala wa galimoto anyalanyaza chizindikiro cha kuima pa mphambano yochuluka magalimoto ndi kulowa m’ngozo yoipa chifukwa cha chimenecho, si liwongo la lamulo. Ngati munthu akhala wosusuka ndipo adwala chifukwa cha kudya mopambanitsa, si liwongo la mlimi amene analima chakudya. Ngati, mosasamala kanthu za kuleredwa bwino, mnyamata achoka pa nyumba anyalanyaza uphungu wabwino wa atate wake ndipo kenako akulowa m’vuto, si atate amene ali wochititsa. Pamenepo kodi nchifukwa ninji Atate wakumwamba, Mulungu, ayenera kunenedwa kuti ndiye wochititsa pamene mtundu wa anthu uchita zolakwa? Kodi liwongolo siliyenera kuikidwa kumene liyenerapa munthu waliwongo’yo?
8. Kodi ndi kutsutsana kotani kumene kukuonekera ngati tinena kuti Mulungu ndiye wochititsa zimene ziri zoipa?
8 Ndiponso, pali kanthu kenanso kokalingalira. Ngati tinena kuti Mulungu ndiye wochititsa zinthu zonga ngati kuvutika ndi njala chifukwa cha kuperewera kwa zakudya, kodi timatamanda yani kaamba ka minda yachonde ndi minda ya zipatso imene imatulutsa zotuta zochuluka kwambiri m’maiko ambiri? Ngati tinena kuti Mulungu ndiye amene amachititsa matenda, kodi timatamanda yani kaamba ka njira zodzichiritsira zodabwitsa za thupi? Ngati tinena kuti Mulungu ndiye wochititsa nyumba zauve zokhala mopanikizana za mu mzinda, kodi timatamanda yani kaamba ka mapiri okongola kwambiri, nyanja zobiriwira, maluwa okondweretsa ndi mitengo yokongola? Mwachionekere, ngati tinena kuti Mulungu ndiye wochititsa mavuto a dziko lapansi ndipo kenako kumtamanda kaamba ka zinthu zabwino za dziko lapansi, nkotsutsana. Mulungu wachikondi sakatulutsa zabwino ndi zoipa zomwe pa nthawi imodzimodzi.
9. Kodi nkoyenera kunena kuti Mulungu kulibe kokha chifukwa chakuti anthu amachita zinthu zolakwa? (Yesaya 45:18)
9 Kunena kuti Mulungu kulibe kumangopangitsa vutolo kukhala lalikulu kwambiri. Kukhulupirira kuti dziko lapansi lino ndi mipangidwe yodabwitsa ya zamoyo zinangochitika ndiko kunyalanyaza zenizeni. Chenicheni ndicho chakuti dziko lapansi liri lokonzekeretsedwa bwino kwambiri kuchirikiza moyo koposa nyumba iri yonse, komabe nyumba iriyonse iri ndi wolinganiza ndi womanga waluntha. Pamenepo bwanji ponena za pulaneti lino limodzi ndi njira zake zabwino kopambana zochirikiza moyo za mpweya, nthaka ndi madzi? Mwanzeru Baibulo limati: “Pakuti nyumba iri yonse iri naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Zowona, anthu ena amanena kuti chifukwa chakuti anthu amachita zinthu zoipa zikutanthauza kuti Mulungu kulibe. Komabe, izi ziri zofanana ndi kunena kuti chifukwa chakuti anthu amene amakhala m’nyumba amachita zinthu zoipa pamenepo nyumbazo ziribe ozilinganiza kapena ozimanga. Kukhalanso kofanana ndi kunena kuti chifukwa chakuti munthu amachita kanthu kena kolakwa iye analibe atate.
10. Kodi tiyenera kuika kuti lochuluka la liwongo la kuipa?
10 Pamenepa, kodi ndani, amene anganenedwe kuti ndiye wochitisa zinthu zowopsa zimene zachitikira banja la anthu? Liwongo lochuluka liyenera kukhala pa anthu eniwo. Kusaona mtima ndi kugwiritsidwa mwala kwa anthu kumachititsa maupandu. Kunyada ndi dyera la anthu zimachititsa maukwati osweka, maudani ndi kusankhana mitundu. Kulakwa ndi kusadera nkhawa kwa anthu zimachititsa kuipitsa ndi utchisi. Kudzitukumula ndi utsiru wa anthu zimachititsa nkhondo; ndipo pamene mitundu yathunthu mwa khungu itsatira atsogoleri a ndale za dziko m’nkhondo zimenezo pamenepo iyo iyenera kugawana liwongo la kuvutika. Njala ndi umphawi kwakukulukulu ziri chifukwa cha kunyalanyaza ndi umbombo wa anthu. Talingalirani: dziko lonse lapansi tsopano limaononga madola oposa mabiliyoni 200 chaka chiri chonse pa zida zankhondo. Ngati zonsezi zikanaonongedwera bwino lomwe pa kulima ndi kugawira zakudya moligana ndi kuthetsa kusoweka kwa nyumba, taganizirani zimene zikadachitidwa!
11. Popeza kuti atsogoleri achipembedzo amapempherera magulu ankhondo a mitundu yawo, kodi tiyenera kunena kuti Mulungu ndiye wochititsa nkhondo zimene magulu ankhondo amenewo akumenya (Yesaya 1:15; Miyamba 28:9)
11 Sitinganenenso kuti Mulungu ndiye wochititsa zolakwa zochitidwa m’dzina la chipembedzo. Mwa chitsanzo, atsogoleri achipembedzo amapempha dalitso la Mulungu pa nkhondo za mitundu yao. Komabe, kawirikawiri, ngakhale kuli kwakuti ku mbali zonsezo, asilikali ophanawo ali a chipembedzo chimodzi! Mulungu sangakhale wochititsa zimene’zo, chifukwa chakuti iye amatsutsa zimene iwo akuchita, akumanena kuti awo amene akumtumikiradi ayenera ‘kukhala ndi chikondi pakati pao.’(Yohane 13:34,35) Ngati alibe chikondi chimenechi, pamenepo Mulungu akunena kuti iwo ali “monga Kaini [amene] anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”(1 Yohane 3:10-12) Kupha anthu m’dzina la Mulungu, kaya mkati mwa zilango zachipembedzo kapena mu nkhondo, nkofananandi ndi kachitidwe kakale ka kupereka ana nsembe kwa milungu yonama, kanthu kamene Mulungu Wamphamvuyonse akunena kuti ‘sanakalamule ndi kuti sikanatuluke mu mtima mwake,’—Yeremiya 7:31.
12. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo akutchedwa “onyenga” m’Baibulo? (Mateyu 15:7-9)
12 Kulowa kwa atsogoleri achipemedzo m’ndale za dziko, kuchirikiza nkhondo, ndi ziphunzitso zonama monga ngati kunena kuti Mulungu ndiye wochititsa kuvutika kwa dziko lonse kumeneku, kapena kuti iye amawotchadi anthu mu helo wamoto weniweni kosatha, ziri zonyansa kwa anthu oganiza, ndi kwa Mulungu.Atsogoleri achipembedzo amene amaphunzitsa ndi kuchita zinthu zotsutsana ndi Mulungu, akuchedwa “onyenga” m’Mau a Mulungu, amene akunenanso kwa iwo kuti: “Mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake,koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m’kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.” (Mateyu 23:27,28) Kunena zowona, Yesu ponena za atsogoleri achipembedzo onyenga anati:”Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi.”—Yohane 8:44.
13. (a) Motero kodi tiyenera kunena kuti Mulungu ndiye wochititsa pamene anthu,ngakhale atsogoleri achipembedzo, achita zolakwa? (b) Komabe, kodi ndi mafunso otani amene angafunsidwebe?
13 Ai, Mulungu sindiye wochititsa zolakwa zimene anthu eniwo akuchita. Ndipo iye sayenera kunenedwa kuti ndiye wochititsa zolakwa zodalitsidwa ndi atsogoleri achipembedzo amene amadzitcha kukhala akutumikira Mulungu koma amene samanena choonadi kapena kuchitsatira. Chabwino, pamenepa, kodi panali kanthu kena kolakwika ndi mmene Mulungu analengera anthu? Kodi iye anapatsa mtundu wa anthu chiyambi choipa?
Chiyambi Changwiro
14. Fotokozani chiyambi chimene Mulungu anapatsa makolo athu oyamba (Genesis 1:26-31; 2:7-9,15)
14 Pamene munthu awerenga machaputala awiri oyamba a bukhu la Genesis, kumakhala kowonekera bwino kwambiri kuti pamene Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi iye anawapatsa chiyambi changwiro. Iye anawalenga ndi matupi ndi maganizo angwiro, kotero kuti matenda ndi imfa sizikanavutitsa. Malo awo okhala anali okongola kwambiri, munda wokongola wa maluwa okongola zomera ndi mitengo yobala zipatso zochuluka. Munalibe kusowa. Koma, munali zochuluka. Ndiponso, Mulungu anaika pamaso pa makolo athu oyamba nchito yokondweretsa ndi zolinga zosonkhezera. Iye anawalangiza kuti afutukulire mikhalidwe yokongola ya paradaiso ameneyo pa dziko lonse lapansi. M’kupita kwa nthawi iwo akanadzathandizidwa mzimenezi ndi ana ambiri angwiro amene iwo akanadzawabala. Motero, potsirizira pake, banja la anthu likanadzakhala mtundu wa anthu wangwiro, wokhala pa dziko lapansi laparadaiso, wosangalala ndi moyo kosatha, ndipo ngakhale wolamulira zinyama mwa chikondi.
15. Kodi ungwiro waumunthu umatanthauzanji, ndipo kodi sumatanthauzanji?
15 Koma kodi nchifukwa ninji zinthu zinadzakhala moipa kwambiri? Kodi chinali chifukwa chakuti Mulungu sanalenge’di anthu angwiro poyamba? Ai, zimenezo siziri choncho, chifukwa chakuti Deuteronomo 32:4 ponena za Mulungu amati,”Nchito yake ndi yangwiro.” Komabe, ungwiro wa anthu sunatanthauze kuti anthu awiri oyambawo anadziwa chiri chonse, kapena akadatha kuchita chiri chonse, kapena sakadatha kuchita chimene chiri cholakwa. Ngakhale zolengedwa zangwiro ziri ndi malire. Mwa chitsanzo, panali malire akuthupi. Ngati iwo sakanadya chakudya, kumwa madzi ndi kupuma mpweya iwo akadafa. Ndiponso iwo sakadachita zinthu zonga ngati kuswa lamulo la mphamvu yokoka mwa kulumpha kuchokera pa malo atali kwambiri ndi kusayembezera kuvulala. Ndiponso iwo anali ndi malire a maganizo. Mwachionekere, Adamu ndi Hava anali ndi zochuluka zoti aphunzire, popeza kuti iwo anali asanazione. Koma muli monse mmene iwo anaphunzirira zochuluka, iwo sakadadziwa zochuluka mofanana ndi Mlengi wawo. Chifukwa cha chimenecho, ngakhale anali angwiro, iwo anaikiridwa malire mwa kukhala mu mpangidwe waumunthu. Ungwiro unangotanthauza kuti iwo anali okwanira, kuti panalibe cholakwika m’kuumbidwa kwao kwakuthupi ndi kwamaganizo.
16 Kodi ndi mkati mwa malire otani amene ufulu waumunthu unalinganizidwa kugwira nchito bwino kwambiri? (1 Petro 2:16)
16 Ndiponso, Mulungu analenga anthu monga okhoza kuganiza, osati oti atsogozedwe ndi nzeru zobadwa nazo zo kha, monga momwe ziriri zinyama. Ndipo ndithudi inu mukuyamikira ufulu woterowo. Inu simukadafuna ali yense azikuuzani, mphindi iri yonse ya moyo wanu, zimene muyenera kuchita. Komabe, ufulu umenewo sunayenera kukhala wotheratu, ndiko kuti, wopanda malire, koma unayenera kukhala wapang’ono. Unayenera kuchitidwa mkati mwa malire a malamulo a Mulungu. Malamulo abwino kwambiri amenewo akakhala owerengeka ndi osavuta, olinganizidwira chimwemwe chachikulu kwambiri cha banja lonse la anthu. Chikondi cha Mulungu pa anthu chinasonyezedwa mwa kufuna kwake kuti iwo amvere malamulo ake, popeza kuti iye anadziwa kuti kulemekeza malamulo amene’wo kukawadzetsera mapindu osatha. Kusalemekeza Mulungu ndi malamulo ake kukaononga chimwemwe chawo. Sikukadzetsa chiri chose chabwino. Kunena zoona, kukadzetsa tsoka lotsimikizirika, chifukwa chakuti Mulungu anachenjeza Adamu ndi Hava kuti ngati iwo atam’siya iwo ‘akafa ndithu.’(Genesis2:17) Motero kuti apitirize kukhala ndi moyo, iwo anafunikira osati kokha kudya chakudya, kumwa madzi ndi kupuma mpweya, koma’nso kutsogozedwa ndi Mulungu ndi malamulo ake.
17. Kodi nchifukwa china chachikulu chotani chifukwa chake anthu afunikira kudalira Mulungu? (Salmo 146:3; Yeremiya 17:5-9)
17 Pali chifukwa china chovuta kwambiri chifukwa chake makolo athu oyamba anafunikira kupitiriza kudalira Mulungu. Chifukwa chimenecho ndicho chakuti anthu sanalengedwe kuti alamulire zochitika zawo bwino lomwe mosadalira Mulungu. Mulungu sanawapatse kuyenera kapena kukhoza kwa kuchita zimenezo. Monga momwe Baibulo likunenera kuti:”Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23)
Kodi Kuipa Kunayamba Motani
18. Kodi nchiani chimene chinalakwika ndi makolo anthu oyamba? (Yakobo 1:14,15; Salmo 36:9)
18 Pokhala ndi chiyambi chabwino kwambiri choterocho, kodi chinalakwika nchiani? Ichi: Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anagwiritsira nchito molakwa ufulu wao wa kusankha. Iwo anasankha kuchita zaozao m’malo mwa kugonjera ku ulamuliro wa Mulungu. Kwenikweni, mkazi’yo anaganiza kuti iwo akadakhala “ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.”(Genesis 3:5) Iwo anafuna kudzisankhira chimene chinali choyenera ndi chimene chinali cholakwa, akumadalira pa kuganiza kwawo kwa iwo eni. Iwo sanawoneretu kuononga kwakukulu kwambiri kumene kukachokera m’kuganiza koteroko. Koma zimenezo ndizo zimene zinachitika, pakuti’Mulungu sanganame.’ (Tito 1:2) Pamene iwo anachoka mu ulamuliro wa Mulungu, chimene chinachitika ndicho, m’lingaliro lalikulu, chofanana ndi chimene chimachitika pamene muchotsa pulagi la fani ya magetsi. Litadulidwa ku magwero ake a mphamvu yochirikiza, fanilo imayenda pang’nopang’ono ndipo potsirizira pake limafika pa kuimiratu. Mofananamo, pamene anthu awiri oyamba’wo anachoka ku Magwero a moyo, Yehova Mulungu, iwo potsirizira pake ananyentchera ndi kufa, monga momwe Mulungu anawachejezera kuti iwo akatero.
19. Kodi nchifukwa ninji mtundu wonse wa anthu unabadwa wopanda ungwiro? (Aroma 5:12)
19 Popeza kuti makolo athu oyamba anapandukira Mulungu iwo asanakhale ndi ana, kupanda ungwiro kunalowa kubadwa kwa mwana wawo woyamba kusanachitike. Adamu ndi Hava anakhala ngati chikombole cholakwika. Chiri chonse chotulutsidwa mwa iwo chinali’nso cholakwika. Iwo akanatha kupitiriza kwa ana awo zokha zimene iwo eni tsopano anali nazo—matupi ndi maganizo opanda ungwiro. Iwo sanalinso angwiro chifukwa chakuti iwo anadzifumutsa ku Magwero amene amachirikiza ungwiro ndi moyo. Yehova Mulungu.Motero mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa Aroma 5:12, munthu ali yense wobadwa kuyambira pa nthawi imeneyo wabadwa wopanda ungwiro, ndipo ali woyenera matenda, ukalamba ndi imfa. Koma Mulungu sanganenedwe kuti ndiye wochititsa zimenezi. Deuteronomo 32:5 (NW) amati:”Iwo okha achita mowononga; iwo saali ana ake, chiremacho nchawo.” Ndipo Mlaliki 7:29, (NW) amati: “Mulungu woona analenga mtundu wa anthu wolungama, koma iwo okha afunafuna zolinganiza zambiri.”
20. Kodi ndi motani m’mene zolakwa za anthu owerengeka zingacititsire upandu kwa ambirimbiri?
20 Koma kodi n’koyenera kuti kusamvera kochitidwa ndi anthu awiri okha kuyenera kuchititsa zotulukapo zowopsa zoterozo kwa ali yense. Eya, tikudziwa kuti kusasamala kwaumunthu kochitidwa ndi munthu mmodzi yekha m’kuchita chinthu chaching’ono chosungitsa m’kumanga nyumba kungachititse tsoka limene lingatayitse miyoyo ya anthu ambiri. Kulephera kusamalira mbali yofananayo mu damu kungachiitse kusweka kwake ndi chigumula chimene chikatha kuchititsa kuononga kwakukulu. Kachitidwe kamodzi ka psete kochitidwa ndi wolamulira mmodzi kangatsegule njira ya kachitidwe kotsatana-tsatanaka cholakwa m’boma, kakumachititsa chivulazo chachikulu kwa anthu mamiliyoni ambiri. M’banja, pamene atate ndi mai apanga chosankha cholakwa, ana awo angabvutike ndi zotulukapo zowopsa. Makolo athu oyamba anapanga chosankha cholakwa. Chifukwa cha chimenecho, banja lonse laumunthu linalowetsedwa m’kupanda ungwiro ndi tsoka.
21. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anachirikiza chilango cha imfa, ndipo komabe kodi ndi motani mmene cifundo chake chinasonyezedwera?
21 Popeza kuti lamulo la Mulungu lunalowetsedwamo, ndi ulemu wake womwe, iye sadakalola kuswedwako kukhala popanda kulimbikitsa lamulo limene’lo. Kodi ndi ulemu wotani umene anthu akakhala nao kaamba ka iye kapena kaamba ka lamulo lake ngati iye sakadachitapo kanthu? Kodi ife lero lino timalemekeza olamulira amene samamvera malamulo awo a iwo eni, kapena amene amalola anthu ena kuwaswa mwadala popanda chilango? Chifukwa cha chimenecho, Mulungu anakwaniritsa chilango chake chofotokozedwa cha kusamvera, chimene chinali imfa.Koma iye mwachifundo analola awiri oyambawo kukhala ndi ana, chimene tiyenera kuyamikira,zikadapanda kutero ife sitikanabadwa.Ndipo ngakhale kuli kwakuti ndife opanda ungwiro chifukwa cha kulephera kwa Adamu ndi Hava, kodi ife sitikukonda kwambiri kukhala amoyo koposa ndi akufa?
22. Kodi ndaninso amene ali ndi mbali yaikulu ya thayo la kuipa? (Mateyu 4:1-11; Aefeso 6:12)
22 Kodi uku ndiko kunena kuti kuipa kunayambika kotheratu ndi anthu? Ayi, pali zambiri. Kulenga kwa Mulungu zolengedwa zalutha sikunalekere kwa anthu. Pofikira pa nthawi imeneyo iye anali atalenga ana ena aluntha osawerengeka kumwamba, zolengedwa zauzimu. Pamene kuli kwakuti izo zinalinso zokhoza kuganiza, izonso zikanafunikira kugonjera ku malamulo abwino ndi oyenera a Mulungu kuti zikhalebe zamoyo. Komabe, mmodzi wa zolengedwa zauzimu zimene’zi anasinkhasinkha malingaliro olakwa. Ndipo pamene munthu asinkhasinkha chimene chiri cholakwa, chimenecho chingakule kufikira pamene iye akuchita chinthu cholakwa chimene iye alinkuchiganizira. Chomwechonso ndi cholengedwa chauzimu chimenechi. Icho chinakulitsa chikhumbo mwa icho chokha kufikira pakuti chinamchititsa kukaikira machitidwe a Mulungu. Icho chinauza mkazi wa Adamu, Hava, kuti iwo akatha kusamvera Mulungu ndipo komabe, icho chinati, “Kufa simudzafai.” (Genesis 3:4) Icho chinakaikira kufunikira kwawo kudalira Mlengi kaamba ka moyo ndi chimwemwe chopitirizidwa. Kwenikweni, icho chinawauza kuti kusamvera kukawapititsiradi zinthu patsogolo, kukumawachititsa kukhala ngati Mulungu. Motero icho chinakaikira kunena zowona kwa Mulungu. Ndipo mwa kukaikira malamulo a Mulungu, icho chinapereka chikaikiro pa njira ya Mulungu yolamulirira—ndithudi, pa kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira. Chifukwa cha zimenezi iye anachedwa Satana, limene likutanthauza wotsutsa, ndi Mdyerekezi, limene likutanthauza woneneza.
Kodi Nchifukwa Ninji Kwaloledwa kwa Nthawi Yaikulu Kwambiri?
23, 24. Kodi nchifukwa ninji nkhanizo zikatenga nthawi kuti zithe?
23 Chifukwa chakuti Mulungu ngwamphamvu kwambiri, iye mosavuta akanatha kufafaniza opanduka aumunthu ndi auzimu ameneŵa pachiyambi. Koma kumeneko sikukanathetsa nkhanizo mokhutiritsa. Kukadalekeranji? Chifukwa chakuti sinali mphamvu ya Mulungu imene inakaikiridwa. Nkhani zimene zinadzutsidwa zinali za makhalidwe. Ndipo nkhani yaikulu pakati pa nkhanizo inali iyi: Kodi njira ya chipanduko ikakhala yopambana? Kodi ulamuliro umene unanyalanyaza Mulungu ukatha kudzetsa mapindu osatha ku banja lonse la anthu? Kodi ulamuliro wa Mulungu pa anthu ukakhala wabwino kwambiri kwa iwo, kapena ulamuliro wa munthu ukakhala bwino kwambiri? Mulungu, mwa nzeru yake, anadziwa kuti imeneyi, ndi nkhani zina zazikulu zimene zinadzutsidwa, zikafunikira nthawi kuti zithe. Motero iye anapereka nyengo ya nthaŵi yotsimikizirika imene ikapatsa anthu mwaŵi wokwanira kufika pa kainde-inde wa zochita zao za ndale za dziko, za makhalidwe a anthu, za maindasitale ndi za sayansi.
24 Nyengo ya nthaŵi imeneyo sikadakhala masiku owerengeka kapena zaka zowerengeka chabe. Ikafunikira mibadwo yambiri kuti yankho lisonyezedwe kotheratu. Milandu ya m’khothi ingatenge milungu kapena miyezi ngakhale kumene anthu aŵiri okha alowetsedwamo. Nkhani zazikulu zimene ziripo zonena za ulamuliro wa Mulungu zikufuna yankho lokwanira, osati kuthetsedwa kwapang’ono. M’njira imeneyi kuthetsedwa kwa nkhani zimenezi sikukafunikira kubwerezedwa pa nthawi ina iri yonse yamtsogolo. Mulungu wachikondi sangalandire china chiri chonse chosakhala kuthetsedwa kotheratu. Ndipo tingakhale okondwa kuti izi ziri choncho, popeza kuti kuthetsedwa kokha koteroko kungatsegulire njira ya mtendere wosatha ndi chisungiko banja lonse la Mulungu la m’chilengedwe chonse, kumwamba ndi dziko lapansi.
25. Mosamala kanthu zakupita patsogolo kwa zinthu zakuthupi, kodi kudzilekanitsa kwa munthu ndi Mulungu kwadzetsa mtendere weniweni ndi chimwemwe?
25 Tsopano zaka zokwanira 6,000 zapita kuyambira pamene choyamba nkhanizo zinadzutsidwa. Kodi nchiani chimene chakhala chotulukapo cha kulekana ndi ulamuliro wa Mulungu? Mitundu yonse ya maboma, mitundu yonse ya magulu a kakhalidwe ka anthu, mitundu yonse ya magulu a chuma, ndi mitundu yonse ya timagulu ta zipembedzo yayesedwa. Koma palibe uli wonse wadzetsa mtendere weniweni, chisungiko, thanzi ndi chimwemwe chosatha. Kodi munthu anganyadire kupita patsogolo kwa zinthu zakuthupi pamene Nkhondo Yachiwiri ya Dziko yokha inaononga miyoyo yoposa mamiliyoni makumi asanu? Kodi ndiko kupita patsogolo kutumiza anthu ku mwezi, pamene maroketi amodzimodziwo okhala ndi zida zankhondo za nyukliya akatha kufafaniza mtundu wa anthu, ndi pamene mamiliyoni mazana ambiri a anthu pa dziko lapansi anali kuvutika ndi njala ndi umphaŵi pa nthaŵi imodzimodziyo imene anthu anayenda pa mwezi? Kodi pali ubwino wotani kukhala ndi nyumba yokhala ndi zabwino zabwino zambiri pamene mabanja akukhadzukana ndi mikangano, pamene chiwerengero cha zisudzulo chikuwonjezereka mosalekeza, pamene kuopa upandu m’chitaganya kukufala, pamene kuipitsa ndi nyumba zaubve zokhala mopanikizana zikuwonjezereka, pamene kutsika mtengo kwa ndalama kukuchititsa mamiliyoni ambiri kuchotsedwa pa nchito, pamene ziwawa, nkhondo zachiweniweni ndi kugwetsedwa kwa maboma ziri zochitika za chaka ndi chaka zimene zikuwopseza malo okhala a munthu ndi kakhalidwe?
26. Kodi nthawi yoperekedwayo yavumbula chiyani ponena za kudzilekanitsa kwa munthu ndi Mulungu? (Salmo 127:1
26 Monga momwe Mlembi Wamkulu wa Mitundu Yogwirizana Kurt Waldheim anabvomerezera chenicheni ndicho: “Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwa zinthu zakuthupi moyo wa anthu sunakhale konse ndi lingaliro lokulirapo la kusasungika koposa limene ukuliwona lero lino.”b [New York times, November 6,1972,tsamba 5] Bukhu lakuti Environmental Ethics limafotokoza’nso kuti: “Munthu, wolengedwa kuti apume mpweya wabwino, amwe ndi kusangalala ndi madzi abwino, ndi kusangalala ndi kukondweretsa kwa malo ake okhala achilengedwe,wasintha malo ake ndipo akuwona kuti sangathe kugwirizana nao. Iye akulinganiza kudzipulula.c Bukhu lakuti Environmental Ethics limafotokozanso kuti: “Munthu, wolengedwa kuti apume mpweya wabwino, amwe ndi kusangalala ndi madzi abwino, ndi kusangalala ndi kukondweretsa kwa malo ake okhala achilengedwe, wasintha malo ake ndipo akuwona kuti sangathe kugwirizana nawo. Iye akulinganiza kudzipulula.” Zoonadi kuloledwa kwa nthaŵi yaitali kwa kuipa kuyenera kusonyeza kwa anthu onse olingalira kuti anthu sanalengedwe ali ndi kukhoza kwa kuyendetsa zochita zawo bwino lomwe popanda chitsogozo cha Mulungu. Ndipo pokhala ndi zaka zikwi zisanu ndi chimodziza kulephera kwa anthu monga umboni munthu ali yense moyenerera sangaimbe Mulungu mlandu wa kusapereka nthaŵi yokwanira kuti anthu ayese. Nthaŵi yoperekedwayo yakhala yokwanira kutsimikizira kuti njira ya chipanduko kwa Mulungu yakhala tsoka lotheratu.
Kuipa Kudzatha Pasachedwa
27. Kodi Mulungu walinganiza kusintha kwakukulu motani? (Miyambo 2:21,22 Aroma 16:20)
27 Banja la anthu likufuna kwambiri kusintha kuti zinthu zikhale bwino. Kwenikweni, tikufunikira dongosolo latsopano kotheratu. Monga momwe katswiri wa za makhalidwe a anthu Erich Fromm anabvomerezera kuti, zoipa m’chitaganya zingachotsedwe “kokha ngati dongosolo lonse monga momwe lakhalira mkati mwa zaka 6,000 za zochitika zapitazo lingalowedwe mmalo ndi lina losiyana kotheratu.”d Chimenecho ndicho kwenikweni chimene Mulungu akulingalira! Pamene nyengo yake ya nthaŵi yoperekedwa itha, Mulungu watsimikiza kochotsa dongosolo la zinthu loipa lonse liripo’li, limodzi ndi awo amene akulikonda.”Oipa onse adzawawononga.”—Salmo 145:20.
28. Kodi Baibulo limatcha chiyani nthawi m’zimene tikukhala, ndipo kodi nchifukwa ninji? (2 Timoteo 3:1-5, 12,13; Mateyu 24:3-14)
28 Kodi zimenezi zidzachitika liti? Posachedwa kwambiri, chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mavuto osafanana ndi ena ali onse amene akantha banja la anthu chiyambire pamene nkhondo yoyamba ya dziko inayamba mu 1914 akupanga chizindikiro chosonyeza chimene chikutchedwa m’Baibulo “masiku otsiriza.” Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza’ano kudzakhala nkhondo za dziko lonse lapansi, upandu wowonjezereka, njala, miliri ya nthenda, kufunafuna zokondweretsa kosaletseka kochitidwa ndi ochuluka, kuchoka ku kukhulupirira Mulungu, chinyengo ndi kuipa kwachipembedzo, ndi zochitika zina zambiri. Zimenezi zikakhala ngati mizera ya chidindo cha chala, yosonyeza motsimikizirika mbadwo wathu kukhala wotsiriza mu umene Mulungu sakalekerera mikhalidwe yowopsa yoteroyo. Yesu ananeneratu kuti nthaŵi yathu idzawona mapeto a dongosolo la zinthu limene tsopano likulamulira dziko lapansi.
29. Kodi tikudziwa motani kuti mapeto a dongosolo ili ali pafupi?
29 Yesu ponena za mbadwo wa anthu chiyambi cha “masiku otsiriza” mu 1914 anatinso: “Indetu ndine-na kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:34) Izi zikutanthauza kuti anthu ena amene anali amoyo pamene Nkhondo Yoyamba ya Dziko inayamba mu 1914 akakhala ali amoyobe kuti awone mapeto a dongosolo iri la zinthu liripoli. Mbadwo wa Nkhondo Yoyamba umenewo ukukalamba kwambiri tsopano, ndipo chimene’chi chiri umboni wamphamvu wakuti mapeto a kuipa akuyandikira mofulumira.
30. Kodi nchiani chimene chidzachitikira magulu onse a ulamuliro wa anthu umene tsopano ukulamulira dziko lapansi? (Zefaniya 3:8 Yesaya 1:28)
30 Pamene mapeto afika, Mulungu adzasonyeza mphamvu yake yaikulu ndi kuloŵelera mwachindunji mzochita za anthu. Magulu onse a anthu otsutsana naye adzaphwanyidwa. Ulosi wa Danieli chaputala 2, vesi 44, umanena izi:”M’masiku a mafumu amenewo Mulungu wa kumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzaonongedwa, ndiponso ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina. Udzaphwanya maufumu onsewa ndi kuwatha, ndipo udzakhala kosatha.” (Revised Standard Version) Magulu onse ovulaza a anthu atachotsedwa, ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi udzayamba ulamuliro wotheratu.
31. Kodi ndi boma lotani limene Mulungu adzapatsa mtundu wonse wa anthu (Mateyu 6:9,10)
31 Chifukwa cha chimenecho, ulamuliro wa Mulungu udzachitidwa ndi boma latsopano, boma lakumwamba, ufumu wa Mulungu.Limenelo ndiro boma limene Yesu Kristu anapanga kukhala chintu chachikulu cha chiphunzitso chake. Ndipo ananeneratu kuti uwo wokha udzalamulira dziko lonse lapansi m’nthaŵi yokwanira. Popeza kuti Ufumuwo udzalamulira uli kumwamba, wotsogozedwa ndi Mulungu, sipadzakhala kuthekera kuli konse kwa kuipitsidwa kwake ndi anthu adyera. Motero mphamvu yolamulira idzakhala kumene inali poyamba, kumwamba, kwa Mulungu. Pokhala ndi ulamuliro wa Mulungu ukulamulira dziko lapansi, lonjezo lake ndiro lakuti “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (Yesaya 26:9) Ndiponso munthu ali yense sadzasochezedwa ndi chipembedzo chonyenga, popeza kuti sichidzakhalako. Ali yense wokhala ndi moyo adzaphunzitsidwa choonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake, kotero kuti, m’lingaliro lokwanira kotheratu,”dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Dziko Latsopano Lolungama
32. M’kulamulira kwa ufumu wa Mulungu, kodi mtendere udzakhala waukulu motani? (Yesaya 2:2-4)
32 M’kulamulira kwa ufumu wa Mulungu, chitaganya cha anthu chatsopano kotheratu chidzapangika, chitaganya chopangika ndi anthu aumulungu. M’dziko latsopano limeneli, chisamaliro chachikulu cha Mulungu kaamba ka ife chidzasonyezedwa ndi zimene akuchita. Choyamba, nkhondo sizidzaononganso mtendere ndi chimwemwe cha anthu. Kulekeranji? Chifukwa chakuti onse amene adzakhala atapulumuka mapeto a dziko iri lonse lapansi loipa liripoli adzakhala ataphunzitsidwiratu njira za mtendere, kotero kuti chitaganya chatsopano cha anthu chidzakhala ndi chiyambi chamtendere. Pamenepo, onse amene akudza kudzakhala m’dziko latsopano limenelo adzapitiriza kulandira maphunziro amodzi-modzi’wo m’kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndicho chifukwa chake lonjezo la Mulungu lidzatsimikizirika kukwaniritsidwa lakuti Mulungu “aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi. (Salmo 46:8, 9) Kodi mtendere umenewo udzakhala wokwanira motani? Mau olosera a Mulungu amati:Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka.—Salmo 37:11.
33. Kodi dziko lapansi lidzaloŵa m’kusandutsidwa kotani?
33 Ndiponso, awo okhala m’dziko latsopano limenelo adzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso amene Mulungu poyambirirapo analilinganizira. Ha, imeneyo idzakhala nchito yokhutiritsa chotani nanga kwa mtundu wa anthu! Ndipo paradaiso atabwezeretsedwa, anthu adzakhala okhoza kusangalala mokwanira ndi nyanja zazing’ono, mitsinje ndi nyanja zazikulu; timapiri ndi mapiri madambo ndi zigwa; maluwa okongola, zomera ndi mitengo; kuphatikizapo nyama zokondweretsa. Ngakhale’nso kuperewera kwa zakudya sikudzachitikanso, pakuti “dziko lapansi lenilenilo lidzaperekadi dzinthu dzake; Mulungu, Mulungu wathu, adzatidalitsa.” Inde, “pa dziko lapansi padzakhala dzinthu dzochuluka; pa nsonga za maphiri padzakhala zosefukira.”—Salmo 67:6; 72:16, NW.
34. Kodi ndi kuchiritsa kwakuthupi kotani kumene kudzachitika?
34 Limodzi ndi mtendere wosatha ndi zakudya zochuluka padzadza thanzi labwino. Popeza kuti Mulungu analenga munthu, iye akudziwa bwino kwambiri koposa dokotala ali yense chimene kwenikweni angachite kuti achiritse wopunduka, kuti apangitse wakhungu kuwona ndi wagonthi kumva, ndi kuchotsa matenda onse, ukalamba ndi imfa. Mphamvu ya Mulungu ya kuchita zimenezi inasonyezedwa ndi Yesu Kristu pa mlingo wosonyeza, kapena waung’ono, pamene anali pa dziko lapansi. Baibulo limatiuza kuti: “Makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalakhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipi Iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opuduka miyendo nayenda ndi akhungu napenya.”—Mateyu: 15:30,31.
35, 36. Kodi ndi motani mmene anthu akufa adzapatsidwira mwaŵi wa kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu? (Yohane 5:28,29: Luka 7:11-15)
35 Yesu anachula Paradaiso wa pa dziko lapansi ameneyu pamene anauza munthu amene anali pachikike pambali pake kuti:”Udzakhala nd ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43, NW) Koma munthu ameneyo anamwalira. Motero kodi iye akanatha motani kulowa m’Paradaiso? Mwa njira ya makonzedwe ena odabwitsa amene amasonyeza mmene Mulungu akusamalirira-mwa njira ya kuuka kwa akufa. Baibulo pa Machitidwe 24:15 limati:” Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Pamene anali pa dziko lapansi,Yesu anaukitsa anthu akufa kuti asonyeze mphamvu ya Mulungu ya kuchita zimene’zi m’kulamulira kwa ufumu wake.
36 Kodi mukuona lingaliro la chiukiriro kukhala lobvuta kulikhulupirira? Komabe ngakhale tsopano mungathe kuona maprogramu a wailesi yakanema okhala ndi anthu amene akhala akufa kwa nthawi yaitali. Inu mumamva mau awo, kuwona machitidwe awo ndi kudziwa mikhalidwe yawo. Ngati munthu chabe angasunge zinthu zoterozo pa matepi a wailesi yakanema, sikukakhala kovuta kwa Mulungu wa Nzeru Zonse kusunga m’maganizo mwake chithuzithunzi chocho lowanacholoŵana cha umunthu ndi mikhalidwe ya munthu ali yense payekha amene iye adzafuna kuwalenganso. Iye wachita zimenezi, ndipo iye adzaukitsira akufa oterowo ku moyo kachiŵiri. M’njira imeneyi, iwonso adzakhala ndi mwawi wa kusangalala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu. Ndipo mwa kukhuthula manda, ndi mwa kuchiritsa anthu matenda, ukalamba ndi imfa zobadwa nazo, Mulungu “adzamezadi imfa kosatha.” (Yesaya 25:8, NW) Motero, anthu adzakhala okhoza kukhala ndi moyo kosatha!
37. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Mulungu adzapereka zoposa chivulazo chiri chonse chimene anthu alandira mosalungama?
37 Mwa njira ya ufumu wake, Mulungu adzasintha kotheratu mkhalidwe woipa umene wakhalapo kwa nthawi yaitali kwambiri! Kwamuyaya Iye adzasonyeza kusamala kwake kwakukulu kwa ife mwa kupereka madalitso amene adzapitilira pa kukonza chivulazo chiri chonse chimene tachilandira m’nthawi yakale. Mavuto akale amene takumana nao m’dongosolo iri liripoli pa nthaŵi imeneyo adzaiwalika zi, ngati titati tiwakumbukire. Lonjezo la Mulungu ndiro: “Ndilenga kumwamba kwatsopano [boma lakumwamba latsopano pa mtundu wonse wa anthu] ndi dziko lapansi latsopano [chitaganya cha anthu olungama]; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.” (Yesaya 65:17,18) Pokhala ndi madalitso abwino kwambiri oterowo patsogolopa, mungathe kuwona chifukwa chake Baibulo limanena kuti Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo.” Ndipo kulekeranji? Pakuti “sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chibvumbulutso 21:4.
Mulungu Amasamala—Kodi Ife Timatero?
38. Kodi Mulungu amafuna anthu a mtundu wotani m’dziko lake latsopano? (Salmo 37:37,38)
38 Chenicheni chakuti Mulungu adzathetsa kuipa posachedwa ndi kudzetsa dziko latsopano lokondweretsa chimasonyeza kuti iye amatisamaladi. Koma kodi ife timam’samala? Ngati timatero, tifunikira kukusonyeza. Kodi tiyenera kuchitanji? Baibulo limati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.” (1 Yohane 2: 17) Mtundu wa anthu amene Mulungu akuwafuna m’dziko lake latsopano ndiwo awo amene akuchita chifuniro chake ndi kugonjera ku ulamuliro wake wolungama. Awa ndiwo mtundu wa anthu amene adzamvera malamulo ake ndi kuthandizira kupanga “dziko lapansi latsopano” kukhala malo abwino kwambiri okhalamo. Anthu amene akutsutsa ulamuliro wa Mulungu akangokhala opangitsa mavuto, motero iwo sadzaloledwa kukhalamo.
39. Ngati mukufuna moyo wamuyaya, kodi ndi kufuna-funa kotani kumene muyenera kupanga? (Miyambo 2:1-6)
39 Kodi mukufuna kukhala m’dziko latsopano lolungama la Mulungu? Pamenepo chinthu choyamba kuti muchite ndicho kuphunzira zofuna Mulungu zokhalira ndi moyo. Kodi kumene’ko ndi kupempha zochulukitsitsa? Ngati inu mukanalonjezedwa nyumba yokongola m’malo onga munda wamaluwa, popanda malipiro, kodi inu simukanapeza nthawi kuti mudziwe mmene mungayenerere? Mawu a Mulungu amalonjeza zoposa kwambiri—moyo wamuyaya pa dziko lapansi laparadaiso—ngati tifunafuna kuti tidziwe chimene chiri chifuniro chake kwa ife, ndiyeno nkuchichita. Baibulo limati:”Moyo wasatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
40. Kodi Baibulo limapereka mapindu ena otani tsopano? (2 Timoteo 3:16,17)
40 Kuphunzira Baibulo kudzapatsanso inu ndi banja lanu chitsogozo chopidulitsa chofunika kwambiri kaamba ka kukhala ndi moyo kwa tsiku ndi tsiku m’nthawi zovuta zino. Ndiponso kumapereka mtendere weniweni wa maganizo, popeza kuti limatiuza chifukwa chake mikhalidwe iri yoipa kwambiri ndi chimene chiri m’tsogolo. Chofunika kopamana, kudzakukhozetsani kukulitsa chikondi chenicheni pa Mulungu, popeza kuti “amakhala wopereka mphotho wa awo omfunafuna mwaphamphu.”—Ahebri 11:6 NW.
41. Kodi ndi chithandizo chotani chimene mboni za Yehova zidzakupatsani kwaulere?
41 Mboni za Yehova mokondwa ndi mwaulere zidzapereka nthawi yao kuti zikuthandizeni kuphunzira zambiri zonena za makonzedwe a Mulungu okhalira ndi moyo m’dziko lake latsopano. Mosakaikiranso, pali mafunso ena, amene muli nawo onena za Mulungu ndi Baibulo.Mboni za Yehova zidzakondwera kukambitsirana nanu ameneŵa pa nyumba panu, kuchokera m’Baibulo lanu. Pamenepo, koposa ndi kutsatira njira ya moyo yanokha kapena kudalira kuganiza kwa anthu opanda ungwiro, mudzatsogozedwa ndi chidziwitso chabwino kwambiri koposa chimene chiripo lero lino. Chifukwa cha chimenecho, pamene nthaŵi idakalipobe inu mukufulumidzidwa kuchita monga momwe uphungu wouziridwa wa Mau a Mulungu umanenera:”Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, . . . pakuti Iye asamalira inu.”—1Petro 5:6,7.
[Mawu a M’munsi]
a Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwa njira ina, mau ogwidwa a Malemba m’kabukhu’ka ngochokera m’Baibulo Lachichewa (Revised Union Nyanja Version) ndi New World Translation of the Holy Scriptures, NW akumakhala chidule chake.
b New York Times, November 6, 1972, tsamba 5.
c Environmental Ethics, lolembedwa ndi Donald R. Scoby, 1971, tsamba 17.
d New York Post, March 30, 1974, tsamba 35.
[Tchati patsamba 22]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
ZONSE MUMBADWO UMODZI
1914
Nkhondo za Dziko
Njala Zazikulu
Mliri ya Nthenda
Maupandu Achiwawa
Kuipitsa kwa Padziko Lonse
Mapeto a Dongosolo Ili
[Chithunzi patsamba 6]
Ngati umphaŵi wa anthu ndi uve ziyenera kunenedwa kuti ndizochititsidwa ndi Mulungu . . .
[Chithunzi patsamba 7]
. . . Kodi ndani amene ayenera kutamandidwa chifukwa cha kukongola kwa dziko lapansi ndi minda yake yachonde?
[Chithunzi patsamba 9]
Dziko lapansi liri lokonzekeretsedwa bwino kwambiri kuchirikiza moyo koposa nyumba iriyonse
[Chithunzi patsamba 9]
Popeza kuti nyumba iriyonse iri ndi womanga, nanga bwanji dziko lapansi!
[Chithunzi patsamba 13]
Baibulo limasonyeza kuti chifuno cha Mulungu chinali kupanga dziko lonse lapansi kukhala munda wamaluŵa, paradaiso, kuti anthu asangalale nalo kosatha
[Chithunzi patsamba 14]
Pamene fani yadulidwa kumagwero ake a mphamvu, imayenda pang’onopang’ono ndi kuima. Mofananamo, pamene mtundu wa anthu unachoka kwa Mulungu, kunyentchera kunatsatirapo
[Chithunzi patsamba 16]
Pamene chinthu chaching’ono chosungitsa chinyalanyazidwa, ngakhale damu lalikulu lingasweke. Pamene makolo athu oyamba anaswa lamulo la Mulungu, chigumula cha kuipa ndi kuvutika chiyanamba
[Chithunzi patsamba 19]
Mlandu wa m’khothi ungatenge milungu ngakhale pamene anthu aŵiri okha aloŵetsedwamo. Nkhani zoloŵetsamo ulamuliro wa Mulungu ziyenera kuthetsedwa kotheratu, kosatha, ndipo kumeneku kukufunikira nthaŵi yokwanira
[Chithunzi patsamba 24]
M’dziko latsopano la Mulungu simudzakhala nkhondo, popeza kuti iye ‘akupangitsa nkhondo kulekeka’
[Chithunzi patsamba 25]
Mtundu wa anthu suudzavutikanso ndi njala
[Chithunzi patsamba 26]
Anthu okalamba adzabweretsedwa kunyonga imene imadza ndi unyamata ndi thanzi langwiro
[Chithunzi patsamba 27]
Akufa osungidwa m’chikumbukiro cha Mulungu adzabwezeretsedwa kumoyo ndi kugwirizanitsidwa ndi okondedwa awo
[Chithunzi patsamba 29]
M’kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu, moyo udzakhala wokondweretsa kwambiri chakuti udzaposa kwambiri kuvutika kulikonse kumene tsopano takumana nako mosalungama
[Chithunzi patsamba 31]
Ngati moyo m’malo okondweretsa unalinkuperekedwa, kodi inu simukanafuna kudziŵa mmene mungayenelere? Dziko latsopano la Mulungu limalonjeza zochuluka kwambiri, koma tiyenera kupeza nthaŵi kuti tiphunzire mmene tingayenelere