Mutu 18
Mabanja Achimwemwe m’Chifuno cha Mulungu
1. Kodi Yehova amachitanji kuchititsa banja lake kukhala lachimwemwe, ndipo chotero kodi n’chifukwa ninji tiyenera kum’thokoza? (Yakobo 1:17)
YEHOVA MULUNGU ndiye “Atate, kwa amene banja liri lonse kumwamba ndi pa dziko lapansi lapezako dzina lake.” Monga “Mulungu wachimwemwe,” iye amadziwa’nso m’mene angapangire banja lake la chilengedwe chonse kukhala lachimwemwe. (Aefeso 3:14, 15, NW; 1 Timoteo 1:11) Iye moolowa manja amasamalira zosowa za ana ake, ndipo kaamba ka zimene’zi tiyenera mosalekeza kum’thokoza, monga momwe anachitira wamasalmo:
“Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake . . . Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimamka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwo mibadwo.”—Salmo 100:3-5.
2. Kodi Mulungu analinganiza kuti lamulo la “kudzaza dziko lapansi” likwaniritsidwe motani? (1 Akorinto 7:10, 11)
2 Yehova wapanga makonzedwe achikondi kopambana kaamba ka mabanja pano pa dziko lapansi. Pamene iye analamula makolo athu oyambirira ‘kubalana ndi kuchuluka ndi kudzaza dziko lapansi,’ kumene’ku sikunayenera kuchitidwa m’njira ya mwamwai. Kunayenera kuchitidwa mwa kakonzedwe kolemekezeka ka ukwati wa anthu. Awiri okwatirana ali onse-mwamuna ndi mkazi—‘akakhala thupi limodzi’ m’chigwirizano chosatha chimene chikakhala chopanda bvuto ndi chisudzulo, ndi chimene chikapereka maziko okhazikika kaamba ka kubala ndi kulera mabanja m’paradaiso wa Mulungu.—Genesis 1:28; 2:22-24.
3. Kodi ndi motani m’mene Yesu anatsimikizirira kupatulika kwa ukwati? (1 Akorinto 6:18)
3 Pamene atsogoleri achipembedzo oipa a m’nthawi ya Yesu anayesa kum’kola ndi mafunso obvuta onena za chisudzulo, iye anatsimikizira kupatulika kwa kakonzedwe koyambirira ka Mulungu ka ukwati:
“Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiri’wo adzakhala thupi limodzi? chotero kuti sali’nso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse . . . Amene ali yense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo.”—Mateyu 19:4-9.
4. Kodi ndi chifuno chotani cha Mulungu kulinga ku dziko lapansi chimene chidzachitidwa potsirizira pake? (Yesaya 45:12, 18)
4 Ha, ndi m’tsogolo mwaulemerero motani nanga m’mene Yehova analinganiza kaamba ka dziko lapansi’li! Popeza kuti munthu analengedwa “m’chifanizo cha Mulungu,” pamenepo mabanja onse a anthu mofananamo akafikira pa kusonyeza umunthu Wake. Potsirizira pake, dziko lonse lapansi likadzazidwa ndi unyinji wa amuna ndi akazi angwiro, abale ndi alongo, onse omatamanda Mulungu, Mlengi’yo. (Genesis 1:27) Chifuno chimene’cho chidzakwaniritsidwa’di!
5. Kodi n’chifukwa ninji maukwati ambiri akulephera lero lino? (Aroma 1:24, 31)
5 Komabe, zimene tikuona lero lino ziri zosiyana kwambiri ndi zimene Mulungu anali kulingalira kaamba ka anthu okwatirana. Ndipo kodi n’chifukwa ninji? Chiri chifukwa chakuti anthu sakusonyeza’nso “chifanizo” cha umunthu wa Mulungu. Maka-maka ‘m’masiku otsiriza’ ano ukwati wasonyezedwa kukhala wopanda kukhulupirika ndi kupanda “chikondi chachibadwidwe,” kotero kuti mliri waukulu wa zisudzulo, mabanja osweka, matenda opatsana mwa kugonana, ana apathengo ndi kutaya mimba zatulukapo. Anthu ambiri alephera kulabadira chilangizo chabwino cha mtumwi Paulo chakuti:
“Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.”—Ahebri 13:4; 2 Timoteo 3:1-5.
6. Kodi ndi motani m’mene tingasungire kugonana ndi ukwati ziri zolemekezeka? (1 Atesalonika 4:3-8)
6 Kodi ndi motani m’mene tingasungire kugonana ndi ukwati ziri zolemekezeka lero lino? Tingatero mwa kupewa “dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro,” ndi kudzibveka ‘umunthu watsopano, umene ukupangidwa kukhala watsopano mwa chidziwitso cholongosoka mogwirizana ndi chifane-fane cha Uyo amene anaulenga,’ Yehova Mulungu.—Akolose 3:5-10.
7. (a) Kodi ndi motani m’mene tingakulitsire umunthu watsopano? (Aefeso 4:22-24) (b) Kodi ndi masitepe oyenera otani amene banja lingatenge kulinga ku kumanga banja logwirizana? (Afilipi 2:2-4)
7 “Umunthu watsopano” umene’wu uli wofunika kwambiri kwa onse amene akufuna kusangalala ndi moyo wa banja wachimwemwe ndi wopindulitsa. Mwa kubvala umunthu watsopano umene’wu, ziwalo za banja zingathe kupeza mapindu a kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a khalidwe labwino a Baibulo onena za ukwati. Ponena za zimene’zi mau ena a Paulo akugwira ntchito akuti:
“Bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma, mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monga’nso Ambuye anakhulukira inu, teroni inu’nso; koma koposa izi zone khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphamphu.” (Akolose 3:12-14)
Inde, chikondi chiri “chomangira cha mtima wamphumphu,” ndipo chimene’chi chimapititsidwa patsogolo m’banja mwa kukhala kwa onse ndi chikondwerero mwa wina ndi mnzake, mwa kuononga nthawi pa zakudya ndi pa zochitika zina m’kulankhulana, mwa kupeza chisangalalo pamodzi m’kusangulutsa, machuthi ndi ntchito zina zolimbikitsa. Mwa kuyesa-yesa kozindikira, onse m’banja-achikulire ndi ana-angakhale ndi phande m’kukulitsa umodzi umene’wu, ndipo chotulukapo cha banja lachimwemwe ndi logwirizana chingathe kukhala chosangalatsa kopambana. Munthu ali yense ayenera kuthandizira mbali yake, monga momwe Paulo akupitirizira kulongosola.
MBALI YA MKAZI
8. (a) Kodi ndi malo otani amene akazi ayenera kukhala nao, ndipo chifukwa ninji? (1 Petro 3:5, 6) (b) Kodi ndi motani m’mene mkazi angapindulire chikondi ndi chiyanjo cha banja lake?
8 Akazi angathe kupindula mwa kulabadira uphungu wa mau a Paulo:
“Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.” (Akolose 3:18)
Umene’wu uli wogwirizana ndi kakonzedwe koyambirira ka Mulungu, kakuti mkazi ayenera kukhala “wothangata monga wokwaniritsa” kwa mwamuna. (Genesis 2:20, NW) Kumene kuli mitu iwiri, kumakhala kukokana ndi kulimbana, kukumachititsa kusagwirizana. Koma kumene mkazi nthawi zonse amasonyeza “ulemu waukulu kwa mwamuna wake” ndi zosankha zake, ngakhale kunyalanyaza zolakwa zake, iye angathe kupanga kuthandizira kwamphamvu kwambiri ku banja logwirizana ndi losangalala. Ngati iye ali wakhama ‘m’kuyang’anira mayendedwe a banja lake,’ kuphatikizapo kulangiza ana ake, amene’wa ‘adzam’cha wodala.’ Ndipo’nso, mwamuna wake adzam’tamanda.—Aefeso 5:33; Miyambo 31:10-31.
9. Kodi ndi uphungu wotani umene Baibulo limapereka ponena za a mu ukwati oskhulupirira? (Aroma 12:17, 18)
9 Ngakhale ngati mwamuna wake ali wosakhulupirira, iye ali chikhalirebe “mutu” wa mkazi wake. Pokhala wokhulupirira, mkaziyo ayenera kupitirizabe kuchita ntchito zake zaukazi, koma ndi chikondwerero chachikondi choonjezereka mu thanzi la mwamuna’yo koposa kale lonse, pakuti amakhala wothangata Wachikristu. (1 Akorinto 11:3) Mtumwi Petro akunena kuti kuli bwino kuti akazi abvale “mzimu wofatsa ndi wachete,” kuti:
“Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngati’nso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.” (1 Petro 3:1-4)
Mwa kupitirizabe kukhala mokhulupirika ndi mwamuna wosakhulupirira, ngakhale kuli kwakuti iye ali wotsutsa ntchito zake zachipembedzo, kudekha kwa mkazi kungafupidwe mwa kupenda kwa pambuyo pake kwa mwamuna wake ndi kulandira “mbiri yabwino.” Muli monse, ana ake ang’ono, ngati ali omvera, amalingaliridwa ndi Mulungu kukhala “oyera” m’kakonzedwe ka banja kamene iye akuchitira khama kukasungabe. Malamulo a khalidwe ofanana’wo amagwira ntchito kumene amuna okhulupirira agwirizanitsidwa mu ukwati ndi akazi osakhulupirira.—1 Akorinto 7:12-16.
MBALI YA MWAMUNA
10. Kodi ndi motani m’mene amuna ayenera kuchitira ndi akazi ao? (Miyambo 5:18)
10 Amuna akapindulitsidwa kwambiri mwa kulabadira mau otsatirapo a Paulo kwa Akolose:
“Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.” (Akolose 3:19:
Umutu wa mwamuna nthawi zonse uyenera kuchitidwa m’njira yachikondi, osati mu mkhalidwe wa nkhanza. Pamene iye ‘akupitirizabe kukonda mkazi wake,’ ayenera kuyesa-yesa kum’sonyeza “ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu,” kulingalira kapangidwe ka malingaliro ake ndi masinthidwe a akazi. (1 Petro 3:7) Asanapange zosankha za banja, ayenera kukambitsirana zinthu ndi mkazi wake ndi kupereka lingaliro lachikondi ku malingaliro ndi zikhumbo zake. Iye nthawi zonse ayenera kulingalira zabwino zake, ndipo maka-maka thanzi lake lauzimu.
11.Kodi n’chifukwa ninji amuna sayenera kukhala aukali kwa akazi ao? (1 Akorinto 11:3; Mateyu 11:28, 29)
11 M’mbali zonse za moyo, mwamuna ayenera kupitirizabe kukonda mkazi wake “monga’nso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha, m’malo mwake.” Mu uthenga Wabwino, sitimawerenga za Yesu kukhala “akupsya mtima kwambiri” ndi mpingo, kodi si choncho? Ndipo’nso amuna sayenera kuchitira akazi mwankhanza. Iwo ayenera kukhala ‘okonda akazi ao monga matupi ao,’ akumawasamalira monga matupi a iwo eni, pakuti, ndithudi, iwo onse ali “thupi limodzi” pamodzi.—Aefeso 5:25, 28-30.
12. Kodi timafuna ana athu kukhala ndi phande m’chiyembekezo chabwino kwambiri chotani? (Salmo 148:12, 13)
12 Koma bwanji za ana athu? Iwo ali a mtengo wapatali kwa ife, ndipo timafuna kuwaona akukhala ndi phande limodzi nafe m’kutamanda Yehova kwamuyaya m’paradaiso wa pa dziko lapansi wa Mulungu. Kenako tidzapenda m’mene tingawathandizirire kufikira cholinga chimene’chi.