Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gh mutu 21 tsamba 183-190
  • Mulungu Apanga “Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Apanga “Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano”
  • Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NTHAWI ZOSANGALATSA MTSOGOLO!
  • “KHALANI OSANGALALA NTHAWI ZONSE”
  • KUYEMBEKEZERA LONJEZO LA MULUNGU
  • Mmene “Miyamba Yatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano” Zikuyambira
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Zolengedwa Zatsopano Zipangidwa!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
gh mutu 21 tsamba 183-190

Mutu 21

Mulungu Apanga “Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano”

1. Kodi “kudziwa” Mulungu ndi Kristu kumatanthauzanji? (Yohane 1:14, 18)

KUDZIWA kwathu Yehova, Ambuye Mfumu ya Chilengedwe Chonse, kudzachititsa madalitso osatha. Monga momwe Yesu ananenera m’pemphero kwa Yehova kuti:

“Ichi chitanthauza moyo wosatha, kulandira kwao chidziwitso cha inu, Mulungu woona yekha, ndi cha uyo amene munam’tuma, Yesu Kristu.” (Yohane 17:3, NW)

Koma kumene’ku kumaphatikizamo zochuluka kwambiri koposa chidziwitso cha m’mutu chabe. Kumafunikira kuphunzira kwathu mikhalidwe yaikulu ya Mulungu ndi ntchito zake, ndi kuyamikira kwathu kweni-kweni mwai waukulu wa kulowa mu unansi wachimwemwe ndi iye pa maziko a nsembe yoombola ya Mwana wake, Yesu Kristu.

2. Kodi kudziwa zifuno za Yehova kuyenera kutisonkhezera motani? (Salmo 112:1)

2 Pokhala mutaphunzira “mbiri yabwino” yonena za chifuno cha Yehova cha kuchotsa m’chilengedwe chonse kuipa konse ndi kuchititsa dziko lapansi’li kachiwiri’nso kukhala mu mkhalidwe woyera, wamtendere ndi wachimwemwe, kodi simukuona kukhala osonkhezereka kutamanda ndi kum’thokoza? Inu muyenera! Ha, ndi kosangalatsa chotani nanga m’mene kuliri kuona zifuno zake zikukwaniritsidwa ndi kudziwa kuti tingathe kukhalamo ndi phande!

NTHAWI ZOSANGALATSA MTSOGOLO!

3. Kodi n’chifukwa ninji kumwamba kukusangalala poona chipembedzo chonyenga chikupasulidwa? (Deuteronomo 32:43)

3 Tsiku lirinkudza mofulumira pamene yehova adzapereka lamulo la kufafaniza ufumu wa pa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga Wachibabulo. Chionongeko chake chidzadza mofulumira, monga ngati “m’ora limodzi.” Ochirikiza ena apapitapo angam’lirire, akumanena kuti “Tsoka, tsoka,” koma awo amene abvutika ndi chitonzo chimene iye wachiika pa dzina la Mulungu adzasangalala:

“Kondwerani pa iye, m’mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.”​—Chibvubulutso 18:19, 20.

4. Kodi n’chifukwa ninji “chisautso chachikulu” chidzakhala chifukwa chochititsa anthu oopa Mulungu kusangalala? (Luka 21:28)

4 Koma si zokha’zo! “Chitsautso chachikulu” chidzapitirizabe kusesa “kuchokera ku mtundu kumka ku mtundu, . . . kuchokera ku malekezero amodzi a dziko lapansi kumka ku malekezero ena a dziko lapansi,” kuononga oipa onse. (Yeremiya 25:32, 33, NW) Namondwe wa chionongeko amene’yo adzadza modzidzimutsa kwambiri, “monga kunakhala masiku a Nowa,” ndipo adzakhala wa kanthawi kukafupi. “Chisautso’cho” chidzakhala chachikulu kwambiri kwakuti Yehova akanapanda “kufupikitsa masiku’wo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense.” Chilengedwe chonse chathunthu chidzachotseredwa awo onse amene amatsutsa chilungamo ndi kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova pa zolengedwa zake. Chimene’cho, ndithudi, chidzakhala chifukwa chochititsa chisangalalo!​—Luka 17:26, 27; Marko 13:19, 20.

“KHALANI OSANGALALA NTHAWI ZONSE”

5. (a) Kodi ndi “miyamba” yakale yotani pa anthu imene idzachotsedwa? (2 Petro 3:7) (b) Kodi ndi kakonzedwe kosatha kotani kamene pa nthawi imene’yo kadzapereka chisangalalo kwa anthu a Mulungu? (Yesaya 32:1)

5 Chisonkhezero chochenjera cha Satana ndi ziwanda zake pokhala chitachotsedwa, ndipo ulamuliro wopangidwa ndi anthu usakutsendereza’nso mofanana ndi “miyamba” yotsendereza pa dziko lapansi, ‘khamu lalikulu” la opulumuka lidzagwira ntchito kufutukulira paradaiso wokongola ku malekezero a dziko lapansi. Iwo “adzadzipereka eni ake” kaamba ka ntchito imene’yi, monga momwe’di amachitira mu ntchito ya Mulungu lero lino. (Salmo 110:3) Ndipo’nso, iwo adzakhala ndi chithandizo chochokera ku kakonzedwe ka Mulungu ka nthawi imene’yo, “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zimene Yehova akuzilenga ngakhale tsopano lino. Iye akutiitana kuti:

“Khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu [ufumu wakumwamba] wosangalala, ndi anthu ake okondwa.”​—(Yesaya 65:17, 18)

“Miyamba yatsopano: idzakhala kakonzedwe kosatha ndi kachikondi koyendetsera zochitika za “dziko lapansi latsopano” – dalitso lamuyaya kwa “anthu” a Yehova ndi “ana” ao.​—Yesaya 66:22.

6. (a) Kodi ndani amene ali “mkwatibwi” wa Mwanawankhosa,” ndipo kodi ndi motani m’mene iye akukhalira ndi phande m’kudalitsa anthu? (Chibvumbulutso 19:6, 7) (b) Kodi ndi unansi wosangalatsa wotani umene munthu pa nthawi imene’yo adzasangalala nawo ndi Mulungu? (Salmo 86:9, 10)

6 Ha ndi chisangalalo chotani nanga chimene chimatsagana ndi phwando la ukwati! Ndipo pamene “Mwanawankhosa” woperekedwa nsembe pa nthawi ina, tsopano Yesu Kristu wokhazikitsidwa pa mpando wachifumu’yo kumwamba, akugwirizanitsidwa kumene’ko ndi “mkwatibwi” wake-ziwalo zoukitsidwa 144,000 za “kagulu ka nkhosa” za opambana​—chisangalalo chidzakhala chachikulu kopambana! Kaguluka “mkwatibwi” wauzimu kamene’ka kakulongosoledwa mokongola m’machaputala otsirizira a Baibulo kukhala mbali ya “miyamba yatsopano” imene ikupereka madalitso pa “dziko lapansi latsopano,” chitaganya cha anthu olungama ndi chooneka. Iye akulongosoledwa kukhala “mzinda woyera’wo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu,” osati mwakuthupi koma m’lingaliro la kutembenuzira chisamaliro ku banja la anthu la pa dziko lapansi ndi kuwachiritsa. Motero mitundu ya pa dziko lapansi idzalowa mu unansi wachimwemwe kopambana ndi Mulungu:

“Mulungu. . . adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake ndi Mulungu yekha adzakhala nao Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhala’nso imfa; ndipo sipadzakhala’nso maliro, kapena kulira, kapena chowawawitsa; zoyamba’zo zapita.”​—Chibvumbulutso 21:1-4.

7. Kodi n’chifukwa ninji malojezo abwino kwambiri amene’wa ali otsimikizirika kukwaniritsidwa? (Yoswa 21:45)

7 “Inu mukunena kuti, “Zosakhulupiririka”? Ai, ziri zokhulupiririka kotheratu! Ziri zotsimikizirika kudza! Pakuti maulosi onse a Baibulo, kuyambira pa lonjezo la Mulungu mu Edene zaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapita’zo, amasumika pa zochitika za tsiku lino, pamene ulamuliro wa Mulungu uyenera kudziwikitsidwa kotheratu kupyolera mwa “mbeu” Yaumesiya. Chifuno chake chonse chachikulu chiyenera kukwaniritsidwa kaamba ka kudalitsidwa kwa “mitundu yonse” imene ikudza kudzam’tumikira mwamphumphu.​—Genesis 22:18.

8. Kodi n’chifukwa ninji chiukiriro chidzakhala nthawi ya chisangalalo? (Miyambo 10:22)

8 Ndipo bwanji ponena za chifuno cha Mulungu cholongosoledwa cha kuukitsa kuchokera kumanda mabiliyoni ambiri a anthu akufa? Kodi tiyenera kunena kuti zimene’zi n’zosakhulupiririka? Ai, pakuti Yesu iye mwini akutitsimikizira kuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi imene onse ali m’manda adzamba mau [ a Yesu], nadzatulukira . . . kukuuka.” (Yohane 5:28, 29) Ha, ndi mfuu zotani za chisangalalo zimene zidzatsagana ndi kugwirizana’nso kumene kudzachitika pa nthawi imene’yo m’dziko lapansi la paradaiso! Ndipo ha, ndi chimwemwe chotani nanga chimene chidzakhalapo m’kuphunzitsa anthu obwezeretsedwa amene’wa ponena za paradaiso wauzimu wa Mulungu! “Mabukhu” a chilangizo adzaperekedwa, ndipo amene’wa adzawathandiza kuchita “ntchito” zabwino, zawachititsa maina ao kukhalabe chilembedwere “m’bukhu la moyo”!​—Chibvumbulutso 20:11-15.

9. Kodi n’chifukwa ninji tingathe kukhala ndi chitsimikiziro chakuti Yehova adzapanga “zinthu zonse kukhala zatsopano”? (Yesaya 55:11)

9 Yehova iye mwini akulengeza kuti: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” Ha, ndi lonjezo lokonderetsa chotani nanga m’mene liriri! Kodi mtumwi Yohane amakaikira kulemba zinthu zodabwitsa zotero’zo? Yehova akum’tsimikiziritsa, kuti: “Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.” Iwo ali monga ngati akwaniritsidwa kale, pakuti Yehova akuonjeza kuti: “Zatha.” ​—Chibvumbulutso 21:5, 6; Aroma 4:17.

10. Kodi ndi motani m’mene “chombo cha m’mlengalenga dziko lapansi” chidzaonekera pa mapeto a “tsiku la kupuma’ la Mulungu? (Salmo 104:1, 24)

10 Zaka chikwi za kubwezeretsa kwaulemerero, chimwemwe ndi kusangalala ziri patsogolo pa anthu. Ndipo ndi kaonekedwe kodabwitsa chotani nanga kamene dziko lapansi lidzapereka pa mapeto a ulamuliro wa zaka chikwi umene’wo wokhala m’manja mwa Yesu ndi “mkwatibwi” wake wakumwamba! Mwakuthupi, mwamakhalidwe ndi mwauzimu-dziko lonse lapansi ndi anthu ake okhalapo mabiliyoni ambiri lidzanyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kumwamba ku ulemerero wa Mlengi wake. “Chombo cha m’mlengalenga dziko lapansi” chidzakhala chisanakongolepo kwambiri ndi kale lonse koposa pa kutha kwa ‘tsiku la kupuma’ lalikulu la Yehova. – Genesis 2:2, 3.

11. Kodi n’chiani chimene chikuchitika pa mapeto a ulamuliro wa zaka chikwi wa Kristu? (Chibvumbulutso 15:3, 4)

11 Pamenepo, ziyambukiro zonse za imfa yochititsidwa ndi uchimo wa Adamu pokhala ‘zitathedwa,’ Yesu momvera “adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndi Atate wake.” Anthu onse, pa mapeto a zaka chikwi, tsopano adzaimirira mwachindunji athayo pamaso pa Yehova kaamba kanjira yao ya m’tsogolo monga zolengedwa zaumunthu zangwiro “m’chifanizo cha Mulungu.” (1 Akorinto 15:24-26; Genesis 1:27) Kwa kanthawi, “adzamasulidwa Satana m’ndende yake” kudzayesa anthu okhalitsidwa angwiro amene’wo, ponena za chosankha chao cha ulamuliro wosatha wa Mulungu. Pamenepo Satana ndi ziwanda zake, limodzi ndi ali yense wa anthu amene akusankha kum’tsatira, adzaponyeredwa “m’nyanja ya moto”​—chizindikiro cha “imfa yachiwiri,” ku imene kulibe chiukiriro.​—Chibvumbulutso 20:7-10, 14.

KUYEMBEKEZERA LONJEZO LA MULUNGU

12. Kodi ndi motani m’mene tiyenera kupangira kuyesa-yesa pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu? (1 Akorinto 15:58)

12 Ndi chisangalalo tikuyembekezera ulamuliro wa pa dziko lonse lapansi wa “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Koma sitiyenera kungokhala! Monga momwe mtumwi Petro akutiuzira kuti:

“Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuziyembekezera monga mwa lonjezo lake, ndipo m’zimene’zi mudzakhala chilungamo. Chotero, okondedwa, popeza mukuyembekezera zinthu zimene’zi, chitani zotheka kuti mupezedwe potsirizira pake opanda banga ndi opanda chirema ndi mu mtendere.” (2 Petro 3:13, 14, NW)

Sitingathe kukhala ndi “mawanga” otisonyeza chifukwa cha kukhala ndi phande m’machita-chita a chipembedzo chonyenga kapena zoipa za dziko. Sitingalole zirema ziri zonse mu umunthu wathu watsopano wonga wa Kristu. Tiyenera kukhala pa mtendere ndi Yehova, ndipo ndi wina ndi mnzake. Umodzi umene’wu tingathe kuusonyeza mwa kuimira mwamphamvu ulamuliro wa Yehova ndi mwa kulimbikitsana ‘kukhala maso.’ Ndipo kodi chifukwa ninji? “Chifukwa munthawi m’mene simuganizira, Mwana wa munthu [Yesu Kristu] adzadza” kudzapereka chiweruzo pa dongosolo la zinthu lakale’li ndi kudzetsa latsopano.​—Mateyu 24:42-44.

13. (a) Kodi ndi chisangalalo chapadera chotani chimene anthu a Yehova angakhale nacho tsopano? (b) Kodi n’chifukwa ninji ‘mbiri yabwino ya ufumu” iri mbiri yabwino kopambana?

13 Imene’yo ndi “mbiri yabwino ya ufumu” yodabwitsa! Ha, ndi chisangalalo chotani chimene anthu onse a Yehova ali nacho tsopano m’kuilengeza m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse”! (Mateyu 24:14, NW) Ndithudi, iri mbiri yabwino yosangalatsa kopambana! Ndipo m’dziko lapansi laparadaiso, pamene Yehova akupitirizabe kugwiritsira ntchito ufumu wa Kristu m’kupanga “zinthu zonse kukhala zatsopano,” mbiri yabwino idzachuluka kwa anthu. Ndithudi, “Mafuko onse a dziko adzadalitsidwa”! (Machitidwe 3:25) Ha, dni kusangalala kotani nanga kumene kudzakhalapo pamene mafuko onse alondola chifuno cheni-cheni m’moyo pansi pa ufumu wakumwamba woyendetsedwa ndi olamulira amene amayamika Yehova monga “Ambuye Mfumu” ndi amene amazindikira kweni-kweni ndi kusamalira anthu! (Chibvumbulutso 6:10) Imene’yi iri’di “mbiri yabwino yaulemerero ya Mulungu wachimwemwe.” Iri mbiri yabwino yokusangalatsani.

[Chithunzi patsamba 184]

Mulungu adzayeretsa dziko lapansi, akumachotsa kuipa konse ndi chisoni

[Chithunzi patsamba 187]

Pamene Mulungu apanga “zinthu zonse kukhala zatsopano,” chiri chonse pa dziko lapansi kachiwiri’nso chidzapereka ulemu kwa Mlengi

[Chithunzi patsamba 189]

“Mbiri yabwino yaulemerero ya Mulungu wachimwemwe” ikuperekedwa KUKUPANGANI kukhala achimwemwe!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena