Mutu 5
Woyambirira Kudzozedwa ndi Mzimu Woyera ndi Mphamvu
1, 2. (a) Kodi Mesiya wolonjezedwa’yo anayenera kudzozedwa ndi yani ndipo ndi chiani?(b) Kodi ndi ulosi wotani wa Yesaya umene iye anayenera kuugwira mau ndi kuugwiritsira ntchito kwa iye mwini?
MAFUMU ndi akulu a ansembe a Israyeli wakale anali kudzozedwera malo a ntchito mwa kutsanuliridwa pamutu mafuta oikira pa malo antchito. Kodi Mesiya wolonjezedwa’yo anayenera kudzozedwa mwa njira imene’yo? Ai! Mesiya weniweni anayenera kukhala munthu amene Mulungu akam’dzoza “ndi mzimu woyera ndi mphamvu.” (Machitidwe 10:38) Iye akakhala uyo amene anabvomerezedwa kugwira mau ndi kugwiritsira ntchito kwa iye mwini mau olosera a Yesaya 61:1-3
2 “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’singa mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku la kubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; ndikakonzere iwo amene alira maliro m’Ziyoni, ndi kuwapatsa chobvala chokometsa m’malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m’malo mwa maliro, chobvala cha matamando m’malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti iye alemekezedwe.”
3. Kodi n’chifukwa ninji anthu a m’nthawi zakale amene mzimu wa wa Mulungu unagwirapo ntchito sanatsimikizire kukhala Mesiya wolonjezedwa’yo?
3 Amuna a m’nthawi zakale anali okutidwa ndi mzimu wa Mulungu kapena unakhala ukugwira ntchito pa iwo kapena anali odzazidwa nawo. Koma iwo sanadzozedwe nawo konse. Chotero iwo sanatsimikizire kukhala Msesiya wolakalakidwa’yo. Zimene’zi zinali choncho ngakhale ponena za Yohane m’batizi, za amene mngelo Gabrieli anali atanena kwa atate wake wansembe Zekariya kuti: “Iye adzadzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira ali m’mimba mwa amake.”—Luka 1:15, NW.
4. Kodi n’chiani chimene Yohane M’batizi, ngakhale kuli kwakuti anali wodzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira m’mimba mwa amake, anabvomereza ponena za Kristu?
4 Ansembe ndi Alevi anatumizidwa kuchokera ku Yerusalemu kukafunsa Yohane iye mwini kuti awauze kuti iye anali yani mwaukumu chifukwa cha ntchito imene iye anali kuchita. Kodi Yonane anayankha motani? “Anabvomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Kristu. Ndipo anam’funsa iye, Nanga bwanji? ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneri’yo kodi? Nayankha, Iai. Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiani za iwe wekha? Anati, Ndine mau a wopfuula m’chipululu, Lungamitsani njira ya Ambuye, monga anati Yesaya mneneri’yo.”—Yohane 1:19-23; Yesaya 40:3; Malaki 4:5, 6; Deuteronomo 18:15-19.
5, 6. (a) Kodi n’chiani chimene Mulungu anatumiza Yohane kukachita ponena za Kristu? (b) Kodi ndi motani m’mene Yohane anadziyerekezerera iye mwini ndi Mesiya kapena Kristu weniweni?
5 Motero Yohane, ngakhale kuli kwakuti anali wodzazidwa ndi mzimu woyera anakana kuti anali Wolonjezedwa’yo wodzozedwa ndi mzimu wa Mulungu. Iye sanayese kukhala Mesiya wo nyenga, koma anabvomereza kukhala kalambule bwalo chabe wa Kristu kapena Mesiya weniweni. Kunena zoona, Mulungu anam’tumiza kudzabatiza Kristu kapena Mesiya weniweni m’madzi. Yohane 1:29-34.
6 Chochitira’nso umboni kuona mtima kwa Yohane m’nkhani’yo ndicho cholembedwa’cho mu Luke 3:15-17 kuti: “Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganiza-ganiza m’mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Kristu; Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: amene chouluzira chake chiri m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m’chiruli chake; koma mankhusu adzatentha m’moto wosazima.”
7. Kodi n’chifukwa ninji kubatizidwa kwa munthu ndi moto kukakhala kosafunika kwambiri koposa ndi kubatizidwa kwa munthu ndi mzimu woyera?
7 Mau a Yohane anasonyeza bwino lomwe kuti Mesiya sakangobatizidwa kapena kudzozedwa ndi mzimu wa Mulungu koma’nso akakhala wokhoza kubatiza ena ndi mzimu woyera. Kukakhala bwino kopambana kwa munthu kubatizidwa ndi mzimu woyera koposa kubatizidwa ndi moto umene ukaononga munthu’yo mongofanana ndi mungu wopanda pake umene umaonongedwa m’moto umene sukuzima kufikira mungu wonse’wo utanyeka.—Mateyu 3:7-12.
8. Kodi n’chifukwa ninji anthu anthu pa nthawi imene’yo anali kuyembekezera kudza kwa Mesiya, ndipo kodi n’chifukwa ninji nkhani’yo inali yofulumira kwa iwo?
8 N’kosadabwitsa kuti “anthu anali kuyembekezera.” Mwina mwake iwo anawerengera kuchokera m’Malemba kuti nthawi inali itakwana yakuti Mesiya atulukire. Chotero iwo anayamba kuganizaganiza ponena zakuti kaya Yohane M’batizi anali Mesiya wolonjezedwa’yo kapena ai. (Danieli 9:24-27) Nkhani yonena za Mesiya kapena Kristu inali yofulumira. Mulungu, Wotumiza Mesiya’yo, sanali kuchedwetsa nthawi’yo kosatha. Iye anali wotsimikizira kutumiza Mesiya, ndipo iye anali ndi nthawi yoikika yochititsira chitsimikiziro chake kuchitika. Iye sali wozengereza, koma iye amasunga ndandanda yake ya nthawi monga momwe yaperekedwera m’Mau ake.
9. Kodi ndi motani m’mene Agalatiya 4:4, 5 amasonyezera kuti Mulungu sali wozenge reza
9 Agalatiya 4:4, 5 amati: “Pokwaniridwa nthawi Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo, kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.”
10. Kodi Mulungu anatumiza Mwana wake kuchokera kuti m’thawi yake, ndi kutuluka mwa mkazi wa mtundu wotani?
10 Mtumwi Paulo, mlembi wa mau amene’wo anali ndi zonena zochuluka za nthawi ndi nyengo m’makonzedwe a Mulungu. Iye akunena kuti Mwana wa Mulungu aneyenera kukhala womasula Ayuda mwa njira ya kuombola. Chifukwa cha chimene’chi iye anayenera kukhala Mesiya, Kristu wao. Kodi Mulungu anam’tumiza kuchokera kuti? Eya, kuchokera kumkwamba kumene “Mwana wobadwa yekha” amene’yu wakhala ali chiyambire pamene Mulungu anam’lenga kale-kale’lo. Kudza kwake kukhla “womvera lamulo” kunatanthauza kuti iye anabadwa monga Myuda, Muisrayeli, chiwalo cha mtundu umene unali m’pangano Lachilamulo ndi Yehova chimene Mose anali nkhoswe yake. Chotero mkazi amene Mwana wa Mulungu anatulukamo anayenera kukhala Mkazi Wachiyuda, iye mwiniyo wokhala womvera chilamulo cha Mose.—Agalatiya 3:19-25.
11. Polingalira kusiyana kwa malo a Mwana wa Mulungu ndi mkasi’yo, kodi n’chiani chimene chinali chofunika m’malo mwakuti Mwana’yo akhale Mesiya?
11 Chozizwitsa chinayenera kuchitika, chimene Mulugu Wamphamvuyonse yekha akanachichita. Mwana wake “wobadwa woyamba,” Mau kapena Logos, anali kumwamba monga munthu wauzimu wamphamvu, pamene mkazi’yo mwa amene iye anayenera kuchokera ngati anafuna kukhala Mesiya, anali pano pa dziko lapansi. Mwana’yo monga momwe iye analiri, sakanatha kulowa m’mimba ya mkazi Wachiyuda amene’yu. Ndiyeno, chiani? Eya, Mwana’yo anayenera kudzikhuthula chiri chonse chimene iye anali pamene anali “m’maonekedwe ngati a Mulungu. Iye anayenera kusamutsiridwa mayo wake kuchokera ku miyamba yosaoneka kumka m’mimba ya mkazi. Motero iye akafikira pa kubadwa “mafanizidwe a anthu.” Zimene’zi zinafunikira kuti Mwana wa Mulungu adzichepetse kwakukulu. (Afilipi 2:5-8) Koma Mwana’yo anali wofunitsitsa kuchita zimene’zi chifukwa cha kukonda Atate wake ndi kaamba ka chifuno cha kutumikira zolinga za Atate wake wakumwamba.
12. Kodi ndani amene anali “mkazi” amene Mulungu anam’sankha, ndipo kodi n’chifukwa ninji Mesiya anayenera kukhala “woyamba kubadwa” wake?
12 Kodi ndi motani m’mene Atate wakumwamba anachitira chozizwitsa chimene’chi? Mwa njira yotani? Chinalowetsamo “mkazi.” Akazi ambiri Achiisrayeli, makamaka awo a pfuko la Yuda, angakhale atafuna kukhala mai wa Mesiya wolonjezedwa’yo. Koma silinali thayo lao kudzisankhira kukhala mai wa Mesiya. Atate wakumwamba wa Mesiya anali Yekha amene akanachita kusankha m’nkhani imene’yi. Iye anatero. Mkazi amene iye anam’sankha anali “namwali” wosakwatiwa. (Yesaya 7:14) Ngati iye akanakhala kuti anali atakwatiwa kale ndipo anali ndi ana, zimene’zi zikanadzutsa mafunso ponena za utate ndi cholowa ndi zoyenera. Chotero “namwali” amene Mulungu anam’sankha anatsimikizira kukhala ‘namwali wosakhudzidwa.’ (Mateyu 1:22, 23) Kubadwa kwa “woyamba kubadwa” wa Mulungu monga munthu wangwiro wa mwazi ndi thupi kunafunikira mofananamo kukhala’nso kubadwa kwa “woyamba kubadwa” wa mkazi’yo. Akolose 1:15; Yohane 3:16, 17.
13. Kodi Mulungu anatumiza Gabrieli kwa yani pa ulendo wachiwiri, ndipo kodi ndi motani m’mene Gabrieli anadzipangitsira kuoneka kwa iye?
13 Mkazi wosankhidwa’yo anayenera kukhala’nso mbadwa ya Mfumu Davide mwana wa Jese. Mu unansi wotero’wo ndi Mfumu Davide, mkazi’yo akapatsa mwana wake woyamba kubadwa kuyenera kwachibadwa ponena za ufumu wa Davide pa mafuko khumi ndi awiri a “nyumba ya Yakobo” (Israyeli). Moyenerera, mkazi wosankhidwa’yo anabadwira mu “mzinda wa Davide,” mzinda wa Betelehemu, m’chigawo cha Yuda. (Luka 2:11) Koma pa nthawi imene Mulungu anadziwitsa mkazi’yo kuti akayanjidwa kwambiri, iye anali kukhala mu tauni la m’Galileya la Nazarete. Pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi izi zisanacitike, Mulungu anali atatumiza mngelo Gabrieli kukalengeza kwa wansembe Zekariya kudza kwa mwana wamwamuna woti adzachedweYohani, ndipo moyenerera Mulungu tsopano anatumiza Gabrieli kwa mai wan’tsogolo wa Mesiya amene Yohane anayenera kum’sonyeza. Mkazi’yo anali namwali Wachiyuda wochedwa Mariya, mwana wamkazi wa Heli wa mzera wachifumu wa Davide. Gabrieli anabvala thupi la umunthu kuti akaonekere kwa Mariya. Moni wake anadabwitsa Mariya. Kodi n’chifukwa ninji mlendo wodzidzimutsa amene’yu ananena kuti Yehova anali ndi mkazi’yo? Kodi n’chifukwa ninji ndi iye?
14. Kodi Gabrieli ananenanji polongosolera Maria chifukwa chake Mulungu anali naye?
14 Chinali chifukwa chakuti Yehova anam’sankha kukhala mai wa mfumu yaulemerero Yaumesiya. Chotero Gabrieli anati: “Usaope, Mariya; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nadzachedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.”—Luka 1:26-33.
15. Kodi mngelo’yo ananena kuti n’chiani chimene chikagwira ntchito pa Mariya, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani?
15 Kodi zimene’zi zikanachitika motani kwa “namwali” wosakwatiwa, ‘namwali wosakhudziwa’? Limene’li ndiro linali funso la Mariya, ndipo likanakhala’nso lathu. Chotero tsopano tiyeni tione chimene chinayenera kuyamba kugwira ntchito pa Mariya. “Ndipo mngelo anayankha nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chake’nso Choyera’cho chikadzabadwa, chidzachedwa Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:34, 35.
16. (a) Kodi n’chifukwa ninji chimene chinayenera kubadwa mwa Mariya chinayenera kukhala kanthu kena ‘koyera”? (b) Kodi Mariya akanayankha motani Gabrieli, koma kodi iye anayankha motani?
16 “Mzimu Woyera unayenera kugwira ntchito, ndipo kumene’ku kukanachititsa kubadwa kwa kanthu kena “koyera.” Kumene’ku kukakhala kubadwa mwa namwali. Kwa Mulungu kumene’ku sikunali chozizwitsa chosatheka kuchichita, pakuti mngelo Gabrieli anatsiriza mwa kunena kwa Mariya kuti: “Palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.” (Luka 1:37) Kodi Mariya anayankha motani zonse’zi? Iye akanatha kunena kuti: ‘Koma, taonani! Ine ndatomeredwa kudzakwatiwa ndi mmisiri wopala matabwa Yosefe mwana Yakobo, wa mzera wachifumu wa Davide. Ndiri ndi thayo la kukhala mai wa ana ake. Sindingathe kuthetsa chitomero changa ndi Yosefe. Mudzangondikhululukira!’ Motero panaonekera kukhala pali zobvuta kwenikweni, koma Mulungu anadziwa’nso za zimene’zi. Chotero, mwa chikhulupiriro, Mariya anayankha Gabrieli kuti: “Onani mdzakazi wa Yehova! Zichitiketu kwa ine mogwirizana ndi mau anu.”—Luka 1:38, NW.
17. Kodi n’chiani chimene tsopano chinachitikira Mwana “woyamba kubadwa” wa Mulungu kumwamba, ndipo kodi n’chiani chimene bwenzi la Mariya Yosefe linauzidwa kuchita?
17 Kukhala ndi pakati kwa Mariya mwa chozizwitsa cha Mulungu Wamphamvuyonse tsopano kunali kutakonzeka. Mwadzidzidzi, mosadziwika kwa Mariya pa dziko lapansi, Mwana “woyamba kubadwa” wa Mulungu anazimiririka kumwamba. Mphamvu yake ya moyo inasamutsiridwa pansi pano m’mimba mwa namwali wosakhudzidwa Mariya. Chotero, “amai wake Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndipo’nso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m’mtima kum’leka iye m’tseri. Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m’kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chiri cha Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”—Mateyu 1:18-21.
18. Kodi Yesu anali kwenikweni mwana wa yani, ndipo kodi ndi motani m’mene dzina lake linaliri lolosera?
18 Dzina’lo Yesu linali lolosera. Liri mpangidwe wofupikitsidwa wa Yehosuwa, kutanthauza “Yehova ndiye Chipulumutso.” Moyenerera, wokhala ndi dzina limene’li anayenera ‘kupulumutsa anthu ake ku machimo ao.’ Iye anayenera kukhala, osati mwana wa Yosefe, koma “Mwana wa Mulungu,” monga momwe Gabrieli ananenera.
19. Kodi n’chifukwa ninji mwana wa Mariya Yesu sanali Mwana watsopano wa Mulungu, ndipo n’chifukwa ninji iye sanali “Mulungu wobvala thupi” kapena “Mulungumunthu”?
19 Mwana wa Mariya woyamba kubadwa wa chozizwitsa’yo sanayenera kukhala Mwana watsopano wa Mulungu, koma anali kwenikweni Mwana wokhalako kale wa Mulungu amene moyo wake unasamutsidwa kuchokera kumwamba kubwera pa dziko lapansi kupyolera mwa Mariya monga amai waumunthu. Moyenerera, iye sakanachedwa chimene anthu ambiri achipembedzo a Chikristu cha Dziko amam’cha “Mulungu wosandulika thupi,” mau amene sangapezedwe m, Baibulo louziridwa. Kumwamba Mwana “woyamba kubadwa” wa Mulungu anakhala ndi dzina laulemu lakuti Mau (kapena, Logos). Chotero, m’Yohane 1:14, timawerenga kuti: “Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate.” Atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko ali olakwa m’kumucha “Mulungu munthu,” pakuti, mu 1 Timoteo 2:5, 6, iye akuchedwa “munthu, Kristu Yesu.” Iye sanadziche kukhala, ndipo sakanena kukhala, Mulungu Wam’mwambamwamba.—Yohane 20:31; Luka 1:32.
ANADZOZEDWA NDI YANI NDIPO NDI CHIANI?
20. Kodi mwana woyamba kubadwa wa Mariya anabadwira kuti, ndipo chifukwa ninji?
20 M’kati mwa kulamulira kwa Kaisara Augusto, mfumu ya Ufumu wachikunja wa Aroma, Yesu anabadwa m’Betelehemu wachikunja wa Aroma, Yesu anabadwa m’Betelehemu wa Yuda, kukwaniritsa ulosi wa Mika 5:2. Kumeneku kunali kuchiyambi kwa mphakasa ya chaka cha 2 Nyengo yathu Ino isanakhale. Pamene Yosefe ndi Mariya anali m’Betelehemu kaamba ka zifuno za kukalembetsedwa m’kaundula, “iye anabala mwana wake wamwumuna woyamba; nam’kulunga Iye m’saru nam’goneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti anasowa malo m’nyumba ya alendo.”—Luka 2:7.
21. Kodi ndani amene anapangidwa kukhala mboni zoona ndi maso za pa dziko lapansi pa usiku wa kubadwa kwa Yesu, ndipo motani?
21 Wodzakhala Mesiya anali atadza! Imene’yo inali mbiri yokondweretsa imene mngelo wa ulemerero wa Mulungu anailengeza kwa abusa oyang’anira khosa zao usiku kumabusa pafupi ndi Betelehemu. “Mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikonwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.” Ngakhale kuli kwakuti Yesu wobadwa chatsopano’yo m’khola la ng’ombe m’Betelehemu sanali kuzidziwa, “dzidzidzi panali pamodzi ndi mngelo’yo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena, Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.” Pamenepo abusa ouzidwa’wo anamka kukafunafuna khanda’lo m’khola mwa ng’ombe ndi kulipeza, ndipo motero iwo anapindulitsidwa mwa kukhala mboni zoona ndi ndi maso za kubadwa kwa Yesu usiku wofunika kwambiri umene’wo.—Luka 2:8-20.
22. Kodi ndi liti pameneYesu anakhala chimene mngelo anam’cha, “Kristu Ambuye” ndipo motani?
22 Kodi ndi liti pamene Yesu anakhala kwenikweni “Kristu Ambuye”? Osati pa tsiku lachisanu ndi chitatu la kubadwa kwake, pamene iye anadulidwa. Iye sanadzozedwe pa tsiku limene’lo. Kunali pamene iye anali ndi zaka makumi atatu. Iye anapita kwa Yohane M’batizi, amene pa nthawi’yo anali kubatiza pa Mtsinje wa Yordano. Iye sanapemphe Yohane kum’dzoza ndi mafuta ali onse aukumu kuti akhale mfumu Yaumesiya pa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli. Iye anapempha kuti abatizidwe m’madzi, monga momwe Ayuda ambiri anali atachitira m’kati mwa miyezi ya ntchito yapoyera ya Yohane. “Pamene anthu onse anabatizidwa, ndi Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo, ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m’thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.”—Luka 3:21-23.
23. Kodi ndi motani m’mene Yohane M’batizi anachitirira umboni wonena za m’mene Yesu anapangidwira kukhala Kristu?
23 Pambuyo pake mneneri Yohane anachitira umboni za chimene’chi kwa ophunzira ake, kwa amene iye anati: “Ndipo sindinadziwa Iye, koma wondituma’yo kudzabatiza ndi madzi. Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.”—Yohane 1:33, 34.
24. Kodi Andreya anauza wake kuti iye wapeza yani, ndipo kodi ndi kubvomereza kotani kumene Nataniyeli anapanga ponena za Yesu?
24 Masiku okwanira makumi anai pambuyo pa ubatizo wa Yesu mu Mtsinje wa Yordano, Yohane anasonyeza awiri a ophunzira ake kwa Yesu. Iwo anatsatira Yesu ndi kulandira chilangizo cha Baibulo chochokera kwa iye. Pokhala wokondwa kwambiri ndi zimene iye anatumba modabwitsa, mmodzi wa iwo, Andreya, anapeza mbale wake wochedwa Petro nati kwa iye: “Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Kristu).” Kanthawi kochepa pambuyo pake Nataniyeli anatengeredwa kwa Yesu. Pambuyo pa kumvetsera Yesu, Nataniyeli anati kwa iye: “Rabi Inu ndinu Mwana wa Mulugu, ndinu Mfumu ya Israyeli.” Chimene’chi nacho’nso, chinali chitsimikiziritso chopangidwa ndi Nataniyeli chakuti Yesu wodzozedwa’yo anali Mesiya, Kristu.—Yohane 1:35-49.
MESIYA WAUZIMU KAPENA KRISTU
25. Mosasamala kanthu za kukhala kwa ubatizo wa Yohane kaamba ka machimo, kodi n’chifukwa ninji Yesu anabatizidwa ndi iye?
25 Popeza kuti Yesu pamene anali pa dziko lapansi anali Mwana waumunthu weniweni wa Mulungu ndipo analibe machimo oti awalape, kodi n’chifukwa ninji anamizidwa ndi munthu amene anali kulalikira ubatizo wa kulapa ndi wa kukhululukidwa kwa machimo? Iye anatero kaamba ka chifuno cha kukwaniritsa ulosi wa Salmo 40:6-8. Ubatizo wake wa m’madzi unachitira chizindikiro kudzionetsera kwake kotheratu ‘kuchita chifuniro chanu, O Mulungu’ monga momwe chifuniro chimene’cho chikabvumbulidwira kwa iye. (Ahebri 10:5-10) Chifuniro chaumulungu chimene’cho chikam’sonyeza m’mene iye angachitire monga Mesiya kapena Kristu.
26. Chimene mau a Mulungu anamvedwa akunena kuchokera kumwamba chinasonyeza kusintha kotani m’moyo wa Yesu, ndipo kodi n’chifukwa ninji chimene’chi chinali chofunika kwa Iye?
26 Pamene Yesu anatuluka m’madzi a ubatizo, mau a Mulungu anamvedwa kuchokera kumwamba, akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Zimene’zi zinasonyeza kusintha m’moyo wa Yesu. M’njira yotani? Chilengezo cha Mulungu chinatanthauza kuti iye tsopano anali atabala Yesu wa usinkhu wa zaka makumi atatu’yo kukhala Mwana wauzimu wa Mulungu. Motero njira inatsegulidwa yakuti Mwana wa Mulungu amene’yu abwerere kumwamba. Kumene’ku kunali kofunika ngakhale kwa Yesu. Kunali monga momwe’di iye analongosolera kwa wolamulira Wachiyuda Nikodemo, kuti: “Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulugu. Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu. Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.”—Yohane 3:3-7.
27. Kodi chilengezo cha Mulungu kuchokera kumwamba ponena za Mwana wake chinasonyezanji ponena za Yesu, ndipo kodi ndi motani m’mene unansi wa Yesu kwa Mariya tsopano unasinthira?
27 Mwa chilengezo chopangidwa kuchokera kumwamba’cho Yehova Mulungu analengeza kuti iye anali atabala Mwana wauzimu wokhala ndi chiyembekezo cha kulowa mu ufumu wakumwamba wa Mulungu. Mariya, mai wa chimene chinali chathupi, sanali amai wa Mwana wauzimu wa Mulungu amene’yu, ndipo pambuyo pake Yesu sakusimbidwa kukhala akum’cha “amai.” Moyenera Yesu akunenedwa kukhala “wobadwa kuchokera mwa Mulungu” amene amayang’anira ophunzira ake, atsatiri ake. Mwa chitsanzo, mu 1 Yohane 5:18 timawerenga kuti “Mwana wobadwa kuchokera kwa Mulungu amam’tetezera, ndipo Woipa’yo samam’khudza.” (The Jerusalem Bible) “Ndiye Mwana wa Mulungu amene amam’sunga ali wosungika, ndipo woipa’yo sangam’khudze.” (The New English Bible) Chotero unansi wa Yesu kwa mai wake wa pa dziko lapansi, Mariya, unasintha. Kuyambira pa nthawi imene’yo kumkabe m’tsogolo iye anadzipereka ku zinthu zauzimu, osati ku kuchita ntchito yopala matabwa m’tauni ya kwa Mariya ya Nazarete.
28. Motero kodi Yesu anadzozedwa kukhala mtundu wotani wa Mesiya, ndi kuti alamulire ali kuti?
28 Pa Mwana wauzimu wa Mulungu, amene anali atangobalidwa kumene’yo, mzimu woyera wa Mulungu unatsika, kudzam’dzoza iye kukhala Mesiya kapena Kristu. Iye anayenera kukhala wamphamvu kwambiri koposa Mesiya waumunthu wa thupi ndi mwazi. Iye anayenera kukhala Mesiya wauzimu, amene potsirizira pake akalamulira mu ufumu wakumwamba wa Mulungu. Pa kukwera kumwamba kwa Mesiya amene’yu “mpando wachifumu wa Davide atate wake” ukakwezedwa kumwamba. Chotero kuyenera kukhala kwakuti ‘akalamulira monga mfumu pa nyumba ya Yakobo kosatha’ ali pa mpando wachifumu wakumwamba.—Luka 1:32, 33.
29. Kodi ndi dzina laulemu lotani limene Yesu monga Wodzozedwa angakhale atalionjezera ku dzdina lake, ndipo kodi iye anadzozedwa ndi chiani?
29 Pambuyo pa kudzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu pa Mtsinje wa Yordano, Yesu akanatha kuonjezera ku dzina lake dzina laulemu lakuti Mesiya kapera Kristu, ndipo moyenerera iye anafikira pa kuchedwa Yesu Mesiya kapena Yesu Kristu. Miyezi ingapo pambuyo pake, pamene Yesu anali pa ulendo wake wobwerera ku Galileya, mkazi wina Wachisamariya anati kwa iye: “Ndidziwa kuti Mesiya adza (wochedwa Kristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.” Pamenepo Yesu modekha anati kwa iye: “Ine wakulankhula nawe ndine amene.” (Yohane 4:25, 26) Monga Mesiya kapena Kristu, Yesu anadzozedwa, osati ndi mafuta aukumu otsanuliridwa pa mutu pake, koma ndi kanthu kena kamene Mulungu yekha akanatha kukatsanulira pa iye monga Mwana wauzimu. Nanga ndi chiani? Mtumwi Petro akuyankha kuti: “Mulungu anam’dzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi Mdierekezi.”—Machitidwe 10:38.
30. Mofanana ndi m’chochitika cha Davide, kodi ndi motani m’mene Yesu anayambukiridwira pa nthawi yomwe’yo pambuyo pa kudzozedwa kwake, ndipo kodi n’chifukwa ninji iye sa nataye mzimu woyera?
30 Pano tikukumbukira kuti, mbusa wachinyamata’yo Davide atadzozedwa ndi mafuta ndi mneneri Samueli, mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu inayamba kugwira ntchito pa iye kuti azichita zinthu zapadera. N’chimodzimodzi’nso pamene Yesu anakhala wodzozedwa kuchokera kumbamba, ndi Mulungu. Luka 4:1, 2 amachitira umboni kuti: “Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordano, natsogozedwa ndi mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi Mdierekezi masiku makumi anai.” Marko 1:12 amati: “Pomwepo Mzimu anam’kangamiza kunka kuchipululu.” Mokondweretsa, chifukwa cha kukhulupirika kwa Yesu m’chipululu poyesedwa ndi Mdierekezi, iye sanataye mzimu woyera; iye sanaleka kukhala Mesiya kapena Kristu. Iye anatsimikizira kukhala wogwirizana ndi chimene ubatizo wake wa m’madzi unachitira chizindikiro.
31. Pambuyo pa kuikidwa m’ndende kwa Yohane, kodi Yesu anabwerera ku Galileya m’mphamvu yotani, ndipo kodi anachita chiani kumene’ko?
31 M’chaka cha 30 C.E. Yohane M’batizi, kalambule bwalo wa Yesu, anaikidwa m’ndende ndi Herode Antipa, wolamulira wa chigawo cha Galileya. Chotero Yesu anachoka ku Yudeya na dzera ku Samariya ndi kubwerera ku Galileya. Kunoko Yesu anagwiritsira ntchito kwa iye mwini Malemba amene iye akanadziwika nawo kukhala Mesiya kapena Kristu. (Mateyu 4:12-17) “Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira. Ndipo Iye anaphunzitsa m’masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.” (Luka 4:12-17) Kudzoza kwa Mulungu pa iye kunam’thandiza pamene anaphunsitsa anthu Malemba Oyera.
32. M’sunagoge wa m’Nazarete, kodi ndi ulosi wotani wa Yesaya umene Yesu anauwerenga mopfuula, ndipo kodi ndemanga yake inali yotani pamenepo?
32 Musunagoge ya tauni lakwao la Nazarete, Yesu anakumbutsa chenicheni chakuti iye anadzozedwa ndi Mulungu mokwaniritsa ulosi wa Yesaya 61:1-3 ponena za Mesiya. Ponena za zimene’zi timawerenga mu Luka 4:16-21, motere:
“Ndipo anadza ku Nazarete kumene analeredwa: ndipo tsiku la Sabata analowa m’sunagoge, monga anazolewera, naimiriramo kuwerenga m’kalata. Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m’mene Iye adafunyulula buku’lo, anapeza pomwe panalembedwa, Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: Anandituma Ine kulalikira am’singa mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenye’nso, kutulutsa ndi ufulu ophawanyika, kulakikira chaka chosankhika cha Ambuye. Ndipo m’mene Iye anapinda buku’lo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m’sunagogemo anam’yang’anitsa Iye. Ndipo anayamba kumena kwa iwo, kuti, Lero lembo iri lakwanitsidwa m’makutu anu.”
33. Kodi “Uthenga Wabwino” umene Yesu anapatsidwa kulengeza unali wonena za chiani, ndipo kodi iye anatumizidwa kukaulengeza mpaka kuti?
33 Ha, ndi njira yabwino kwambiri chotani nanga imene ulosi wa Yesaya unaneneratu kaamba ka Wodzozedwa wa Yehova! Ha, ndi mokondweretsa chotani nanga m’mene mphamvu yogwira ntchito ya Yehova imene iye anadzozedwa nayo inayenera kugwirira ntchito kupyolera mwa iye! M’kati monse mwa zaka zitatu zotsala za utumiki wake wa pa dziko lapansi Waumesiya iye mwachikondi anachita ntchito yolosera yochokera kwa Mulungu imene’yo. “Mbiri yabwino” imene iye analengeza kwa osauka inali uthenga wa ufumu wa Mulungu Waumesiya. Kwa khamu lanjala limene linafuna kum’gwira iye anati: “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi yina’nso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.”—Luka 4:43.
34. Kodi ndani amene anatsagana ndi Yesu pamene iye anamka nalalikira malo ndi malo?
34 Cholembedwa cha pambuyo pake chimatiuza kuti: “Katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye [atumwi] khumi ndi awiri’wo, ndi akazi ena amene anachiritsidwa mizimu yoipa ndi nthenda zao, ndiwo, Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye, ndi Yohane, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.”—Luka 8:1-3.
35. Kodi ndi motani m’mene Yesu anafutukulira ntchito yolalikira?
35 Si kokha kuti Yesu iye mwini analengeza mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu, koma iye anatumiza ophunzira ake kukachita kukalikira kofanana’ko. Pambuyo pa choposa chaka chimodzi cha kuphunzitsidwa ndi iye, ophunzira ake khumu ndi awiri anatumizidwa okha kukalalikira ufumu. Luka 9:1, 2, amatiuza kuti: “Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiri’wo nawa patsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda. Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.” Chaka chotsatirapo Yesu anaonjeza ena makumi asanu ndi awiri ku gulu lolalikira’lo: “Zitatha izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiri awiri pamaso pake ku mudzi uli wonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini. Ndipo ananena kwa iwo, Ndipo m’mudzi uli wonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwe’zi akupatsani; ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.”—Luka 10:1-9.
36. Kodi n’chiani chimene chinayenera kukhala kutseri kwa alaliki amene’wo pamene iwo anali kuchitira umboni pamaso pa akuluakulu olamulira, ndipo chotero kodi n’chifukwa ninji kulalikira Ufumu kwatsimikizira kukhala kosakhoza kuletsedwa m’mthawi yathu?
36 Mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu inali kutseri kwa Yesu wodzozedwa’yo m’kuchita kulalikira kwake. Inayenera’nso kukhala kutseri kwa alaliki amene’wa amene Yesu anawatumiza. Sukawagwiritsa mwala pamene iwo anaitanidwa pamaso pa akuluakulu olamulira. Yesu anati: “Musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.” (Mateyu 10:18-20; Luka 12:11, 12) Zimene’zi zinayenera kukhala choncho ponena za olalikira mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu ngakhale m’kati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu” alipo’wa. (Mateyu 24:3, 9-14) Chiri chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu uli kutseri kwa kulalikidwa kwa ufumu Waumesiya umene tsopano wakhazikitsidwa kumwamba m’manja mwa Mesiya Yesu kuti kulalikira’ko kwatsimikizira kukhala kosakhoza kuponderezedwa ndi anthu.—Marko 13:10-13.
37. Kodi ndi chochitika chotani chimene chikusimbidwa mu Luka 5:17-26 chosonyeza kuti mphamvu ya kuchiritsa ya Yesu sinafooketsedwe ndi chitsutso chachipembedzo?
37 Popeza kuti Yesu anakhala ndi kudzozedwa kwake, osati kuchokera kwa anthu, koma kuchokera kwa Atate wake wakumwamba, iye “anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi Mdierekezi pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.” (Machitidwe 10:38) Chitsutso chanjiru chochitidwa ndi atsogoleri achipembedzo sichinafooketse mphamvu imene inali kuchi titsa zozizwitsa. Ponena za chochitika chimodzi chapadera, kwalembedwa kuti: “Panali tsiku li—modzi la msiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo amene anachokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya [Yehova] inali ndi Iye yakuwachiritsa.” Mosasamala kanthu za mkhalidwe wa udani wa atsogoleri achipembedzo amene’wo Yesu anachiritsa wamanjenje wobvutika, ndipo anthu okondweretsedwa kwambiri’wo anati: “Lero taona zodabwitsa.”—Luka 5:17-26.
38. Kodi Yesu anapatsa yani thamo kaamba ka zozizwitsa zake, ndipo kodi iye anachenjeza otsutsa ake onyenga ponena za chimo lotani?
38 Kaamba ka machiritso ake ozizwitsa. Yesu anapereka thamo kwa Wowachititsa weniweni. Chotero, kwa awo amene anam’suliza za kukhala wogwirizana ndi Satana Mdierekezi, amene iwo anam’cha Beelzebule, mkulu wa ziwanda,” Yesu anati: “Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu.” Chifukwa cha chimene’cho, iye anachenjeza otsutsa’wo kuti “chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa . . . amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudza’yo.” Otsutsa’wo anali atachita chimo losakhululukidwa lotero’lo mwa kunena mwanjiru kuti chimene mwachionekere chinali chochita cha mzimu woyera wa Mulungu kukhala chochititsidwa ndi Mdierekezi.—Mateyu 12:24-32.
WOCHEDWA “MWANA WA MULUNGU MONGA MWA MZIMU”
39. Mosemphana ndi lingaliro lofala Lachiyuda, kodi n’chiani chimene Malemba ao Achihebri analengeza ponena za chokumana nacho cha Mesiya?
39 Kale’lo m’nthawi ya Yesu panali malingaliro olakwa onena za mtundu wa munthu umene Mesiya akakhala ndi njira imene yasonyezedwa kaamba ka iye. Otsutsa Yesu sanaone kuti kunalembedwa m’Malemba ao enieni Achihebri kuti Mesiya anayenera choyamba kubvutika monga mwa chifuniro cha Mulungu, ngakhale mpaka kufikira imfa. Monga wamkulu wa “mbeu” ya “mkazi” wa Mulungu, “chitende” chake chinayenera ‘kuzunzundidwa.’ (Genesis 3:15) Maulosi Achihebri atakwaniritsidwa m’nkhani imene’yi, mtumwi Petro anasonyeza chenicheni chimene’chi kwa khamu la Ayuda m’kachisi pa Yerusalemu kuti: “Zimene Mulungu analalikiratu m’kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Kristu, iye anakwaniritsa chotero.”—Machitidwe 3:18.
40. Kodi ndi mwa mau otani kwa atumwi ake Yesu anasonyeza kuti iye anadziwa kuti Mesiya anayenera kubvutika ndi kufa?
40 Kuchokera m’Malemba Achihebri Yesu anadziwa kuti Mesiya anayenera kubvutika ndi kufa. Ngakhale kuli kwakuti atumwi ake anam’zindikira kukhala Mesiya, iye anawadabwitsa mwa kuwauza kuti iye anayenera kubvutika ndi imfa yochititsa manyazi. Pamene mtumwi Petro anatsutsa lingaliro limene’lo, Yesu anati kwa iye: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa susamalira za Mulungu, koma za anthu” Kalambule bwalo wa Yesu, Yohane M’batizi anabvutitsidwa ndi adani ndi zimene iwo anafuna kum’chitira, Yesu anati, ndipo “choncho’nso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo.”—Mateyu 16:21-23, 17:12, 13.
41. M’zaka za zana loyamba C.E., kodi ndi motani m’mene mpingo wa ophunzira a Kristu unalingaliridwira chifukwa cha m’mene iye anafera?
41 Potsirizira pake Yesu anaphedwa monga wonenera mwano Mulungu ndi wochititsa anthu kupandukira Ufumu Wachiroma. Kumene’ku kunatsimikizira kukhala chopinga kwa Ayuda ndi Amitundu omwe, ponena zakulandira kwao Yesu monga Mesiya wolonjezedwa. Zoposa zaka makumi awiri mphambu zisanu pambuyo pake, Ayuda m’Roma anasonyesa mkhalidwe wao kulinga ku mpingo wa ophunzira a Yesu mwa kunena kwa mtumwi Paulo woikidwa m’ndende’yo kuti: “Za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponse ponse.”—Machitidwe 28:22.
42. Monga momwe kwasonyezedwera m’chochitika cha mtumwi Paulo, kodi n’chiani chofunika kwa Akristu kuchitsimikizira kuchokera m’Malemba ponena za Mesiya?
42 Chifukwa cha chimene’cho kunafikira kukhala kofunika kwa Akristu kutsimikizira kuti imfa ya Yesu pa mtengo wozunzirapo kunja kwa Yerusalemu, m’malo mwa kum’pangitsa kusakhala Mesiya wolonjezedwa wa m’Malemba Oyera, inatsimikizira kwenikweni kuti iye anali Mesiya weniweni, Kristu wa Mulungu. Mwa chitsanzo, tiyeni titenge chochitika cha mtumwi Paulo m’sunagoge pa Tesalonika, Makedoniya: “Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m’malembo, natanthauzira, natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndipo’nso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.” (Machitidwe 17:1-3) Zaka zina pambuyo pake, mtumwi Paulo anaimirira monga wandende pamaso pa bwanamkubwa Wachiroma Festo ndi mlendo mfumu Agripa kudzafotokoza mlandu wake. Pomaliza kudzikanira kwake iye anati:
“Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, kuwachitira umboni ang’ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika; kuti Kristu akamve zowawa, kuti Iye woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.”—Machitidwe 26:22, 23.
43. Kodi Paulo anakhala mboni ya chozizwitsa chotani cha Mulungu, ndipo kodi ndi motani m’mene Petro amasonyezera chifukwa chake chimene’chi chinali chozizwitsa cha Mulungu cha chikulu kopambana?
43 Paulo anakhala mboni ya chiukiriro, pamene iye molimba mtima analengeza pamaso pa Festo ndi Agripa. (Machitidwe 26:12-18) Ndipo’nso, mu 1 Akorinto 15:3-8, Paulo akuchitira umboni kuti, kutembenuka kwake kusanachitike, panali “abale oposa mazana asanu” amene anali mboni zoona ndi maso za chenicheni chakuti Yesu anali ataukitsidwa kuchokera kwa akufa. Chiukiriro cha Yesu Kristu chimene’chi kuchokera wa akufa pa tsiku lachitatu la imfa yake chinatsimikizira kukhala chozizwitsa cha Mulungu chachikulu kopambana. Koma Mulungu anali ndi mphamvu yaikulu kwambiri yakuti n’kuchichita. Kodi n’chifukwa ninji zinali choncho? Mtumwi Petro akusonyeza cifukwa chake, pamene iye akulemba kuti: “Kristu adafa kamodzi kwatha ponena za machimo, munthu wolungama kaamba ka osalungama, kuti akakutsogolereni kwa Mulungu, iye akumaphedwa m’thupi lanyama, koma akumakhalitsidwa ndi moyo mu mzimu. Mu mkhalidwe wotere’wu iye anapita’nso nalakikira mizimu yokhala m’ndende.”—1 Petro 3:18,19. NW.
44. Malinga ndi kunena kwa Petro, kodi Yesu anapangitsidwa kukhala wamoyo monga chiani?
44 Kodi Petro anatanthauzanji? Ichi: Chakuti Mulungu Wamphamvuyonse sanaukitse Yesu monga munthu wathupi koma anamuukitsa monga munthu wauzimu, munthu wosakhoza kubvunda kapena munthu wauzimu wosatheka kufa.
45, 46. (a) Pambuyo pa kutsika kwa mzimu wa Mulungu pa iye pa Mtsinje wa Yordano, kodi Yesu analengezedwa kukhala chiani? (b) Mwa chiukiriro chake kuchokera kwa akufa kodi Yesu analengezedwa kukhala Mwana wa Mulungu mogwirizana ndi chiani?
45 Thupi lanyama la Yesu linafesewa mu imfa, monga nsembe kuti Mulungu alifafanize. Chotero Yesu anaukitsidwira ku moyo wakumwamba wokhala ndi “thupi lauzimu,”laulemerero, lobvekedwa kusakhoza kufa, losadzafa’nso. (1 Akorinto 15:42-54) Kalekale, patsiku la kubatizidwa kwa Yesu m’madzi, Yehova Mulungu anam’bala mwa njira ya mzimu Wake woyera kuti akhale kuyambira pa nthawi imene’yo kumkabe m’tsogolo Mwana wa Mulungu wokhala ndi chiyembekezo cha cholowa chakumwamba. Kuti atsimikizire kubalidwa kwa Yesu Mulungu analankhula ali kumwamba, akumalengeza kuti Yesu wodzozedwa’yo anali Mwana Wake wauzimu wokondedwa ndi wobvomerezedwa. (Mateyu 3:13-17) Koma pa tsiku la chiukiriro cha Yesu ku imfa Mulungu anam’lenga kukhala Mwana wobadwa ndi mzimu kotheratu wa Mulungu. Ndicho chifukwa chake Paulo akulemba kuti:
46 “Uthenga Wabwino wa Mulungu, umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m’malembo oyera, wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi, amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero [motani?] ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu.”—Aroma 1:1-4.
47. Mu Aefeso 1:19-21, kodi ndi motani m’mene Paulo amanenera za ukulu wa chozizwitsa cha Mulungu m’kuukitsa Yesu?
47 Pochitira umboni ukulu wa chozizwitsa cha Yehova m’kuukitsa Yesu Kristu monga mzimu wosakhoza kufa, mtumwi Paulo akulemba’nso kuti: “Monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba, imene anachititsa mwa Kristu, m’mene anamuukitsa kwa akufa, nam’khazikitsa pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi alamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lochedwa, si m’nyengo yino ya pansi pano yokha, koma’nso mwa iyo ikudza”—Aefeso 1:19-21; Afilipi 2:5-11; 1 Petro 3:21, 22.
48. Kodi ndani amene ali “mkazi” wotanthauzidwa m’Genesis 3:15, ndipo mwa kuukitsa Yesu kodi ndi bala lotani limene Mulungu anapoletsa?
48 Mwa kuchita chiukiriro chodabwitsa cha Yesu Kristu chimene’chi, Singa’anga wakumwamba, Yehova, anachiritsa bala limene Chinjoka Chachikulu’cho, Satana Mdierekezi, chinalichititsa pa “chitende” cha “mbeu” ya “mkazi” mwa njira ya gulu lake loipa la pa dziko lapansi. (Genesis 3:15) “Mkazi” m’chinsinsi cha Mulungu chimene’chi anali, osati Hava wochimwa’yo kapena namwali wosakhudzidwa Wachiyuda Mariya, koma gulu longa mkazi lakumwamba la Mulungu lopangidwa ndi zolengedwa zoyera zauzimu. Gulu limene’lo linapereka Mwana wo badwa yekha wa Mulungu kaamba ka utumiki pano pa dziko lapansi monga Mesiya wolonjezedwa.—Yerekezerani ndi Agalatiya 4:25, 26.
49, 50. Kodi Wamkulu wa “mbeu” ya “mkazi” wa Mulungu tsopano ali wokhoza kuchita chiani, ndipo kodi ndi zinthu zotani zimene ife tikululutira zimene ziyenera kudza kupyolera mwa iye?
49 Wamkulu wa “mbeu” ya “mkazi” wa Mulungu tsopano ali wokhoza kuzunzunda Chinjoka Chachikulu’cho, Satana Mdierekezi, mutu ndi kuchiphawanya ndi “mbeu” yake yonse. Ife, kaya ndife Ayuda kapena Amitundu, sitifunikira’nso kuyembekezera kudza kwa Mesiya m’thupi ku dziko lathu lapansi’li. Iye anadza ndi kukwaniritsa ntchito yake pa lapansi m’zaka za zana loyamba za Nyengo yathu Ino. (1 Yohane 4:2; 2 Yohane 7) Tsopano iye akupfupidwa ndi ulemerero kumwamba. Iye ali Mesiya kapena Kristu wauzimu, wokhoza kuchita zochuluka kwambiri koposa Mesiya kapena Kristu wapadziko lapansi waumunthu.
50 Ulemerero wonse upite kwa Yehova Mulungu, amene anadzoza Mwana wake Yesu “ndi mzimu woyera ndi mphamvu” kuti akhale Mesiya wamtengo wapatali: Onse alulutiretu madalitso akulu osatha amene alonjezedwa kudza kwa anthu onse kupyolera mwa Mesiya wauzimu wolemekezedwa’yo, Kristu wa Mulungu!—Machitidwe 10:38; Genesis 22:18.