Mutu 8
“Mzimu wa Moyo Wochokera kwa Mulungu Unawalowera”
1. Malinga ndi kunena kwa mau a Yesu m’Mateyu 28:18-20, kodi ndi ntchito yapadera yotani ya mzimu woyera imene idzalekeka posachedwapa?
NTCHITO yapadera ya mzimu woyera wa Mulungu yakhala ikuchitika tsopano kwa zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai ndipo iyenera kulekeka posachedwapa. Pamene ileka, pamenepo kupangidwa kwa ophunzira a Mesiya Yesu kudzalekeka. Mwana wa Mulungu woukitsidwa’yo anasonyeza chimene’chi pamene, pa phiri la m’chigawo Chachiroma cha Galileya, iye ananena kwa atumwi ake kuti: “Ulamuliro wonse wapatsidwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi. Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, mukumawabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi mzimu woyera, mukumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse ndakulamulirani. Ndipo onani! ndiri nanu masiku onse kufikira mapeto a dongosolo la zinthu.”—Mateyu 28:18-20, NW.
2. Kuphatikiza pa Yesu Kristu wolemekezedwa’yo, kodi n’chiani’nso chimene chinayenera kukhala ndi ophunzira ake kufikira “mapeto a dongosolo la zinthu”?
2 Atumwi amene’wo anali odziwa bwino kwambiri mzimu woyera umene’wo umene m’dzina lake iwo analamulidwa kubatiza awo onse okhala ophunzira a Kristu ochokera m’mitundu yonse. M’kati mwa zaka zao za chigwirizano cha thithithi ndi Mbuye wao Yesu, iwo anaona kugwira kwake ntchito mwamphamvu kupyolera mwa iye m’kulalikira Ufumu, kuphunzitsa ndi kuchita zozizwitsa. (Machitidwe 10:38) Pa usiku wa Paskha wao wotsirizira limodzi naye pa Nisan 14, 33 C.E., kaamba ka chitinthozo chao iye anati kwa iwo: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko silingathe kum’landira.” (Yohane 14:16, 17) Chotero, si kokha kuti Yesu Kristu woukitsidwa ndi wolemekezedwa’yo akakhala ndi ophunzira ake kufikira “mapeto a dongosolo la zinthu,” koma nkhoswe yao yogwira ntchito, mzimu woyera, mofananamo ikakhala nao kufikira pa nthawi’yo, pakuti akakhala nao “ku nthawi yonse.”
3, 4. (a) Kodi n’chifukwa ninji funso likufunsidwa ponena zakuti kaya Yesu Kristu wakhala ali ndi Chikristu cha Dziko masiku onse kufikira tsopano. (b) Kodi Yesu ananena kuti n’chiani chimene chiri chinthu chotsimikiziritsa kaya ngati mzimu woyera unali ndi odzicha kukhala Akristu’wo.?
3 Zimene’zo zikutikondweretsa lero lino! Pano tiri m’nyengo ya nthawi imene’yo yochedwa “mapeto a dongosolo la zinthu.” (Mateyu 24:3) Chiyambire pa kuulika kwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko mu 1914 zochitika m’dziko kudza’nso pakati pa ophunzira a Kristu zikukwaniritsa zimene Yesu anazineneratu monga momwe unasonyezedwera m’Mateyu 24:3 kufikira 25:46 (Ndipo’nso Marko 13:3-37; Luka 21:7-36) Yesu Kristu, pochita “ulamuliro wonse” kumwamba ndi dziko lapansi, wakhala ali ndi ophuzira ake “masiku onse” kufikira tsopano. “Nkhoswe” yolonjezedwa’yo, mzimu woyera, wakhala nawo’nso. Koma masiku ano ambiri amanena kukhala ophunzira a Kristu kapena Akristu. Malinga ndi ziwerengero zofalitsidwa pasachedwapa, Chikristu cha Dziko chiri ndi ziwalo za chalichi zoposa mamiliyoni mazana asanu ndi anai. Chifukwa cha chimene’cho, kodi tiyenera kuyang’ana ku Chikristu cha Dziko kaamba ka umboni wakukhala pafupi nawo kwa Kristu? Kodi mzimu woyera wagwira ntchito mwa icho?
4 Chabwino, kodi m’nkhani imene’yi funso liyenera kuyankhidwa kokha mogwirizana ndi chiwerengero cha awo amene amadzicha kukhala Akristu? Ai, pakuti Yesu anati chinthu chotsimikiziritsa ndicho ntchito zabwino:
“Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Mtengo uli wonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.
“Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchita’yo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.”—Mateyu 7:16-21.
5. Kodi Chikristu cha Dziko lero lino chiri chochuluka “zipatso za mzimu” kapena “ntchito za thupi”!
5 Kuyambira pa nthawi imene Chikristu cha Dziko chinakhazikitsidwa m’zaka za zana lachinai C.E. ndi mfumu yosabatizidwa yachikunja Yachiroma, Kostantini Wamkulu, zipatso zake sizinakhale zabwino. Pambuyo pa zaka mazana khumi andi asanu ndi limodzi za mwai wakukulitsa “zipatso za mzimu,” gulu lake lachipembedzo siliri lochuluka mu “chikondi, chisangalalo, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” M’malo mwake, “ntchito za thupi” zimasonyeza Chikristu cha Dziko.—Agalatiya 5:19-23.
6, 7. Kodi Chikristu cha Dziko chiri chofanana m’mbali zotani ndi mpingo wa mu Laodikaya, ndipo kodi icho chalapa ndi kulabadira chilangizo cha Yesu cha mpingo umene’wo?
6 Kuonjezerekaonjezereka kwa ziwalo zachalichi, za Chikristu cha Dziko, lero lino kuli kofanana ndi kwa “mpingo wa ku Laodikaya.” M’Chibvumbulutso 3:14-18, Yesu Kristu wolemekezedwa’yo ku mpingo’wo akuti:
“Ndidziwa nchito zako, kuti suli wozizira kapene wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapene wotentha. Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula m’kamwa mwanga. Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndiri nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, wakhungu, ndi wausiwa; ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyengeka m’moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukadzibveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m’maso mwako, kuti ukaone.”
7 Kodi Chikristu cha Dziko chalapa ndi kulandira chilangizo chochokera kwa Kristu chotero’cho? Kachitidwe kake kokangalika m’mkhondo ziwiri za dziko, kuzunza kwake magulu achipembedzo a anthu ochepa, kukondetsa kwake zinthu zakuthupi, chimasomaso chake, kulowerera kwake m’ndale za dziko m’malo mwakuti chilamulire ndi kupitirizabe dongosolo lakale la zinthu liripo’li zonse’zi ndi zinthu zina zambiri zimayankha kuti Ai!
8. Kodi n’chifukwa ninji Yesu wolemekezedwa’yo ali woyenerera, kunena kwake titero, kulabvula m’kamwa mwake Chikristu cha Dziko ndi kusachigwiritsira ntchito m’ntchito ya lero lino?
8 M’kati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu,” Yesu Kristu analibe njira ina yoti atenge koma ‘kum’labvula’ m’kamwa mwake. Mwauzimu, iye sali wozizira mokondweretsa kapena wotentha mosonkhezera kwa iye. Iye sangathe kuchimeza kotero kuti achipangitse kukhala chopindulitsa kwa iye. Icho chiri ‘chofunda’ m’kudzinenera molakwa kukhala Chachikristu ndipo pa nthawi imodzimodzi’yo chikumadzipangitsa kukhala bwenzi ndi chipangizo cha dziko iri. Chimene’chi Mfumu yolamulira’yo Yesu Kristu sangachisunge m’mimba. Iye anachizindikira kukhala mdani wa Mulungu Atate wake. (Yakobo 4:4) Iye samagwirizana ndi adani a Atate wake. Icho sichiri naye m’paradaiso wauzimu. Chotero iye sangachigwiritsire ntchito m’ntchito imene iye anaineneratu kaamba ka ophunzira ake enieni pa nthawi ino.—Mateyu 24:14.
9. Chifukwa cha kuchita ntchito zake m’dzina lachipembedzo, kodi Chikristu cha Dziko chinadzipanga kukhala chodedwa m’mitundu yonse, kapena kodi icho chinalunjikitsa udani umene’wo kwa yani?
9 Chikristu cha Dziko chachita ntchito zake ndi kupitirizabe zochita zake m’dzina la chipembedzo. Kodi ntchito zimene’zi zachipangitsa kukhala ‘chodedwa ndi mitundu yonse chifukwa cha dzina langa [la Kristu]’? (Mateyu 24:9) Mosemphana ndi zimene’zo, icho chatsogolera m’kupangitsa ena kukhala odedwa motero. Ndani? Mbiri yamakono ikuwasonyeza. M’kati mwa NkhondoYoyamba ya Dziko panali kagulu ka m’mitundu yonse ka ophunzira Baibulo kamene kanali kusonyeza kuchokera m’Malemba ouziridwa kuti “nthawi za Akunja” zinatha m’chaka chimene Nkhondo Yoyamba inaulika—1914. (Luka 21:24, Authorized Version) Chotero mitundu yonse, iyo yodzicha kukhala Yachikristu ndi iyo yosatero, inayenera kuonongedwa kaamba ka kutsutsa kwao ufumu wokhazikitsidwa’wo wa Yesu Kristu, Mfumu imene tsopano ikulamulira kumwamba pa dzanja lamanja la Mulungu. Awo onse ofuna kupulumuka chionongeko limodzi ndi Chikristu cha Dziko afunikira kutuluka m’Chikristu cha pakamwa pokha, kutuluka m’machalichi a Chikristu cha Dziko. Ziphunzitso zolimba mtima zotero’zo zochitidwa ndi ophunzira Baibulo mosamalitsa zinaputa udani wa pa dziko lonse kwa iwo.
10. M’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko kodi Chikristu cha Dziko chinali ndi cholinga cha kufafaniza kagulu kachipembedzo kati, ndipo mwa njira ya chiani?
10 Gulu lachipembedzo la ochepa lodedwa limene’li linapangidwa ndi Akristu odziwidwa monga Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse. M’ntchito yao ya kuphunzitsa Baibulo ndi kulengeza iwo anagwiritsira ntchito mabukhu a Watch Tower Bible and Tract Society, imene malikulu ake ali mu Brooklyn, New York. Pa ophunzira Baibulo amene’wa Chikristu cha Dziko chinalunjikitsapo moto wake m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko. Icho chinatsimikiza kuzifafaniza. Atsogoleri ake achipembedzo monyenga anazineneza ndi kupambana magulu a ndale za dziko ndi a chiweruzo a dziko lino kutenga njira zowatsendereza.
11. Kodi n’chifukwa ninji Watch Tower Bible and Tract Society inanenezedwa kukhala ndi liwongo?
11 Kuletsedwa kwa mabuku a Watch Tower Bible and Tract Society kunatsatirapo. M’maiko osiyanasiyana malamulo otsutsana ndi Ophunzira Baibulo anapangidwa. M’malo ena unzika wokonda dziko unasonkhezeredwa mpaka kufika pa kukolezeredwa kukhala kachitidwe ka chiwawa motsutsana ndi kagulu ka mtendere konamiziridwa kamene’ka. M’ngululu ya 1918 amuna apadera amene anagwirizanitsidwa ndi malikulu a pa Brooklyn a Sosaite anatengeredwa ku ndende m’ndende yachibalo, monamiziridwa!
12. Kodi n’chiani chimene Chibvumbulutso 11:7-12 chimasonyeza ponena zakuti kaya Chikristu cha Dziko chinapha koteheratu ntchito ya mboni?
12 Tsopano prezidenti ndi mlembi ndi wosunga chuma a Watch Tower Bible nad Tract Society ndi antchito ena anzao asanu ndi mmodzi odziwika pokhala ataikidwa m’ndende monga ngati apandu, Chikristu cha Dziko chinalingalira kuti chapha gulu la mboni zokhulupirika za ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu wokhala m’manja mwa Yesu Kristu. Koma kodi nkhonya yakupha’yo inaponyedwa? Kwa kanthawi mitembo ya mboni za Ufumu’zo inaonekera kukhala yakufa’di. Koma kodi izo zinakhala zosagwira ntchito kosatha? Kanenedwe kophiphiritsira ka Chibvumbulutso 11:7-12 kamayankha kuti:
“Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chirombo chokwera kutulika m’phompho chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo. Ndio mitembo yao idzakhala pa khwalala la mudzi waukulu, umene uchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Aigupto, pamenepo’nso Ambuye wao anapachikidwa. Ndipo mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lake, osalola mitembo yao iikidwe m’manda. Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.
“Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chiriri; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya. Ndipo anamva mau akulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kumka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.”
13. Mwa lingaliro la Chikristu cha Dziko, kodi n’chiani chimene chinali m’tsogolo mwa gulu la mboni’lo, koma kodi ndi mphamvu yotani imene icho sichinailingalire?
13 Kwa kanthawi, kofanana ndi masiku atatu ndi theka, gulu la olengeza maulosi a Baibulo ndi mboni za ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu linali mu mkhalidwe wochititsa manyazi pamaso pa anthu onse. Anthu amene anazunzidwa ndi kulakikira zoona za Baibulo anasangalala ndi kuponderezedwa kwa mboni za Ufumu’wo. Mwa lingaliro la Chikristu cha Dziko, gulu la mboni linali ‘lakufa.’ Koma kodi mzimu wa Mulungu una unaonongedwa, unaphedwa? Sunatsimikizire kukhala wakufa pamene mtembo wa Yesu Kristu wopachikidwa’yo unali gone m’manda kwa mbali za masiku atatu. Chotero, zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai pambuyo pake, sunatsimikizire kukhala ‘wakufa’ pambuyo pa kufa kwa gulu la mboni za Ufumu “masiku atatu ndi nusu,” kunena moyerekezera.
14. Kuti Mateyu 24:14 akwaniritsidwe, kodi n’chiani chimene chinali chofunika, ndipo kodi n’chiani chimene chinachitika m’ngululu ya 1919?
14 Nthawi tsopano inali itafika m’chaka chachisanu cha “mapeto a dongosolo la zinthu.” Kuneneratu kwa Yesu, m’Mateyu 24:14 NW, kunayenera kukwaniritsidwabe: “Mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Chikristu cha Dziko, chokhala ndi mawanga a mwazi wa nkhondo ya dziko, sichinali choyenera kapena choyera mokwanira kukwaniritsa ulosi umene’wo. Kodi, nangano, n’chiani chimene chinalipo choti chichitidwe? Mzimu wa Mulungu Wamphamvuyonse unayenera kuyamba kugwira ntchito. Uwo unatero, osati kuchirira Chikristu cha Dziko chokhala ndi liwongo la mwazi’cho, koma m’malo mwa mboni za Ufumu zoonekera kukhala ngati ‘zakufa’zo.’ Mogwirizana ndi chithunzithunzi cha m’Chibvumbulutso 11:11, “mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chiriri.” Ngululu ya chaka cha pambuyo pa nkhondo cha 1919 inali nthawi ya kuwapatsa‘nso mphamvu.
15. Kodi ndani amene anayamba kugwira ntchito atamasulidwa, ndipo kodi ndi chisamaliro chotani chimene chinaperekedwa chatsopano ku Mateyu 24:14?
15 Modabwitsa, kumapeto kwa March 1919, akuluakulu a Watch Tower Bible and Tract Society ndi andende anzao anamasulidwa atapereka ndalama za chikole ndipo anayamba kugwira ntchito. Ulosi wa Yesu m’Mateyu 24:14 unakhala ndi chisamaliro chatsopano. Mau odabwitsa ananenedwa ponena za uwo m’kope la Nsanja ya Olonda (Yachingelezi) ya July 1, 1920, tsamba 199, 200. Linasonyeza bwino lomwe kuti kulalikira pa dziko lonse konenedweratu’ko sikunali kulalikira kochitidwa m’kati mwa zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo za “Nyengo ya Uthenga Wabwino, konena za ufumu ulinkudza. Kunali kulalikira konena za ufumu wokhazikitsidwa kale. Chotero kulalikira’ko kunali ntchito yolengeza yoti ichitidwe kuyambira mu 1914 C.E. kumkabe m’tsogolo.
16. Kodi ndi motani m’mene bvumbulutso limene’lo linayambukirira mboni’zo ndipo kodi chaka cha 1919 chinatsirizidwa ndi chochitika chotani?
16 Bvumbulutso lochitidwa ndi “mzimu wa choonadi” limene’li linaika moyo watsopano m’kulalikira Ufumu kwa mboni’zo. Monga mapeto akulu a 1919, chaka cha kupatsidwa’nso nyonga, msonkhano wa onse wa pambuyo pa nkhondo woyamba wa mboni za Ufumu’wo ukanachitidwa kwa masiku asanu ndi atatu pa Cedar Point, Ohio. Zikwi zikwi zochokera ku United States ndi Canada zinafikapo. Prezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, amene tsopano anachotseredwa zinenezo zonama za pambuyo pa nkhondo, analengeza ntchito yatsopano ya Ufumu patsogolo. Iye anakambira nkhani omvetsera okwanira 7,000.
17. Kodi panali chifukwa chotani kwa adani’wo choopera kukwezedwa kwa mboni’zo kuchokera ku mkhalidwe wakufa?
17 Pa kudzutsidwa’nso kodabwitsa kwa mboni za ufumu wokhazikitsidwa’wo, mantha akulu anagwera adani onse a Ufumu’wo, maka-maka pa Chikristu cha Dziko. Ngati adani’wo anali ndi chifukwa chochitira mantha pa nthawi’yo, ngakhale kuli kwakuti mboni za Ufumu’zo zinali otsalira apang’ono, iwo anali ndi chifukwa chachikulu koposa choopera pambuyo pake. Mboni zimene’zo zinayenera kupatsidwa kuchuka kwa pa dziko lonse kumene sikunaperekedwe kwa ophunzira a Kristu pa nthawi iri yonse yakale yolongosoledwa. Iwo anakodoledwera ku kuchuka kwapamwamba kwambiri monga ngati ndi mau akulu ochokera kumwamba, akunena kwa iwo kuti: “Kwerani kuno.”
18. Kodi ndi motani m’mene mu 1922 mboni’zo zinasonyezera kuti sizinabwerere m’mbuyo pa ntchito imene inayenera kupereka kudziwika kwa pa dziko lonse?
18 Iwo sanaleke kulowa m’kulengeza Ufumu kumene kunayenera kuwakwezera ku kuchuka kwa poyera kwapamwambamwamba. Posonkhezeredwa ndi mzimu wopatsa nyonga wa Mulungu, iwo mopanda mantha anayamba ntchito. Kutenthedwa maganizo kunaonjezeka pa mzonkhano wa onse wachiwiri mu Ceder Point, Ohio, mu 1922, pamene prezidenti wa Watch Tower Society anafika pa chimake pa nkhani yake yapadera ndi mau onenedwa mwamphamvu akuti, “Lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake”! Zikwizikwi za osonkhana’wo zinabvomereza mokondwera kwambiri chiitano champhamvu cha kulalikira Ufumu kufikira mapeto chimene’chi!
NTHAWI YOYENERA KAAMBA KA KUCHITIRA UMBONI UFUMU KWA PA DZIKO LONSE
19. Kodi n’chifukwa ninji cholembedwa cha m’Chibvumbulutso 11:15-18 chinali choyenerera kwa Yohane kuchipereka pambuyo pa cholembedwa chake chonena za kupatsidwa’nso moyo kwa mboni’zo?
19 Kunali kaamba ka kulalikira Ufumu kwa pa dziko lonse kotero’ko kuti “mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu” unaowa mwa mboni zoponderezedwa mu 1919 C.E. Moyenerera kwambiri, pamenepa, mtumwi Yohane mwamsanga akutsataniza cholembedwa chake chonena za mboni ziwiri zokwezedwa’so ndi cholembedwa chotsatirapo’chi:
“Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba, ndipo panakhala mau akulu m’Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.
“Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu, nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu. Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneri’wo ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.”—Chibvumbulutso 11:15-18.
20. (a) Kodi chilengezo chopfuula chimene’cho chinali mbiri ya kumwamba kokha? (b) Polingalira kuneneratu kwa Yesu, kodi tsopano panabuka chofunika kaamba ka yani?
20 Chilengezo choperekedwa mopfuula chimene’cho chakuti, “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi,” chiyenera kubwerezedwa’nso tsopano pa dziko lapansi ndi mboni zodzozedwa za Yehova. Iye anatenga ufumu wake wa dziko lapansi pa mapeto a thawi za Akunja mu 1914. Umene’wu unakhala mbiri osati ya kumwamba kokha. Inalowetsamo dziko la mtundu wa anthu. Iwo anayenera kuimva bwanji popanda olalikira, olengeza? Yesu ananeneratu kuti ikalalikidwa pa dziko lonse lapansi mapeto a dongosolo iri la zinthu asanadze. Otsalira a ophunzira ake odzozedwa anali anthu amene anapatsidwa ntchito ya kuchita kulalikira’ko kuyambira pa kukhalitsidwa’nso moyo kwauzimu mu 1919 kumkabe m’tsogolo.—Mateyu 24:14, NW; Marko 13:14, 15; Aroma 10:14, 15; onani Yesaya 32:15.
21. Kodi n’chifukwa ninji ophunzira odzozedwa a Yesu sali odzitukumula m’kuchita kulalikira Ufumu, monga momwe Chikristu cha Dziko chinganenere, ndipo kodi n’chifukwa ninji Zekariya 4:6 ayenera kukhala woona ponena za iwo?
21 Otsalira a ophunzira odzozedwa a Yesu Kristu ndiwo amene anatumidwa ndi kutumizidwa kukalalikira. (Yesaya 61:1-3) Ngati Chikristu cha Dziko chiwatsutsa kuti iwo ali odzitukumula m’kuchita kulalikira Ufumu kumene’ku, nanga kodi n’chifukwa ninji Chikristu cha Dziko chenicheni’cho sichimalakikira? Koma icho sichikutero. Icho chimakhala ndi phande m’ndale za dziko za m’dziko ndipo chimapereka dalitso lake ku Mitundu Yogwirizana yosakhala Yachikristu. Popeza kuti otsalira ali ochepa kwambiri poyerekezera ndi mamiliyoni mazana ochuluka a ziwalo za chalichi za Chikristu cha Dziko, kuyenera kukhala koona ponena za otsalira odzozedwa monga momwe Yehova ananenera mu Zekariya 4:6 kuti: “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga.”
22. Titatsimikizira ndi kulalikira Ufumu kumene kukuchitidwa, kodi ndani amene ali anthu pa amene Yoweli 2:28, 29 wakwaniritsidwapo?
22 Mzimu woyera, umene Yehova anauneneratu kuti adzautsanulira m’masiku otsiriza, sunaleka kugwira ntchito, pakuti otsalira akupitirizabe kubatiza ophunzira a Kristu m’dzina la mzimu umene’wo. (Mateyu 28:19, 20; Yoweli 2:28, 29; Machitidwe 2:14-21) Chifuno cholengezedwa’cho kutseri kwa kutsanulira kwa Mulungu mzimu wake pa thupi liri lonse chinali chakuti oulandira’wo pa nthawi’yo anenere. Maumboni akutsimikizira kuti otsalira a ophunzira odzozedwa a Kristu akhala akuchita kunerera kumene’ko ku mitundu yonse kaamba ka umboni mochirikiza ufumu wa Mulungu. Moyenera, pamenepa, iwo ayenera kukhala anthu amene atsanuliridwa kwenikweni mzimu wa Mulungu. Mzimu umene’wo uli kutseri kwa kulalikira kwao kwa pa dziko lonse. Kodi n’kutsutsiranji zimene’zi.
23. M’kati mwa zaka khumi ndi ziwiri zotsatirapo za kunenera kotero’ko, kodi ndi kuchitira umboni yani kumene kunaperekedwa, ndipo kodi n’chifukwa ninji umene’wu unali wofunika?
23 Pambuyo pa zaka khumi ndi ziwiri za kunenera kumene’ko ponena za ufumu wa Mulungu, otsalira odzozedwa anakhala odziwa bwino kwambiri Yehova Mulungu, Magwero a kumwamba a mzimu wotsanulidwa’wo. Iwo anali ataonjezera kuchitira kwao umboni ponena za iye ndipo anachititsa dzina lake kulengezedwa kukhala Dzina lakikulu kopambana m’chilengedwe chonse. Iwo anadzisonyeza kwenikweni kukhala mboni Zake ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi kukhala kwao “anthu kaamba ka dzina lake.” (Yesaya 43:10-12; Machitidwe 15:14, NW) Tiyeni tisanyozetse kufunika ndi kukhala kwa pa nthawi yake kwa kuchitira umboniYehova kudza’nso Mesiya wake Yesu. Mogwirizana ndi ulosi wa Yoweli 2:28-32 kunayenera kuyambirira lisanadze “tsiku la Yehova lalikuli ndi loopsya.” Ngati anthu akadapanda kuuzidwa, sakanatha kuitanira pa munthu woyenera kaamba ka chipulumutso m’kati mwa “tsiku” limene’lo. Yoweli 2:32 akutilangiza kuti ali yense amene “adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” Umboni wa kwa Yehova
24. Mu 1931 kodi ndi dzina latsopano lotani limene otsalira odzozedwa anadzitengera, ndipo kodi n’chifukwa ninji chimene’chi sichinali chizindikiro cha kungokhala osagwira ntchito?
24 Chotero sanali malunji chabe kuti pa Sande, July 26, 1931, pa msokhano wa m’mitundu yonse wa Gulu la Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse pa Columbus, Ohio, odzera msonkhano zikwi mazana ambiri’wo ndi mtima wonse anadzilandirira chilengezo cha kuchedwa dzina Lamalemba ndi latanthauzo. Dzina limene odzera msonkhano’wo analitenga mwa kubvomereza Chilengezo’cho linali “Mboni za Yehova.” Pambuyo pa kachitidwe kotengedwa pa msonkhano wa mitundu yonse m’Columbus, mipingo ya Gulu la Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse pa dziko lonse lapansi inabvomereza chilengezo chofanana’cho. Mwa njira imene’yo iwo anadzilengeza kukhala Mboni za Yehova. Chimene’chi sichinali chizindikiro cha kukhala osagwira nchito ku mbali ya otsalira odzozedwa a Aisrayeli auzimu. Mwa kuchita mathayo amene dzina’lo limaika pa iwo, iwo akhala mogwirizana ndi dzina lao latsopano limene’li.
25. Kodi ndi motani m’mene mboni za Ufumu zopatsidwa’nso moyo’zo zakwezedwera pa malo a ntchito apadera mogwirizana ndi dzina laumulungu’lo ndipo limodzi ndi kulandiridwa kwa thayo la pa Yesya 43:10-12?
25 Mosatsutsika, “mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu” unali utalowa mwa otsalira odzozedwa ndipo iye anawaitanira ku malo apadera pamaso pa adani ao onse. Mosaopa adani amene’wo, iwo analabadira chiitano cha Mulungu chakuti, “Kwenani kuno.” (Chibvumbulutso 11:11, 12) Iwo sanachite manyazi ndi kukhala ndi dzina laumulungu’lo dzina lopatulika kopambana. Kulalikira ndi kunenera kwao ku nyumba ndi nyumba ndi ku mzinda ndi mzinda kwa dzina limene’lo kunachititsa kukuzidwa kwa dzina limenelo pa dziko lonse lapansi. Pano potsirizira pake pali ochirikiza amakono a dzina lalikulu kopamana m’chilengedwe chonse! N’zachisoni kuti, mtundu wakale wa Israyeli wakuthupi unalephera kukhala chimene ulosi wa Yesaya 43:10-12 unanena, choyamba, kwa iwo kuti: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.” Chotero otsalira amakono Aisrayeli auzimu mokondwa amalandira thayo la kukhala Mboni za Yehova.
26. Kodi ndi mu mkhalidwe wauzimu wotani monga momwe wasonyezedwera ndi wa mu mpingo wa Sarde, Asia Minor, mu umene otsalira opatsidwa’nso mphamvu’wo sakufuna kulowamo?
26 Tsopano popeza kuti otsalira a Aisrayeli auzumu apatsidwa’nso mphamvu ndi “mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu,” iwo samafuna kulowa mu mkhalidwe umene unasonyezedwa ndi mpingo wa m’Sarde, Asia Minor. Yesu anati kwa uwo:
“Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa. Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira, zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga. Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvano; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidza pa iwe.”—Chibvumbulutso 3:1-3.
27. Kodi otsalira odzozedwa a Aisrayeli auzimu amalabadira mau a Yesu a m’Chibvumbulutso 2:5 kuti asataye mwai wotani?
27 M’dziko lodetsedwa mwachipembedzo lino otsalira a Aisrayeli auzimu afuna kuwala ngati zounikira, akumaunikira pa dzina la Mulungu ndi pa zifuno zake za kupulumutsa mtundu wa anthu. Iwo ali odikira kuti asataye mwai wa kukhala, monga gulu, choikapo nyale chauzimu. Iwo amalabadira mau a Yesu Kristu wolemekezedwa’yo ku mpingo wina wa mu Efeso wakale akuti:
“Nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.”—Chibvumbulutso 2:5.
“KHAMU LALIKULU” LIMAITANIRA PA DZINA’LO
28. M’kati mwa Nkhondo Yachiwiri ya Dziko, pamene chirombo chotuluka m’phompho kachiwiri’nso chinachita nkhondo ndi otsalira odzozedwa, kodi n’chifukwa ninji chokumana nacho chao m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Ddziko sichinadzibwereze?
28 Mu 1939-1945 C.E. nkhondo yachiwiri ya dziko inadzetsa chipasuko pa mtundu wa anthu. Koma kodi chokumana nacho cha m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko chinachitika’nso ponena za otsalira a Aisrayeli auzimu opatsidwa’nso moyo, amene, chiyambire 1931, akhala akuchedwa Mboni za Yehova’ wo? Mosasamala kanthu za chizunzo chachipembedzo choipitsitsa m’kati wa Nkhondo Yachiwiri ya Dziko, pamene “chirombo chakutuluka m’phompho” kachiwiri’nso chinachita nkhondo ndi otsalira, zolembedwa zikuyankha kuti Ai! Chizunzo chachiwawa sichinapmbane m’kuletsa kuchitira umboni Ufumu kochitidwa ndi otsalira odzdozedwa’wo. Iwo anapitirizabe “kudzazidwa ndi mzimu” wochokera kwa Wopatsa Moyo wao wakumwamba. (Aefeso 5:18, NW) Iwo anapitirizabe kukhala ndi moyo mwauzimu mwa kugwira ntchito m’kuchitira umboni Ufumu, mobisa, ngati nkofunika. Pamene analetsedwa ndi maboma a ndale za dziko ndi okhala ndi magulu ankhondo kulalikira mbiri yabwino yonena za ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa’wo, iwo anapemphera kwa iye kaamba ka kulimba mtima kuti apitirizebe mokhulupirika m’kukwaniritsa ntchito yao ya kulalikira.
29. Kodi ndi motani m’mene chotulukapo cha zapita’zo kwa otsalira chakhalira chofanana ndi chochitika chosimbidwa m’Machitidwe 4:31?
29 Chotulukapo kwa iwo chinali chofanana ndi cha m’chochitika cha mpingo wa Yerusalemu, atumwi ataletsedwa ndi akuluakulu achipembedzo kuleka kulalikira Kristu. “Ndipo anadzazidwa onse ndi MzimuWoyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.” (Machitidwe 4:31) Mofananamo, kufikira lero lino, otsalira amasonyeza kukhala kwao odzazidwa ndi mzimu woyera ndipo mwamphamvu amapitirizabe ‘kulankhula mau a Mulungu molimbika mtima.’ Chifukwa cha chimene’cho, “choikapo nyali” cha otsalira sichinachotsedwe pa malo ake.
30. (a) Kodi otsalira odzozedwa amachitanji ndi dzina la Mulungu? (b) Kodi n’chifukwa ninji, polingalira Chibvumbulutso 6:14-17, pali chifukwa chakuti anthu afunsire kaya ngati otsalira ndiwo okha okhosa “kupulumuka” pa tsiku la Yehova?
30 Otsatira odzdozedwa iwo eni’wo ‘amaitainira pa dzina la Yehova’ ndi kulilengeza pa dziko lonse. Komabe, kodi iwo ndiwo okha lero lino amene akuyembekezera “kupulumuka” m’kati mwa “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsya”? (Yoweli 2:31, 32) Limene’li ndiro funso limene ambiri amene Sali otsatira akakonda kuti liyankhidwe, pakuti ponena za “tsiku loopsya” limene’lo Chibvumbulitso 6:14-17 chimati:
“Ndipo kumwamba [maboma a ndale za dziko okwezeka olamulira anthu] kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m’malo mwao. Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe, a mapiri; nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa; chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?”
31. (a) Kodi n’chiani chimene chiri yankho la funso lonena za anthu olongosoledwa pamwambapo’wo ponena za kupulumuka bwino lomwe pa tsiku la Yehova? (b) Kodi ndani amene samagwirizana ndi mafumu a dziko lapansi ndi ogwirizana nawo ao m’kufuulira chitetezo cha pa dziko lapansi?
31 Yankho la funso’lo lonena za onse olongosoledwa pamwambapo amene alephera kuitanira pa dzina la Yehova kaamba ka chipulumutso ndiro lakuti, Palibe ali yense wa iwo adzaima ali wobvomerezeka ndi kupulumutsidwa wamoyo pa ‘Tsiku Lake lakikulu.’ Mkuntho wophiphiritsira umene’wu umene uyenera kuwaononga ukusonyezedwa m’chaputala chotsatirapo cha bukhu’li, m’Chibvumbulutso 7:1-3. Pambuyo pa kuchula kumene’ko, tikuuzidwa za akapolo a Mulungu 144,000 amene asindikizidwa chizindikiro pa mphumi ndi “chizindikiro cha Mulungu wamoyo.” Amene’wa akuchedwa Aisrayeli, osati Aisrayeli akuthupi achibadwidwe monga ngati aja amene anabvomereza kuphedwa kwa Mwanawankhosa wa Mulungu, koma Aisrayeli auzimu amene akutsatira Mwanawankhosa Yesu monga Mesiya. (Chibvumbulutso 7:4-8; 14:1-5) Atangotha kuona amene’wa, kodi n’chiani chimene chikutsegulidwa kuti tichione? Chiwerengero cha anthu chosawerengeka chimene sichikugwirizana ndi mafumu a dziko lapansi ndi ogwirizana nawo m’kuitana mapiri a maboma ndi mathanthwe kuwabisa ku mkwiyo wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa wake. Iwo samaopa mkwiyo wa Mulungu.
32. Kodi “khamu lalikulu” limene’li limanena kuti limapeza kuti chipulumutso chao, ndipo limodzi ndi phindu lotani kwa iwo eni?
32 Pamene tikuwenenga Chibvumbulutso 7:9-17, tiyeni tione kuti “khamu” losawerenga limene’li likunenedwa kukhala ‘likutuluka m’chisauto chachikulu’:
“Taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uli wo nse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atabvala zobvala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwao; ndipo apfuula ndi mau akulu, nanena, Chipulumutso wa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.
“ . . . Iwo obvala zobvala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti? . . . Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. Chifukwa chake ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo am’tumikira Iye usana ndi usiku m’kachisi mwake; ndipo Iye waukhala pa mpando wachifumu adzawacitira mthunzi, sadzamva’nso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chiri chonse; chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misoszsi yonse pamaso pao.”
33. Kodi ndi zinthu zotani zimene zimasiyanitsa “khamu lalikulu” limene’li ndi Aisrayeli auzimu 144,000 ochulidwa papitapo’wo, ndipo kodi n’chifukwa ninji iwo ali oyenerera kutumikira Mulungu m’kachisi wake wauzimu?
33 “Khamu lalikulu”losawerengeka’lo siliri mbali ya Aisrayeli auzimu owrengeka 144,000. Iwo sanasindikizidwe chizindikiro pa mphumi zao ndi “chizindikiro cha Mulungu wamoyo.” Iwo sakuonedwa kukhala ataima pa Phiri la Ziyoni wakumwamba limodzi ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. Iwo sakunenedwa kukhala ‘atagulidwa pakati pa mtundu wa anthu monga zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.’ Ponena za mtundu, poyerekezera ndiAisrayeli auzimu’wo 144,000, iwo ali Amitundu, monga anthu a mitundu yonse. Komabe iwo afika pa kudziwa Yehova Mulungu ndi kum’zindikira kukhala atakhala pa mpando wachifumu wa m’chilengedwe chonse, monga Mfumu ya m’’Chilengedwe Chonse. Iwo amadziwa ndi kubvomereza amene ali Mwanawankhosa wophedwa wa Mulungu, pakuti iwo amasonyeza chikhulupiriro m’mphamvu yoyeretsa ndi yotsuka ya mwazi wake m’malo mwakuti apeze kaonekedwe koyera pamaso pa Mulungu wokhala pa mpando wake wachifumu’yo. Pokhala oyeretsedwa motero, iwo amapereka utumiki wapatulika kwa iye usana ndi usiku m’mabwalo a pa dziko lapansi a kachisi wake wauzimu.
34. Kodi “khamu lalikuru” likunenedwa kukhala litapangika ndi “nkhosa” zotani, ndipo kodi iro liri ndi chiyembekezo chotani kaamba ka moyo wa m’tsogolo?
34 Bwanji ponena za chiyembekezo chimene iwo onse ali nacho? Sichiri chiyembekezo cha kumwamba. Chibvumbulutso 7:17 chimawayerekezera ndi nkhosa, zimene Mwanawankhosa ali Mbusa wao. “Akasupe a madzi a moyo” ku amene iye akuwatsogolera’ko ali “akasupe” otulutsa makonzedwe a Mulungu kaamba ka moyo waumunthu wangwiro m’paradaiso wa pa dziko lapansi wolonjezedwa. Iwo ali mbali ya “nkhosa” zophiphiritsira zimene Mbusa Wabwino waziperekera moyo wake waumunthu. Atatha kunena za “khola” limene Yohane M’batizi monga “wapakhomo” anatsegula khomo lake mu 29 C.E., Yesu anapitiriza kunena kuti: “Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izi’nso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhla gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:3, 16) Chifukwa cha chimene’cho, “khamu lalikulu” la Chibvumbulutso 7:9-17 liri ndi “nkhosa zina” zimene ziri ndi moyo lero lino ndi zimene zimadzipereka ku kutsatira Yesu Kristu, Mbusa Wabwino.
35. Kodi ‘khamu lalikulu” likukhala “gulu limodzi” ndi yani pansi pa “mbusa mmodzi”?
35 Nanga, kodi “khamu lalikulu” limene’li, linakhala “gulu limodzi” pansi pa mbusa mmodzi” ndi yani? Ndi “nkhosa” za “khola” lina, zimene ziri, otsalira a “kagulu kankhosa” ka Aisrayeli auzimu. (Luka 12:32; 1 Petro 2:25) Ngakhale kuli kwakuti “khamu lalikulu” siliri m’pangano latsopano limene Yesu Kristu analichitira unkhoswe kaamba ka Israyeli wauzimu, iye akuligwirizanitsa ndi otsalira monga “gulu limodzi m’khola limodzi. Kodi Mbusa Wabwino’yo wakhala akuchita zimene’zo kuyambira liti kumkabe m’tsogolo?
36, 37. (a) Kodi kuyamba kwa kusonkhanitsidwa kwa “nkhosa zina” kunasonyezedwa ndi chochitika chotani? (b) Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene chinaikidwa pamaso pao, mowasangalatsa kwambiri?
36 Kuyambira 1935 kumkabe m’tsogolo. Pa mapeto May wa chaka chimene’cho msonkhano wa masiku asanu wa mboni Zachikristu za Yehova unali kuchitika pa chigawo cha Colombia cha Washington, U.S.A. Panali anthu oitaniridwa mwapadera ku msonkhano umene’wu amene anagwirizana ndi otsalira odzozedwa ndipo komabe amene anali okondweretsedwa ndi kupulumuka “chisautso chachikulu” ndi kulowa, osafa, m’dongosolo latsopano la Mulungu limodzi ndi paradaiso wa padziko lapansi. Iwo analibe zikhumbo zakumwamba. Moyo wosatha pa dziko lapansi laparadaiso ukakwaniritsa kotheratu chikhumbo cha mtima wao.
37 Pamenepo, chisangalalo chao chinali chachikulu, pa msonkhano wa pa Washington pamene prezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society analongosola nkhani yonena za “khamu lalikulu,” lonenedwa m’Chibvumbulutso 7:9-17, Authorizsed Version. Iye analongosola momvekera bwino kuti ‘khamo’lo silinali kagulu kauzimu kapena kobadwa ndi mzimu; silidzakhala ndi mkhalikwe wa angelo kumwamba kotero kuti kakathandize olowa nyumba limodzi ndi Kristu 144,000. Linali kwenikweni kagulu ka pa dziko lapansi kokhala ndi chiyembekezo cha moyo waumunthu wangwiro wopanda mapeto m’paradaiso wa pa dziko lapansi pansi pa ufumu wa Kristu. Tsopano, mwa njira ya Mbusa Wabwino Yesu Kristu, Yehova Mulungu anali kuyamba kusonkhanitsa “khamu” lake limene’li kulowa mu utumiki wokangalika limodzi ndi otsalira odzozedwa.
38. Kodi ndi motani m’mene “mzimu”wa awo a “khamu lalikulu” unachitira ndi chiyembekezo choikidwa pamaso pao, ndipo kodi ndi chiyembekezo chotani kuyambira pa nthawi imene’yo chimene chaikidwa kwakukulu pamaso pa onse ofunafuna Mulungu?
38 Mtima ya mazana ochuluka amene analipo pa msonkhano wa pa Washington umene’wo inali isanakondweretsedwepo ndi chiyembekezo cha kukhala olowa nyumba limodzi ndi Kristu. Koma tsopano pa kulongosoledwa bwino kwa chiyembekezo ca pa dziko lapansi chimene chiri m’Chibvumbulutso 7:9-17, “mzimu” wao, mphamvu yobvomeresa yokhala m’kati mwao, inachititsa kulabadira kochokera mu mtima. Iwo analulutira chiyembekezo chimene’cho ndi kuombera manja kwamphamvu kwambiri. Pambuyo pake, pamene zikwi zina’nso zinawerenga m’masamba a magazini a Nsanja ya Olonda kutulutsidwa’nso kwa nkhani yonena za “khamu lalikulu,” nawo’nso, “mzimu” wao, unabvomereza. Kuyambira pa nthawi imene’yo, chiyembekezo cha “khamu lalikulu” chasonyezedwa kwakukulu kwa onse ofunafuna Mulungu pa dziko lonse lapansi. Zikwi mazana ochuluka abatizidwa m’dzina la Mwana wa Mulungu ndipo aikidwa mu mzera wa kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chabwino kwambiri chimene’cho.
39. Kodi ndi polingalira kusiyana kotani pakati pa iwo ndi otsalira odzozedwa funso likufunsidwa ponena zakuti kaya “nkhosa zina” zodzipereka ndi zobatizidwa ziri ndi mzimu woyera pa izo?
39 Ndithudi, “nkhosa zina zodzipereka ndi zobatizidwa za “khamu lalikulu” zimene’zi sizinabalidwe kukhala ana auzimu a Mulungu, okhala ndi cholowa chakumwamba. Izo siziri Aisrayeli auzimu. Izo sizinalowetsedwe m’pangano latsopano limodzi ndi mwai wa kukhala “ufumu wa ansembe ndi mtundu woyera” wa Mulungu. (Eksodo 19:5, 6, NW) Izo sizinasindikizidwe chizindikiro ndi mzimu wa Mulungu monga chizindikiro cha pasadakhale cha cholowa chao chakumwamba. Iwo sanadzozedwe ndi mzimu wa Mulungu monga oyembekezera kukhala olowa nyumba limodzi ndi Kristu mu ufumu wake wakumwamba. (Yesaya 61:1-3; 1 Yohane 2:20, 27; 2 Akorinto 1:21, 22) Komabe kodi iwo ndi mzimu woyera pa iwo.
40. Kodi ndi umboni Wamalemba wotani umene ulipo wosonyeza kaya munthu pa dziko lapansi amene ali wodzipereka kwa Mulungu ayenera kubadwa ndi mzimu wa Mulungu m’malo mwakuti akhale ndi mzimu woyera womagwira ntchito pa iye?
40 Maumboni amayankha kotheratu kuti Inde! Maka-maka kuyambira 1935 C.E., “khamu lalikulu” lagwira ntchito limodzi ndi otsalira odzozedwa, obadwa ndi mzimu. Iwo apatsidwa umboni wokhutiritsa wakuti mzimu woyera wa Mulungu ukugwira ntchito pa iwo. Munthu wa pa dziko lapansi safunikira kubadwa ndi mzimu wa Mulungu m’malo mwakuti mphamvu Yake yogwira ntchito igwire ntchito pa iye. Yang’anani pa mneneri Mose, pa Wowerza Otiniyeli, pa Woweruza Gideoni, pa Woweruza Samsoni, pa Mfumu Davide, pa Yohane M’batizi. Inde, yang’anani pa aneneri onse a Chikristu chisanakhale amene mzimu wa Yehova unawadzera ku kuwauzira kulemba mabukhu a Baibulo kuyambira Genesis kukafika ku Malaki. N’zoona kuti palibe chiyembekezo cha kumwamba chimene chinaikidwa pamaso pa anthu akale amene’wo komabe Yehova Mulungu anaika mzimu wake pa iwo chifukwa chakuti iwo anadzipereka kwa iye ndipo mwachikondi anadzipereka kaamba ka utumiki wake. Mulungu anawakuta ndi mphamvu yake yogwira ntchito. Iye anawadzadza ndi mzimu wake woyera. Uwo unagwira ntchito pa iwo.
41. Polingalira chiwerengero chaching’ono cha awo opanga otsalira odzozedwa lero lino, kodi ndi motani m’mene Mulungu watsimikizirira kuti ntchito ya kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira ikuchitidwa pa mlingo wa pa dziko lonse lapansi?
41 Lero lino, kodi otsalira a Aisrayeli auzimu odzozedwa ndi mzimu alipo angati? Malinga ndi chiwerengero cha awo amene amadya chizindikiro cha mkate ndi vinyo pa phawando la chaka ndi chaka la Mgonero wa Ambuye, pa tsopano lino iwo alipo opitirira 9, 000. Koma Akristu obatizidwa amene’wo amene mzimu wao umabvomereza moyamikira ku chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso pano pa dziko lapansi alipo oposa mamiliyoni awiri. Nanga, ndani, amene amachita mbali yaikulu ya kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira kwa pa dziko lonse’ko? (Mateyu 24:14, NW; 28:10, 20) Otsalira odzozedwa omakalamba’wo, pokhala owerengeka, sakanatha konse kuchita ntchito yonse. Chotero, mzimu wa Mulungu, womagwira ntchito mwamphmvu pa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” wawatheketsa limodzi ndi otsalira odzozedwa’wo kuchita ntchito ya kuchitira umboni kwa pa dziko lonse kosafanana ndi kwina kuli konse m’mbiri Yachikristu.
42, 43. (a) Kaamba ka kuchitidwa kwa kulengeza ufumu Waumesiya kwa pa dziko lonse’ko, kodi awo okhalamo ndi phande amapereka thamo kwa yani? (b) Kodi ndi polingalira malemba otani kuti iwo amakhulupirira kuti iwo anakhala ndi chitsogozo cha angelo?
42 Kulengezedwa kwa Uthengo Wabwino wa Ufumu tsopano kukumvedwa pa dziko lonse lapansi m’maiko ndi zisimbu za m’nyanja oposa 205. Mipingo yoposa 40,000 ya olengeza Ufumu okangalika ikusangalala m’paradaiso wauzimu pa dziko lonse lapansia
43 Kulengezedwa ufumu wa Mulungu kwakukulu kwambiri kumene’ku kaamba ka dongosolo lake latsopano, ngakhale mpaka kukafika ku malekezero a dziko lapansi, kunafunikira kugwira ntchito zolimba kochuluka ku mbali ya awo okhala ndi phande m’kulengeza’ko, ndipo zonse’zi popanda malipiro (Mateyu 10:8) Koma olengeza Ufumu amene’wa, mboni Zachikristu za Yehova, samadzitengera thamo kaamba ka chipambano chachikulu chimene’chi. Iwo amabvomereza kuti iwo ali ziwiya chabe zokhala m’manja mwa Mulungu. Kulimba mtima ndi nyonga zochitira ntchito yoperekedweratu imene’yi iwo amanena kuti zimachokera kwa mzimu wa Mulungu. Iwo amazindikira’nso kuti iwo ali’nso ndi chichirikizo cha angelo ndi chitsogozo pamene akuchita ntchito yobvomerezedwa ndi Mulungu’yo. Iwo amakhulupirira zimene Ahebri 1:14 amanena m’kunena za angelo kukhala monga “mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso” Ndipo’ nso, ponena za nthawi yathu yeniyeni’yi, “mapeto a dongosolo la zinthu,” Yesu anati: “Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake ku mphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.”—Mateyu 24:3, 30, 31.
44. (a) Kodi n’chifukwa ninji kugwiritsiridwa ntchito kwa angelo kotero’ko sikuli kodabwitsa? (b) Kaamba ka kulekanitsidwa kwa Akristu onyengezera ndi enieni, ndi kaamba ka kusonkhanitsidwa kwa “khamu lalikulu” la nkhosa zina kodi ndani amene chithandizo chao chosaoneka chinanenedweratu?
44 Kodi pali chinthu chiri chonse chodabwitsa ponena za zimene’zo? Ai! Eya, m’nthawi zakale, za Chikristu chisanakhale angelo akumwamba anathadiza ndi kutsogolera alambiri okhulupirika a Yehova Mulungu. (Genesis 32:1, 2, 24-30; Eksodo 14:19, 20; 2 Mafumu 6:15-17; Yesaya 37:36; Salmo 34:7) Lero lino ndiyo nthawi ya kusonkhanitsa pamodzi olowa nyumba enieni a ufumu wa Mulungu ndi ya kupatula amene’wa pa Akristu onyengezera a Chikristu cha Dziko, ndipo chotero kaamba ka nthawi yobvuta ino otsalira odzdozedwa anayenera kukhala ndi chithandizo cha angelo, malinga ndi kunena kwa Mateyu 13:39-43, 49, 50, ndi Chibvimbulutso 14:6. Chifukwa cha chimene’cho, angelo okhala pansi pa Kristu Mfumu’yo amachita mbali yotsogoza yosaoneka m’kusonkhanitsidwa kwa otsalira a ophunzira ake odzozedwa, “osankhidwa ake.” Angelo okhala pansi pa ulamuliro wake iye amawagwiritsira’nso ntchito m’kusonkhanitsa khamu lalikulu kopambana otsalira odzozedwa’wo, amene ali, “khamu lalikulu” la ‘nkhosa zake zina.’—Mateyu 25:31-46; Yohane 10:16.
CHIUKIRIRO CHOPHIPHIRITSIRA
45, 46. (a) Kodi n’chifukwa ninji palibe maziko onyozera tsiku la tizinthu tating’ono polingalira chozizwitsa chodabwitsa cha Mulungu monga momwe chinaphiphiritsiridwira mu Ezekieli 37:1-14? (b) Kaamba ka kubwezeretsedwa kwa Aisrayeli okhala mu ukapolo’wo pa dziko lakwao, kodi Yehova akaika chiani mwa iwo?
45 Chotero, pamenepa, kodi pali’nso maziko ali onse kwa ali yense ‘opeputsira tsiku la tinthu tating’ono’? (Zekariya 4:10) Ha, ndi ntchito zotsatizanatsatizana zodabwitsa zotani nanga zimene zinayamba kupangika pamene, kale’lo mu 1919 C.E., “mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unawalowera,” ndiko kuti, mwa otsalira odzozedwa oonekera kukhala akufa’wo! (Chibvumbulutso 11:11) Chinali chozizwitsa chamakono cha chiukiriro ponena za Mulungu Wamphamvuyonse. Chiri ndi chofanana nacho chake m’chimene mneneri Ezkieli anaona, pamene iye anaona masomphenya a chigwa chimene chinali chodzala mafupa ouma, ndi omwazikana a Aisrayeli akufa. Matupi a Aisrayeli amene’wo anabwezeretsedwa, koma matupi’wo anali chikhalirebe akufa. Ndiyeno, momvera lamulo la Mulungu, Ezekieli ananenera pa iwo. Kodi n’chiani chimene chinachitika? “Mpweya unawalowa ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chiriri, gulu la nkhondo lalikulu ndithu.”—Ezekieli 37:1-10.
46 Kodi masomphenya a Ezekieli’wo akakwaniritsidwa pa anthu osankhidwa a Mulungu amene pa nthawi’yo anali kubvutika m’Babulo? Kuti awatsimikiziritse kuti masomphenya a kubwezeretsedwa amene’wa akakwaniritsidwa, Yehova anauzira Ezekieli kunena kuti: “Ndizalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m’dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kuchichita, ati Yehova.—Ezekiel 37:11-14; yerekezerani Yesaya 32:15-18.
47. (a) Atabwezeretsa otsalira ake odzozedwa, kodi ndi kaamba ka chifuno chotani iye anaika mzimu wake pa iwo? (b) Kodi ndi motani m’mene ziyambukiro zopatsa nyonga za chimene’chi zakhalira zogwirizana ndi Aroma 8:11.
47 Mzaka zanthu zana la makumi awiri, pambuyo pa Nkhondo Yoyamba ya Dziko mu 1918, otsalira odzozedwa anapatsidwa’nso moyo mwauzimu ndipo anayenda kutuluka mu ukapolo ku Babulo Wamkulu, ufumu wa pa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, m’malo mwakuti ayambire’nso ntchito yao ya Ufumu. Kaamba ka chifuno chimene’cho, Yehova anawabwezeretsa ku malo ao oyenera pa dziko lapansi, ku unansi wobvomezeka ndi iye. Iye anaika mzimu wake pa iwo, kuti achite mwaufulu, mosabisa, m’ntchito ya Ufumu. “Pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Kuyambira pa nthawi imene’yo, ndi moyo wotani nanga umene otsalira omasulidwa’wo asonyeza mu utumuki wake waufumu, ndipo’nso, pambuyo pake, “khamu lalikulu” la antchito anzao onga nkhosa’wo! Mphamvu yoyera ya Yehova yogwira ntchito yakhala yochititsa zimene’zi monga momwe’di Aroma 8:11 amatikumbutsira kuti: “Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsa’nso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.”
48. Kodi ndi mphamvu yotani imene iri ndi otsalira ogwirizana ndi “khamu lalikuru”
48 Pamenepo, tiyeni patsogolo, mogwirizana O otsalira inu ndi inu a “khamu lalikulu”! Mphamvu yosagonjetseka imene iri kutseri kwa dongosolo latsopano likudza’lo la Mulungu iri nanu. (Zekariya 4:6) Kupitirizabe kwanu kulalikira “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu” kudzadzetsa kubvutika ndi chitonzo zoonjezereka. Koma kukumana kwanu ndi zimene’zi kaamba ka Yehova Mulungu ndi Kristu wake kuli ulemu waukulu kopambana wothekera. Kumbukirani kuti: “Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.” (1 Petro 4:14) Chitonzo chochokera kwa adani a ufumu wa Mulungu sichiri chizindikiro cha kusakondwera kwake. Kuchipirira kwanu kuli umboni wakuti kukunyozetsani. Kumakupatsani ulemu ndi kukupangani kukhala ngati Kristu. Kumakusonyezani kukhala oyenerera utumiki wolemekezeka m’dongosolo latsopano la Mulungu likudza’lo. Chotero dzioneni kukhala achimwemwe ndi oyanjidwa kopambana!
[Mawu a M’munsi]
a Onani 1981 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 24-31.