Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 2 tsamba 18-37
  • Wolamulira Amene Amadziwa Mapeto Kuyambira Pachiyambi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wolamulira Amene Amadziwa Mapeto Kuyambira Pachiyambi
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KULENGEDWA KWA MBONI
  • MBONI ZA YEHOVA ZAMAKONO
  • UYO AMENE AMADZIWA MAPETO KUYAMBIRA PA CHIYAMBI
  • MALONJEZO AKE ABWINO NGOTSIMIKIZIRIKA
  • Mlandu wa Bwalo la Milandu la Chilengedwe Chonse Womwe Umakuyambukirani
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mudzakhala Mboni ya Mulungu Wowona?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mboni Zotsutsa Milungu Yonama
    Nsanja ya Olonda—1995
  • “Inu Ndinu Mboni Zanga”
    Nsanja ya Olonda—2014
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 2 tsamba 18-37

Mutu 2

Wolamulira Amene Amadziwa Mapeto Kuyambira Pachiyambi

1. Mosafanana ndi atsogoleri a ndale za dziko, kodi tiyenera kutembenukira kuti kuti tidziwe za m’tsogolo?

M’KATI mwa nyengo zonse kuyambira m’nthawi ya Babulo wakale kufikira tsopano, olamulira a ndale za dziko afunsira openda nyenyezi ndi alauli kapena olankhula ndi mizimu kuti adziwe zimene ziri m’tsogolo. Iwo afuna-funa kudziwiratu kwauzimu kuti kuwathandize m’kulamulira anthu ao mwachipambano. Mbiri ya ndale za dziko kufikira m’zaka makumi awiri mphambu zisanu zotsirizira za zaka za zana la makumi awiri imatsimikizira kuti chidziwitso chonse chosonkhanitsidwa motero chawalepheretsa. Chotero mkhalidwe wa ndale za dziko zaudziko uli wosonkonezeka. Olamulira a zochitika za anthu sakudziwa kotembenukira. Mitundu iri m’bvuto ndipo ikutembenukira ku njira zopsyinja, ndipo anthu ali ndi chifukwa chiri chonse choopera kuti zoipa kwambiri zidzachitika. Kaamba ka mankhwala eni-eni iwo sangatembenukire kwa munthu ali yense pa dziko lapansi. Njira yokha yopambana yotembenukirako ndiyo kutalikirana ndi openda nyenyezi, olankhula ndi mizimu ndi magwero a kulankhula ndi mizimu a chidziwitso chao chosocheretsa ndi kuyang’ana kwa wolamulira Wamkulu wa zinthu zonse, Mulungu Wam’mwamba-mwamba kwa amene kukuchokera boma la dziko lonse likudza’lo!

2. Kodi umboni wa umulungu umakhala pa kukhoza kotani ponena za ulosi?

2 Palibe wolemba mbiri, palibe munthu wophunzira bwino, angakane kuti kuyambira m’nthawi zakale-kale mitundu ya dziko yakhala ndi milungu yao, yooneka ndi yosaoneka. Eya, mwamsanga pambuyo pa mapeto a Nkhondo Yachiwiri ya Dziko mu 1945 mfumu ya Japan inakana kunena kwakuti iye anali Mulungu, mbadwa ya mulungu wachikazi Wachijapana Amaterasu, ndipo komabe, kufikira lero lino, ambiri a chipembedzo cha makolo amaumirirabe ku kulambira mfumu m’Maiko Akum’mawa. Yochedwa “milungu” ya mitundu imene’yi inali ndi aneneri ao pa dziko lapansi. Mwa chitsanzo, m’zaka za zana lakhumi Nyengo yathu Ino isanakhale, panali aneneri a mulungu Baala okwanira mazana anai kudza makumi asanu mu mtundu wa ku Middle East wa Israyeli, m’kati mwa kulamulira kwa Mfumu Ahabu ndi Mfumukazi Yezebeli, monga momwe kwasimbidwira m’bukhu la 1 Mafumu, chaputala cha khumi ndi chisanu ndi chitatu, vesi la makumi awiri mphambu awiri. Aneneri amene’wo ananeneratu za m’tsogolo m’dzina la mulungu wao. Ngati ulosi wonenedwa m’dzina la mulungu sunakwaniritsidwe, unatsimikizira mulungu’yo kukhala wonyenga, mulungu wosakhalako. Kunena zoona, umboni wa mulungu wosakhalako. Kunena zoona, umboni wa mulungu woona unali pa kukhoza kwake kukwaniritsa ulosi wake!

3. Kodi aneneri ayenera kukhala mboni za milungu yao m’mbali zotani?

3 M’chiyeso chotha makani cha ulosi chimene’chi, kodi ndani amene anatsimikizira kukhala Mulungu weni-weni, Mulungu wamoyo ndi woona? Aneneri a milungu ya amitundu anaima monga mboni zotulutsa zeni-zeni zonena za milungu yao ndi kusonyeza kuti maulosi amene milungu yao inanena akwaniritsidwa. Kodi ali yense wa milungu ya mitundu imene’yi ananena maulosi amene ali opindulitsa lero lino, amene akukwaniritsidwa m’nthawi zathu? Kodi munthu ali yense ndi bukhu liri lonse la mbiri, lingapereke monga umboni umodzi wa maulosi otero’wo? Palibe ali yense lero lino angatero? Ndipo komabe pali Mulungu mmodzi amene amadzipereka kukhala wofunitsitsa kudzipereka ku chiyeso chaulosi’cho, kutsimikizira kuti iye ali Mulungu mmodzi wamoyo ndi woona amene ali ndi kudziwiratu ndipo angathe kuneneratu za m’tsogolo ndi amene maulosi ake nthawi yonse’yi akwaniritsidwa. Iye angatulutse mboni zake limodzi ndi umboni wa mu mbiri mochirikiza kukhala kwake Mulungu wa ulosi woona. Kodi Iye ndani? Kodi dzina Lake ndani?

4-6. Kodi ndi chitokoso chotani chimene Yesaya 43:9 akupereka kwa milungu ya mitundu?

4 Mmodzi wa aneneri ake amene anakhala ndi moyo m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu Nyengo yathu Ino isanakhale anali Yesaya mwana wa Amozi, nzika ya ufumu wa ku Middle East wa Yuda. Mzimu wouzira unadza pa iye ndipo motero iye anagwiritsiridwa ntchito monga wonenera kutulutsa chitokoso chotsatirapo’chi kwa milungu yonse ya amitundu, kuti:

5 “Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo [milungu ya amitundu ndi anthu] anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge [milungu monga] mboni zao, kuti [monga milungu] abvomerezeke ndi olungama; pena amve [mitundu ndi magulu a mitundu] nanene zoonadi.”—Yesaya 43:9.

6 M’mau amene’wo, milungu ya mitundu ndi ya magulu a mitundu ikutokosedwa ponena za mphamvu yao ya kulosera. Kodi ndi uti pakati pa milungu ya mitundu yotero’yo amene ali wokhoza kulengeza molosera zimene zanenedweratu m’mavesi oyambirira a chaputala cha ulosi wa Yesaya chimene’chi? Kodi ndi uti pakati pa milungu ya mitundu imene’yo angathe kutichititsa kumva pasadakhale zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa m’tsogolo muno, osanena kanthu za zinthu zotsirizira za m’tsogolo?

7. Kodi ndani amene ayenera kutumikira monga mboni zao ndipo kodi ndani amene ayenera kuimva?

7 Iloleni milungu ya mitundu imene’yi itulutse mboni zao pa dziko lapansi zoti zichitire umboni kuti milungu imene’yi yachita zinthu za mtundu wolosera molondola, kotero kuti itsimikizire mwa mboni zimene’zi kuti iyo iri milungu yoona ndi yodalirika ndipo iri yoyenerera kuchedwa yoongoka, yolungama, ndi yolungamitsidwa kotheratu m’kukhala yolambiridwa monga milungu yokhala ndi kukhoza kuneneratu m’tsogolo mosalephera. Kapena, lolani mitundu ndi magulu a mitundu osonkhanitsidwa’wo amve mboni za milungu zimene’zo ndi kupereka umboni wa mboni zimene’zo ndi kunena kuti zimene iwo akuchitira umboni ziri zolondola, zoona, ziri zeni-zeni za mu mbiri. Milungu yotokosedwa ya mitundu’yo yatsimikizira kukhala yosakhoza kutulutsa mboni zotero’zo. Iribe mboni zao zimene umboni wao tingaunene kuti: “Ndiwo choonadi!”

8. Kodi wotokosa’yo akudzidziwitsa kukhala yani?

8 Ndipo tsopano pakudza chilengezo cha wotokosa’yo: Malinga ndi kunena kwa Baibulo la American Standard Version (AS), wotokosa’yo akudzidziwikitsa chimene iye ali ndi dzina, kuti: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga amene ndam’sankha; kuti iwe undidziwe ndi kundikhulupirira, ndi kuzindikira kuti Ine ndine: ndisanakhale ine panalibe Mulungu wopangidwa, ndipo’nso sipadzakhala wina pambuyo panga. Ine, Inetu, ndine Yehova; ndipo popanda ine palibe mpulumutsi. Ndalengeza, ndipo ndapulumutsa, ndipo ndasonyeza; ndipo panalibe mulungu wachilendo pakati panu: chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu. Inde, chiyambire pamene tsiku linayamba Ine ndine; ndipo palibe wina amene angalanditse m’dzanja langa: ndidzagwira ntchito, ndipo kodi ndani angaidodometse?”—Yesaya 43:10-13; onani’nso New World Translation of the Holy Scriptures.

9. Kodi Yehova wapanga yani kukhala mboni zake, ndipo motani?

9 Molimba mtima Uyo amene anadzutsa mafunso otokosa’wo akudzidziwikitsa kukhala Yehova. Pamene kuli kwakuti milungu yotokosedwa’yo singatulutse mboni zao kuti zipereke umboni wa umulungu wao, Yehova angatulutse mboni Zake. Mboni zake zikuoneka. Iye wazitulutsa, ndipo iye amazichula ndi kuzikumbutsa za m’mene izo zinakhalira mboni Zake. Kodi izo ndizo ayani? Yehova amanena za izo kukhala kagulu kogwirizana, akumazichula monga kagulu kamodzi, “Mtumiki wanga amene ndam’sankha.” Izo zimakhala zosiyana ndi mitundu ndi magulu a mitundu amene milungu yao yochuluka Yehova akuitokosa. Mboni za Yehova ndizo mtumiki wake, mtundu wake wokha wosankhidwa. Kuti mtundu umene’wu ukhale mboni zake zachiungwe, Yehova waupanga kukhala kagulu kake ka mtumiki kuti iko kam’dziwe: kuti kam’zindikire ndi kum’khulupirira, ndi kuika chikhulupiriro pa iye, ndipo chotero kuzindikira kuti iye ndi Yemweyo, wosasinthika, Mulungu wosatha. Mwa njira imene’yi iwo angakonzekeretsedwe kutumikira monga mboni zake pamaso pa mitundu yonse yolambira mafano ya dziko.

10. Kodi ndi motani m’mene kuliri kuti panalibe mulungu wopangidwa asanakhale Yehova?

10 Pamaso pa Mulungu amene’yu, Yehova, panalibe munthu kapena chinthu chothero’cho chonga mulungu wopangidwa. Osati kuti Yehova Mulungu iye mwini analengedwa ndi munthu wina. Ngati, mofanana ndi osakhulupirira Mulungu amakono, tikanaumirira kuti Yehova Mulungu anapangidwa, tikayenera kukakamizika moyenerera kufunsa kuti, Kodi ndani amene anapanga Yehova Mulungu? Limene’lo likanachititsa funso lakuti, Nangano, ndani amene anapanga wopanga Yehova Mulungu? Ndipo’nso, Kodi ndani amene anapanga uyo amene anapanga wopanga Yehova Mulungu? Kunena zoona, sitiyenera kufika ku mapeto a kufunsa funso limodzi-modzi’lo mobwereza-bwereza. Motero chozizwitsa chonena za Umulungu chikangopangitsidwa kukhala chouma, kukhala chobvuta kwambiri ndi kuchititsa kusakhutira ku maganizo olingalira mwanzeru. Nkhani yonena za kupanga ingaleke kufunsidwa kokha pamene ifika pa Wopanga wosalengedwa amene nthawi zonse wakhala, Wopanga wopanda chiyambi. Mneneri Mose, amene anali mmodzi wa mboni zimene zinapanga kagulu ka Yehova ka “mtumiki,” akuthetsa nkhani’yo m’njira yosabvuta ndi yopulumutsa nthawi kopambana, ponena kwa Ambuye Yehova, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi kuti: “Kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, inu ndinu Mulungu.”—Salmo 90:1, 2.

11. Kodi n’chifukwa ninji kuli kwakuti panalibe mulungu wopangidwa asanakhalepo Yehova?

11 Nanga, kodi n’chifukwa ninji, Yehova anati: “Ndisanakhale ine panalibe Mulungu wopangidwa”? (Yesaya 43:10) Chinali chifukwa chakuti mitundu yolambira mafano ya dziko inali itapanga milungu yao yonyenga, koma iyo sinapange Yehova monga Mulungu. Iwo sanakhalepo Yehova asanakhalepo m’kupanga milungu yao yonyenga. Yehova, monga Mlengi wa dziko lapansi ndi okhalapo ake, anali patsogolo pa mtundu uli wonse. Chifukwa cha chimene’cho, panalibe mulungu wopangidwa ndi mitundu yolambira mafano’yo Yehova asanakhaleko.

12. Kodi n’chifukwa ninji sipadzakhala mulungu wopangidwa pambuyo pa Yehova?

12 Si zokha’zo, koma, Yehova akuti, “ndipo’nso sipadzakhala wina pambuyo panga.” (AS) Yehova pokhala Mulungu ‘woyambira ku nthawi yosayamba kufikira ku nthawi yosatha.’ sadzaleka kukhalako. Mitundu yolambira mafano’yo, posakhala yamuyaya, idzachoka pa dziko lapansi m’kati mwa bvuto lalikulu kopambana la dziko limene liri patsogolo’pa, pamene Yehova wosatha’yo adzakhalapobe kosatha. Chotero, mitundu’yo sidzakhalapo iye asanakhale, koma Iye iwo asanakhale. Chifukwa cha chimene’cho, n’kosatheka kwa mitundu yolambira mafano’yo kupitirizabe kupanga milungu yao yonyenga pambuyo pa Yehova. Milungu yao yopangidwa kapena yopangidwa ndi anthu idzaonongeka limodzi nawo. (Yesaya 2:18-21) Koma Yehova Mulungu woona wa ulosi amakhalapobe kwamuyaya. Ndipo’nso, mboni zake zokhulupirika zidzapitirizabe kukhalapo kwamuyaya, zopezeka nthawi zonse kuchitira umboni mwa mau kuchirikiza Umulungu wa Yehova.

13. Kodi ndi m’zochitika zotani milungu iri yonse sinapitirize kukhalapo pambuyo pa Yehova?

13 Yambiri ya mitundu yakale, Babulo, Asuri, Amedi ndi Aperesi, Edomu (Idumeya) Moabu, Amoni ndi ina, kwa nthawi yaitali kuyambira pamenepo yakhala kulibe, ndipo milungu yao yopangidwa’yo inachoka limodzi nawo. Ponena za milungu imene’yo ya mitundu, Yehova Mulungu anganene kuti: “Pambuyo panga panapitirizabe kukhala popanda wina. Ine—Ndine Yehova, ndipo popanda ine palibe mpulumutsi.”—Yesaya 43:10, 11, NW.

KULENGEDWA KWA MBONI

14, 15. Kodi ndi motani m’mene Yehova analengera mboni zake, akumatero mosathandizidwa?

14 Kuti akhale ndi mboni, Mulungu wopanda chiyambi amene’yu amene analibe wina amene anam’panga anayenera kuchita, kunena kapena kulosera kanthu kena, ndipo chimene’chi pamaso pa openyerera kapena patsogolo pa awo amene anapindula nacho. Iye analenga’di mboni mwa kuchita kanthu kena kwa iwo, kotero kuti iwo moonadi akanena kanthu kena konena za iye. Kunena zoona, iye anapulumutsa mboni zimene’zi, monga momwe iye anali ataneneratu kuti akachita. Ndipo zimene’zi iye anazichita popanda chithandizo cha ali yense wochedwa “mulungu.” M’njira imene’yi iye anasonyeza moonekera kuti iye anali Mulungu, Mulungu mmodzi yekha wamoyo ndi woona. Nazi zimene iye anapitirizabe kutikumbutsa m’mau ena a mneneri Yesaya:

15 “‘Ine mwini ndanena ndipo ndapulumutsa ndipo ndachititsa kuti zimvedwe, pamene panalibe pakati panu mulungu wachilendo. Chotero inu ndinu mboni zanga,’ ndiwo mau a Yehova, ‘ndipo Ine ndine Mulungu. Ndipo’nso nthawi zonse ndine Yemweyo; ndipo palibe ali yense wochititsa chipulumutso m’dzanja langa. Ndidzagwira ntchito, ndipo kodi ndani amene angaletse [ntchito yanga]? ’”—Yesaya 43:12, 13, NW.

16. Kodi oomboledwa’wo anayenera kunena kuti anapeza kuti chipulumutso?

16 Opulumutsidwa’wo sanali okhoza kunena kuti chipulumutso chao chinachokera kwa wina ali yense koma kwa Uyo amene ananeneratu kuti akachichititsa. Kachitidwe kake ka chipulumutso kamene iye anakachititsa kumvedwa kuli konse. Chotero opulumutsidwa ake’wo anali ndi thayo la kukhala mboni zake, m’malo mwakuti atsimikiziritse zimene ena anangozimva mwapang’ono. Iye anadzitsimikizira kukhala Mulungu, ndipo chotero iye sanali Mulungu wopanda mboni zenizeni za choonadi chimene’chi.

17. Pamene Iye achitapo kanthu, kodi n’chifukwa ninji palibe ali yense angakuletse?

17 Ndipo’nso, iye anali Mulungu Wamphamvuyonse, pakuti palibe ali yense amene akanatha kudzilanditsa kapena kulanditsa wina ali yense m’dzanja la Yehova. Pamene Yehova achita kanthu, palibe munthu ali yense ali wokhoza kukaletsa kapena kukabweza. Chimene iye amaneneratu kapena amalosera, iye ali wamphamvu mokwanira kuchichititsa kukwaniritsidwa.

18. Kodi ndi motani m’mene Yehova anabwerezera chipulumutso, koma pa mlingo wokulirapo kwambiri?

18 Yehova anapulumutsa kagulu kake ka “mtumiki” wa mboni pa nthawi ina kale, mu 1513 B.C.E., ndipo iye angathe kukuchita’nso, pa mlingo wokulirapo’di kwambiri. Iye anapulumutsa Israyeli ku Ufumu wa Igupto, pamene unali ulamuliro wa dziko lonse, Ulamuliro wa Dziko Woyamba pa mbiri ya Baibulo. Ngakhale Ufumu wa Babulo wapambuyo pake’wo, Ulamuliro wa Dziko Wachitatu m’mbiri ya Baibulo, sukakhala wamphamvu mokwanira kuletsa chipulumutso chachiwiri cha mtumiki wa Yehova. Poyang’ana m’tsogolo ku chipulumutso chotero’cho m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi Nyengo yathu Ino isanakhale, Mulungu Wamphamvuyonse anapitirizabe kunena mwa mneneri wake Yesaya patatsala zaka mazana awiri kuti: “Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israyeli: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babulo, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Akasidi m’ngalawa za kukondwa kwao. Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israyeli, Mfumu yanu.”—Yesaya 43:14, 15.

19. Kodi ndi motani m’mene Woombola’yo Yehova anapangitsira amalinyero a Akaldayo kulira mokuwa?

19 Motero, monga ngati kuti chipulumutso cha anthu ake okhala mu ukapolo Israyeli chinali chitachitika kale, Mulungu amene anali wochititsa kulengedwa kwa mtundu umene’wo akunena za iye mwini kukhala Mombolo wake, Wopulumutsa wake ku Ulamuliro wa Dziko wa Babulo. Kaamba ka iwo iye akatumiza magulu ankhondo ogwirizana a Amedi ndi Aperesi, otsogozedwa ndi Koresi Wamkulu, kugubuduza Ufumu wa Babulo m’chaka cha 539 B.C.E., Ngalawa zonse za Babulo pa Mtsinje wa Firate, kaya zankhondo kapena zamalonda, sizidzakhala zokhoza kuimitsa kugwa kwa Babulo. M’malo mwa mfuu zachipambano, amalinyero adzalira mokuwa. Kodi n’chifukwa ninji siziyenera kukhala choncho pamene ngalawa zao zinamira pamene m’tsogoleri wa magulu ankhondo Koresi anachititsa madzi a Mtsinje wa Firate kupambutsiridwa kumbali kuchoka ku ngalande yake ya nthawi zonse m’malo mwakuti magulu ake ankhondo aolokere pa matope a mtsinje’wo ndipo motero kulowa mu mzinda’wo kudzera ku zipata za madzi a kumaso?

20. Kodi Koresi Wamkulu anathyolera yani mipingiridzo ya ndende, ndipo motani?

20 Babulo wakale monga ulamuliro wa dziko wa ndale za dziko anakana kutsegula mpangidwe wake wa ndende umene iye anagwira nawo Aisrayeli otengedwa ukapolo’wo, okhalitsidwa mamailo chikwi kutali ndi kwao, Yerusalemu ndi dziko la ufumu wa Yuda. Koma, m’kukwaniritsa ntchito yake yonenedweratu mogwirizana ndi ulosi wa Yesaya (44:28-45:4), Koresi wogonjetsa’yo anasonkhezeredwa kuchitapo kanthu kuthyola mipingiridzo ya ndende ndi kulola andende Achiisrayeli okonda ufulu’wo kubwerera ku dziko lao lopasulidwa’lo mu 537 B.C.E. Yehova Mulungu, Wokwaniritsa maulosi, analola kuti ngongole ya Wolanditsa Koresi isungidwe kuti adzalipidwe ndi Iye. Monga Mombolo wa Israyeli iye anafupa Koresi moyenerera.—Yesaya 43:3, 4.

21. Motero kodi ndani amene anatsimikizira kukhala Mfumu ya Israyeli womasulidwa’yo?

21 Pa chionongeko chopweteketsa mtima cha Yerusalemu ndi kachisi wake chochitidwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E., mafumu Achiisrayeli analeka kukhala pa “mpando wachifumu wa Yehova” pa malikulu amene’wo. (1 Mbiri 29:23) Koma tsopano, mwa kulanditsa kwake anthu ake okhalitsidwa akapolo’wo ku Babulo mu 537 B.C.E., Yehova Mulungu anatsimikizira kuti iye anali chikhalirebe Mfumu yao ya kumwamba. (Yesaya 52:7; Mateyu 5:35) Mulungu wao, osati cholengedwa china chaumunthu, ndiye amene anali Mfumu yao. Iwo, choyamba, anali nzika Zake. Iwo anayenera kupereka kukhulupirika kwao kwa Iye, monga momwe kuliri kuti iwo anapeza chimasuko chao kuchokera ku Babulo kwa Iye, osati kwa woimira wake wa pa dziko lapansi, Koresi Mperesi. Iye anali ataneneratu kuwaombola kwake kwa wosunga ndende wao Babulo, ndipo iye sakanaswa pangano lake loperekedwa. Chotero, tsopano, osati makolo ao okha akale, koma iwo eni’wo anakhala’nso mboni Zake.

22, 23. (a) Kodi ndi m’mbali yotani m’mene Yehova moyenerera anganene kuti, “Ine ndiri woyamba ndi womariza”? (b) Kodi mboni zake za cheni-cheni chimene’chi ziri kuti?

22 Ngati zonse’zi sizinatsimikizire kuti Iye anali Mulungu mmodzi wamoyo ndi woona, kodi n’chiani’nso chimene chikafunidwa kwa iye? Kuyambira pachiyambi kufikira mapeto, kuyambira ku nthawi zonse zakale kufikira ku nthawi zonse za m’tsogolo, iye yekha ndiye amene ali ndi malo a Umulungu. Mboni za Mulungu wake pa dziko lapansi pano si zosowa. Mwachionekere ali pa malo ake apamwamba a Umulungu, iye angapereke chilengezo chake china chotokosa pamaso pa milungu ya amitundu onse kuti:

23 “Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibe’nso Mulungu. Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazitsire Ine anthu akale? milungu’yo iwadziwitse zomwe zirinkudza, ndi za m’tsogolo. Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimene’zo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine alipo’nso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindiziwa liri lonse.”—Yesaya 44:6-8.

24, 25. Kodi n’chifukwa ninji uli ulemu kuchedwa mboni Zake?

24 Kodi ife lero lino tikumva bwanji ndi nkhani imene’yi? Kodi ali yense wa ife akaona kukhala wolemekezedwa ngati Mulungu wa Baibulo Loyera, Yehova, akananena nafe kuti: “Inu ndinu mboni zanga”? Tikakhala ndi chifukwa chomvera kukhala olemekezedwa, pakuti kumene’ku kukatiika m’kagulu kolemekezedwa kopambana.

25 Mneneri Yesaya iye mwini anali mmodzi wa mboni za Yehova, kodi si choncho? Ndithudi bukhu lolosera’lo la Yesaya, la utali wa machapula makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi chimodzi, ndi mau ambiri ogwidwamo monga momwe akupezekera m’Malemba ouziridwa Achikristu, kuyambira pa Mateyu mpaka ku Chibvumbulutso, onse amatsimikizira kuti Yesaya anali wapadera monga mboni ya Yehova. Ndipo bwanji ponena za Yesu Kristu iye mwini? Kodi ali yense kumwamba kapena pa dziko lapansi angakane kuti iye, naye’nso, anali mboni ya Yehova? Palibe ali yense kuli konse ndi wa pa nthawi iri yonse amene amaposa iye monga mboni yotero. Monga Myuda wachibadwidwe kapena Muisrayeli, Yesu Kristu anali mbali ya mtundu umene’wo kwa umene mau a Yesaya 43:10 ananenedwa’ko kuti: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha.” Ngati palibe munthu ali yense akutero, mtumwi Yohane akum’cha “Yesu Kristu, Mboni Yokhulupirika’yo.” Ndipo’nso Yohane akugwira mau Yesu Kristu woukitsidwa kukhala akunena kuti: “Izi anena Amen’yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu.”—Chibvumbulutso 1:5; 3:14.

MBONI ZA YEHOVA ZAMAKONO

26, 27. (a) Kodi n’chifukwa ninji Akristu eni-eni ayenera’nso kukhala mboni za Yehova? (b) Kodi iye wawalanditsa ku gulu la ufumu uti?

26 Popeza kuti Yesu Kristu anali ndipo anabvomereza kukhala mboni ya Yehova, kodi n’kosayenera kuti ophunzira okhulupirika a Kristu lero lino ayenera kudzizindikira kukhala mboni za Yehova ndi kubvomereza kukhala otero? Ndithudi ai! Otsanzira Yesu Kristu okhulupirika amene’wa amayesa-yesa kukhala mogwirizana ndi kudzinenera kwao kwa kukhala mboni za Yehova mwa kuchitira umboni Iye ndi ufumu Wake pa dziko lonse, mogwirizana ndi mau a Yesu a ulosi a pa Mateyu 24:14. Yehova, amene iwo ali mboni zake, ndiye Mulungu amene iwo amam’lambira monga Mulungu mmodzi wamoyo ndi woona. Iwo amam’zindikira kukhala Uyo amene anawalanditsa ku gulu la ndale ndi chipembedzo lamphamvu kwambiri koposa Babulo pa Mtsinje wa Firate, ndiko kuti, kuchokera ku chimene bukhu lotsirizira la Baibulo limacha Babulo Wamkulu.

27 Ophunzira Baibulo ambiri alingalira kuti Babulo Wamkulu anaphiphiritsira Chalichi Chachiroma Katolika chokhala ndi malikulu ake pa mzinda wokhala ndi mapiri asanu ndi awiri wa Roma. Ena am’lingalira kukhala akuphiphiritsira Chikristu cha Dziko chodetsedwa ndi mwazi limodzi ndi chisonkonezo chake cha timagulu tambiri ta chipembedzo. Koma Baibulo limadziwikitsa Babulo Wamkulu kukhala ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, kuphatikizapo Chikristu cha Dziko.—Chibvumbulutso 14:8; 17:3 mpaka 18:4.

28. Kodi ndani amene ali Koresi Wamkulu, ndipo kodi ndi motani m’mene iye wakhalira ngati chiombankhanga?

28 Chikristu cha Baibulo, osati Chikristu cha Dziko, chimaima molekana ndi Babulo Wamkulu kotheratu ndi moonekera bwino. Pali Akristu oona lero lino amene angathe kuchitira umboni Yehova kukhala atwalanditsa ku ufumu wachipembedzo wa dziko wa Babulo Wamkulu. Iwo amadziwa kuchokera m’maulosi a Baibulo kuti Yehova ananeneratu chilanditso chamakono’chi, monga momwe’di iye anachiphiphiritsira ndi chilanditso cha otsalira a Aisrayeli olapa ku Babulo wakale mu 537 B.C.E. Iwo amadziwa kuti, kuti awalanditse Yehova wagwiritsira ntchito wina wake wamphamvu kwambiri koposa Koresi Wamkulu wakale, amene anachokera kum’mawa kwa Babulo kudzam’gubuduza monga ulamuliro wa dziko lonse. Yehova anagwiritsira ntchito monga wolanditsa mboni Zake zamakono uyo amene Iye anam’dzoza ndi mzimu Wake woyera pa ubatizo wake mu Mtsinje wa Yordano, Yesu Kristu. Wodzozedwa’yo ndiye Koresi wophiphiritsiridwa, ndipo iye akuchita mwaliwiro ngati chiombankhanga kuthamangira ku kachitidwe ka kulanditsa mboni za Yehova zamakono ku Babulo Wamkulu. Mboni zolanditsidwa’zo ziri zothokoza kwa Yehova kaamba ka kuitana Koresi Wamkulu kuwakwatula ngati chiombankhanga pa Babulo Wamkulu ndi kuwamasula m’ndende yake yachipembedzo.

29, 30. Kodi n’chiani chimene mboni za Yehova zingachitire umboni ponena za uphungu Wake?

29 Chikhulupiriro cha mboni zolanditsidwa zimene’zi mwa Yehova monga Mulungu chalimbikitsidwa. Mwa izo zokha zimadziwa motsimikizira kuti iye ananeneratu chilanditso chao kale-kale ndi kuti iye wachichititsa’di kweni-kweni. Kuli kolimbikitsa chikhulupiriro kwa iwo kudziwa kuti uphungu umene iye mwini anatsimikizira kuuchita wautsatira’di mpaka kufika ku chipambano lero lino. Afunseni, ndipo adzachitira umboni ponena za m’mene Mulungu wao wakhalira wochita mogwirizana ndi chilengezo chake cholosera mu Yesaya 46:8-11, kumene timawerenga kuti:

30 “Kumbukirani ichi, nimuchirimike, mudzikumbutse’nso, olakwa inu. Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibe’nso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibe’nso wina wofana ndi Ine; ndilalikira za chimariziro kuyambira chiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachititidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse; ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum’mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera ku dziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichita’nso.”—Onani’nso The Jewish Publication Society of America Bible.

UYO AMENE AMADZIWA MAPETO KUYAMBIRA PA CHIYAMBI

31, 32. Kodi ndi motani m’mene Yehova anasungira uphungu wake wotsutsana ndi Asuri?

31 Amene’yu ndiye mtundu wa Mulungu wosagonjetseka amene mitundu yonse ya dziko lapansi iyenera kuchita naye lero lino. Chifukwa chakuti iye ndiye Mulungu wa uphungu wosalakwa, iye ndiye Mulungu’yo ‘wakulalikira chimariziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale anena zinthu zimene zisanachitidwe.’ (Yesaya 46:10) Iri nthawi yabwino kwambiri yakuti mitundu ya pa dziko lapansi ilingalire Mulungu amene’yu Yehova mwamphamvu ndi kulingalira uphungu wake wokhala ndi cholinga umene ukuonekera bwino lomwe utalembedwa m’Baibulo Loyera. Iye ali wokhoza kuona monga mdani ulamuliro wa dziko uli wonse umene ulipo lero lino, muli monse m’mene ungakhalire ndi zida zankhondo zamphamvu za nyuklea. M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. iye analingalira motero Ulamuliro wa Dziko wa Babulo, umene unali kutsendereza mopanda chifundo mboni zake. Asanachite ndi umene’wo iye anatokosa woukira wina wa mboni zake, ndiko kuti, ulamuliro wa Dziko wa Asuri, ndi kutumiza otsala a asilikali ake ankhondo oukira’wo akuzandira kubwerera ku mzinda wao wamalikulu Nineve atachititsidwa manyazi m’nkhondo. M’mau olembedwa mu Yesaya 14:24-27, iye ananeneratu zimene iye akachita kwa Asuri wokonda nkhondo’yo, kuti:

32 “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala; kuti Ine ndidzatyola Asuri m’dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo gori lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphuzi pao. Umene’wu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo iri ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse. Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?”

33, 34. Kodi ndi motani m’mene kuchita uphungu wake kwa Yehova kunayambukirira Sanakeribu?

33 Lero lino, zaka zoposa 2,700 pambuyo pake, n’kuyenera kwathu ndi mwai kufunsa kuti, Kodi zinthu zinachitika monga momwe’di Yehova analingalirira ndi kukwaniritsidwa monga momwe’di anadzilangizira? Kodi Yehova wa makamu anathyola woukira Wachisuri m’Dziko Lolonjezedwa la Yehova ndi kum’pondereza m’mapiri a dziko limene’lo? Kuti tipeze yankho, zokha zimene tiyenera kuchita ndizo kutembenukira ku usiku uja m’chaka cha 732 B.C.E. Nthumwi ya Mfumu Sanakeribu inali itapereka lingaliro lake lotsirizira pa Yerusalemu. Yehova mwa mneneri wake Yesaya pamenepo anatumiza yankho lake lonyodola kwa Sanakeribu, amene pa nthawi’yo anali kuzinga Libina, pafupi-fupi mamailo makumi awiri (makilomita 32) kumadzulo kwa Yerusalemu. Ndiyeno ankhondo a Sanakeribu zikwi zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu anagona usiku’wo tulo tatikulu ta tapa-tapa kwakuti sanauke’nso. Ndi nkhonya yakupha yakachete-chete mngelo wa Yehova anawapha.

34 Podzuka m’mamawa, Sanakeribu wodzitamandira’yo ayenera kukhala ataopsyedwa pakuona msasa wa asilikali ake ankhondo. Atapsyinjika, iye potsirizira pake anadzindikira kuti iye sakanatha kumenyana mwachipambano ndi Mulungu wotero’yo wonga Yehova. Chotero ndi magulu ankhondo otsala’wo pa usiku woopsya umene’wo anatuluka m’dziko la Yuda kubwerera ku malikulu a Asuri, Nineve. Ngati Yehova akanatha kuchita kupha kotero’ko kwa magulu ankhondo a Sanakeribu pa mtunda wa mamailo makumi awiri kapena kuposa kuchokera ku Yerusalemu, kodi Mulungu amene’yu akanachitanji ku gulu lankhondo la Asuri atakhala pafupi m’kuzinga pa Yerusalemu peni-peni’po? Kunali kochititsa mantha kwambiri kwa Sanakeribu kukulingalira. Iye sanayese konse kuopsyeza mzinda wa Mfumu Yaikulu Yehova kachiwiri’nso.—Yesaya 36:1 mpaka 37:38; 2 Mbiri 32:20-22.

35. Kodi dzanja lake tsopano latambasulidwa kaamba ka kuchita uphungu wotani?

35 Munomo m’chochitika cheni-cheni cha mbiri yakale muli chakudya chochuluka cha maganizo ku mbali ya Ulamuliro wa Dziko wamakono wa Angelezi ndi Amereka, inde, ku mbali ya gulu la mitundu ya Chikomyunizimu, kudza’nso ku mbali ya mitundu yonse ya lero lino mosasamala kanthu za mpangidwe uli wonse wa ndale za dziko umene iwo angakhale nao. Iwo akuchita ndi Mulungu mmodzi-modzi’yo Uyo amene anachita uphungu wake kulinga kwa Mfumu Sanakeribu wolamulira wa Ulamuliro wa Dziko wa Asuri, umene unalamulira dziko m’kati mwa zaka za zana lachisanu ndi chitatu ndi chisanu ndi chiwiri B.C.E. Mulungu mmodzi-modzi’yu, Yehova, wadziwikitsa maganizo ake ponena za mitundu yonse yomachita tsopano pa malo ochitikira zochitika a dziko a zaka zino za zana la makumi awiri, ndipo zimene iye waganiza ponena za iwo ndi zimene ife a mbadwo uno tiri otsimikizira kuziona m’nthawi yathu. Uphungu wake wa iye mwini umene waubvumbulira kwa ife. Timaupeza utalembedwa pa masamba a Baibulo, ndipo kodi ndani lero lino pa dziko lapansi amene ali ndi kukhoza kuswa uphungu Wake? Dzanja lake lamphamvu tsopano likutambasulidwa kuti lipereke uphungu wake wachiweruzo, ndipo ngakhale mitundu yonse itaphatikizidwa pamodzi singathe kuletsa dzanja lake ndi kupewa chionongeko.

MALONJEZO AKE ABWINO NGOTSIMIKIZIRIKA

36. Kodi n’chifukwa ninji lingaliro Lake ndi uphungu ponena za boma siliri malingaliro opanda pake?

36 Lero lino mtundu wa anthu ukuyang’anizana ndi chionongeko chochitidwa ndi Nkhondo Yachitatu ya Dziko ya nyuklea ndi kusakazidwa kwa malo okhala a munthu achilengedwe. Chotero bwanji ponena za uphungu wa Yehova wonena za boma la dziko? Kuyambira pa nthawi yeni-yeni imene munthu analakwa ndi kuyamba kuyenda pa njira ya boma lake losadalira pa Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu walingalira za boma la dziko kukhala chothetsera chokha cha mabvuto omaonjezereka’wo ndi zothetsa nzeru za mtundu wa anthu. Iye mwamsanga analangiza mobvomereza boma la pa dziko lonse lapansi lotero’lo, lokhala ndi iye mwini monga Wolamulira Wapamwamba-mwamba. Lingaliro lake ndi uphungu siziri malingaliro opanda pake a maganizo ake. Iye amadziwa kweni-kweni m’mene angakwaniritsire zimene iye waganiza ndi kulinganiza. Iye amadziwa m’mene lingaliro lake ndi uphungu zidzachitidwira, ndipo amadziwa amene adzakhala mapeto. Iye ali ndi mphamvu yonse ndi nyonga yaikulu imene ingam’chititse kufikira mapeto a ulamuliro amene’wo. Chifukwa cha chimene’cho iye ndiye ‘Uyo wolalikira chimariziro kuyambira pachiyambi.’ Iye ndiye Wolamulira amene amadziwa mapeto kuyambira pachiyambi. (Yesaya 46:10) Chifukwa cha kudziwiratu kwake kolondola kwa zimene adzachita, iye ndiye “Yehova, amene achita zinthu zimene’zi, kudziwika kuyambira kale.”—Machitidwe 15:17, 18; Amosi 9:12, NW.

37, 38. Kodi Genesis 3:15 ndi Chibvumbulutso 11:15-18 amasonyezanji ponena za chidziwitso cha Yehova ponena za boma?

37 M’bukhu leni-leni’lo limene Baibulo limayamba nalo pa Genesis 3:15, wolamulira Wamphamvuyonse wa chilengedwe chonse anadziwitsa lingaliro lake lalikulu ponena za boma la dziko limene lidzakhala chosowa chofunika kwambiri cha nzika zonse za dziko lapansi. M’bukhu leni-leni’lo limene Baibulo limatsiriza nalo, pa Chibvumbulutso 11:15-18, Wolamulira woyenerera wa mtundu wonse wa anthu akupereka kulongosola kolosera kwa kutenga kwake ulamuliro wake woimikidwa kwa nthawi yaitali’wo, kuti:

38 “Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba, ndipo panakhala mau akulu m’Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko wayamba kukhakhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake [“mbeu” ya mkazi yonenedweratu m’Genesis 3:15]: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi. Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yao, anagwa nkhope zao pansi nalambira Mulungu, nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu. Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneri’wo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko lapansi.”

39. Kodi ndi m’njira yotani Yehova ayenera kuchititsira ufumu wake kuonekera kwa ife?

39 Pamene tiyang’ana pa mikhalidwe ya dziko lero lino, kodi sitimaona kuti iri nthawi yabwino kwambiri kwa Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse yakuti aononge awo akuononga dziko lapansi? Ife sitikufuna kuti lionongedwe kufikira pa mkhalidwe wakuti anthufe sitingakhalepo’nso! Kuli kofunika kotheratu kuti “ufumu wa dziko” ukhale ufumu wa Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, limodzi ndi “Kristu wake” monga mnzake m’boma. Iye ayenera kulamulira monga mfumu kwamuyaya, ndipo ayenera kupangitsa ufumu wake kuonekera kwa tonsefe pa dziko lapansi mwa kuononga awo amene amaononga chuma chake, dziko lapansi. Chibvumbulutso 11:15 chimanena za uwo kukhala wotsimikizirika kotheratu, monga ngati kuti wachitika kale. Chilengezo chimene’cho chiri lonjezo laumulungu limene liri losaiwalika. Silidzalephera konse!

40. Kodi n’chifukwa ninji malonjezo ake, abwino kwambiri koposa aja a kwa Israyeli, ali otsimikizirika?

40 Liri lonjezo loperekedwa ndi Mulungu limene limasonyeza zabwino kwa anthu onse a mbadwo wathu amene amalaka-laka dziko la mtundu wa anthu lokhala pansi pa boma la dziko lonse loyendetsedwa ndi munthu amene mokhulupirika amasunga pangano lake. Zoona, iye amalonjeza zinthu pafupi-fupi zosakhulupiririka. Iye tsopano akulonjeza zinthu zazikulu kwambiri koposa zinthu zimene zinalonjezedwa kwa anthu a Yehova Israyeli, zaka zoposa mazana khumi ndi asanu Nyengo yathu Ino isanakhale. Komabe, Yehova ali wamphamvu mokwanira kukwaniritsa zinthu zabwino kwambiri zotero’zo.

41, 42. Kuti Yoswa 21:44, 45 alembedwe, kodi Yehova anachita ntchito zotani?

41 Kuti alanditse anthu ake okhalitsidwa akapolo’wo, Israyeli, kunafunikira kuti Yehova aleketse kugwira kwa Ulamuliro wa Dziko wa Igupto. Ndiyeno iye anayenera kugawanitsa madzi a Nyanja Yofiira kuti anthu ake olanditsidwa’wo aoloke pouma. Kenako iye anayenera kuchititsa madzi’wo kumiza asilikali ankhondo okwera pa akavalo ndi magaleta limodzi ndi Farao wao wodzitukumula’yo. Zaka makumi anai pambuyo pake Yehova anayenera kusonkhanitsa pamodzi madzi a liyambwe a Mtsinje wa Yordano m’malo mwakuti anthu ake aoloke kumka ku Dziko Lonlonjezedwa. Ndiyeno kwa zaka zisanu ndi chimodzi iye anayenera kuwamenyera nkhondo, akumagwetsa malinga a Yeriko ndi kugonjetsa mbali yaikulu kwambiri ya dziko’lo kotero kuti aligawire kwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli. Mosasamala kanthu za zopinga zonse zazikulu, Mulungu, amene samanama, anakwaniritsa lonjezo lake kwa anthu ake. Pochitira umboni cheni-cheni cha mu mbiri chimene’cho, Woweruza Yoswa, wolowa m’malo mwa mneneri Mose, analemba mau okumbukirika awa:

42 “Yehova anapereka adani ao onse m’manja mwao. Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.”—Yoswa 21:44, 45; 23:10.

43. Kodi ndi nthawi yotani imene ikuyandikira pamene tidzachitira umboni wakuti, “Zoonadi!”?

43 Tsopano tsiku lalikulu’lo likuyandikira pamene ziwalo za pa nthawi’yo zokhala ndi moyo za mbadwo wathu uno zidzakhala zokhoza kuchitira umboni kuti palibe lonjezo limodzi mwa malonjezo onse abwino a Mulungu onena za boma la dziko lolungama limene lalephera. Iye adzakhala atachititsa onse kukwaniritsidwa. Chotero ndi chidaliro choteratu mwa Iye tingayambe kupenda mosamalitsa malonjezo ake odabwitsa onena za boma la dziko lonse. Tidzakhalatu achimwemwe ngati potsirizira pake tingakhale mboni zake ndi kunena ponena za lonjezo lake kuti: “Zoonadi!”—Yesaya 43:9, 10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena