Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 3 tsamba 37-64
  • Masinthidwe a Dziko Onenedweratu Kufikira ku Ufumu wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masinthidwe a Dziko Onenedweratu Kufikira ku Ufumu wa Mulungu
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • LOTO LA MASINTHIDWE A ULAMULIRO WA DZIKO
  • ULAMULIRO WA DZIKO WA GRISI (WA MAKEDONIYA)
  • UFUMU WONGA CHITSULO
  • ULAMULIRO WINA WA DZIKO UKUPHATIKIZIDWAMO
  • MAPAZI A MBALI INA CHITSULO NDI MBALI INA DONGO
  • Kuimirira ndi Kugwa kwa Fano lalikulu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu a M’tsiku Lathu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kuneneratu Nthawi ya Ulamuliro wa Dziko
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Danieli
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 3 tsamba 37-64

Mutu 3

Masinthidwe a Dziko Onenedweratu Kufikira ku Ufumu wa Mulungu

1. Kodi nthawi zathu’zi zikumka ku masinthidwe akulu kopambana onse otani?

“NTHAWI ZOMASINTHA”—mau amene’wo amalongosola chimene mbadwo uno wakhala ukuchipyola chiyambire pa chaka choyamba nyengo yatsopano chimene’cho cha 1914 C.E. Mofanana ndi poona kachipangizo koonera maonekedwe osiyana-siyana pamene katembenuzidwa, mikhalidwe ya zinthu yasintha. Kodi masinthidwe’wo akhala kufuna—kwa angati a ife? Si tonsefe tiri okondwa. Timapeza chikondwerero chochepa m’kuchita mosemphana ndi malingaliro athu abwino kwambiri kotero kuti tisinthire ku masinthidwe osafunika. Nthawi ya kusintha kwakukulu kopambana ya zonse zimene anthu akumana nazo iri pafupi! Nthawi’yo yolinganizidwa, ndipo mwamwai kusintha kwakukulu kwambiri komachitika’ko kudzalamuliridwa, kaamba ka zabwino kopambana zosatha za onse okonda nthawi zabwino zokhazikika.

2. Kodi ndi ku magulu ankhondo otani, okhala ndi cholinga cha kusintha, kumene chitsutso chikuperekedwabe?

2 Kodi ndi motani m’mene tingakhalire otsimikira ponena za zimene’zi? Lero ino tikuona magulu ankhondo a ndale za dziko amphamvu amene akuonjezera nyonga chaka ndi chake okhoterera ku kusintha, nkhope ya dziko, kunena kwake titero. Iwo ali okhuturitsidwa maganizo kuti m’tsogolo mwa mtundu wa anthu muli m’manja mwao. Chimene ife, anthu achikati-kati, tikakonda kukhala nacho sichikukhudza magulu okonda kusintha osintha dziko. Chiwerengero chachikulu cha anthu chimakonda kwambiri njira yakale yochitira zinthu, yoyendetsera zinthu, limodzi ndi kuloledwa kwa mlingo wokulira wa kudzisankhira kwa munthu mwini. Magulu ankhondo a ndale za dziko amene amaumirira ku njira yochitidwa kwa nthawi yaitali yoyendetsera zochitika za anthu ali chikhalirebe amphamvu, ndipo kulimba-limbabe, ngakhale kuli kwakuti n’kulimba-limbabe, ngakhale kuli kwakuti n’kulimba-limba, ngakhale kuli kwakuti n’kulimba-limba kofooka, ku magulu ankhondo omakula-kula amene ali ndi cholinga cha kuzula ndi kusintha njira zakale zochitira ndi zabwino za mtundu wa anthu.

3. Kodi ndi motani m’mene magulu akulu awiri a ndale za dziko akuchitiriana lina ndi linzake?

3 Motero tiri ndi magulu awiri akulu kwambiri pa dziko lapansi lero lino. Kagulu kamodzi kofuna kusintha kwa boma kofulumira ndi kopanda chifundo kwachiukiro kamene mofala kamanenedwa kukhala chipani chokonda kusintha. Kagulu kenako, kamene kamakhala ndi chigwirizano champhamvu ndi zakale ndi mapangidwe ake ndi mipangidwe, moyenerera kwambiri kamachedwa chipani chosakonda kusintha. Modabwitsa, tingapeze kuti boma la mtundu limene linakhazikitsidwa mwa chipanduko chachiwawa limakhala losakonda kusintha pambuyo pa nthawi yaitali. Iro limagwirizana ndi osakonda kusintha. Kukuonekera kuti nkhondo yotha makani pakati pa okonda kusintha ndi osakonda kusintha ikuyandikira mofulumira. Pa tsopano lino magulu awiri a ndale za dziko’wo akuyesa-yesa kuyanjana lina ndi linzake. Mwakunja, iwo amaonekera kukhala aubwenzi kwa wina ndi mnzake. Koma nthawi zonse pamakhala mau obisidwa amene amasungidwa mu mtima pamene akukambitsirana. Kwakukulu-kulu, pa phata peni-peni pa zinthu, iwo ali osiyana. Iwo samasanganizika konse-monga momwe’di chitsulo cholimba sichingasanganizikire ndi dongo la woumba mbiya.—Danieli 2:43.

4. Nkhondo Yoyamba ya Dziko isanachitike kodi ndi mkhalidwe wa dziko wotani umene sunali kuyembekezeredwa?

4 Umene’wu ndi mkhalidwe watsopano ku mbiri ya anthu. Wayambika maka-maka m’zaka zathu za zana la makumi awiri. Nkhondo ya dziko ya 1914-1918 isanachitike, mkhalidwe umene ulipo pa dziko lonse lero lino ndithudi sunali kuyembekezeredwa, sunali kunenedweratu. Ngakhale atsogoleri a ndale za dziko amene afunsira alauli ndi openda nyenyezi sanalandire lingaliro liri lonse la zimene’zi kale’lo nkhondo ya dziko yoyamba isanasokoneze kudzikhutira kwao. Chitanganya cha anthu pokhala chitagawanika kwambiri mwandale za dziko monga momwe chiririmu lero lino, ndipo chakhala choncho chiyambire pa Nkhondo Yoyamba ya Dziko, ndithudi sikunaonedweretu ndi munthu wosaona patali. Koma kodi tikuzindikira kuti mkhalidwe wa ndale za dziko wa zochitika za anthu umene’wu unasonyezedweratu molosera zaka zoposa 2,580 zapita’zo, kapena pafupi-fupi m’chaka cha 605 Nyengo yathu Ino isanakhale?

5, 6. Kale’lo mu 605 B.C.E. kodi ndani amene sakananeneratu mkhalidwe wa lero lino?

5 Deti lakale limene’lo likatifikitsa ku nthawi pamene Babulo anali ulamuliro wa dziko lonse. M’kusonyeza ulamuliro wake wa pa dziko lonse Ulamuliro wa Dziko wa Babulo umene’wu unaononga mzinda wochuka pa dziko lonse wa Yerusalemu ndi kachisi wake woperekedwa ku kulambiridwa kwa Mulungu wa Ahebri, Yehova. Kalekale’lo kukanakhala kosatheka kwa mlauli, wopenda nyenyezi kapena munthu wina wamba kuneneratu mkhalidwe wa zinthu za m’nthawi yathu.

6 Zimene’zo ziyenera kubvomerezedwa ndi tonsefe!

7. Kodi kulinganiza njira ya boma la dziko n’kwa yani?

7 Chabwino, pamenepa, kodi tiri ndi umboni wotani wakuti ali yense kumwamba kapena pa dziko lapansi akukuneneratu? Pafupi-fupi kosakhulupiririka monga momwe kungaonekere, tiri nao umboni wotero’wo. Ukuchokera kwa Uyo amene analinganiza njira ya boma laumunthu kuyambira m’nthawi ya Babulo kufikira m’nthawi yathu. Umboni ulipo woti usonyeze kuti njira ya maulamuliro a dziko otero’wo inalinganizidwa ndi kuti njira yolinganizidwa kaamba ka iwo imene’yo kufikira tsopano inatsatiridwa m’mbiri ya anthu. Zonse’zi zinayenera kulowetsamo masinthidwe m’nthawi ndi nyengo ya zinthu zofunika kwambiri, ndipo’nso kuchotsedwa kwa nzera umodzi wa olamulira a dziko moyanja kagulu kena katsopano ka olamulira a dziko, ngakhale ka pfuko losiyana. Kanalowetsamo’nso kusintha kwakukulu kopambana ndi kusamutsidwa kwa ulamuliro wa dziko kumene kukuchitika m’mbiri yonse ya anthu, kusintha kumene kuli patsogolopa kaamba ka mbadwo uno wa mtundu wa anthu. Kulinganizidwa kolondola kotero’ko kwa njira ya boma la dziko la mtundu wa anthu kumafunikira munthu wina wauzimu, amene amadziwa kuyambira pachiyambi mapeto akulu. Kumafunikira Mulungu, osati wochedwa “mulungu wa dongosolo iri la zinthu,” koma Mulungu Wamphamvuyonse, Mulungu Wanzeru Zonse, Mlengi wa munthu.—2 Akorinto 4:4; Aroma 11:33, NW.

8, 9. (a) Kodi ndandanda ya mbiri ya anthu imene’yi inabvumbulidwa kwa yani? (b) Kodi iye ananenanji moyamikira kwa Magwero ake a chidziwitso?

8 Kulinganiza kwake njira’yo kapena kulinganizidwa kwa mbiri ya anthu kunayenera kubvumbulidwa kwa wina wake pa dziko lapansi, kuti iye alembe ndi kuzinsunga m’zolembedwa kotero kuti tonsefe titembenukire’ko. Wina wake amene’yo anali mnyamata Wachihebri wochedwa Danieli. Ngati iye akanapanda kukhala wolambira wa Mulungu Wamphamvuyonse ndi Wanzeru Zonse, chibvumbulutso chimene’chi sichikanakhala konse chitapangidwa kwa iye. Iye anapeza tanthauza la bvumbulutso’lo lopangidwa kwa iye. Ndicho chifukwa chake Danieli, m’bukhu lake la ulosi, analemba mau othokoza mwachiyamikiro kwa Magwero a Chidziwitso chake Aumulungu amene’wa kuti:

9 “Limekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zake; pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira. Iye adzabvumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mu mdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye. Ndikuyamikani, ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mpahamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano; ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.”—Danieli 2:20-23.

10, 11. Pamene anauzidwa loto lake, kodi Nebukadinezara ananenanji ponena za Mulungu?

10 Pamene mneneri Danieli anabvumbulira wolamulira woiwala-iwala’yo wa Babulo “mlandu wa mfumu” woiwalidwa’wo, m’tsogoleri wa ndale za dziko wamkulu kopambana wa pa nthawi’yo amene’yu, Nebukadinezara, anali woona mtima mokwanira kubvomereza kuti Mulungu Wam’mwamba-mwamba yekha akanatha kupanga bvumbulutso lotero’lo ponena za m’tsogolo mwamdima ndi mobisidwa pa nthawi’yo. Mwaulemu kwambiri kwa Danieli iye anati:

11 “Ndithudi Mulungu wa amuna inu ndiye Mulungu wa milungu ndi Mbuye wa mafumu ndi Wobvumbula zinsinsi, chifukwa chakuti unali wokhoza kubvumbula chinsinsi chimene’chi.”—Danieli 2:47, NW

12. Kodi ndi motani m’mene atsogoleri a ndale za dziko a lero lino amasiyanira ndi Nebukadinezara?

12 Kodi ndi wolamulira wa ndale za dziko uti lero lino, atatha kuwerenga cholembedwa cha Danieli chonena za chinsinsi chobvumbulidwa’cho ndiyeno n’kuchiyerekezera ndi njira ya boma la dziko lonse kufikira tsopano, akapanga kubvomereza kotero’ko konena za Mulungu wa Danieli ndi wa anzake atatu Achihebri? Mosaphula kanthu tikufuna-funa wolamulira wa ndale za dziko woona mtima ndi wodzichepetsa wotero’yo amene amasonyeza kuti iye akulola chinsinsi chobvumbulidwa kwa Danieli’cho kutsogoza njira ya kachitidwe kake. Chifukwa cha chimene’cho kusintha kwa pa dziko lonse kumene kuyenera kudzetsedwa posachedwapa ndi Wosintha Waumulungu wa nthawi ndi nyengo kudzawafikira onse ndi mphamvu yoononga.

13. Kodi Nebukadinezara anadandaulira yani za loto lake loiwalidwa’lo?

13 Kodi n’chiani chimene chinakhutiritsa mnereri Danieli kudza’nso mtsogoleri wa ndale za dziko wochuka wa pa nthawi’yo, Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo, kuti Uyo amene akanatha kupereka kuoneratu kotero’ko kwa zaka zikwi zochuluka za mbiri ya anthu ndipo motero “kulengeza mapeto kuyambira pachiyambi” anayenera kukhala Mulungu Wamphamvuyonse? (Yesaya 46:10, Authorized Version) Zinali zofunika zosatheka ndi anthu zimene zinapinga bvumbulutso lotero’lo. M’chaka chachiwiri cha ulamuliro wake monga wogonjetsa Yerusalemu ndi kachisi wolambirira wa Yehova, iye analota loto. Pouka kuchokera ku tulo, iye sanalikumbukire. Iye anabvutika maganizo kwambiri ndi nkhani’yo chifukwa chakuti loto loiwalidwa’lo linaonekera kukhala likupereka uthenga wofunika kopambana kwa iye. Iye anaika pa chiyeso chachikulu kwambiri openda nyenyezi ndi ansembe ake ochita matsenga mwa kupempha kuti iwo ayenera, osati kokha kumasulira loto’lo, koma, choyamba, kulikumbutsa maganizo a mfumu. Chifukwa chakuti iwo anacha pempho limene’lo kukhala losayenera kotheratu, Mfumu Nebukadinezara analamula kuti ayenera kuphedwa monga onyenga m’kuneneratu kwao kolosera. Koma chakuti iye anali wosokonezeka maganizo m’kupanga chosankha chotero’cho ngakhale katswiri wophunzira za maganizo wochuka kopambana wa lero lino angabvomereze.

14. Kodi ndi motani m’mene Danieli anapezera chidziwitso chofunika chopulumutsa moyo’cho?

14 Kufulumira kwambiri kumene kulipo tsopano kunayambukira mneneri Danieli, chifukwa chakuti anali kulingaliridwa kukhala wopambana pakati pa amuna anzeru a Babulo. Iye anapempha mkulu wa akalinde a mfumu chifukwa chake iye anadza .kudzapha iye ndi atsamwali ake atatu Achihebri, Hananiya, Misaeli ndi Azariya. Atauzidwa, Danieli anapempha kuyembekezera kwa tsiku limodzi lokha la nthawi ya kuphedwa kwa amuna anzeru a Babulo. Iye anali ndi chidaliro chakuti palibe chiri chonse chimene chinali chosatheka kwa Mulungu wake, Yehova. Mapemphero ophatikizidwa pamodzi a Danieli ndi atsamwali ake atatu Achihebri’wo sanatsimikizire kukhala akulunjikitsidwa kwa mulungu wonyenga ndi wongoyerekezera. Ponse pawiri loto la Nebukadinezara ndi tanthauzo lake lofunika pa dziko lonse’lo zinabvumbulidwa kwa Danieli “m’masomphenya a usiku” olosera otumizidwa ndi Mulungu wake Yehova. (Danieli 2:19) Atadalitsa Wochita zinthu zosatheka ndi anthu’yo ndi kupereka thamo kwa Iye, Danieli anafunsa Arioki mkulu wa akalinde a Mfumu Nebukadinezara kukam’perekeza kwa mfumu yobvutika maganizo ya Ufumu wa Babulo.

15, 16. Kodi chimene’chi chinakakamiza kuyesedwa kwa yani, ndipo kodi Danieli anapereka kwa yani thamo?

15 Miyoyo ya Danieli ndi atsamwali ake atatu Achihebri inali pa ngozi. Ngati sakanakumbutsa mfumu’yo loto loiwalidwa’lo ndiyeno, pa maziko amene’wa, kupereka kulongosola kukhutiritsa, iwo akanayenera kuphedwa limodzi ndi amuna onse anzeru a ku Babulo. Zimene’zi zinakakamiza mayeso, osati a munthu, koma a Mulungu weni-weni wa chilengedwe chonse, pakuti openda nyenyezi a Babulo ndi ansembe ochita matsenga anali atalephera kale. Mwa chimene Danieli tsopano anabvumbulira wolamulira wa Ulamuliro wa Dziko wa Babulo, iye anakhala mboni ya Yehova yapadera, imodzi ya mboni za Yehova za Chikristu chisanakhale. (Yesaya 43:10-12; 44:8) Monga chitsanzo chabwino kwambiri cha mboni za Yehova zonse zamakono, Danieli sanadzitengera thamo kaamba ka zimene iye tsopano anali atangotsala pang’ono kuzibvumbulira m’tsogoleri wa ndale za dziko wochuka kopambana wa dziko, koma anapereka ulemerero kwa ‘Mulungu weni-weni wa kumwamba’ mwa kunena kuti:

16 “Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuchiululira mfumu; koma kuli Mulungu Kumwamba wakubvumbulutsa zinsinsi: Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m’mtima mwanu pakama panu, ndi awa.”—Danieli 2:27, 28.

17. Kodi ndi motani m’mene Yehova anakuzira mphamvu yake monga “Wobvumbula zinsinsi”?

17 Ngati loto la Nebukadinezara likanagokhala loto wamba, lopanda tanthauzo longa amene amachitika kwa ali yense, silikanalembedwa m’Mau a Mulungu, Baibulo. Linali loto lokhala ndi cholinga lotumizidwa ndi Mulungu “wakubvumbulutsa zinsinsi,” koma likanakhala lopanda tanthauzo likanapanda kufotokozedwa. Ndipo komabe, Mulungu Wamphamvuyonse wa kumwamba anafafaniza kukumbukiridwa konse kwa loto’lo m’maganizo mwa Nebukadinezara. Kodi Yehova sanali kulepheretsa chifuno chake m’kuchita chimene’chi, m’kupangitsa maganizo a mfumu’yo kukhala opanda kanthu? Kutali-tali. M’malo mwake, iye anali kukhazikitsa maziko okulitsira mphamvu yake yoposa yaumunthu. Iye anali kupangitsa bvuto limene mulungu yekha, Mulungu woona yekha, akanalithetsa.

18. Kodi ndi motani m’mene mfumu inakakamizikira kutsimikizira kuti Mulungu aliko?

18 Mwa njira yake yochitira ndi nkhani yokhala ndi kufunika kwa pa dziko lonse imene’yo, Yehova anakupangitsa kukhala kofunika kuti umboni wa mphamvu yaumulungu uperekedwe kwa “mfumu ya mfumu” ya pa dziko lapansi ya m’nthawi yakale imene’yo. Mfumu’yo inachititsidwa kugwiritsira ntchito ulamuliro wake wotheratu ndi kufuna kukumbutsidwa loto’lo ndi kumasulira kwake. Iye anakufuna, ndipo anayenera kukulandira pamene kunaperekedwa kwa iye mozizwitsa. Kaya Nebukadinezara anakukonda kapena ai, iye anapeza zimene iye anali kufuna. Motero, pa kuyambika kwa ulamuliro wosatsutsidwa wolamulidwa ndi Ulamuliro wa Dziko wa Babulo, m’tsogoleri wa ndale za dziko wamkulu kopambana amene’yu anatsimikiziridwa kuti kuli Mulungu, kuti Mulungu aliko!- Danieli 2:1, 28.

LOTO LA MASINTHIDWE A ULAMULIRO WA DZIKO

19. Kodi n’chiani chimene Yehova adzasonyeza atsogoleri a ndale za dziko ponena za kucha dziko lapansi kukhala lao?

19 Pali mwambi wakale wakuti: “Munthu amalinganiza, koma Mulungu amatsimikizira chimene chidzachitika.” Zimene’zi ziri choncho ponena za zochitika za dziko. Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi ali wokondweretsedwa kweni-kweni ndi zochitika za dziko pa dziko lathu lapansi’li. Iye ali ndi chikondwerero pa zimene zikuchitika pano, chifukwa chakuti dziko lapansi pa limene tikukhalapo ndi Lake, osati malo oyenerera a ulamuliro wa Chikomyunizimu kapena mademokrase okhala ndi ndalama zoyendetsera bizinesi (capital). Chakuti zabwino Zake pa dziko lapansi ziri pa malo oyambirira ndipo zidzafunsiridwa ndi kusamaliridwa potsirizira pake, Yehova anazisonyeza m’loto limene mneneri wake Danieli analibvumbulira Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo pachimake pokondweretsa pa ulamuliro wake, pamene unali kuyedzamira ku kupanga dziko lonse lapansi kukhala loyenera kugonjetsedwa nawo. Momvetsera kopambana, mfumu’yo inamvetsera Mau a Mulungu ndipo sinawalingalire mwamasewera, pamene mneneri wa Yehova Danieli anapitiriza kunena kuti:

20. Kodi loto limene Danieli anakumbutsa mfumu linali lotani?

20 “Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikulu. Fano’li linali lalikulu, ndi kunyezimira kwake kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ake anali oopsya. Fano iri tsono, mutu wake unali wagolidi wabwino, chifukwa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa, miyendo yake yachitsulo, mapazi ake mwina chitsulo mwina dongo. Munali chipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fano’li pa mapazi ake okhala chitsulo ndi dongo, nuwaphwanya. Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezeka’nso malo ao; ndi mwala udagunda fano’wo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.”—Danieli 2:31-35.

21. Kodi ndi motani m’mene Mulungu motero anasonyezera kuti iye anadziwa “mapeto” kuyambira “pachiyambi”? ?

21 Tingathe kuyerekezera m’mene Mfumu Nebukadinezara anadzidzimukira ndi kulongosola kouziridwa kumene’ku. Kunayenerana ndendende ndi loto’lo monga momwe analionera! Fano lalikulu limene’li limene linali ndi kunyezimira kothobwa m’maso kotero’ko linali lija limene linachititsa kuopa ndi mantha, ndipo linali loopsya kaamba ka ukulu wake. Kodi ndi motani m’mene iye akanaliiwalira? Koma iye anaiwala! Ngati kulota’ko sikukanakumbukiridwa, uthenga umene linalinganizidwira kupereka ukanataika kosatha. Pokhala lotumizidwa mwachionekere ndi mphamvu yaumulungu, kwa uyo amene pa nthawi’yo anali “mfumu ya mafumu” a dziko, liyenera kukhala linali ndi uthenga wa pa nthawi yake wokhala ndi chotulukapo cha pa dziko lonse. Mulungu yekha akanatha kutulutsa m’masomphenya a usiku kwa Danieli zimene zinafafanizika kotheratu m’maganizo a Nebukadinezara. Koma kodi Mulungu mmodzi-modzi’yo akanatha kumasulira kulongosola tanthauzo la loto loiwalidwa’lo? Ndithudi Mulungu amene anaumba ndi kutumiza loto’lo ayenera kudziwa chimene iye anatanthauza nalo. Iye akanatha kufotokoza chimene chifanizo chonga munthu’cho chinatanthauza, kuyambira kumutu mpaka kuphazi. Mwa kupereka loto lathunthu, limene linabvumbula m’mene chifanizo chokhala ndi tanthauzo’cho chinachotsedwera, iye anasonyeza kuti Iye anadziwa ndipo anali “kulengeza chimariziro kuyambira pachiyambi.” Chotero ‘pitirizatu,’ O Danieli!

22. Kodi n’chifukwa ninji ife tiri okondweretsedwa kwambiri ndi loto’lo koposa m’mene inaliri mfumu’yo?

22 Kungobvumbula loto lolosera’lo sikunali kokwanira. Kufotokozedwa kwake’nso ndiko kumene kukanapangitsa Danieli ndi amuna ena onse anzeru a Babulo kusiyidwa osaphedwa. Danieli analandira kulongosoledwa kwa chifanizo cha m’loto’cho, koma kodi kumasulira kwake kukakhutiritsa Mfumu Nebukadinezara, wolamulira wachikunja amene anaononga kachisi wa yehova pa Yerusalemu, kukhala kolondola? Kodi ndiko kumasulira kumene kumatikhutiritsa ife lero lino, kusangokhala kwabwino ndi koyenera koma’nso kogwirizana ndi ndi Mau ena onse obvumbulidwa a Mulungu, Baibulo louziridwa? Ife lero lino, amene mwachionekere tikukhala ndi moyo pa nthawi ya “mapeto” a kukwaniritsidwa kwake ayenera kukhala okondweretsedwa nawo kwambiri koposa Nebukadinezara, amene anali kukhala pa nthawi ya “chiyambi” cha kukwaniritsidwa kwa loto’lo. Iye sanachititsidwe mantha ndi kuphwanya kwa pa dziko lonse kumene kuyenera kuchitika. Ife tikutero!

23. Kodi Danieli ananena kuti mutu wa golidi wa fano’lo unaphiphiritsira chiani? Chifukwa ninji?

23 Arioki, mkulu wa akalinde a Nebukadinezara, angakhale ataleka kugwiritsa lupanga lake pamene Danieli anapitirizabe kunena kwa Mkulu wa gulu la ankhondo’yo kuti: “Iri ndi loto; kumasulira kwake tsono tikufotokozerani mfumu. Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemu; ndipo pali ponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m’mlengalenga, m’dzanja lanu, nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutu’wo wagolidi.”—Danieli 2:36-38.

24. Chotero, pamenepa, kodi “fano’lo” linayamba ndi woyambitsa Babulo?

24 Kuuzidwa kwa Nebukadinezara pa chiyambi cha kulongosoledwa kwa fano limene’lo kuti kunam’lowetsamo ndipo kunayamba kweni-kweni ndi iye kuyenera kukhala kutaonjezera chikondwerero chake m’kumasuliridwa kwa loto lonse’lo. Kuuzidwa kwake kuti iye anaimiridwa ndi mutu wopangidwa ndi chitsulo cha mtengo wapatali kopambana chodziwika pa nthawi’yo sikukanachitira mwina koposa kum’kondweretsa ndi kum’pangitsa kuona kuti ulemu woyenera unali kuperekedwa kwa iye. Mutu wa golidi’wo moyenerera unaimira mfumu, “mfumu ya mafumu” imene Mulungu wa kumwamba anailola kukhala wolamulira wa dziko, wolamulira wa Ulamuliro wa Dziko wa Babulo. Chotero chinthu chimene chinaphiphiritsiridwa ndi fano’lo la zitsulo zosiyanasiyana silinayambe ndi Nimrode Mkusi wa pfuko la Hamu, amene anakhazikitsa Babele woyambirira kapena Babulo zaka zoposa 1,500 zapita’zo.—Genesis 10:8-10; 1 Mbiri 1:10.

25. Kodi linayamba ndi Ulamuliro wa Dziko Woyamba, kapena wachiwiri?

25 Ndipo’nso fano lophiphiritsira’lo silinayambe ndi Ulamuliro wa Dziko wa Igupto, ufumu Wachihamu umene unali Ulamuliro Woyamba wa Dziko wolembedwa m’mbiri ya Baibulo. (Genesis 10:6; 13, 14; 12:11 kufikira 13:1; Salmo 78:51; 105: 23, 27; 106: 21, 22) Ndipo’nso, fano lophiphiritsira’lo silinayambe ndi Ulamuliro wa Dziko wa Asuri, ufumu Wachisemu umene unakhala Ulamuliro Wachiwiri wa Dziko wa mbiri ya Baibulo. Genesis 10:21, 22; 2:14; 25:18; 2 Mafumu 15:19-22) Mu 632 B.C.E. Nebukadinezara anagwirizana nawo m’kugubuduza ulamuliro wa Dziko wa Asuri ndipo motero kukhazikitsa Ufumu watsopano wa Babulo umene unakhala monga Ulamuliro Wachitatu wa Dziko wa mbiri ya Baibulo.—Nahumu 2:8 mpaka 3:18; Zefaniya 2:13.

26. Kodi n’chifukwa ninji “fano” linagwira ntchito kuyambira pa kuonongedwa kwa Yerusalemu kumkabe m’tsogolo?

26 Pafupi-fupi zaka makumi awiri mphambu zisanu pambuyo pake, Mfumu nebukadinezara atagwiritsiridwa ntchito monga chipangizo choonongera Yerusalemu wosakhulupirika’yo, mau a mneneri Danieli anagwira ntchito: “Pali ponse pokhala ana a anthu Iye [Mulungu wa kumwamba] anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m’lengalenga, m’dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse.” (Danieli 2:38) Zinali choncho, chifukwa chakuti, pa kuonongedwa kwa Yerusalemu kochititdwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E., ufumu weni-weni wa Yehova Mulungu unaleka kukhalapo pa dziko lapansi.—1 Mbiri 29:23; 2 Mbiri 36:17-21.

27. Kodi mtapo uli wonse wa “fano’lo unaphiphiritsira chiani, mwandale za dziko?

27 Monga momwe Danieli ananenera kwa Nebukadinezara, “inu ndinu mutu’wo wagolidi,” fano lathunthu lachitsulo’lo linaphiphiritsira mpambo wa mafumu kapena olamulira a dziko. Kweni-kweni, “mutu wagolidi” unaphiphiritsira zambiri koposa Nebukadinezara iye mwini. Unaphiphiritsira mzera wa mafumu olamulira umene unakhazikitsidwa mwa iye. Motero mutu wagolidi wathunthu, unaphiphiritsira, Nebukadinezara iye mwini, kenako mwana wake wamwamuna wamkulu Evili Merodaki, kenako Nabonidasi mkamwini wa Nebukadinezara, ndipo potsirizira pake Belitsazara chidzukul cha Nebukadinezara. (2 Mafumu 25:27-30; Yeremiya 52:31-34; Danieli 5:10, 11, 18, 22) Mzera wa mafumu umene’wu unaima ngati woimira wa Ulamuliro wa Dziko wa Babulo. Chifukwa cha chimene’cho, mpambo wa zitsulo zinai m’fano la loto la Nebukadinezara umaimira mpambo wa maulamuliro a dziko amene achita ulamuliro wa dziko popanda chidodometso chochokera kwa Mulungu (kaya ufumu wophiphiritsira wa pa dziko lapansi kapena ufumu wophiphiritsiridwa wa kumwamba). Kumasulira loto’lo kwa Danieli kumatsimikizira nsonga imene’yi.

28, 29. Kodi n’chifukwa ninji ufumu wotsatirapo, wotsikirapo kwa Babulo, sunachulidwe?

28 Posonyeza ulamuliro wa Dziko umene unayenera kuchitidwa ndi otsatira Ulamuliro wa Dziko wa Babulo, Danieli anapitirizabe ndi kumasulira kwake, akumanena kwa Nebukadinezara, “mfumu ya mafumu” kuti: “Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi.”—Danieli 2:29.

29 Danieli sanachule dzina ufumu umene’wo, “wochepa” kwa Nebukadinezara, umene unayenera kutsatirapo mwamsanga Ulamuliro wa Dziko wa Babulo utangochoka. Kuuchula kukanachititsa Ulamuliro wa Dziko wa Babulo kukhala maso motsutsa wokhumbira ulamuliro wa dziko wam’tsogolo. Koma kuchokera m’maulosi oyambirira a Yesaya (13:1-17; 21:2-9) Danieli angakhale atadziwa kuti Amedi, wogwirizana naye wa Aperisi, akalowetsedwamo m’kuchotsa Babulo pa malo okwezeka a ulamuliro wa dziko.

30. Kodi ndi motani m’mene Danieli akanadziwira wogubuduza Babulo?

30 Danieli akanatha’nso kudziwa kuchokera mu Yesaya 44:24 mpaka 45:7 kuti Yehova akagwiritsira ntchito munthu wochedwa Koresi, amene anatsimikizira kukhala Mperisi, kudzetsa kubwezera kwaumulungu pa Ulamuliro wa Dziko wa Babulo kaamba ka kuononga Yerusalemu ndi kachisi wake wa kulambiriramo Yehova. (Yesaya 46:11) Monga wophunzira wa ulosi wa Yeremiya, Danieli, anadziwa’nso kuti Amedi anali apadera m’kuzingidwa kotsirizira kwa Babulo ndipo akakhala ndi mbali m’kugubuduza wozunza anthu ake amene’yu. (Yeremiya 51:28; Danieli 9:2) Koma Danieli pa nthawi imene’yo sanaulule chidziwitso chimene’chi kwa Nebukadinezara, amene sakanatha kukhalabe ndi moyo kudzaona kugubuduza kumene’ku. Kodi n’chifukwa ninji iye ayenera kupangitsidwa kukhala wodera nkhawa?

31. Kodi ndi motani m’mene Danieli anakhalira ndi mwai wa kusonyeza wolowa m’malo mwa Babulo?

31 Mneneri Danieli anali ndi mwai wa kusonyeza, titero kunena kwake, “ufumu” kapena ulamuliro wa dziko umene unaphiphiritsiridwa ndi mkuwa wa loto la fano. Pamenepa panali pa usiku wa m’mphakasa mu 539 B.C.E. pamene chidzukulu cha Nebukadinezara, Mfumu Belitsazara, anali kuchita phwando lachifumu limodzi ndi akulu-akulu ake chikwi m’kati mwa mzinda wozingidwa’wo wa Babulo. Pa chimake pa phwando’lo dzanja lozizwitsa linalemba pa khoma mau amphamvu akuti: “Mene Mene Tekel Ufarsin.” Monga chithandizo chotsirizira, Mfumu Belitsazara woopsyedwa’yo anayenera kupempha Danieli kumasulira mau olembedwa ndi manja pa khoma amene’wa. M’kulongosola liu lotsirizira’lo “Ufarsin,” limene liri liu la zochuluka la “Peres,” Danieli anati kwa Belitsazara: PERESI, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.” Usiku womwe’wo ozinga’wo analowa m’Babulo, Mfumu Belitsazara anaphedwa, ndipo Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi unakhazikitsidwa. Popeza kuti Amedi ndi Aperisi anali mbadwa za Yafeti, ulamuliro wa dziko tsopano unasintha kuchoka ku pfuko la Semu kumka ku pfuko la Yafeti.—Danieli 5:1-31; 6:12; Estere 1:19.

32. Kodi Amedi ndi Aperisi anali “otsika” kwa Babulo m’njira yotani?

32 Monga momwe siliva aliri wotsika kwa golidi, Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi unali wotsika kwa Babulo. M’njira yotani? M’chakuti sunadzikweza pamwamba kwambiri monga momwe unachitira Ufumu wa Babulo, umene unaononga mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake wa kulambiridwa kwa Yehova. Motero mfumu ya Babulo, Nebukadinezara, anaonekera kukhala akudzikweza pamwamba pa Yehova Mulungu, amene dzina lake linali kuchulidwa pa mzinda wa Yerusalemu kumene mafumu a mzera wachifumu wa Davide anakhala pa “mpando wachifumu wa Yehova.” (1 Mbiri 29:23; Yesaya 14:4-14) Ndipo’nso, ndi kugubuduzidwa kumene’ko kwa ufumu weni-weni wa Yehova m’chaka cha 607 B.C.E., nyengo ya zaka 2,520 yochedwa “nthawi za Amitundu” kapena “nthawi zoikidwiratu za mitundu” inayamba. (Luka 21:24, AV; NW) M’malo mwa kuyesa “kufanana ndi Wam’mwamba-mwamba’yo,” Mfumu Koresi wogonjetsa Babulo anazindikira Umulungu wa Yehova.

33. Kodi ndi motani m’mene Koresi anagwirizanitsira njira yake ndi ya ulosi wa Yesaya?

33 Mozindikira chifuniro cholongolosedwa cha Yehova, Mfumu Koresi anayesa kugwirizanitsa njira yake ya kachitidwe ndi zimene Yehova ananeneratu ponena za iye mu Yesaya, chaputala cha makumi anai mphambu zinai ndi makumi anai mphambu zisanu. Chotero, m’537 B.C.E., iye analola gulu la Aisrayeli odzipereka ndi atumiki ao kutuluka m’ndende yao Yachibabulo ndi kubwerera ku dziko la kwao, kukamanga’nso mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake woyera. Koma ufumu weni-weni wa Yehova sunakhazikitsidwe’nso kumene’ko, wokhala ndi mbadwa yachifumu ya Mfumu Davide yomakhala pa “mpando wachifumu wa Yehova” pa Yerusalemu.—2 Mbiri 36:20-23; Ezara 1:1 mpaka 2:2.

ULAMULIRO WA DZIKO WA GRISI (WA MAKEDONIYA)

34. Kodi n’chiani chimene womasulira Danieli ananena ponena za wolowa m’malo mwa Amedi ndi Aperisi?

34 Mosasamala kanthu za malingaliro ake m’njira ya chifundo kwa anthu osankhidwa a Yehova, Ulamuliro wa Dziko wa Perisi sunakhalebe kufikira m’zaka zathu zino za zana la makumi awiri. Ponena za wolowa m’malo wotsatirapo wa Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi, mneneri Danieli anapitirizabe kunena ndi Nebukadinezara kuti: “Ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi.”—Danieli 2:39.

35. Kodi ndi liti pamene Danieli anadziwa kudziwika kwa wolowa m’malo mwa Amedi ndi Aperesi?

35 Mau amene’wo akasonyeza kuti “ufumu” wachitatu,” wonga mkuwa, kapena ulamuliro wa dziko ukakhala wofutukuka kwambiri koposa kaya Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi kapena wa Babulo. Popeza kuti mkuwa uli chitsulo cha mtengo wapatali mocheperapo, chotsikirapo kwa siliva, ulamuliro wa dziko unalinkudza umene’wu ukakhala wotsikirapo ku Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi. M’mbali imene’yi sunalemekezedwe ndi mwai uli wonse wofanana ndi uja wa kulanditsa anthu a Yehova okhalitsidwa akapolo ku undende wao m’Babulo. M’nthawi ya chidzukulu cha Nebukadinezara, Mfumu Belitsazara, Danieli womasulira maloto’yo anazindikira amene akakhazikitsa ulamuliro wa dziko “wachitatu” wonga mkuwa umene’wo. Akakhala wogonjetsa Wachigriki. Palibe umboni wakuti Danieli anaulula chidziwitso chimene’chi chonena za masiku a m’tsogolo kwambiri kwa Mfumu Belitsazara.

36. Kodi ndi motani m’mene kugubuduzidwa kwa Amedi ndi Aperisi kunaphiphiritsiridwira kwa Danieli?

36 M’kulongosola loto lolosera limene linatumizidwa kwa Danieli m’limene iye anaona nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri ikugonjetsedwa ndi mbuzi yamanyenje ya nyanga imodzi, mngelo woyera wa Yehova anati: “Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziwiri ndizo mafumu a Mediya ndi Perisiya. Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene [kapena, Grisi], ndi nyanga yaikulu iri pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba. Ndi kuti zinaphuka zinai m’malo mwake mwa iyo itatyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtundu’wu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.”—Danieli 8:20-22.

37. Kodi n’zachamuna zotani zimene “mfumu yoyamba” ya Ufumu wa Grisi inachita?

37 Chotero, zaka zoposa mazana awiri pasadakhale, kunanenedweratu kuti “ufumu” umene unaphiphiritsidwa ndi mimba ndi chuuno za mkuwa za fano la m’loto’lo ukakhala Ulamuliro wa Dziko wa Grisi. ‘Mfumu yake yoyamba’ inatsimikizira kukhala wogonjetsa dziko, Alexander III wa Makedoniya, amene anayamba kugonjetsa Ufumu wa Perisiya. Mu 334 B.C.E. iye anachititsa kugonjetsedwa kotheratu kwa mfumu wa pa nthawi’yo ya Perisiya nakhazikitsa Ulamuliro wa Dziko wa Grisi (Makedoniya). Mu 332 B.C.E. Alexander Wamkulu analowetsa chigawo cha Yudeya, kuphatikizapo Yerusalemu, mu ulamuliro wake. Pambuyo pake, Igupto anagwera kwa iye, ndipo mzinda wa Alesandriya unakhazikitsidwa m’menemo m’malo mwakuti ukumbutse dzina lake. Dooko latsopano la Igupto limene’li linakhala lolemera kwambiri, ndipo linafikira kukhala ndi chiwerenegero cha Ayuda ochulukirapo.

38. Kodi ndi motani m’mene kunakhalira kotheka kuwerenga Baibulo lathunthu m’Chigriki?

38 Chifukwa cha zigonjetso zake zonse mpaka kukafika ku Mtsinje wa Indus wa India ndi kutsika mpaka ku Igupto, ndi kukhazikitsa kwake magulu a asilikari ankhondo m’maiko ogonjetsedwa’wo, Chigriki chofala cholankhulidwa ndi asilikali ankhondo a Alexander Wamkulu chinakhala chinenero cha m’mitundu yonse cha pa nthawi’yo. Icho chinatumikira monga njira yolankhulirana ya mitundu yonse, ndipo m’zaka za zana lachitatu B.C.E. Ayuda olankhula Chigriki a Alesandriya, Igupto, anayamba kutembenuza Malemba ouziridwa Achihebri kuwaika m’Chigriki chofala. Chitsogozo chimene’chi chinatsatiridwa ndi olemba ouziridwa amene anatulutsa mabukhu a Malemba Achikristu makumi awiri mphambu asanu ndi awiri, kuyambiri pa Mateyu kukafika ku Chibvumbulutso. Mwa njira imene’yi kunakhala kothekera kuti Baibulo louziridwa lonse lathunthu liwerengedwe kuli konse ndi olankhula ndi kuwerenga Chigriki chofala.

39. Kodi ndi motani m’mene “mafumu anai” a njira Yachigriki anabukira monga momwe kunalosereredwa?

39 M’chaka cha 323 B.C.E., Alexander Wamkulu, woimiridwa ndi “nyanga yaikulu” ya tonde wa mbuzi wamanyenje’yo, anakafera ku Babulo, malikulu a pa nthawi ina a Ufumu wa Babulo. M’kupita kwa nthawi ufumu wake waukulu’wo unagawanidwa ndi akazembe ake ankhondo Achigriki anai. Kumeneku kunachititsa maufumu anai a Ahelene kapena opangidwa kukhala Achigriki. Yudeya ndi Yerusalemu potsirizira pake anakhala mbali ya ufumu woyambidwa ndi Kazembe wankhondo Seleucus I Nicator. Ndithudi, palibe uli wonse wa maufumu anai a Ahelene amene’wa umene unalingana ndi ufumu waukulu wa Alexander Wamkulu. Modabwitsa’di, ulosi’wo unakwaniritsidwa kwakuti mwa “nyanga yaikulu’yo” (Alexander Wamkulu) mukatuluka ‘nyanga zinai’ (maufumu anai a Ahelene), koma popanda uli wonse wa anai’wo wokhala ndi mphamvu ndi ukulu wa ufumu wa Alexander. Komabe, maufumu ang’ono anai amene’wa pamodzi anasungabe kulamulira kwa Ulamuliro wa Dziko wa Grisi, woimiridwa ndi mbali ya mkuwa ya fano.

UFUMU WONGA CHITSULO

40. Kodi ndi motani m’mene Ulamuliro wa Dziko wa Roma unakhazikitsidwira pofika m’30 B.C.E.?

40 Nthawi inapitabe mpaka kudzafika m’zaka za zana loyamba za nyengo yathu Ino isanakhale. Nthawi inafika yakuti “Mulungu wa kumwamba,” Yehova, asinthe nthawi ndi nyengo ndi kuchotsa mafumu ndi kukhazikitsa mafumu kuti adzetse ulamuliro wa dziko watsopano. (Danieli 2:19, 21) Roma, Italiya, tsopano unali ulamuliro umene unalinkudza wa ndale za dziko woulingalira. M’chaka cha 63 B.C.E. Kazembe Wankhondo Wachiroma Pompey analanda Yerusalemu ndipo anafutukulira ulamuliro Wachiroma pa Yudeya. M’chaka cha 30 B.C.E. chigonjetso chotheratu chinachitidwa pa wotsirizira wa maufumu anai a Ahelene, ndipo Igupto anakhala chigawo cha Aroma. Kumene’ku kunasonyeza kukhazikitsidwa kwa Ulamuliro wa Dziko Wachiroma m’chaka cha mazana asanu kudza makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha “nthawi za Akunja” kapena “nthawi zoikidwiratu za mitundu.” Yerusalemu anapitirizabe kukhala wopanda mfumu ya mzera wachifumu wa Davide wa pfuko la Yuda. “Mpando wachifumu wa Yehova” sunali’nso chikhalire pa malikulu a Ayuda Yerusalemu.—1 Mbiri 29:23.

41. Kodi Danieli anafotokoza mtapo wachinai, chitsulo, kukhala chiani?

41 Pano tikuona kukwaniritsidwa kwa zimene mneneri Danieli anali atauza Mfumu Nebukadinezara pomasulira loto loiwalidwa la fano limene linapangidwa ndi mitapo inai. M’kumasulira mtapo wachinai, chitsulo, imene miyendo ya fano’lo inapangidwa nayo, Danieli anati: “Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonse’zi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.”—Danieli 2:40.

42. Kodi ndi motani m’mene Ufumu Wachiroma sunasonyezere ulemu kwa olalikira Ufumu?

42 Ulamuliro wa Dziko wa Roma unaphwanya Ulamuliro wa Dziko wa Grisi ndipo unameza otsalira a Maulamuliro a Dziko a papitapo wa Amedi ndi Aperisi ndi wa Babulo. Uwo sunasonyeze ulemu uli wonse kaamba ka “ufumu wa kumwamba,” “ufumu wa Mulungu,” umene unalengezedwa ndi Yesu Kristu ndi ophunzira ake a m’zaka za zana loyamba. M’chaka cha 33 C.E. uwo unaipitsa Tsiku la Paskha Wachiyuda mwa kuphera Yesu pa mtengo wozunzirapo kunja kwa malinga a Yerusalemu. Ndipo’nso m’chaka cha 64 C.E., pambuyo pa kutentha mbali ina ya mzinda wa Roma, uwo unayamba kuzunza ophunzira okhulupirika a Yesu Kristu, m’njira imene’yi kuyesa kuphwanya ndi kuswa Chikristu choona.

43. Kodi ndi liti ndipo ndi motani m’mene Ufumu Wachiroma unaonongera Yerusalemu?

43 M’chaka cha 70 C.E., m’kuyesa-yesa kwake kuletsa chipanduko cha Ayuda, Roma anakuona kukhala kofunika kuphwanya ndi kuswa Yerusalemu, kum’sandutsa ndi kachisi wake wokongola’yo kukhala mabwinja. Ayuda 97,000 osapangidwa kukhala Akristu’wo amene anakhoza kupulumuka chionongeko choopsya chimene’cho cha mzinda wao woyera anabalalitsidwa monga akapolo ogwidwa kumka ku mbali zosiyana-siyana za Ufumu Wachiroma. Zimene’zi zinachitika m’chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha “nthawi za Akunja,” ndipo panali patatsalabe zaka 1,844 kukafika ku mapeto a Nthawi za Akunja.

44, 45.Kodi kupondereza Yerusalemu kwa Akunja kweni-kweni kumatanthauzanji?

44 Yesu Kristu, m’kati kuneneratu chionongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma otsogozedwa ndi Kazembe wankhondo Tito, mwana wa Mfumu Vespasian, anati: “Ndipo [Ayuda okhala m’chigawo cha Aroma cha Yudeya] adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza [Yerusalemu] kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.” (Luka 21:20-24) Mwa mau amene’wo Yesu Kristu sanatanthauze kuponderezedwa kwa malo wamba a mzinda kochitidwa ndi osakhala Ayuda kapena mitundu Yachikunja. Kale’lo mzinda wa Yerusalemu unaimira zoposa zimene Yerusalemu wa lero lino, malikulu a Ripabliki la Israyeli, lokhala ndi prezidenti wake wosankhidwa mwademokratiki ndi Nyumba ya Malamulo, imaimira. Kale’lo m’nthawi ya Kristu, Yerusalemu ndi Kachisi wake anaimira “mzinda wa Mfumu yaikulu,” Yehova. (Mateyu 5:35, 4:5) Mzinda wokhala ndi mpando wachifumu wa ufumu weni-weni wa Yehova pa nthawi ina umene’wu pa dziko lapansi unali chizindikiro cha ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi mfumu yake yodzozedwa ya mzera wachifumu wa Davide.

45 Ndipo chotero ufumu Waumesiya, umene mbadwa zachifumu za Davide zinasungabe Ulemu wake, ndiwo chinthu chimene chinayenera kuponderezedwa ndi Akunja kufikira “nthawi zoikidwiratu za mitundu” pakuti kupondereza kumene’ku popanda chidodometso cha Mulungu kunatha. Mapeto a Nthawi za Akunja ndiwo kumene zaka zathu za zana la makumi awiri zikulowetsedwamo!

ULAMULIRO WINA WA DZIKO UKUPHATIKIZIDWAMO

46. Kodi Mfumu Yachiroma Konstantini anadzetsa ufumu wa Mulungu?

46 Pamene tikuyang’ana m’mbuyo kuchokera m’zaka zathu zino za zana la makumi awiri, tikufunsa kuti: Kodi “ufumu wachinai” umene’wo monga momwe unaphiphiritsiridwira ndi miyendo yachitsulo ya fano la loto la Nebukadinezara unakwaniritsidwa kotheratu mu Ufumu Wachiroma kapena Ulamuliro wa Dziko wokha’wo? Baibulo leni-leni’lo limasonyeza kuti sizinayenera kukhala motero. Kodi ziri choncho motani? M’masiku a Mfumu Konstantini m’zaka za zana lachinai, Ufumu Wachiroma unakhala “Mkristu,” koma kumene’ku kunangokhala mwa lamulo la mfumu chabe ndipo mwa dzina chabe. Kusintha kwa mkhalidwe wachipembedzo kumene’ku sikunapange ulamuliro wa dziko watsopano, ulamuliro wa dziko Wachikristu; sikunadzetse ufumu wa Mulungu wonga umene unalalikidwa ndi Yesu Kristu. Komabe, ulamuliro wa dziko watsopano unadza pambuyo pa kupita kwa zaka mazana ambiri—m’njira yeni-yeni ya ndale za dziko. Umene’wu unasonyezedwa m’bukhu lotsirizira la Baibulo, m’Chibvumbulutso 17:9, 10, NW.

47. Kodi mitu isanu ndi iwiri ya “chirombo” imaphiphiritsiranji?

47 M’menemo, ponena za mkazi wachigololo wachipembedzo, Babulo Wamkulu, kukhala akukwera chirombo chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi, timawerenga kuti: “Pano ndipo pamene pali chidziwitso cha nzeru: Mitu isanu ndi iwiri’yo itanthauza mapiri asanu ndi awiri, pa amene mkazi’yo amakhalapo. Ndipo pali mafumu asanu ndi awiri: asanu agwa, imodzi iriko, ina’yo sinafikebe, koma pamene iyo ifika iyenera kukhala kanthawi.” Kuchokera m’kalongosoledwe ka zizindikira kamene’ka pano kopezeka m’bukhu la Chibvumbulutso, chirombo chimaphiphiritsira dongosolo la ndale za dziko pa dziko lapansi. Mitu isanu ndi iwiri ya chirombo imaimira umutu pa dongosolo la ndale za dziko, osati umutu wa isanu ndi iwiri yonse’yo pa nthawi imodzi, koma umutu wochitidwa ndi mutu umodzi umodzi wophiphiritsira kufikira pa wachisanu ndi chiwiri ndi wotsirizira. Moyenerera mitu isanu ndi iwiri’yo imaimira “mapiri asanu ndi awiri,” amene akulamulira dziko lapansi’lo. Ndipo’nso, moyenerera kwambiri, mitu isanu ndi iwiri’yo imaimira “mafumu asanu ndi awiri,” pakuti mafumu ndiwo mitu ya Boma ndipo amachita umutu kapena ulamuliro. Mofanana ndi m’fano la loto la Nebukadinezara, mafumu’wo amaimira maufumu kapena maulamuliro a dziko.

48. Kodi ndani amene anali “mafumu” asanu amene anagwa Roma asanadze?

48 Ponena za “mafumu asanu ndi awiri’wo” mtumwi Wachikristu Yohane analemba pafupi ndi mapeto a zaka za zana loyamba C.E. kuti: “Asanu agwa, imodzi iriko.” (Chibvumbulutso 17:10; NW) Pa nthawi imene Yohane analemba Chibvumbulutso iye anali kusungidwa monga wandende pa chisumbu cholangirapo cha Patmo chifukwa cha kukhala Mkristu. (Chibvumbulutso 1:1, 2, 9) Chotero, polemba kuti, “Asanu agwa, imodzi iriko,” Yohane akusonyeza “mfumu” yachisanu ndi chimodzi. Imodzi imene’yo inalipo m’nthawi ya Yohane. Chotero, pamenepa, kodi ndi ulamuliro wa dziko uti umene Yohane akuusonyeza ndi mau akuti’wo “imodzi iriko”? Si wina’nso koma Ulamuliro wa Dziko wa Roma. Pano ukuikidwa pa kukhala Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chimodzi malinga ndi kunena kwa ulosi wa Baibulo. Pamenepa, kod ndani, amene anali “mafumu” asanu amene anali atagwa ulamuliro wa Dziko wa Roma usanakhale, umodzi umodzi? Woyamba, Ulamuliro wa Dziko wa Igupto, wachiwiri, Ulamuliro wa Dziko wa Asuri, wachitatu, Ulamuliro wa Dziko wa Babulo; wachinai, Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi; ndipo wachisanu, Ulamuliro wa Dziko wa Grisi.

49. Kodi “mfumu” yachisanu ndi chimodzi inagwetsedwa ndi yani, ndipo liti?

49 Komabe, Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chimodzi unayenera’nso kugwa, pakuti mngelo’yo kwa mtumwi Yohane anati: “Imodzi iriko, inayo sinafikebe.” (Chibvumbulutso 17:10, NW) Zimene’zi zinasonyeza kuti ulamuliro wa dziko wachisanu ndi chiwiri unayenera kudzabe, kuti ulingane ndi mutu wachisanu ndi chiwiri wa chirombo. M’nthawi ya mtumwi Yohane ‘mutu wachisanu ndi chiwiri’ umene’wo, kapena ‘phiri lachisanu ndi chiwiri,’ kapena mfumu yachisanu ndi chiwiri’ unali chinsinsi. Koma zaka mazana ambiri za mbiri ya dziko chiyambire pa nthawi ya Yohane yabvumbula chinsini’cho. Pamenepa, kodi, Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri wa ulosi wa Baibulo ndi uti? Unadza m’chaka cha 1763 C.E., mu mpangidwe wa Ufumu wa Britain, Britannia amene analamulira nyanja zisanu ndi ziwiri.

50. Kodi ndi motani m’mene Ulamuliro wa Dziko Wauwiri wa Angelezi ndi Amereka unakhalirako?

50 Zaka khumi ndi ziwiri pambuyo pake, mu 1775, maiko khumi ndi atatu olamulidwa ndi anthu achilendo a ku Amereka anakhadzuka ku Ufumu wa Britain, kukhazikitsa Ripabliki la Amereka, United States of America. M’kupita kwa nthawi Ripabliki la Amereka lolankhula Chingelezi’lo linaona kukhala koyenera kugwira ntchito pamodzi ndi Ufumu wa Britain wolankhula Chingelezi, ponse pawiri m’nthawi ya mtendere ndi m’nthawi ya nkhondo, chinthu chimene chinagogomezeredwa m’kati mwa Nkhondo za Dziko’zo Yoyamba ndi Yachiwiri. Kweni-kweni, pamenetu, pakhala Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Britain ndi Amereka. Chotero, kwa zaka zambiri tsopano chiyambire pa Chipanduko cha Amereka cha 1775-1783 kuphatikizidwa pamodzi kwa ndale za dziko kwa Angelezi ndi Amereka kwakhala Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri. Uwo umachita monga chirombo cha nyanga ziwiri.—Chibvumbulutso 13:11.

51. Kodi n’chifukwa ninji miyendo yachitsulo’yo inaphiritsira zochuluka koposa Ufumu Wachiroma?

51 Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri ‘unafika’ m’nthawi ya Yehova ya kusintha kukhazikitsidwa kwa ufumu wake Waumesiya kusanachitike. Ponena za Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri, Chibvumbulutso 17:10, NW chimati: “Koma pamene iyo ifika iyo iyenera kukhala kanthawi.” Chigawo cha Amereka cha Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri changochita kumene phwando lake lokumbukira chaka chake cha mazana awiri. Imene’yi iri “kanthawi” kakafupi kwambiri poyerekezera ndi nyengo ya nthawi ya Ulamuliro wa Dziko wa Roma ya pafupi-fupi zaka mazana khumi ndi asanu ndi atatu. Pofika pa tsopano lino “kanthawi” kamene’ko kayenera kukhala katatsala pang’ono kutha, malinga ndi ndandanda ya nthawi ya Yehova. Chinthu chimodzi chiri chotsimikizirika kuchokera mu ulosi wa Baibulo: Ufumu Waumesiya wa Mulungu sunalinganizidwe kudza kufikira choyamba Maulamuliro a Dziko Asanu ndi Awiri amene’wo ataonekera pa dziko. (Chibvumbulutso 17:11-14) Polingalira zonse’zi, kukukhala koonekera bwino kwambiri kuti miyendo yachitsulo ya fano la loto la Nebukadinezara inaphiphiritsira woposa Ulamuliro wa Dziko wa Roma. Iyo inaphiphiritsira’nso mphukira ya ndale za dziko yochokera mu Ufumu wa Roma, ndiko kuti, Ulamuliro wa Dziko wa Angelezi ndi Amereka, Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiriwi, umene watsimikizira kukhala ulamuliro wa dziko waukulu kopambana onse mwa lingaliro laumunthu. Uwo nawo’nso wakhala ngati chitsulo, chitsulo cholimba!

MAPAZI A MBALI INA CHITSULO NDI MBALI INA DONGO

52. Kodi n’chiani chimene Danieli ananena ponena za mapazi a mbali ina chitsulo mbali ina dongo?

52 Tsopano tikupita ku mbali zotsirizira za loto lolosera limene mfumu ya Babulo inalota koma inaliiwala. Mfumu Nebukadinezara anafuna kudziwa chimene mapeto a loto’lo anatanthauza, ndipo chimodzi-modzi ife lero lino. Chithokozo kwa Yehova Mulungu, Danieli anauziridwa kulongosola zinthu moonjezereka, kuti: “Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumu’wo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosanganizika ndi dongo. Ndi zala za mapazi, mwina chitsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumu’wo, mwina wolimba mwina wogamphuka. Ndi umo mudaonera chitsulo chosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzaphatikizana, monga umo chitsulo sichimasanganizikana ndi dongo.”—Danieli 2:41-43.

53. Kodi mapazi amene’wo amaphiphiritsira mkhalidwe wotani wa ndale za dziko? Liti?

53 M’mau olosera amene’wo tikuptsidwamo chitsanzo cha ufumu wogawanika. Popeza kuti ndimo m’mene fano lophiphiritsira la maulamuliro a dziko otsatana-tsatana amakhalira potsirizira, mkhalidwe wa ulamuliro wa dziko wogawanika umene’wu uyenera kukhala wotero lero lino, m’zaka zathu za zana la makumi awiri. Uli choncho! Kaamba ka chifukwa choyenera chimene’chi tiyenera kukhala tiri pafupi ndi kuzimiririka kwa fano lokhala kwa nthawi yaitali lophiphiritsira la ulamuliro wa dziko limene’li. Pamene potsirizira pake fano lophiphiritsira’lo lichoka, kenako chiani? Malinga ndi kunena kwa “anthu anzeru” a dziko lino, kuchoka kotero’ko kudzakhala chinthu choipa kwambiri chimene chingachitike. M’lingaliro lao, kukatanthauza chipolowe ndi chisokonezo. Chotero iwo amayesa kuchititsa fano’lo kukhalapobe.

54. Kodi Danieli akusonyeza kuti dongo loumbidwa’lo limaphiphiritsira chiani?

54 Zochitika za dziko zikali chikhalirebe mu mthunzi wa Ulamuliro wa dziko Wachisanu ndi Chiwiri, umene zigawo zake zonse ziri ndi zida zankhondo zamphambvu za mabomba a nyuklea ndi zipangizo zoziponyera. Chotero m’dongosolo lolamulira la ulamuliro mukali chikhalirebe nyonga ya chitsulo limodzi ndi mphamvu yake ya kuphwanya ndi kuswa. Koma Ulamuliro wa Dziko wa Angelezi ndi Amereka umene’wu, limodzi ndi ogwirizana nawo ake, uli ndi mbali ina, mbali yamakono kwambiri, yolimbana nayo. Mbali imene’yi inaphiphiritsiridwa ndi dongo lachinyontho loumbidwa m’fano la mloto la Nebukadinezara. Kodi iro limaphiphiritsiranji ponena za nthawi yathu? Kaamba ka kuunikiridwa kwathu kulongosola kwa Danieli kumati: “Iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzaphitikizana, monga umo chitsulo sichimasanganizikana ndi dongo.” Chifukwa cha chimene’cho, dongo’lo limaphiphiritsira “ana a anthu, kapena, kweni-kweni, ‘mbeu ya anthu.’—Danieli 2:43.

55. Kodi ndi motani m’mene pakhalira kusanganizikana ndi “ana a anthu”?

55 Dongo liri chizindikiro choyenerera kwambiri cha ‘mbeu ya anthu,’ pakuti Yobu 4:19 amanena za anthu kukhala “iwo akukhala m’nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m’pfumbi.” Ndipo munthu wopsyinjika kwambiri’yo Yobu kwa Yehova Mulungu anati: “Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi; ndipo kodi mudzandibwezera kupfumbi?” (Yobu 10:9) Mosasamala kanthu za mkhalidwe wa kusachedwa kusweka wa “dongo” limene “ana a anthu” apangidwa nalo, kodi mkhalidwe wa ulamuliro wa anthu m’zaka za makumi otsirizira ano a kukhalapo kwake wakhala ukumka kuti? Ai, osati kwa Mulungu Mlengi wa “dongo” lopatsidwa moyo’lo, koma kwa zolengedwa za dongo, kwa anthu wamba, “proletariat” monga momwe Aroma akale anachera kagulu ka anthu kotsikitsitsa kapena kosaukitsitsa kamene sikanapereka chiri chonse koma ana (proles) ku Boma la ndale za dziko. Ulamuliro wakale wa kumakolo wakhala wokakamizika kumvetsera moonjezereka-onjezereka ku mfuu ya anthu wamba ya kukhala ndi phande m’maboma owalamulira.

56. Kodi n’chifukwa ninji palibe kugwirizana pakati pa chitsulo ndi dongo?

56 Komabe, sipangakhale ukwati pakati pa boma lakale lolamulidwa ndi olemekezeka ndi otsendereza ufulu ndi anthu wamba amene amakonda masinthidwe akulu ndi otheratu m’boma. Zosachitika’di monga momwe sipangakhalire kusanganizika kwa chitsulo ndi dongo! Kupangidwa kwa maboma kukhala a demokratiki mwa zipanduko kapena mwa njira zina kwachititsa mipangidwe yaikulu ya maboma opangidwa ndi anthu wamba. Ndipo otsirizira’wa amaima m’malo osangonjera ku Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri wonga chitsulo, Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka. Kufikira tsopano mipangidwe iwiri ya ulamuliro’yo yakhala yokhoza kukhalira limodzi, koma sipanakhale kugwirizana kweni-kweni pakati pao. Maboma ndi magulu a maboma okonda kusintha ndi a anthu wamba angaonekere kukhala amphamvu kwambiri ndi kuonekera kukhala akuposa Ulamuliro wa Dziko wa Angelezi ndi Amereka m’nyonga. Komabe iwo ali osachedwa kusweka mofanana ndi zolengedwa zaumunthu za dongo, zimene zimachirikiza maboma okonda kusintha. Iwo sangathe kulimbikitsa fano lophiphiritsira la ulamuliro wa pa dziko lonse kukaniza kusintha kwa pa dziko lonse kukudza’ko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena