Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my nkhani 105
  • Akuyembekezera m’Yerusalemu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akuyembekezera m’Yerusalemu
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuwonekawoneka Komalizira, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuwonekera Komaliza, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my nkhani 105

NKHANI 105

Akuyembekezera m’Yerusalemu

ANTHU ali pano’wa ndi atsatiri a Yesu. Amumvera nakhala m’Yerusalemu. Ndipo akali chiyembekezerere onse pamodzi, phokoso likudzaza nyumba’yo. Likumveka ngati chimphepo champhamvu. Ndiyeno malirime a moto akuonekera pa mitu pa ali yense wa ophunzira’wo. Kodi mukuona moto’wo pa ali yense wa iwo? Kodi zonse’zi zikutanthauzanji?

N’chozizwitsa! Yesu wabwerera kumwamba ali ndi Atate wake, ndipo akutsanulira mzimu woyera pa atsatiri ake. Kodi mukudziwa chimene mzimu’wu ukuwachititsa kuchita? Onse akuyamba kulankhula zinenero zosiyana-siyana.

Anthu ambiri m’Yerusalemu akumva phokoso limene likumveka ngati chimphepo champhamvu, nadza kudzaona chimene chikuchitika. Ena ali anthu ochokera ku mitundu ina amene adza kuno kaamba ka phwando la Aisrayeli la Pentekoste. N’zodabwitsa zotani zimene alendo’wa akulandira! Akumva ophunzira’wo akulankhula m’chinenero cha kwao ponena za zodabwitsa zimene Mulungu wachita.

Alendo’wo akuti: ‘Anthu’wa onse ngochokera ku Galileya. Nangano, ndi motani m’mene kuliri, kuti akukhoza kulankhula zinenero zosiyana-siyana’zi za kumaiko a kumene tachokera?’

Petro tsopano akuimirira nawalongosolera. Akukweza mau ake nauza anthu’wo m’mene Yesu anaphedwera ndi kuti Yehova anamuukitsa. Petro akuti: ‘Tsopano Yesu ali kumwamba ku dzanja lamanja la Mulungu. Ndipo watsanulira mzimu woyera wolonjezedwa’wo. N’chifukwa chake mwaona ndi kumva zozizwitsa’zi.’

Ndiyeno, Petro atanena zinthu’zi, ambiri akumva chisoni kwambiri ndi zimene zinachitidwira Yesu. Iwo akufunsa kuti, ‘Tidzachita chiani?’ Petro akuwauza kuti: ‘Mufunikira kusintha miyoyo yanu ndi kubatizidwa.’ Chotero pa tsiku’lo anthu 3,000 anabatizidwa nakhala otsatira Yesu.

Machitidwe 2:1-47.

Mafunso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena