Mutu 8
Chotandizira Kupirira Pobvutika
1, 2. Kodi nchifukwa ninji ophunzira a Yesu Kristu sangapewe kubvutika?
PA NTHAWI ina m’miyoyo yathu, tingafunikire chithandizo pa zobvuta zathu, ngakhale motayadi mtima. Ngati masoka otsatanatsatana akatigwera m’kutsatana kofulumira, ife mosabvuta tikadzipeza tikulowa m’kutaya mtima. Katunduyo angaonekere kukhala wolemera kwambiri kosati ife nkumunyamula. Ha, ndi kwabwino chotani nanga m’mene kuliri kupeza chithandizo pa nthawi yoteroyo!
2 Kukhala kwathu ophunzira a Mwana wa Yehova Mulungu sikumatichotsera kufunikira kwathu chithandizo. Ife sitiri osakhoza kugweredwa masoka. Zogwera anthu onse zikupitirizabe kuphatikizamo kudwala, ngozi, maliyambwe, zibvomezi, mikuntho, upandu, zisalungamo ndi chitsenderezo. Sitiyenera kuyembekezera Mfumu Yaikuluyo kugwiritsira ntchito mphamvu yake kuyendetsa zinthu zachibadwa ndi mikhalidwe ya pamalo kotero kuti ife, monga atumiki ake, tikhale mwapadera opanda kubvutika kuli konse kochititsidwa ndi zinthu zimenezi. Nthawi ya Mulungu ya kuchotsa ziyambukiro zonse zopweteka za uchimo wa anthu ikali mtsogolo. Ngati iye tsopano anachititsa anthu ake kukhala ndi ‘moyo wopanda zaupanda,’ ife mosakaikira tikanaona ziwerengero zazikulu zikudza mu unyinji wao kudzamtumikira-ndithudi kaamba ka zifukwa zadyera, osati chifukwa cha chikondi ndi chikhulupiriro.—Yerekezerani ndi Yohane 6:10-15, 26, 27.
3, 4. Kodi ndi kubvutika kotani kumene Akristu oona amakumana nako kumene ena samakumana nako, ndipo kodi zimenezi zingadzetse funso lotani?
3 Si kokha kuti tikakumana mosapeweka ndi nsautso kuchokera ku mikhalidwe yosakondweretsa, koma, chifukwa chakuti ndife atumiki a Yehova, tingakumanenso ndi chizunzo-mwina mwake kuchokera kwa achibale, kuchokera kwa anansi kapena ocheza nawo, kapena kuchokera kwa akuluakulu a boma. Yesu Kristu anafika mpaka pa kunena kuti: “Adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Zenizeni zikusonyeza kuti zimenezi zachitika, m’zaka zenizeni zino za zana la 20.
4 Kodi nchifukwa ninji Mulungu Wamphamvuyonse amalola atumiki ake kukumana ndi ziyeso zosiyanasiyana? Popeza kuti njira yao ya moyo simatsimikiziritsa kwa iwo kukhala opanda masoka ofalawo ndipo popeza kuti kulondola njira imeneyo kungathedi kuwapangitsa kukhala ‘odedwa,’ munthu angadabwe m’mene njira yoteroyo ya moyo ikakhaliradi yabwino kopambana. Kodi pali mapindu olingana nawo, inde, oposa nsautsozo? Kodi pangakhaledi chimwemwe chachikulu kwambiri m’kupirira ziyeso zina koposa ndi kuchipewa? Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza m’kupirira pokumana ndi ziyeso za zitsenderezo zazikulu kwambiri? Mayankho a mafunso amenewa angatithandize kwambiri ndi kutilimbikitsa.
KODI AMENE ALI NDI THAYO LENILENI?
5. Kodi nchiyani chimene tifunikira kuzindikira ponena za magwero a kubvutika?
5 Nkofunika kwambiri kuti ife tisaiwale kuti Atate wathu wakumwamba sindiye magwero a kubvutika. Iye sanadzetse uchimo m’dziko. Mwana wauzimu wa Mulungu anasankha kupandukira Wompanga, motero kudzipanga iye mwini kukhala Satana, wotsutsa Wam’mwambamwambayo. Chifukwa cha chisonkhezero chake, anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, mwadala anaswa lamulo la Mulungu, akumadzitengera chilango cha imfa pa iwo eni. (Genesis 3:1-19; Yohane 8:44) Chifukwa chakuti Adamu anaononga ungwiro wake, ana ake onse anabadwira mu uchimo, ogonjera ku kudwala, kufooka, ukalamba ndi imfa. (Aroma 5:12) Monga obadwa tiri ochimwa, ife tonse timaperewera pa kukhala mtundu wa munthu amene ife timafuna kukhala ndipo tiyenera kukhala. Mwa mawu athu ndi machitidwe, ife mosakhala mwadala tingakhumudwitse ena, tikumaonjezera ku masautso ao. Chotero tifunikira kukumbukira kuti Mulungu sindiye amene ali ndi liwongo kaamba ka zobvuta zochititsidwa ndi kupanda ungwiro kwathu kwa ife eni kapena zija za anthu anzathu. Ngati lamulo lake likanamveredwa, matenda, kufooka, ukalamba ndi zochititsa zambiri za kubvutika sizikanakhalako konse.
6. Kodi Yehova amamva bwanji ndi nkhanza ya munthu kwa munthu mnzake?
6 Ndiponso, Atate wathu wakumwamba samabvomereza nkhanza ya munthu kwa munthu mnzake. Baibulo limati: “Kupondereza wandende ali yense mdziko, kukaniza munthu zoyenera zake monyoza Wam’mwambamwamba, kuletsa chiweruzo cholungama m’makhoti-zinthu zoterozo Ambuye sanazibvomereze.” (Maliro 3:34-36, The New English Bible) Awo amene amachitira moipa anthu anzawo, moswa lamulo la Mulungu, adzayimbidwa mlandu ndi iye. “Kubwezera kuli kwanga, Ine ndizabwezera, ati Ambuye.” (Aroma 12:19) Chifukwa cha chimenecho, tifunikira kukhala osamala kuti tisapsere mtima Atate wathu wakumwamba chifukwa cha kubvutika kumene kumatulukapo pamene anthu mwadala ndi mopanduka anyalanyaza lamulo la Mulungu.
7. Popeza kuti Yehova Mulungu walola mikhalidwe kubuka imene imachititsa kubvutika kwa ife, kodi nchiyani chimene tiyenera kunena ponena za zifukwa zake zochitira motero?
7 Ndithudi, Yehova Mulungu ali ndi kukhoza kuletsa Satana, ziwanda, anthu oipa ndi kukhala ochimwa kwa anthu kusachititsa mitundu yonse ya mikhalidwe yobvuta. Komabe, popeza kuti iye amalola mikhalidwe yosautsa kulowetsamo ngakhale atumiki ake, imeneyi iyenera kukhala kaamba ka zifukwa zabwino.
KAAMBA KA PHINDU LA “ZOTENGERA ZACHIFUNDO”
8. Kodi ndi zifukwa zotani zimene zikuperekedwa mu Aroma 9: 14-24 ponena za chifukwa chake Yehova Mulungu samachitapo kanthu mwamsanga motsutsana ndi awo amene amachititsa kubvutika?
8 Malemba amalongosola kuti chifuno cha Mulungu m’kusachitapo kanthu mwamsanga motsutsana ndi awo odzetsa kubvutika kwakukuluko pa ena chiri kaamba ka phindu la potsiriza pake la anthu okonda chilungamo. M’kalata yake yomka kwa Aroma, mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti:
“Kodi chiripo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni. Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo. Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi. Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.
“Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuno chake? Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mawu? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero? Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi ntchintchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi? Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko? Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?”—Aroma 9:14-24.
9. Kodi ndi motani m’mene Farao anadzibvumbulira kukhala ‘chotengera cha mkwiyo’?
9 Chimene Yehova Mulungu angachititse kapena angachilole kubuka m’miyoyo ya anthu chingathe kubvumbula mtundu wa “zotengera” zimene iwo ali. Farao amene Yehova, kupyolera mwa Mose ndi Aroni, anampatsa chidziwitso cha kumasulidwa kwa Aisrayeli okhalitsidwa akapolowo anapitirizabe kudzichititsa iye mwini kukhala wouma khosi kwa Wam’mwambamwambayo. Pamene miriri inadza motsatanatsatana pa Aigupto, Farao uyu anakhala wouma khosi moonjezereka m’kukana kwake kulola aisrayeli kutuluka mu Igupto monga anthu omasuka. Chotero iye anadzibvumbula kukhala ‘chotengera cha mkwiyo,’ choyenerera kuonongedwa chifukwa cha kunyoza mopandukira ulamuliro wa Mfumu Yaikulu, Yehova Mulungu. Pa nthawi imodzimodziyo, kuchitiridwa mwankhanza ndi kosayenera kochitiridwa Aisrayeli kunasonyeza kuti iwo moyenerera anali kufuna kuchitiridwa chifundo, kumveredwa chisoni kapena kukomeredwa mtima.
10. Mwa kulola Farao kukhalabe m’njira yake yonyozayo kwa kanthawi, kodi ndi motani m’mene Yehova anadzipangirira dzina lalikulu?
10 Onaninso, kuti mtumwi Paulo anasonya ku chenicheni chakuti dzina la Mulungu linalowetsedwamo m’kulola kwa Yehova Farao kupitirizabe kunyoza mouma khosi. Ngati wolamulira wodzitukumula ameneyu akaonongedwa pa nthawi yomweyo, sipakanakhala mwai wakuti mphamvu ya Yehova Mulungu ibukitsidwe m’njira yaikulu kwambiri ndi yosiyana kwambiri, kuchititsa manyazi milungu yochuluka ya Aigupto ndi ansembe ochita matsenga. Miriri khumi, imene inatsirizidwa ndi chionongeko cha Farao ndi magulu ake onse ankhondo pa Nyanja Yofiira, inali chisonyezero champhamvu kwambiri cha mphamvu ya Mulungu kwakuti kwa zaka zambiri pambuyo pake mitundu yozungulirapo inali ikadanenabe za izo. Motero dzina la Yehova linabukitsidwa pa dziko lonse lapansi, kukumachititsa ulemerero ndi ulemu ku dzina limenelo, ndi kusonkhezera anthu a mtima wolungama kuzindikira kukhala kwake wapamwamba.—Yoswa 2:10, 11; 1 Samueli 4:8.
11. Kodi ndi motani m’mene Aisrayeli anapindulira ndi chokumana nacho chao ndi Farao?
11 Ndithudi, Aisrayeli, monga “zotengera zachifundo,” anapindula ndi zimene Wammwambamwambayo anachita. Kubvomereza kwake chitsenderezo ndiyeno nkuchithetsa m’chisonyezero chachikulu kompambana cha mphamvu kunawathandiza kumdziwa bwino kwambiri, kukumawapatsa mwai wa kuona ukulu wake kumene sikukanatha kuonedwa mwa njira ina. Ngakhale kuli kwakuti kunali kowawa, chokumana nacho cha Israyeli mu Igupto ndithudi chiyenera kukhala chitawathandiza kuona kufunika kwa kukhala ndi chikhulupiriro m’mphamvu yake yopulumutsa, kudzanso kukhala ndi kuopa Mulungu kwabwino. Zimenezi zinali zofunika kwambiri ngati iwo akanati apitirizebe kulondola njira ya moyo imene ikatsogolera ku chimwemwe, chisungiko, mtendere ndi thanzi labwino.—Deuteronomo 6:1-24; 28:1-68.
12. Monga momwe kwasonyezedwera ponena za chochitika cha Yobu, kodi kulola kwa Yehova kubvutika kumatitheketsa kuchitanji?
12 Monga momwedi kuliri kuti chikhoterero cha mitima ya anthu chinaonekera pa nthawi imeneyo, chimodzimodzi kuyesedwa ndi mayesero zimene zingatigwere mwa chilolezo cha Mulungu zingathe kubvumbula kaya utumiki wathu kwa iye ule ndi cholinga choyenera. Kunena kotsutsa kwa mdani wa Mulungu. Satana, ndiko kwakuti awo amene amachita chifuniro cha Mulungu ali kwenikweni adyera. Ponene za Yobu wokhulupirikayo, mdaniyo analengeza kuti: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza pfupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.” (Yobu 2:4, 5) Mwa chipiriro chokhulupirika poyesedwa, timakhala ndi phande m’kutsimikizira kunena kotsutsa kwa Satanako kukhala bodza ndi kukhala ndi phande m’kudziwikitsidwa kwa dzina labwino la Atate wathu wakumwamba, amene amadalira atumiki ake okhulupirika. Bwanji ngati Yehova atalola Satana, mwa njira ya oimira ake, kuchititsa Akristu oona kuchitiridwa mwankhanza kwambiri kumene kukachititsa imfa kapena kubvulaza kopundula? Bwanji ngati ena ake anafikiradi pa kugwiridwa chigololo kapena kuchitiridwa moipa mwa njira zina? Zinthu zimenezi nzobvutitsa maganizo. Komabe palibe chiri chonse chimene chiri choposa mphamvu ya Atate wathu wakumwamba kuchikonza kotheratu m’nthawi yake yokwanira. Chotero, mu zochitika zina, iye angakuone kukhala koyenera kulola chiyesocho kufikitsidwa pa mlingo wopambanitsa motero. Kupyolera mwa kukhulupirika, ngakhale kufika pa kufa, atumiki a Mulungu motero akupatsidwa mwai wa kusonyeza mosakanika kukhala koonadi kwa kudzipereka kwao.
13. Kodi mau a 1 Petro 1:5-7 amabvumbulanji ponena za kubvutika kumene Akristu angachititsidwe kukhala nako?
13 Zodabwitsa monga momwe zingaonekerere kwa ena, ziyeso zimene ife tingalowetsedwemo, kaya zochititsidwa ndi zochititsa zachilengedwe kapena zochokera ku chizunzo, zingadzetsebe kuongokera mwa ife mwa njira ya munthu mwini. Mtumwi Petro anasonyeza zimenezi. Atatha kusonyeza kuti Akristu “akusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu’ kotero kuti chipulumutso chao chotsirizira chitsimikiziridwe, mtumwiyo akufotokoza kuti:
“M’menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundu mitundu, kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwa ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu Kristu.”—1 Petro 1:5-7.
14. Kodi nchifukwa ninji Akristu angasangalale pamene iwo ‘akumvetsedwa chisoni’ ndi ziyeso?
14 Monga momwe Petro akubvomerezera, kubvutika kumene ife tingakumane nako sikosangalatsa konse. Tingamvetsedwedi “chisoni” kapena kumvetsedwa kupweteka ndi ziyeso. Komabe, tingathe, pa nthawi imodzimodziyo, kusangalala. Chifukwa ninji? Ku mbali ina, chisangalalocho chimachokera m’kuzindikira kuti pali phindu lauzimu lopezedwa kuchokera m’kupirira bwino lomwe posautsidwa. Kodi phindu lauzimu limenelo nchiyani?
NJIRA IMENE KUBVUTIKA KUNGAYERETSERE CHIKHULUPIRIRO
15. Kodi ziyeso zingakhale ndi chiyambukiro chotani pa chikhulupiriro?
15 Mtumwi Petro anayerekezera ziyambukiro zimene ziyeso zingakhale nazo pa chikhulupiriro cha Mkristu ndi kuyengedwa kwa golidi ndi moto. Njira yoyengera imachotsamo zosafunika, ikumasiya golidi yekha. Mtengo woonjezeredwa kwambiri wa golidiyo ndithudi umapangitsa njira yoyengerayo kukhala yoyenera. Komabe, monga momwe Petro ananenera, ngakhale golidi woyesedwa ndi moto ali wokhoza kuonongeka. Iye angathe kusumbudzuka kapena kuonongedwa mwa njira zina. Koma siziri choncho ndi chikhulupiriro choyesedwa kapena choikidwa pa mayeso. Chikhulupiriro chenicheni sichingathe kuonongedwa.
16. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kwambiri kwa ife kukhala ndi chikhulupiriro chosanyenga?
16 Ngati titi tipeze chibvomerezo cha Mulungu, nkofunika kotheratu kuti tikhale ndi chikhulupiriro choterocho. Baibulo limatiuza kuti: “Popanda chikhulupiriro kuli kosatheka kukondweretsa [Mulungu] bwinobwino.” (Ahebri 11:6, NW) Zowonadi, chikhulupiriro chimene chikutsimikiziridwa kukhala chowona poyesedwa chimaposadi kwambiri golidi woyengedwa. Mtsogolo mwathu mwamuyaya mumadalira pa chikhulupiriro choterocho.
17. Kodi ndi mafunso otani amene angafunsidwe ponena za chiyambukiro cha ziyeso pa chikhulupiriro?
17 Koma kodi ndi motani mmene ziyeso zingayeretsere chikhulupiriro kotero kuti ‘chikapeze chochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu Kristu’? Zimenezi zingathe kuchitika m’njira zosiyanasiyana.
18. Kodi ndi motani m’mene chikhulupiriro chingadzibvumbulire m’chiyeso, ndipo kodi ndi motani m’mene kumeneku kungatilimbikitsire?
18 Ngati chikhulupiriro chathu chiri champhamvu, chidzatitonthoza ndi kutichirikiza m’kati mwa nthawi ya bvuto. Pamenepo, pokhala titapyola chiyeso chimodzi bwino lomwe, timalimbikitsidwa kukumana ndi chiyeso china chiri chonse. Chokumana nachocho chidzakhala chitasonyeza zimene chikhulupiriro chathu chingatichitire.
19. Kodi chiyeso chakutichakuti chingasonyezenji ponena za zofooka m’chikhulupiriro, ndipo kodi ndi motani m’mene kumeneku kungatithandizire?
19 Ku mbali ina, chiyeso chakutichakuti chingasonyeze zofooka za umunthu, mwina mwake kunyada, kuuma khosi, kusadekha, kukhala waudziko kapena kukonda zosabvuta ndi zosangalatsa. Mikhalidwe yoteroyo imachokeradi m’zofooka za chikhulupiriro. Kodi ziri choncho motani? M’chakuti izo zimabvumbula kuti munthuyo sakudzigonjetsera iye mwini mokwanira ku chitsogozo ndi chifuniro cha Mulungu ponena za iye. Iye sali wokhutiritsidwa maganizo kuti Atate wake amadziwadi bwino kopambana chimene chidzatsogolera ku chimwemwe, ndi kuti kutsatira chilangizo cha Mulungu nthawi zonse kudzadzetsa dalitso. (Ahebri 3:12, 13) Pamene ziyeso zionetsa zofooka, Mkristu angathe kuchititsidwa kuona kufunika kwa kulimbikitsa chikhulupiriro chake kuti akhalebe mtumiki wobvomerezeka wa Wam’mwambamwambayo.
20. Pamene ziyeso zibvumbula zofooka m’chikhulupiriro chathu, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita?
20 Chifukwa cha chimenecho, ngati mkhalidwe wakutiwakuti usonyeza nthenya m’chikhulupiriro chathu, tingathe kudzipenda ife eni ndi kutsimikizira njira zoongolerera zimene zingatengedwe. Munthu achita bwino kudzifunsa kuti: ‘ Kodi nchifukwa ninji chikhulupiriro changa chiri chofooka? Kodi ine ndimanyalanyaza phunziro ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu? Kodi ndimagwiritsira ntchito mokwanira mwai wa kusonkhana ndi okhulupirira anzathu kuti tilimbikitsidwe ndi zisonyezero zao za chikhulupiriro? Kodi ndimayedzamira ku kudalira kwambiri pa ine mwini koposa mmene ndinayenera kuchitira, m’malo mwa kuika nkhawa ndi zolemetsa zanga zonse pa Yehova Mulungu? Kodi mapemphero, mapemphero ochokera mu mtima, alidi mbali ya tsiku ndi tsiku ya moyo wanga?’ Pamene mbalizo zangotsimikiziridwa pamene pafunikira kuongokera, tifunikira kupanga kuyesayesa kupanga masinthidwe m’njira yathu ya moyo, ndi cholinga cha kulimbikitsa chikhulupiriro chathu.
21. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi ‘kupezedwa kwa chikhulupiriro chathu kukhala chochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu Kristu’?
21 Mwa kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka chitsogozo ndi kudalira mwa iye modekha kuti atisonyeze njira yomka ku mpumulo kuchoka ku ziyeso zathu, tingathe kulola mikhalidwe yobvuta imeneyi kutithandiza kukhala autimiki ake abwino kwambiri. Pamenepo chikhulupiriro chathu ‘chidzapezedwadi chochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu Kristu.’ Mwana wa Mulungu ‘adzatamanda,’ kuthokozera kapena kuyamikira chikhulupiriro chathu. Mwa njira ya chikhulupiriro chathu, iye adzatifupa kwambiri, motero kutipatsa kuika “ulemerero” pa ife. Pamaso pa Yehova Mulungu ndi angelo, iye ‘adzatilemekeza’ monga ophunzira ake. (Yerekezerani ndi Mateyu 10:32; Luka 12:8; 18:8.) Zimenezi zidzatanthauza kukhala namo pamaso pathu mtsogolo mosatha mwa kukhala ndimoyo kwachimwemwe. Koma kodi tingachitenji pamene tikukumana ndi kubvutika kwambiri kuti tichititse chikhulupiriro chathu kusafooka?
M’MENE TINGACHITIRE PAMENE TIRI PA CHITSENDEREZO CHAMPHAMVU
22. Kodi ndi kuzindikira kwathu chenicheni chotani ponena za utali wa ziyeso kumene kungatithandize kupirira?
22 Chinthu chimodzi chimene chingatithandize kupirira ziyeso zobvuta bwino lomwe ndicho kuzindikira kukhala kwake zakanthawi. Kuyengedwa kwa golidi kumakhala ndi chiyambi ndi mapeto. Chimodzimodzinso ndi nsautso iri yonse imene tikumana nayo sidzaptirizabe kosatha. Ngati tilingalira nthawi zonse lonjezo la Mulungu la moyo wamuyaya wopanda matenda, kulira kapena kumva zopweteka, pamenepo ngakhale kubvutika koipitsitsa m’dongosolo lino la zinthu kungathe kuonedwa kukhala ‘kwakanthawi chabe ndi kopepuka.’ (2 Akorinto 4:17) Yang’anani m’tsogolo ku nthawiyo pamenedi “zinthu zakale sizidzakumbukika, ngakhale kulowa mu mtima.” (Yesaya 65:17) Ha, ndi kokondweretsa kwambiri chotani nanga m’mene kuliri kudziwa kuti zokumana nazo zobvuta zimenezo sizidzakhalanso pa nthawi imeneyo zikumbukiro zopweteka!
23. Kodi nchifukwa ninji kubvutika kawirikawiri sikukadza pa ife chifukwa cha khalidwe labwino?
23 Ndiponso, kukumana kwathu ndi kubvutika kwambiri kochitidwa ndi anthu kawirikawiri sikumakhala kwa tsiku ndi tsiku. Khalidwe lathu labwino limaperekadi chifukwa chochepa choti ali yense atibvulazire. Iyo pokhala ntchito ya akuluakulu a boma kusingitsa lamulo ndi bata, iwo angatamandedi atumiki a Yehova kaamba ka kukhala osunga lamulo. M’nthawi zamakono, ngakhale otsutsa akakamizika kunena mawu obvomereza ofanana ndi aja amene ananenedwa ndi adani a mneneri wokhulupirika wa Mulungu Danieli: “Sitidzamtola chifukwa chiri chonse Danieli amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.” Inde, Danieli anali “wokhulupirika; ndipo sanaona chosasamala kapena cholakwa chiri chonse mwa iye.” (Danieli 6:4, 5) Chenicheni chakuti khalidwe labwino mwa iro lokha kawirikawiri silikakhala chifukwa cha kukhala kwa Mkristu wodedwa chingakhale chifukwa chake mtumwi Petro anafunsa funso lotsatirapoli: “Ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino?”—1 Petro 3:13.
24. Kodi nchifukwa ninji anthu sangatibvulaze kosatha?
24 Komabe, mwa funso lakeli, mtumwiyo m’malo mwake angakhale anali kufunsa kuti: ‘Kodi ndani amene ngachititse chibvulazo chenicheni kwa Mkristu wolungama?’ Palibe munthu ali yense amene angadzetse chibvulazo chotheratu pa ife. Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti: “Musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.” (Mateyu 10:28) Inde, anthu angafike pa kutipha, koma iwo sangathe kuchotsa kuyenera kwathu kwa kukhala zamoyo. Mulungu Wam’mwambamwambayo, mwa njira ya Mwana wake, angathe ndipo adzabwezera moyo kwa atumiki ake okhulupirika. Ndiye Yehova yekha amene angathe kuononga kuyenera kwathu kwa kukhala ndi moyo monga zamoyo kwamuyaya, akumatipereka ife ku imfa yopanda chiyembekezo cha chiukiriro.
25, 26. (a) Kodi nchifukwa ninji tingakhale achimwemwe pobvutikira chilungamo? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuopa choopedwa ndi ozunza athu?
25 Chifukwa cha zowona zimenezi, mtumwi Petro akanatha kunena kwa abale ake Achikristu kuti: “Ngatinso mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa.”—1 Petro 3:14.
26 Ngati tibvutika “chifukwa cha chilungamo,” tingathe kukhala achimwemwe chifukwa chakuti tiri ndi chikumbu mtima choyera pamaso pa Mulungu ndi anthu. Tikubvutika kaamba ka chifukwa choyenera. Chikhutiro chachikulu cha m’katikati ndi mtendere zimachokera m’kuchita chimene tikudziwa kukhala chokondweretsa kwa Wam’mwambamwambayo. Komabe, monga momwe mtumwiyo anasonyezera, kuti tichite zimenezi bwino lomwe kumadalira pa kusagonjera ku mantha. Mtumwiyo pano angakhale akunena za mantha amene ozunza angawachititse mwa kudzetsa kwao nsautso pa anthu a Mulungu. Kapena, angakhale mantha amene ozunza angawachititse mwa kudzetsa kwao nsautso pa anthu a Mulungu. Kapena, angakhale mantha amene ozunzawo iwo eni angakhale nawo. Mwa chitsanzo, chifukwa cha kusakhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova Mulungu, kupyolera mwa Kristu, adzaukitsa akufa, adani a Akristu oona amaopa kuopseza kwa kuphedwa akali achichepere. (Ahebri 2:14, 15) Komabe, ife atumiki a Mulungu, sitifunikira kuopa zimene osakhulupirira amaziopa, pakuti ife tamasulidwa ku kuopa imfa yoteroyo ndipo timadziwa kuti Atate wathu wakumwamba sadzatisiya konse. Chifukwa cha chimenecho, sitiyenera kukhala ‘odera nkhawa,’ monga ngati mwa kuukira mu mkwiyo ozunza oterowo.
27, 28. Kodi ndi motani m’mene uphungu wa 1 Petro 3:15 ungatithandizire pamene tatengeredwa pamaso pa akulu a boma ndi kufunsidwa mwaukali, monyozetsa?
27 Bwanji ngati tinayenera kutengeredwa pamaso pa akuluakulu a boma ndi kufunsidwa mwaukali, monyozetsa? Sitidzafuna konse kubwezera mofananamo. Chidaliro chathu chakuti Mulungu akutichirikiza chingathe kutipatsa kulimba mtima, koma sichimapereka chodzikhululukira nacho chokhalira woputa ndeu kapena wachipongwe. (Yerekezerani ndi Machitidwe 4:5-20.) Uphungu wa mtumwiyo ndiwo wakuti: “Mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Ngati tilephera kulabadira chilangizo chimenechi ndi kudzilola ife eni kusonyeza kunyoza ndi kupanda ulemu, tidzaleka kubvutikira chilungamo. Olamulira a boma akaona kukhala olungamitisidwa kuchita motsutsana nafe chifukwa cha kuuma khosi kopanda ulemu. Anthu audziko amakalipa mopsa mtima, kuwawidwa mtima ndi kuipidwa kwambiri pamene iwo aona kuti zoyenera zao zikuchitiridwa molakwa. Mkristu ayenera kukhala wosiyana.
28 Monga momwe mtumwiyo akulangizira, pansi pa mikhalidwe yoteroyo tifunikira kukumbukira Mbuye kapena mwini wathu, kukumbukira chitsanzo chake. Tifunikira kukhala osamala kuti tipatse Yesu Kristu ulemu waukulu kopambana, tikumamninkha malo opatulika m’mitima yathu. Ife ndife ophunzira ake, ndipo timafuna kulankhula ndi wofunsa ali yense monga ngati kuti tinali kuimirira pamaso penipeni pa Ambuye wathu. Chifukwa chokhalire ndi kaimidwe kathu kachikristuka chiyenera kuperekedwa m’njira yodekha mwaulemu ndi mwamtima pansi.
CHIYAMBUKIRO CHABWINO PA OTSUTSA
29. Kodi kupirira mokhulupirika kwa munthu poyesedwa kungakhale ndi chiyambukiro chotani pa otsutsa?
29 Kupirira mokhulupirika pobvutika kungatumikirenso kutontholetsa otsutsa. Mtumwi Petro akupereka chimenechi kukhala chisonkhezero chosungira chikumbu mtima choyera mwa kunena kuti: “Khalani ndi chikumbu mtima chabwino, kotero kuti pamene iwo akunenerani motsutsa akachite manyazi awo amene akunenera monama khalidwe lanu labwino mogwirizana ndi Kristu.” (1 Petro 3:16, NW) Otsutsa omaona kudekha, khalidwe losadandaula m’limene atumiki a Mulungu akuchitira angachite manyazi chifukwa cha kukhala atawanenera monama. Zimakhaladi choncho pamene tichitira otsutsa mokoma mtima.—Aroma 12:19-21.
30. (a) Kodi nchifukwa ninji palibe phindu kubvutikira kuchita zoipa? (b) Ponena za kubvutikira chilungamo, kodi nchifukwa ninji Petro ananena kuti, “ngati chifuniro cha Mulungu chifuna kutero”?
30 Chenicheni chakuti mapindu oterowo angadze kuchokera ku kupirira mokhulupirika pokumana ndi chitsutso kaamba ka chilungamo chimaonjezera mphamvu ku mawu otsatirapo a Petro: “Pakuti kuli bwino kubvutika chifukwa chakuti ukuchita zabwino, ngati chifuniro cha Mulungu chifuna kutero, koposa ndi chifukwa chakuti ukuchita zoipa.” (1 Petro 3:17, NW) Kodi pakakhala ubwino wotani m’kubvutika kwa munthu monga mbala, wambanda, wozemba kukhoma msonkho kapena monga munthu amene amanyoza ulamuliro monamizira kukhala wopembedza Mulungu kapena changu chonyengezera? Kulangidwa kwake kaamba ka zimenezi kukangodzetsa chitonzo pa iye mwini ndi okhulupirira anzake. Koma Mkristu womapirira modekha kuchitiridwa moipa mosakuyenerera angathe kuchititsa ena kugwidwa mtima ndi mphamvu yopatsa nyonga imene imachirikiza olambira oona ndipo kuleketsa zonamizira chowonadi cha Mulungu ndi ochichirikiza ake. Popeza kuti kubvutika kumene kumagwera Mkristu kumadza pa iye mololedwa ndi Mulungu, Petro sanali kunena zinthu monama koma ananena moyenera kuti “ngati chifuniro cha Mulungu chifuna kutero.”
NJIRA YOPINDULITSA MONGA MOMWE KWASONYEZEDWERA M’CHOCHITIKA CHA YESU
31. Kodi ndi motani mmene kupirira mokhulupirika kwa Yesu Kristu pobvutika kunapindulitsira?
31 Chakuti kupirira kokhulupirika pobvutika kungathe kutsogolera ku madalitso akulu kwa Mkristu chikusonyezedwa bwino lomwe m’chochitika cha Yesu Kristu. Pokhala wopanda uchimo, iye sanachite kanthu kali konse koyenera kuchitiridwa nako moipa. Komabe kupirira kwake posautsidwa, ndipo potsirizira pake kufa imfa yochititsa manyazi pa mtengo, kunachititsa mapindu akulu kwambiri kwa ife ndipo kunachititsa kufupidwa kwake kwambiri. Mtumwi Petro analemba kuti:
“Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu; m’menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m’ndende, imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalawa, m’menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.”—1 Petro 3:18-20.
32. Kodi ndi motani m’mene ife tapindulira ndi kupirira kwa Kristu pobvutika mpaka kufika pa imfa?
32 Chinali chifukwa chakuti Yesu Kristu anasunga umphumphu wopanda cholakwa pobvutika kuti iye anakhala wokhoza kupereka moyo wake monga nsembe yaumunthu yangwiro. Motero imfa yake inatsegula njira kwa anthu ‘yomkera kwa Mulungu,’ akumayanjanitsidwanso ndi Wam’mwambamwambayo ndi kuwaikira pamaso pawo chiyembekezo cha moyo wosatha. Polingalira za kukhala kwathu titapindula kwambiri ndi kufa kwa Kristu kaamba ka ife, kodi ife sitiyenera kukhala ofunitsitsa kutsatira chitsanzo chake ndi kubvutikira chilungamo?
33. Kodi chiukiriro cha Yesu Kristu chiyenera kukhala chitsimikiziritso cha chiyani kwa ife pamene tikukumana ndi chiopsezo cha imfa chifukwa kukhala ophunzira ake?
33 Ndiponso, monga momwe zinaliri m’chochitika chake, tingathe kukhala ndi chitsimikiziro chakuti kupirira kwathu kokhulupirika kudzadalitsidwa. Chenicheni chakuti Yesu Kristu ‘anakhalitsidwa wamoyo mumzimu’ kapena anaukitsidwira ku moyo wauzimu chikukhala monga chitsimikiriziro chosasinthika chakuti ophunzira ake adzakhalitsidwanso moyo.—1 Akorinto 15:12-22.
34. Chifukwa cha mbiri yake ya kukhulupirika, kodi Yesu Kristu anali wokhoza kuchitanji mogwirizana ndi mizimu yoipa?
34 Chifukwa chakuti iye anatuluka ali wopambana mwa chipiriro chokhulupirika, Mwana wa Mulungu, monga munthu wauzimu, anali wokhoza kulengeza uthenga wachiweruzo kwa “mizimu inali m’ndende.” Popeza kuti kusamvera kwa mizimu imeneyi kukugwirizanitsidwa ndi nthawi ya Nowa, iwo ayenera kukhala ana a Mulungu aungelo amene anasiya malo ao oyambirira kumwamba nayamba kukhala ndi akazi monga amuna okwatira. (Genesis 6:1-4) Iwo akunenedwa kukhala “mizimu inali m’ndende” chifukwa chakuti chilango chawo chinaphatikizamo mpangidwe wa kuletsedwa, kuletsedwa kwamuyaya ku malo ao oyambirira pakati pa angelo okhulupirika. Mawu a Yuda amatsimikizira kuti uthenga wa chiweruzo chachitsutso wokha ungathe kulunjikitsidwa kwa angelo akugwa amenewa: “Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, [Mulungu] adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.” (Yuda 6) Kunali kupirira kokhulupirika kwa Yesu kufikira imfa kumene kunamuyeneretsa kukhalitsidwanso moyo ndipo chotero kumuika mu mkhalidwe wa kulalikira kapena kulengeza chiweruzo chachitsutso choterocho kwa angelo akugwawo.
35. Kodi nchifukwa ninji chenicheni chonena za kulalikira chionongeko kwa Yesu kwa “mizimu inali mndende” kungatilimbikitse ife kupirira mokhulupirira?
35 Kulalikira chionongeko cha mizimu yoipa kumeneku kuyenera kutilimbikitsa kupirira mokhulupirika pamene tikumana ndi nsutso. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti makamu a mizimu yoipa oterowo kwakukulukulu ndiwo amene ali ndi thayo la kusonkhezera mtundu wa anthu wotalikirana ndi Mulunguwo kutsutsana ndi ophunzira a Yesu Kristu. Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu wa dongosolo iri la zinthu wachititsa khungu maganizo a osakhulupirira, kuti kuunika kwa mbiri yabwino yaulemerero yonena za Kristu, amene ali chifanefane cha Mulungu, kusawawalire.” (2 Akorinto 4:4, NW) “Ife [Akristu] tiri ndi nkhondo, osati yolimbana ndi mwazi ndi thupi, koma yolimbana ndi maboma, yolimbana ndi maulamuliro yolimbana ndi olamulira a dziko a mdima uno, yolimbana ndi makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba.” (Aefeso 6:12, NW; onaninso Chibvumbulutso 16:13, 14.) Chotero, chenicheni chakuti Yesu Kristu woukitsidwayo akanatha kulalikira uthenga wotsutsa mizimu yoipa chikupereka chitsimikiziritso chakuti, potsirizira pake, chisonkhezero chawo chaudani chidzathesedwa kotheratu. (Yerekezerani ndi Marko 1:23, 24.) Ha, ndi mpumulo wodabwitsa chotani nanga m’mene zimenezi zidzakhalira!
36. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu anafupidwira chifukwa cha kukhulupirira kwake? (b) Polingalira udindo wa Yesu, kodi ndi motani m’mene tiyenera kulingalirira ponena za kubvutika kaamba ka dzina lake?
36 Kuphatikiza pa kukhala woukitsidwa kuchokera kwa akufa monga mtumiki wobvomerezedwa wa Mulungu ndipo motero kutheketsedwa kulunjikitsa uthenga wa chiweruzo wotsutsa angelo osamverawo, Yesu Kristu anakwezedwa kwambiri. Mtumwi Petro akutiuza kuti: “Amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m’Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.” (1 Petro 3:22) Mawu onenedwawa akugwirizana ndi mawu a Yesu mwini pambuyo pa chiukiriro chake kuchokera kwa akufa: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi.” (Mateyu 28:18, NW) Anthu ambiri akhala ofunitsitsa kubvutika ndipo ngakhala kutaya moyo weniweniwo ali mu utumiki wotumikira wolamulira waumunthu amene anali ndi ulamuliro wochepera kwambiri. Iwo amakulingalira kukhala ulemu waukulu kutumikira mfumu ina kapena Mfumu yaikazi mwa njira imeneyi. Kodi ndi mokulira chotani m’mene ife tiyenera kuonera kukhala olemekezedwa chifukwa cha kukhala okhoza kubvutika chifukwa cha kukhala okhulupirika kwa Mfumu yathu yakumwambayo, Yesu Kristu!
TSANZIRANI YESU KRISTU
37. Kodi ndi chitsanzo cha yani chimene ife tiyenera kufunafuna kuchitsanzira pokumana ndi nsautso?
37 Pamenepotu, pobvutika, nthawi zonse yang’anani kwa Mwana wa Mulungu monga chitsanzo chanu. Mtumwiyo akulemba kuti: “Popeza kuti Kristu anabvutika m’thupi, nanunso dzikonzereni kaimidwe ka maganizo kofananako; chifukwa chakuti munthu amene wabvutika m’thupi walekana nalo tchimo, ndi cholinga chakuti akakhale ndi moyo nthawi yake yotsalirayo m’thupi, osatinso kaamba ka zilakolako za anthu, koma kaamba ka chifuniro cha Mulungu.”—1 Petro 4:1, 2, NW.
38. Kodi kaimidwe ka maganizo ka Yesu Kristu kanali kotani?
38 Kodi kaimidwe ka maganizo ka Yesu kanali kotani? Iye modzichepetsa anadzigonjetsera ku kusautsidwa pathupi ndi kutukwanidwa zounjikidwa pa iye, potsirizira pake kufa imfa yopweteka ya pa mtengo wozunzirapo. Mwa kusabwezera kwake mofananamo, Mwana wa Mulungu anakwaniritsa mawu olosera awa: “Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga, Kotero sanatsegula pakamwa pake.”—Machitidwe 8:32, Yesaya 53:7.
39. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti ife tasiya machimo?
39 Ife atumiki a wammwambamwambayo tidzafuna kupirira mofananamo pobvutika, osagonjera ku mzimu wa kupanduka kapena kubwezera. Pakuti kwa ife kuopseza ozunza athu, kufunafuna mwai wa kuwabvulaza, kukatisonyeza kukhala tikali ogonjera ku zikhumbo za thupi lochimwa. Kubvutika kuli konse kumene tingakumane nako kochititsidwa ndi anthu kuyenera kotheratu kukhala chifukwa chakuti sitikutsatira njira yadyera ndi njira za dziko lino. (Yohane 15:19, 25) Motero ife tingathe kusonyeza kuti mu khalidwe, mawu ndi machitidwe, ife tikukhala ndi moyo, ‘osatinso kaamba ka zikhumbo za anthu koma kaamba ka chifuniro cha Mulungu.’
CHIFUKWA CHOKHALIRA ACHIMWEMWE
40. Kodi nchifukwa ninji kuyenera kukhala kutaonekera kukhala kwachilendo kwa okhulupirira a m’zaka za zana loyamba kulowa m’kubvutikira Kristu?
40 Kalelo m’zaka za zana loyamba C.E., anthu ochuluka olambira mafano sanakumane ndi kubvutika pa zifukwa za chipembedzo. Komabe, ali onse amene anakhala Akristu, anakhala odedwa. Kukhala ukuzunzidwa kunali chokumana nacho chachilendo, chodabwitsa. Kunali kosiyana kwambiri ndi madalitso amene kulandira “mbiri yabwino” kunawapatsa. Akristu amenewo anafuna kwambiri lingaliro loyenera la kubvutika. Mawu otsatirapo a mtumwi Petro analidi otonthoza kwa iwo:
“Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zake, kondwerani; kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu. Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.”—1 Petro 4:12-14.
41, 42. (a) Mogwirizana ndi 1 Petro 4:12-14, kodi ndi motani m’mene tiyenera kulingalirira kubvutikira chilungamo? (b) Kodi kubvutika koteroko kumatsimikiziranji?
41 M’malo mwa kulingalira modabwa kapena mwachikakasi kubvutika kumene kungatigwere, tingachione kukhala kutikonzekeretsa kukhala ndi phande m’madalitso amene adzalandiridwa pa bvumbulutso la Mbuye wathu. Petro anatchula za kubvutika kukhala kubvutika ‘kwamoto,’ popeza kuti zitsulo zimayengedwa ndi moto. Mofananamo, Mulungu amalola atumiki ake kuyengedwa kapena kuyeretsedwa kupyolera mwa zisautso zimene iwo amakumana nazo. Ndithudi, Yehova Mulungu sanatipange ife kukhala ochimwa. Koma, popeza kuti ife ndife, ochimwa, iye angatilole kukumana ndi kubvutika kwina monga njira imodzi yotiyeretsera. Kubvutika kumene ife tingakumane nako kungatithandize kukhala okoma mtima kwambiri, kukhala odzichepetsa kwambiri, kukhala omvera chisoni kwambiri ndi omvetsetsa m’kuchita ndi anthu anzathu. Ndiponso, pamene ife enife tapirira ziyeso zazikulu, mawu athu a chitonthozo ndi chilimbikitso kwa ena amakhala olemerera kwambiri. Awo amene tikuwatonthoza amadziwa kuti tikumvetsetsa zimene iwo akukumana nazo.
42 Popeza kuti Mwana wa Mulungu anabvutika, zobvuta zimene ife tikukumana nazo ziri chotsimikiziritsa kuti ife tiridi ophunzira ake, omasangalala ndi umodzi limodzi naye. Yesu anati kwa atumwi ake: “Kumbukirani mawu amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilonda Ine, adzalondalonda inunso.” (Yohane 15:20) Mwa kuzunzidwa kaamba ka zifukwa zofananazo ndi za Mbuye wathu ndi kukumana ndi nsautso kaamba ka chilungamo monga momwe anachitira iye, ‘tikukhala ndi phande m’kubvutika kwa Kristu.’ Ndipo monga momwe kuliri kuti kukhulupirika kwake kunatsogolera ku kufupidwa kwake ndi Atate wake wakumwamba, kukhulupirika kwathu kopitirizabe m’kupirira mu nsautso kumatitsimikiziritsa za kukhala obvomerezeka pa bvumbulutso la Mwana wa Mulungu. Ndithudi chisangalalo chathu chidzakhala chachikulu pa kupatsidwa kwathu pa nthawiyo moyo wopanda mapeto m’dongosolo latsopano kumene zonse zochititsa zisoni ziripozi sizidzakhalakonso.
43. Kodi kupirira mokhulupirika pobvutika kumatsimikizira kuti tiri ndi mzimu wotani pa ife, ndipo chifukwa ninji?
43 Monga momwe Petro nayenso anafotokozera, kusenza chitonzo kaamba ka dzina la Kristu, ndiko kuti, chifukwa cha kukhala ophunzira ake, kuyenera kukhala kochititsa chimwemwe. Kumatsimikizira kuti awo otonzedwa moterowo kapena kunyozedwa ali ndi mzimu wa Mulungu kapena “mzimu wa ulemerero” wolemekezeka umene umachokera kwa Mulungu. Pokhala woyera, mzimu umenewo ungathe kukhala kokha pa anthu amene ali oyera kapena opanda uchisi mwa lingaliro la Mulungu.
44. Kodi ndi mtundu wotani wa kubvutika umene tiyenera kupewa?
44 Ndicho chifukwa chake kuli kofunika kwambiri kuti titsimikizire kuti kubvutika kuli konse kotigwera sikunganenedwe kukhala kochititsidwa ndi kachitidwe kolakwa ku mbali yathu. Mtumwi Petro akufulumiza kuti: “Komabe, ali yense wa inu asabvutike monga wakupha munthu kapena mbala kapena wochita zoipa kapena wolowerera m’nkhani za ena.”—1 Petro 4:15, NW.
45. Kodi nchiyani chimene chimatulukapo pamene wodzitcha kukhala Mkristu abvutikira upandu?
45 Munthu amene amadzinenera kukhala Mkristu ndi amene akhala ndi liwongo la upandu kwa munthu mnzake sangayembekezere kusalandira chilango. (Yerekezerani ndi Machitidwe 25:11.) Chilango chimenecho chidzadzetsa chitonzo pa iye mwini, mpingo umene amagwirizana nawo ndi dzina la Kristu. Iye samapeza chisangalalo chiri chonse, koma manyazi.
46. (a) Kodi kulowerera m’za ena nkutani? (b) Kodi ndi motani m’mene Mkristu angabvutikire monga wolowerera m’za ena?
46 Kulowerera m’nkhani za anthu ena kungathe kuchititsa munthu kukhala wodedwa. M’mene munthu amakhalira wolowerera kukusonyezedwa ndi liwu Lachigriki lotembenuzidwa kukhala “kulowerera” limene Petro analigwiritsira ntchito. Kwenikweni limatanthauza “woyang’anira chimene chiri cha munthu wina.” Mwina mwake chifukwa cha kukhala atapeza chidziwitso Chamalemba, Mkristu tsopano angaone tsopano kukhala woyeneretsedwa kuuza ena anthu a dziko m’mene angayendetsere zinthu zawo za iwo eni. Iye angaumirize malingaliro ake a iye mwini onena za miyezo ya kabvalidwe, kulanga ana, kuchita ndi ukwati ndi zobvuta za kugonana, zosangalatsa, chakudya ndi zina zofanana nazo. Pamene iye adzilowetsa iye mwini, osapemphedwa, m’zobvuta za munthu mwini za ena, akumawauza zimene iwo angachite kapena kusachita, iye akuyesa kukhala “wonyang’anira” wa zinthu zao. Kumeneku kawirikawiri kumakumana ndi kuipidwa. Wolowerera m’nkhani za enayo angauzidwe mwa mawu osakhuluwika kusamalira zinthu za iye mwini. Iye angakumanedi ndi kuchitiridwa moipa mwakuthupi kuchokera kwa anthu amene akuchita mokwiya ndi kulowerera kwake m’miyoyo yao yamtseri. Wolowerera m’nkhani za ena amene amayesa kufufuzafufuza m’nkhani zimene ziribe kanthu ndi iye amadzitengera bvuto pamtu pake pa iye mwini ndipo amaimira molakwa Chikristu ndi uthenga wake kwa akunja. Ndithudi, ngakhale mu mpingo, mulibe malo a olowerera m’nkhani za ena.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:13.
47. Kodi ndi motani m’mene kupirira kwa Mkristu pobvutika kungadzetsere ulemerero kwa Mulungu?
47 Mosemphana ndi manyazi a kubvumbulidwa poyera kukhala woswa lamulo kapena monga wolowerera m’zochitika za ena, kubvutika monga Mkristu kumadzetsa ulemu. Petro akulemba kuti: “Ngati iye abvutika monga Mkristu, asachite manyazi, koma apitirizetu kulemekeza Mulungu m’dzina limeneli.” (1 Petro 4:16, NW) Pamene nsautso igwera ifeyo chifukwa cha njira yathu Yachikristu, kupirira kwathu m’menemo modekha ndi mosandandaula kumadzetsa ulemerero kwa Wam’mwambamwambayo. Kumatsimikizira kuti zimene tiri nazo monga Akristu-unansi wamtengo wapatali ndi Mulungu ndi Kristu, chikumbu mtima choyera, thanzi lauzimu ndi chiyembekezo cholimba cha mtsogolo-ziri chuma chamtengo wapatali kwambiri. Timasonyeza kuti ife tiri ofunitsitsa kubvutika ndipo, ngati kuli kofunika, kuchifera, ndipo kumeneku kumalemekezetsa Mulungu amene ife mwaphamphu timamtumikira. Kugonjera ku chitsenderezo ndi kukana chikhulupiriro chathu, m’malo mwake, kukanyozetsa dzina lake. Kwa openyerera, kukachititsa kudzutsidwa kwa chikaikiro ponena za mtengo wosayerekezereka wa kukhala wophunzira wa Yesu Kristu. —Yerekezerani ndi Aefeso 3:13; 2 Akorinto 6:3-10.
MPANGIDWE WA CHILANGO KAPENA KUPHUNZITSA
48. Kodi ndi motani m’mene 1 Petro 4:17-19 amasonyezera kuti ife sitiri opanda chithandizo pamene tikukumana ndi bvuto kaamba ka chilungamo?
48 Taona kuti kubvutika mosayenera kwa Akristu kungathe kuletsedwa ndi Yehova Mulungu m’mphamvu yake yonseyo, koma kuti iye amakulola kaamba ka zifukwa zabwino. Pa nthawi ino, Wam’mwambamwambayo samasiya konse atumiki ake opanda chithandizo. M’kufotokoza mfundo imeneyi mtumwi Petro akulemba kuti:
“Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani? Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokha kokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti? Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m’manja mwa Wolenga wokhulupirika.”—1 Petro 4:17-19.
49. (a) Kodi “nyumba ya Mulungu” yakhala iri pa chiweruzo kuyambira liti? (b) Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kugamula kotsirizira kumene kudzaperekedwa?
49 Monga “nyumba ya Mulungu,” mpingo Wachikristu unayamba mu 33 C.E. Kuyambira pa nthawi imeneyo kumkabe mtsogolo ziwalo zake zakhala zikuweruzidwa ndi Mulungu. Kulabadira kwao ku chifuniro chake, ndi kaimidwe kao ka maganizo, mawu ndi machitidwe kulinga ku zinthu zimene Yehova Mulungu amalola kuwagwera kumakhala zochuluka ponena za chimene chidzakhala kugamula kotsirizira. Nthawi zina zimene Yehova Mulungu amaona kukhala zoyenera kuzilola kuti iwo akumane nazo zingakhale zopweteka kwambiri. Koma chizunzo chimadzetsa mpangidwe wa chilango chimene Mulungu angathe kuchichititsa kudzetsa phindu kwa anthu ake.—Ahebri 12:4-11; onaninso Ahebri 4:15, 16, kumene kukusonyezedwa kuti kubvutika kumene Yesu Kristu anakumana nako kunamkonzekeretsa kukhala mkulu wa ansembe womvera chisoni ndi wachifundo.
50, 51. Kodi ndi motani mmene zokumana nazo za Yosefe ndi Paulo zimasonyezera kuti Yehova angathe kusintha kukhala dalitso chinthu chenichenicho chimene anthu angachigwiritsire ntchito m’kuyesayesa kutibvulaza?
50 Mwa kuchitira moipa, anthu okhala pansi pa uyang’aniro wa Satana angayese kuononga chikhulupiriro chathu. Koma Yehova angathe kulepheretsa cholinga chawo choipacho. Inde, pamene kuli kwakuti iye mwiniyo amada choipa, atate wathu wakumwamba angathe kuchititsa chimene chalinganizidwa kutibvulaza kutulutsa zotulukapo zina zabwino. Tatengani chochitika cha mwana wamwamuna wamng’ono wa Yakobo Yosefe. Abale ake a mai wina anamda namgulitsa kukhala kapolo. Kwa zaka zambiri, Yosefe anabvutika kwambiri, kuphatikizamo kuikidwa m’ndende mosayenera. Komabe, pambuyo pake, Yehova Mulungu, anagwiritsira ntchito mkhalidwe umenewo kusunga lamoyo banja la Yakobo. Ponena za zimenezi, Yosefe anauza abale ake a mai winawo kuti:
“Tsopano musapwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo. Zaka ziwiri muli njala m’dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga. Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m’dziko lapansi. Ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikulu. Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Fararo, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto.”—Genesis 45:5-8.
51 Mofananamo, pamene mtumwi Paulo anadzipeza iye mwini atabindikiritsidwa pa Roma, mkhalidwe wosayenera umenewu unatumikira kupititsa patsogolo njira ya kulambira kowona. M’kalata yake yomka kwa Afilipi, iye analemba kuti:
“Tsopano ndikufuna kukutsimikizirani, abale, kuti zimene zinandichitikira zachititsadi kupititsidwa patsogolo kwa kulalikidwa kwa mbiri yabwino. Kotero kuti zadziwika kwa Asilikali onse Olonda mfumu ndi kwina kuli konse kuti chiri chifukwa cha Kristu kuti ine ndiri m’ndende, ndipo chotero ochuluka a abale Achikristu alimbikitsidwa kopambanadi ndi chitsanzo changa cha kulengeza uthenga wa Mulungu mopanda mantha a zotulukapo.”—Afilipi 1:12-14, An American Translation, 1944 edition.
52. Kodi nchifukwa ninji “munthu wosapembedza ndi wochimwa” sangayembekezere kudzionetsa?
52 Popeza kuti Yehova Mulungu amalola atumiki ake okhulupirika kukumana ndi kubvutika kwambiri kuti awayeretse ndi kuti iwo asonyeze kudzipereka kwao, kodi ndi motani m’mene tigayerekezererere kuti ‘munthu wosapembedza ndi wochimwa’ mu mpingo Wachikristu kapena “nyumba ya Mulungu” akaonekeramo’ pamaso Pake limodzi ndi “munthu wolungama” mu mpingo umodzimodziwo? Wamasalmo akufotokoza kuti: “Oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.” (Salmo 1:5) Ayi, oipa sadzaimirira monga obvomerezedwa koma adzatsutsidwa. Iwo angapezeke mu msonkhano wa olungama, koma iwo ‘sadzaonekera’ konse mwachiyanjo pamaso pa Mulungu. Chifuwa cha zimene okhulupirira onse ayenera kukumana nazo m’dziko lino, kupulumutsidwa kwao kotsirizira kaamba ka moyo wosatha kumafunikira kuyesayesa kwenikweni, chikondi ndi chikhulupiriro m’njira ya chilungamo. Chifukwa cha chimenecho, chipulumutso chao chiri “limodzi ndi kubvutika.” Chifukwa cha chimenecho kuli koyenera kwa ziwalo zonse za mpingo Wachikristu (“nyumba ya Mulungu”) kupewa kukhala “osapembedza” ndi “ochimwa” m’nthawi yoikika’ ya chiweruzo imeneyi.—1 Petro 4:17, 18; Miyambo 11:31.
53. (a) Pokumana ndi kubvutika, kodi ndi chitonthozo chotani chimene tingapeze kuchokera ku chenicheni chakuti Yehova ali “Wolenga wokhulupirika” ? (b) Kodi ndimotani m’mene tiyenera kuchitira kwa ozunza athu?
53 Ziyeso zimene sitingathe kuzipirira mwa nyonga ya ife eni zingatigwere. Komabe, ziribe kanthu kuti mkhalidwe wathu wafikira kukhala womvetsa chisoni chotani, Yehova Mulungu angathe kutilimbikitsa ndi kuchotsa chibvulazo chonse chimene ife tingakumane nacho. Pamene tidzipereka ife eni kwa iye motheratu, iye angathe kulimbikitsa mwa njira ya mzimu wake kupirira pobvutika. Pokhala, monga momwe Petro akulongosolera, “Wolenga wokhulupirika,” Mulungu amene ife tingathe kumkhulupirira, iye sadzatsimikizira kukhala wosakhulupirika ku lonjezo lake la kuthandiza atumiki ake. (1 Petro 4:19) Chidziwitso chimenechi chingathe kutithandiza kupewa kuchita m’njira yonyozetsa Mulungu kwa ozunza athu. M’malo mwa kumenyana nawo, kubwereza mofanana, tidzafuna kupitirizabe kuchita zabwino.—Luka 6:27, 28.
54. Kodi ndi motani m’mene timadzichepetsera ife eni pansi pa dzanja la Mulungu, ndipo kodi ndi motani m’mene kumeneku kumatipindulitsira?
54 Ngati tidzipereka modzichepetsa ku chimene chingatigwere, kusunga mkhalidwe wonga wa Kristu, tingathe kukhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzatikweza. Palibe chiyeso chimene chidzapitirizabe kosatha. Chidzakhala ndi mapeto. Malinga ngati ife tidzisungira ife eni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu pamene tikuchitiridwa moipa, timapitirizabe kukhala m’dzanja la Yehova. Ndipo dzanja limenelo lingathe kutinyamula, likumatikweza monga obvomerezedwa ake, atumiki oyesedwa. Zimenezi ndizo zimene mtumwi Petro akunena kuti ndi zabwino: “Dzichepetseni, chifukwa cha chimenecho, pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti iye akukwezeni m’nthawi yokwanira; pamene mukuponyera nkhawa zanu zonse pa iye, chifukwa chakuti iye amakusamalirani.”—1 Petro 5:6, 7, NW.
55. Ngakhale kuli kwakuti sitingathe kuthawa ziyeso, kodi ife tingadzimasule ife eni ku chiyani, ndipo motani?
55 Ha, ndi kolimbikitsa chotani nanga m’mene kuliri kudziwa kuti Yehova mowona mtima amatisamalira! Chikondi chake chimakondweretsa mitima yathu; mzimu wake umatipatsa nyonga ndi kutilimbikitsa. Pamenepo, pamene chiyeso chakutichakuti chitha ndipo ife tikuyang’ana mmbuyo pa chikondi chokoma mtima cha Yehova, ife timachititsidwa kudza pafupi kwambiri ndi iye. Mkhalidwewo uli wofanana ndi uja wa mwana woyamikira amene waona chikondi ndi chisamaliro cha makolo odera nkhawa m’nthawi ya kudwala kwambiri. Chidaliro chake ndi chikondi zimalimbikitisidwa kwambiri. Zowona, pamene mikhalidwe iri yobvuta kwambiri, sitingangoithawa. Koma tingathe kutula nkhawa zathu kapena kubvutika maganizo pa Yehova Mulungu. Sititofunikira kuda nkhawa ponena za kutalika kwa nthawi imene tingakhale okhoza kupirira kumenyedwa mwankhanza ndi gulu lachiwawa lokwiya, ziukiro za chigololo chogwirira zochitidwa ndi oukira, kapena nkhanza zina. Mwa chitandizo cha Atate wathu wachikondi wa kumwamba, ife tingathe kupirira ndi kupeza chipambano cha makhalidwe pa ozunza athuwo mwa kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu wathu. Chitsimikiziro chimenechi chimatichotsera nkhawa zimene zikatichotsera mtendere wa maganizo ndi mtima umene uli wofunika kwambiri m’kukhalabe kwathu oima nji pokumana ndi ziyeso.
56. Kodi nchifukwa ninji kutula nkhawa zathu pa Yehova sikumatanthauza kuti ife tingathe kukhala osadera nkhawa ndi kachitidwe kathu ku ziyeso?
56 Komabe, zimenezi sizikuthanthauza kuti, mwa kuponyera nkhawa zathu pa Yehova, ife tsopano tingathe kukhala amphwayi kapena onyalanyaza. Tiri ndi mdani. “Khalani odzisungira dikirani,” analemba motero Petro. “Mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”—1 Petro 5:8.
57. Kodi Satana ali wokondweretsedwa kuchitanji?
57 Mogwirizana ndi uphungu wa mtumwiyo, siti ngathe kukhala osasamala polumana ndi masautso. Mdaniyo akungoyembekezera mpata woti atichititse kugwa. Ngati Satana angathe kutipangitsa kukaikira kukhulupirika kwa abale athu kapena mwa njira ina kutifooketsa mwauzimu, iye adzatero. Kwa ife kuleka kusonkhana ndi mpingo Wachikristu kapena kuleka kunena mawu osonyeza chikhulupiriro chathu kwa ena kukatanthauza kumezedwa ndi Satana, “mkango wobuma” umene uli wopenyetsetsa nyama yoti ilikwiridwe yosachenjera.
58. Kodi ndi chidziwitso chotani ponena za abale athu chimene chingatithandize kukhala okhulupirika?
58 Kuti tisungebe kukhala maso kwathu, kukatithandiza kukumbukira nthawi zonse kuti sitiri tokha m’kupirira kubvutika. Pa dziko abale athu Achikristu akupirira mitundu yosiyanasiyana ya nsautso. Ndipo, mwa chithandizo cha mzimu wa Mulungu, iwo akupambana m’kupirira mokhulupirika ziyeso. Kuzindikira kumeneku kungathandize kupewa kugwera m’kungwidwa ndi misampha ya Satana, pakuti kumatipatsa chidaliro chakuti ifenso tingathe kupirira mwa nyonga ya Yehova. Chotero, pamenepa, “ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zirimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.”—1 Petro 5:9.
59, 60. Kodi ndi motani m’mene tingapezere mapindu akulu kopambana m’ziyeso zathu?
59 Popeza kuti Yehova Mulungu amafuna kuti ife tipambane ndi kupeza chipulumutso, mwachidaliro tingayangane kwa iye kaamba ka chithandizo. Pa nthawi imodzimodziyo, tingalandire chiri chonse chimene chingatigwere mwa chilolezo cha Mulungu monga chilango cha mtengo wapatali chotipangitsa kukhala achikwanekwane, Akristu okula mokwanira, amphamvu m’chikhulupiriro. Mtumwi Petro mokondweretsa anafotokoza, motere:
“Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Kristu mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chirema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. Kwa Iye kukhale mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.”—1 Petro 5:10, 11.
60 Monga momwe kuliridi kuti Yesu anabvutika kwakanthawi pamene anali pa dziko lapansi ndiyeno iye anakwezedwa kwambiri, momwemo ophunzira a Mwana wa Mulungu akuyembekezera mfupo yaulemerero. Ngati kubvutika kumene kungatigwere mwa kulola kwa Mulungu kutipangitsa kukhala amphamvu kwambiri m’kulabadira kwathu ku miyezo ya Baibulo, ndi ophunzira a Mwana wa Mulungu odzichepetsa kwambiri, omvera chifundo ndi omvera chisoni kwambiri, mpangidwe umenewu wa kuphunzitsidwa kapena kuumbidwa udzakhala utachita chifuno chake. Kuti zikhalire mmenemo, tifunikira kudalira Atate wathu wakumwamba mokwanira, tiri ndi chidaliro chakuti chiri chonse chimene iye amachilola kudza potsirizira pake chidzachititsa ubwino wathu wamuyaya ndi chimwemwe ngati ife modzichepetsa tichibvomereza. (Aroma 8:28) Mu mzimu wa mtumwi Petro, tingathe kukweza mawu athu, kunena kuti: ‘Chithokozo kwa Mulungu kaamba ka kutilola kuphunzitsidwa ndi ziyeso ndi kutithandiza kukhala olimba nji ndi amphamvu monga atumiki ake obvomerezeka ndi kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha!’