Kodi N’chifukwa Ninji Munthu Amafa?
8 Yehova anafuna kuti munthu apange dziko lonse lapansi kukhala lokongola—paradaiso kuti onse asangalale nalo.—Genesis 1:28
Anthuwo akanatha kukhala ndi moyo kosatha akadakhala kuti Adamu ndi Hava adamvera Yehova. Iwo anauzidwa kusadya za mumtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.—Genesis 2:15-17
9 Mngelo wina anakhala woipa nagwiritsira ntchito chinjoka kuchititsa Hava ndi Adamu kusamvera Mulungu.—Genesis 3:1-6
10 Mngelo amene ananyenga Hava anayamba kutchedwa ‘njoka yokalambayo, Mdierekezi ndi Satana.’—Chivumbulutso 12:9
11 Yehova anathamangitsa m’paradaiso aŵiri osamverawo.—Genesis 3:23, 24
12 Adamu ndi Hava anabala ana, koma banja lonse silinali lokondwa.—Genesis 3:17, 18
13 Iwo anayenera kukalamba ndi kufa, monga momwe Yehova anali atanenera.—Genesis 3:19; Aroma 5:12
14 Chotero iwo anafa mofanana ndi nyama.
Miyoyo yonse pa dziko lapansi imafa.—Mlaliki 3:18-20; Ezekieli 18:4