Boma Lakumwamba Lidzetsa Madalitso pa Dziko Lapansi
41 Yehova anapanga Yesu kukhala Mfumu kumwamba.—Yesaya 9:6; Danieli 7:13, 14; Machitidwe 2:32-36
42 Iye adzalamulira pa dziko lonse lapansi.—Danieli 7:14; Mateyu 28:18
43 Kodi mukukumbukira chimene chidzachitikira anthu oipa?—Salmo 37:9, 10; Luka 13:5
44 Kodi mukukumbukira dzina la mngelo woyambirira amene anachimwa? Yesu adzam’chotsa ndi angelo ena oipa. Mafano awo ndi zifanizo zidzawonongedwa.—Ahebri 2:14; Chivumbulutso 20:2, 10
45 Yesu adzachita zinthu zambiri zabwino kwa anthu omvera.—Ahebri 5:9
46 Palibe aliyense amene adzadwalanso.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 22:1, 2
Kodi mukukumbukira mmene Yesu anachiritsira anthu odwala?
47 Aliyense adzakhala ndi zinthu zabwino.—Yesaya 65:17, 21-23
48 Mulungu amakumbukira ngakhale anthu amene afa. Iye adzagwiritsira ntchito Yesu kuwadzutsira ku moyo kachiŵirinso. Kumeneku kumatchedwa chiukiriro.—Yohane 5:28, 29; 11:25
49 Anthu onse oipa ataphedwa, palibe amene adzafanso. Ngakhale nyama zakuthengo sizidzakhala zoopsa. Aliyense adzakhala wachimwemwe kosatha.—Chivumbulutso 21:4; Yesaya 65:25; Salmo 37:11, 29