Nyimbo 50
Kuyankha Chikondi cha Mulungu
1. Inu ndinu Mulungu; Timkonda mtima wonse
Yehova wotamandikanu.
Titama dzina lanu, Mawu anu mwa zimene
tiphunzira njira zanu.
Musonyeza chifundo, Muchita molungama;
Musonyeza mphamvu ndi nzeru.
Tidziŵa kuti tikakhala owona mtima,
Mudzatipatsa madalitso.
2. Munatikonda ife; Nafe tikukondani
Inu kuchokera mumtima.
Kuyeretsa dzinalo, Kuvumbula chikondi chanu,
Kristu ’nadza ndi moyo.
Palibenso chikondi Kuti wina apatsa
Moyo wake mongatu nsembe.
Kuti ife tisawonongeke timamvera
Uphungu ndi chilangizocho.
3. Sitidzapatutsidwa Pautumiki wathu;
Tidzanenabe chowonadi.
Mwautumiki wathu Tidzamkabe tikwanitsa
chikondi kwa anthu onse.
Pakumatumikira Chikondano chathuchi
Chivumbula otsata Kristu.
Zinthutu zake za Ufumu tisamalira;
Poyembekezera lonjezo.