Nyimbo 57
Anthu Achimwemwe a Yehova
1. Achimwemwe ndi odziŵatu lipenga,
Odziŵa cho’nadi, Adzadalitsidwa.
Adzayendabe mukuunika kwa inu;
Apeza chimwemwe potumikira.
(Korasi)
2. Makamu a Satana apondereza;
Ntchito zichuluke; Thamo limveketu.
M’lungu wakonza pothaŵirapo ofatsa;
Ateteza ofuna chilungamo.
(Korasi)
3. Popatuka ena tisataye mtima.
Ngakhale akana, Tidzakhala maso.
Tipiriretu pomasonyeza umphumphu;
Popeza M’lungu amayamikira.
(KORASi)
Chifundo chanu, muchisonyeza
Kwa olengezabe dzina lanulo.
Mwa Mawu anu awona cho’nadi,
Asonyeza chikhulupiriro.