Nyimbo 114
Chikondi cha Mulungu Chokhulupirika
1. M’lungu ndi chikondi.
Chimatikondweretsa.
Anatuma Mwanake,
Anapereka dipo,
Tipeze chilungamo,
Ndi moyo wamuyaya.
(Korasi)
2. M’lungu ndi chikondi.
Ntchitozo nza umboni.
Amatikonda ife,
Ufumu ndi wa Kristu
Kukwanitsa lumbiro.
Ufumuwo wabadwa.
(Korasi)
3. M’lungu ndi chikondi.
Natumiza mtendere.
Natipatsa ‘kapolo,’
Ndi kupatsidwa ntchito,
Yakudziŵitsa dzina,
La Yehova Mulungu.
(Korasi)
4. M’lungu ndi chikondi.
Tisonyeze chikondi.
Ndi kuthandiza ena,
Kupeza chilungamo.
Tilalike ponsepo,
Chitonthozo padziko.
(KORASI)
Inu nonse aludzu,
Idzani mudzamwetu,
Madziwo kwaulere;
Chifundo cha M’lungu.