Nyimbo 154
Yehova, Mlengi Wathu
1. Yehova Mfumu anapanga dzikoli.
Anawapatsa anthu kukhalamo.
Angelo zikwizikwi anafuula
Mulungu atatha; linakongola.
2. Dzikoli lidzakhala Paradaiso.
Ndicho chifuno chake cha Yehova.
Tchimo linayamba ndi kupandukira.
Lidzatha mwamsanga; timakondwera.
3. Kudza kwa Ufumu kudzakonza zinthu.
Timayembe kezeradi nthaŵiyo.
Mokondwera timalengeza mbiriyo,
Kuŵalitsira anthu chowonadi.
4. Tiyang’ana kwa Yehova mwachikondi,
Ndiye Mlengi wathu, wotamandidwa.
Anapangira anthu zonse mwanzeru!
Timtame timtumikire ndi mtima.