Nyimbo 167
Tiyamika Wotipatsa Moyo
1. Zikomodi Ya wakumwambanu.
Tingachitenji kukutamani?
Mosamalitsatitsate Kristu,
Titukulira manja m’mwambamo.
2. Tiri okondwa Mfumu yosatha;
M’mwamba ndi dziko zitumikira.
Tisiya zonse tirinazozi,
M’kulambiridwa, ndi malamulo.
3. Munakhazika Ufumu wanu;
Tiri nanu unansi wabwino.
Tidikiranu nzeru yanuyo,
Kutitu ife tilambire’nu.
4. Titumikenu mosangalala,
Tidziŵitse chowonadi chanu.
Dalitsanitu zochita zathu,
Mzimu wanuwo utilimbitse.